Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 48

NYIMBO 97 Moyo Umadalila Mau a Mulungu

Kuculukitsa Mikate Mozizwitsa

Kuculukitsa Mikate Mozizwitsa

“Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa ine sadzamva njala.”​—YOH. 6:35, Buku Lopatulika.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kukambilana cocitika copezeka mu Yohane caputala 6 comwe cimafotokoza mmene Yesu anaculukitsila mikate na nsomba kuti khamu la anthu lidye. Ndipo tione zimene tiphunzilapo pa cocitika cimeneco.

1. Kodi mkate unali wofunika motani kwa anthu ochulidwa m’Baibo?

 MKATE unali cakudya ca masiku onse kwa anthu ambili ochulidwa m’Baibo. (Gen. 14:18; Luka 9:3) Cakudyaci cinali cofunika kwambili moti nthawi zina, Baibo imaseŵenzetsa mawu akuti “mkate” potanthauza cakudya cimene anthu amadya. (1 Maf. 17:11, 12) Yesu anaseŵenzetsa mkate m’zozizwitsa zake ziŵili zodziŵika pamene anaculukitsa cakudya. (Mat. 16:9, 10) Cimodzi mwa zocitika zimenezi cipezeka mu Yohane caputala 6. Pamene tikambilana nkhani imeneyi, tidzaona maphunzilo amene tingatengepo masiku ano.

2. Ni pa cocitika citi pamene anthu ambili anafunikila cakudya?

2 Ophunzila a Yesu atabwelako kumene anatumidwa kukalalikila, Yesu anawatenga pa ngalawa kudutsa nawo Nyanja ya Galileya kuti akapume. (Maliko 6:7, 30-32; Luka 9:10) Iwo anapita ku malo a kwaokha kufupi na mzinda wa Betsaida. Posakhalitsa, khamu la anthu lofika m’masauzande linafika kwa iwo. Yesu sanawanyalanyaze anthuwo. Mokoma mtima, iye anaseŵenzetsa nthawi yake kuwaphunzitsa za Ufumu komanso kucilitsa odwala. Koma cakumadzulo, ophunzila ake anayamba kudzifunsa za kumene angapeze cakudya cimene angadyetse khamu lonselo. N’kutheka kuti ena mwa anthuwo analiko na cakudya cocepa. Koma ambili a iwo anali kufunika kupita m’midzi kuti akagule cakudya coti adye. (Mat. 14:15; Yoh. 6:4, 5) Kodi Yesu akanacita ciyani?

KUCULUKITSA MIKATE MOZIZWITSA

3. Kodi Yesu anauza atumwi ake kuti awacitile ciyani anthuwo? (Onaninso cithunzi.)

3 Yesu anauza atumwi ake kuti: “[Anthuwa] safunika kucoka; inuyo muwapatse cakudya.” (Mat. 14:16) Zimenezi zinali kuoneka zosatheka cifukwa panali amuna pafupifupi 5,000. Ndipo kuŵelengela akazi na ana, n’kutheka kuti anthuwo anali kufika 15,000. (Mat. 14:21) Kenako Andireya, mmodzi wa atumwiwo anakamba kuti: “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balele ndi tinsomba tiŵili. Koma nanga zimenezi zingakwanile cigulu ca anthu conseci?” (Yoh. 6:9) Mkate wa balele unali cakudya cimene cinali kudyedwa kwambili na anthu osauka komanso anthu ena. Ndipo nsomba ziŵilizo ziyenela kuti zinali zothilidwa mcele komanso zouma. Komabe, cakudya cimene mnyamatayo anali naco cinali cocepa kwambili pociyelekezela na anthu amene analipo.

Yesu anasamalila zosoŵa zakuthupi komanso zakuuzimu za anthu (Onani ndime 3)


4. Kodi tingaphunzilepo ciyani pa Yohane 6:11-13? (Onaninso zithunzi.)

4 Yesu anafuna kuwaceleza anthuwo. Conco anawauza kuti akhale pansi m’magulu pa udzu wobiliŵila. (Maliko 6:39, 40; ŵelengani Yohane 6:11-13.) Kenako Yesu anayamikila Atate wake kaamba ka mkate na nsombazo. Panali poyenela kucita zimenezo cifukwa m’ceniceni, Mulungu ndiye anali Mpatsi wa cakudyaco. Citsanzo ca Yesu cimeneci citiphunzitsa phunzilo lofunika kwambili lakuti nthawi zonse tiyenela kupemphela tisanadye cakudya. Ndipo tiyenela kucita zimenezi kaya tili kwatokha kapena pagulu. Kenako Yesu anauza atumwi ake kuti agaŵile cakudyaco, ndipo anthuwo anadya na kukhuta. Panalinso zakudya zotsalila zimene Yesu sanafune kuti ziwonongeke. Conco, Yesu anauza ophunzila akewo kuti awonkhanitse cakudya cotsalaco kuti cikagwilitsidwe nchito pa nthawi ina. Yesu anatisiyila citsanzo cabwino pa nkhani yoseŵenzetsa zinthu zathu mwanzelu. Ngati ndinu kholo, mungaŵelengenso nkhani imeneyi na ana anu na kukambilana maphunzilo amene angatengepo pa nkhani ya kupemphela, kuceleza, komanso kuwolowa manja.

Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimatengela citsanzo ca Yesu copemphela nikalibe kuyamba kudya?’ (Onani ndime 4)


5. Kodi anthu anafuna kucita ciyani Yesu atawacitila cozizwitsa? Nanga iye anatani?

5 Anthu anali odabwa poona mmene Yesu anali kuphunzitsila komanso poona zozizwitsa zake. Anthuwo anali kudziŵa kuti Mose anakamba kuti Mulungu adzawaukitsila mneneli wapadela. Cotelo, n’kutheka kuti anthuwo anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi mneneli ameneyo ni Yesu?’ (Deut. 18:15-18) Ngati n’telo, n’kutheka kuti anthuwo anali kuona kuti Yesu angakhale wolamulila wabwino amene angathe kumapeleka cakudya kwa munthu aliyense mu Isiraeli. Conco, khamu la anthulo linafuna ‘kugwila [Yesu] kuti amuveke ufumu.’ (Yoh. 6:14, 15) Ngati Yesu akanalola zimenezi kucitika, ndiye kuti akanakhala kuti akutengako mbali m’ndale za Ayuda amene anali kulamulidwa na Aroma. Koma sanalole kuti zimenezi zicitike. Baibo imakamba kuti Yesu ‘anacoka n’kupita ku phili kwayekhayekha.’ Conco, ngakhale kuti ena anamukakamiza kutengamo mbali m’zandale, iye sanatelo. Pali phunzilo lofunika kwambili kwa ife pamenepa!

6. Tingacite ciyani kuti tionetse kuti tifuna kutengela citsanzo ca Yesu? (Onaninso cithunzi.)

6 N’zoona kuti ena sangatipemphe kuculukitsa cakudya, kucilitsa odwala mozizwitsa, kapena kutiika kuti tikhale wolamulila wawo. Koma iwo angatilimbikitse kutengako mbali m’zandale mwa kuvota, kapena kukamba mawu okhalila kumbuyo munthu winawake amene iwo aona kuti angasinthe zinthu. Komabe, citsanzo ca Yesu citionetsa bwino zimene tiyenela kucita. Iye anakana kutengamo mbali m’ndale za dzikoli moti pambuyo pake anafika pokamba kuti: “Ufumu wanga si wam’dzikoli.” (Yoh. 17:14; 18:36) Akhristu masiku ano ayenela kutengela kaganizidwe ka Yesu komanso kacitidwe kake ka zinthu. Monga mmene Yesu anacitila, nafenso timacilikiza Ufumu wa Mulungu, kuuzako ena za Ufumuwo, komanso kuupemphelela kuti ubwele. (Mat. 6:10) Tiyeni tibwelelenso ku cocitika cija cofotokoza pamene Yesu anaculukitsa mikate mozizwitsa na kuona zina zimene tingaphunzilepo.

Yesu anapeleka citsanzo kwa ophunzila ake kuti sayenela kutengako mbali m’zandale monga mmene iye anacitila (Onani ndime 6)


“TANTHAUZO LA COZIZWITSA CA MITANDA YA MKATE”

7. Kodi Yesu anacita ciyani? Nanga kodi atumwi ake anacita ciyani? (Yohane 6:16-20)

7 Pambuyo podyetsa khamu la anthu lija, Yesu na atumwi ake anacoka pa malowo na kubwelela ku Kaperenao pabwato. Kenako iye anapita ku phili. Anatelo pofuna kupewa kuti khamu la anthulo lisamulonge ufumu. (Ŵelengani Yohane 6:16-20.) Pamene atumwiwo anali kupalasa bwatolo, anayang’anizana na cimphepo camphamvu ca mkuntho cimene cinapangitsa mafunde pa nyanjapo. Kenako Yesu anabwela kwa iwo akuyenda pa madzi. Ndipo anauza mtumwi Petulo kuti nayenso ayende pa madzipo. (Mat. 14:22-31) Yesu atangokwela m’bwatolo, cimphepo camkuntho cija cinaleka. Zimenezi zinacititsa ophunzilawo kukamba kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” a (Mat. 14:33) Ngakhale n’telo, iwo anali asanaone kugwilizana pakati pa cozizwitsa cimeneci na zimene zinacitika pamene anali na khamu la anthu lija. Onani zimene Maliko analemba. Iye anati: “Ophunzilawo anadabwa kwambili cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la cozizwitsa ca mitanda ya mkate ija, ndipo m’mitima yawo zinali kuwavutabe kumvetsa.” (Maliko 6:50-52) Iwo anali asanamvetse kuculuka kwa mphamvu zocitila zozizwitsa zimene Yehova anali atapatsa Yesu. Posakhalitsa, Yesu anakambanso za cozizwitsa ca mikate ndipo anatipatsa phunzilo lofunika.

8-9. N’cifukwa ciyani khamu la anthu linali kum’funafuna Yesu? (Yohane 6:26, 27)

8 Khamu la anthu limene Yesu anadyetsa, linaika kwambili maganizo awo pa kukhutilitsa zofuna zawo komanso zikhumbo zawo zakuthupi. Motani? Tsiku lotsatila, iwo anapeza kuti Yesu na atumwi ake anali atacoka kudela lawo. Conco, khamu la anthu linakwela mabwato ocoka ku Tiberiyo na kulowela ku Kaperenao kukafunafuna Yesu. (Yoh. 6:22-24) Kodi iwo anacita zimenezo cifukwa cakuti anali kufuna kumvetsela zambili za Ufumu? Ayi. Iwo anacita zimenezo cifukwa cakuti anali kufuna kuti Yesu awapatse mkate wina. Tidziŵa bwanji zimenezi?

9 Onani zinacitika khamu la anthu lija litapeza Yesu pafupi na mzinda wa Kaperenao. Yesu mosapita m’mbali anauza anthuwo kuti anabwela kudzam’funafuna cifukwa anali kufuna kukhutilitsa njala yawo yakuthupi. Ngakhale kuti anthuwo ‘anadya mikate n’kukhuta,’ Yesu anawauza kuti cakudya cimeneco “cimawonongeka.” Conco, iye anawalimbikitsa kuti ayenela kuyesetsa kukhala na cakudya “cimene cimabweletsa moyo wosatha.” (Ŵelengani Yohane 6:26, 27.) Yesu anawauza kuti Atate wake angawapatse cakudya cimeneco. Anthuwo anadabwa pomwe anamva kuti kuli cakudya comwe cimabweletsa moyo wosatha! Kodi n’cakudya citi cimene cimabweletsa moyo wosatha? Ndipo kodi omvetsela a Yesu akanacita ciyani kuti alandile cakudya cimeneco?

10. Kodi anthuwo anafunika kucita ciyani kuti ‘akakhale ndi moyo wosatha’?

10 Zikuoneka kuti Ayudawo anaona kuti ayenela kucita nchito zinazake kuti alandile cakudya cimeneco. N’kutheka kuti anali kuganizila za kutsatila Cilamulo ca Mose. Komabe, Yesu anawauza kuti: “Zimene Mulungu akufuna kuti muzicita ndi zakuti muzisonyeza cikhulupililo mwa amene anamutuma.” (Yoh. 6:28, 29) Kuonetsa cikhulupililo mwa amene Mulungu anamutuma n’kofunika kuti munthu ‘akakhale ndi moyo wosatha.’ Ni iko komwe, Yesu anali ataikambapo kale mfundoyi. (Yoh. 3:16-18, 36) Ndipo pa nthawi ina, Yesu anakambanso zina zimene munthu ayenela kucita kuti akapeze moyo wosatha.​—Yoh. 17:3.

11. Kodi Ayuda anaonetsa bwanji kuti anaika kwambili maganizo awo pa cakudya cakuthupi? (Salimo 78:24, 25)

11 Ayudawo sanakhulupilile zimene Yesu anawauza zakuti iwo ayenela kuika cikhulupililo cawo mwa iye kuti akapeze moyo wosatha. Conco iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo mucita cizindikilo cotani kuti ife ticione n’kukukhulupililani?” (Yoh. 6:30) Kenako iwo anauza Yesu kuti makolo awo m’nthawi ya Mose anali kulandila mana mozizwitsa. Cakudya cimeneco cinali cakudya cawo ca tsiku na tsiku. (Neh. 9:15; ŵelengani Salimo 78:24, 25.) Zinali zoonekelatu kuti maganizo a anthu m’khamulo anali pa kukhala na cakudya ceniceni cakuthupi. Ndipo pamene Yesu anachula za “cakudya ceniceni cocokela kumwamba,” cimene cinali kudzawapatsa moyo wosatha mosiyana na mana, iwo sanafune ngakhale kumufunsa zimene anatanthauza. (Yoh. 6:32) Iwo anaika kwambili maganizo awo pa zofuna zawo zakuthupi, ndipo ananyalanyaza mfundo za coonadi zimene Yesu anali kufuna kuwagaŵila. Kodi tiphunzilapo ciyani pa cocitika cimeneci?

ZIMENE ZIYENELA KUKHALA ZOFUNIKA KWAMBILI KWA IFE

12. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cinthu cofunika kwambili paumoyo?

12 Onani phunzilo lofunika kwambili limene titengamo mu Yohane caputala 6. Zinthu zimene tiyenela kuona kuti ndiye zofunika kwambili paumoyo wathu ni zosoŵa zathu zauzimu. Kumbukilani kuti Yesu anagogomeza mfundoyi pomwe anali kukaniza mayeselo a Satana. (Mat. 4:3, 4) Ndipo pa ulaliki wake wa paphili, iye anafotokoza kufunika kozindikila zosoŵa zathu zauzimu na kuzikhutilitsa. (Mat. 5:3) Conco, tingadzifunse kuti: ‘Kodi mmene nimacitila zinthu paumoyo wanga, nimaonetsa kuti nimaika kwambili maganizo anga pa kusamalila zosoŵa zanga zakuuzimu m’malo moganizila kwambili zosoŵa zanga zakuthupi?’

13. (a) N’cifukwa ciyani tinganene kuti palibe colakwika kusangalala na cakudya? (b) Ni cenjezo liti limene Paulo anapeleka? (1 Akorinto 10:6, 7, 11)

13 Palibe colakwika ciliconse kupemphela kuti tikhale na zinthu zakuthupi komanso kusangalala nazo. (Luka 11:3) Baibo imafotokoza kuti palibe colakwika ciliconse kuti munthu “adye, amwe ndi kusangalala cifukwa coti wagwila nchito mwakhama.” Ndipo imawonjezelanso kuti zimenezo “n’zocokela m’dzanja la Mulungu woona.” (Mlal. 2:24; 8:15; Yak. 1:17) Ngakhale n’telo, tiyenela kuona zinthu zakuthupi moyenela. Mtumwi Paulo anatsindika bwino mfundoyi pomwe anali kulembela kalata Akhristu omwe posapita nthawi anali kudzaona mapeto a dongosolo la Ciyuda. Iye anawakumbutsa zimene zinacitikila Aisiraeli kumbuyoku kuphatikizapo zimene zinacitika pomwe iwo anali pafupi na Phili la Sinai. Iye anacenjeza Akhristuwo kuti: “Tisamalakelake zinthu zoipa ngati mmene [Aisiraeli] anacitila.” (Ŵelengani 1 Akorinto 10:6, 7, 11.) Yehova anali kupatsa Aisiraeliwo cakudya mozizwitsa. Koma cifukwa cakuti anthuwo anali na dyela lofuna zakudya zina, makonzedwe a cakudyaco anakhala “zinthu zoipa.” (Num. 11:4-6, 31-34) Ndipo pomwe Aisiraeliwo analambila mwana wa ng’ombe wa golide, anaonetsa kuti anali kuika kwambili maganizo awo pa kudya, kumwa, komanso kusangalala kuposa kumvela Yehova. (Eks. 32:4-6) Paulo anafotokoza cocitikaci monga cenjezo kwa Akhristu amene anali kuyembekezela mapeto a dongosolo la Ciyuda omwe anali kudzafika mu 70 C.E. Nafenso tikukhala kumapeto a dongosolo lino la zinthu. Conco, m’pofunika kumvela cenjezo limene Paulo anapeleka.

14. Ponena za cakudya, kodi tingayembekezele zotani m’dziko latsopano?

14 Pamene Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphela kuti “mutipatse cakudya cathu ca lelo,” anatiuzanso kuti tizipemphela kuti cifunilo ca Mulungu “cicitike monga kumwamba cimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:9-11) Kodi m’maganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padziko pa nthawiyo? Cifunilo ca Mulungu cimaphatikizapo kuti tidzakhale na cakudya cabwino. Yesaya 25:6-8 imaonetsa kuti anthu adzakhala na cakudya ca mwanaalilenji komanso cokoma pansi pa Ufumu wa Yehova. Ndipo Salimo 72:16 limatiuza kuti: “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.” Kodi mukuyembekezela nthawiyo pamene mudzaphika cakudya cokoma cimene mumacikonda kwambili? Kapena cakudya cinacake cimene musanaciphikepo? Mungayembekezelenso kudzakhala na munda wanu-wanu wampesa na kudya zipatso zake. (Yes. 65:21, 22) Ndipo aliyense padziko lapansi adzasangalala na zinthu zabwino zimenezi.

15. Ni maphunzilo otani amene adzapelekedwe kwa amene adzaukitsidwa? (Yohane 6:35)

15 Ŵelengani Yohane 6:35. N’ciyani cidzacitikila aja amene anadya mkate na nsomba zimene Yesu anaculukitsa? Ngakhale kuti ena mwa iwo sanaonetse cikhulupililo mwa Yesu, n’kutheka kuti iwo adzaukitsidwa ndipo tingadzaonane nawo. (Yoh. 5:28, 29) Oukitsidwawo adzafunika kudziŵa tanthauzo la mawu a Yesu akuti: “Ine ndine cakudya copatsa moyo. Aliyense wobwela kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono.” Iwo adzafunika kuonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo ya Yesu na kukhulupilila kuti iye anapeleka moyo wake kaamba ka iwo. Panthawi imeneyo, padzakhala pulogilamu yauzimu yophunzitsa anthu amene adzaukitsidwa komanso ana amene azidzabadwa pa nthawiyo. Kuthandiza anthu kukulitsa ubale wawo na Yehova kudzakhala kosangalatsa kwambili kuposa kudya cakudya cokoma kwambili ca m’dziko latsopano! Inde, zinthu zauzimu zidzakhala zofunika kwambili kwa ife pa nthawiyo.

16. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

16 Tangokambilanako zina mwa zocitika za mu Yohane caputala 6. Komabe, Yesu anali na zina zowonjezela zimene anafuna kuwaphunzitsa zokhudza “moyo wosatha.” Ayuda amene Yesu anali kulankhula nawo anafunika kumvetsela mwachelu ku zimene anali kukamba. Nafenso tiyenela kucita cimodzimodzi. Tidzapitiliza kukambilana Yohane caputala 6 m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 20 Munapeleka Mwana Wanu Wokondeka

a Kuti mupeze mfundo zina zowonjezela pa cocitika cosangalatsaci, onani buku lakuti, Yesu​—Ndi Njila, Choonadi Ndi Moyo, tsa. 131, komanso buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo, tsa. 185.