Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZIMENE MUNGACITE PA KUŴELENGA KWANU

Anthu Okhulupilika Amasunga Malonjezo Awo

Anthu Okhulupilika Amasunga Malonjezo Awo

Ŵelengani Oweruza 11:30-40 kuti muphunzile ku cocitika ca Yefita na mwana wake wamkazi pa nkhani yosunga malonjezo.

Mvetsani nkhani yonse. Kodi Aisiraeli okhulupilika anali kuwaona bwanji malonjezo awo kwa Yehova? (Num. 30:2) Kodi Yefita na mwana wake wamkazi, anaonetsa bwanji kuti anali na cikhulupililo mwa Yehova?​—Ower. 11:9-11, 19-24, 36.

Kumbani mozamilapo. Kodi Yefita analonjeza ciyani kwa Yehova? Nanga anatanthauza ciyani pamene anapanga lonjezolo? (w16.04 7 ¶12) Ni zinthu ziti zimene Yefita na mwana wake anadzimana kuti akwanilitse lonjezo lake? (w16.04 7-8 ¶14-16) Kodi ni malonjezo otani amene Akhristu angapange masiku ano?​—w17.04 5-8 ¶10-19.

Onani zimene muphunzilapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘N’ciyani cinganithandize kusunga lonjezo langa la kudzipatulila?’ (w20.03 13 ¶20)

  • ‘Kodi ningadzimane zinthu ziti kuti nicite zambili potumikila Yehova?’

  • ‘N’ciyani cinganithandize kusunga lonjezo langa lokhalabe wokhulupilika kwa mnzanga wa mu ukwati?’ (Mat. 19:5, 6; Aef. 5:28-33)