NKHANI YOPHUNZILA 50
NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”
Makolo—Thandizani Ana Anu Kulimbitsa Cikhulupililo Cawo
“Muzindikile cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.”—AROMA 12:2.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mfundo zothandiza makolo kukambilana bwino na ana awo pamene akuwathandiza kulimbitsa cikhulupilillo cawo mwa Mulungu komanso pa Baibo.
1-2. Kodi makolo angacite ciyani mwana wawo akayamba kufunsa mafunso okhudza zimene timakhulupilila?
AMBILI angavomeleze kuti kulela ana ni nchito yaikulu. Ngati ndinu kholo ndipo muli na mwana wamng’ono, tikuyamikilani cifukwa ca khama lanu polimbitsa cikhulupililo cake. (Deut. 6:6, 7) Pamene mwana wanu akukula, angayambe kufunsa mafunso pa zimene timakhulupilila, monga kufunsa cifukwa cake tiyenela kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino.
2 Poyamba, mungayambe kuda nkhawa poganiza kuti mwana wanu wayamba kufunsa mafunso amenewa cifukwa cakuti waleka kukhulupilila kwambili Mulungu komanso Baibo. Koma zoona zake n’zakuti pamene ana akusinkhuka, afunika kufunsa mafunso kuti alimbitse cikhulupililo cawo. (1 Akor. 13:11) Conco simuyenela kuda nkhawa mwana wanu akamafunsa mafunso pa zimene timakhulupilila. Muyenela kuona kuti umenewo ni mpata womuthandiza kukulitsa luso lake la kuganiza.
3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 M’nkhani ino, tikambilane mmene makolo angathandizile ana awo (1) kulimbitsa cikhulupililo cawo, (2) kumvetsa cifukwa cake ayenela kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino, komanso (3) kukhalila kumbuyo zimene amakhulupilila. Pamene tikambilana zimenezi, tionenso cifukwa cake m’poyenela ana kufunsa mafunso otelo. Tionenso zimene banja lingacitile pamodzi kuti makolo apeze mpata wokambilana na ana awo zimene timakhulupilila.
THANDIZANI MWANA WANU KULIMBITSA CIKHULUPILILO CAKE
4. Ni mafunso ati amene mwana wanu angafunse? Ndipo n’cifukwa ciyani angafunse mafunso amenewa?
4 Makolo acikhristu ayenela kudziŵa kuti mwana wawo sangakhale na cikhulupilillo mwa Mulungu, cabe cifukwa cakuti iwo ali na cikhulupililo. Simunabadwe na cikhulupililo mwa Yehova. Nawonso ana anu sanabadwe na cikhulupililo. Conco, mwanayo akamakula, angafunse mafunso monga akuti: ‘Ningatsimikize bwanji kuti Mulungu aliko? Kodi niyenela kukhulupilila zimene Baibo imakamba?’ Ni iko komwe, Baibo imatilimbikitsa kugwilitsa nchito “luso la kuganiza,” komanso ‘kufufuza zinthu zonse n’kuzitsimikizila.’ (Aroma 12:1; 1 Ates. 5:21) Koma ni motani mmene mungathandizile mwana wanu kulimbitsa cikhulupililo cake?
5. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuti aziikhulupilila Baibo? (Aroma 12:2)
5 Limbikitsani mwana wanu kupeza maumboni akuti zimene Baibo imakamba n’zoona. (Ŵelengani Aroma 12:2.) Mwana wanu akamafunsa mafunso, muonetseni mmene angapezele mayankho pogwilitsa nchito zida zofufuzila, monga Watch Tower Publications Index na Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Mu Buku Lofufuzila Nkhani la Chichewa, pa mutu waukulu wakuti “Baibulo,” pa kamutu kakuti “Kuuzilidwa ndi Mulungu,” angapeze maumboni oonetsa kuti Baibo si buku wamba lolembedwa na anthu. M’malomwake, ni “mawu a Mulungu.” (1 Ates. 2:13) Mwacitsanzo, angafufuze za mzinda wakale wa Asuri wa Nineve. Kale, akatswili ena a Baibo anali kunena kuti mzinda wa Nineve unali wongopeka. Koma podzafika mzaka za m’ma 1850, akatswili a zofukula anapeza matongwe pansi pa nthaka. Zimene anapezazo zionetsa kuti Baibo imakamba zoona. (Zef. 2:13-15) Kuti adziŵe mmene kuwonongedwa kwa mzinda wa Nineve kunakwanilitsila ulosi wa m’Baibo, angaŵelenge nkhani yakuti “Kodi Mudziŵa?” mu Nsanja ya Mlonda ya November 2021. Limbikitsani mwana wanu kuyelekezela zimene amaŵelenga m’zofalitsa zathu na zimene mabuku ena odalilika amakamba. Kucita izi kudzam’thandiza kulimbitsa cikhulupililo cake cakuti zimene Baibo imakamba n’zoona.
6. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuona umboni wakuti zimene Baibo imakamba n’zoona? Pelekani citsanzo. (Onaninso cithunzi.)
6 Thandizani mwana wanu kuganizila cifukwa cake zimene Baibo imakamba n’zoona. Makolo, muli na mipata yosiyanasiyana yokambilana na ana anu zinthu zokhudza Baibo kapena zokhudza kukhulupilila Mulungu. Mipata imeneyi ingapezeke mukapita kumalo osungilako zinthu zakale, mukapita ku paki, kapena mukapita kukaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Mwacitsanzo, pamene mukuona zinthu zakale za ku miziyamu, kaya mwapitako mwacindunji kapena mukuzionela pa foni, mungaonetse mwana wanu mmene zocitika za m’mbili yakale kapena zinthu zina zikugwilizanila na Baibo. Kucita izi kungam’thandize kuona kuti zimene Baibo imakamba n’zoona. Mwina mungaphunzitse mwana wanu za mwala wolembedwa na Amowabu. Mwalawo wakhalapo kwa zaka 3,000, ndipo pali dzina la Mulungu lakuti Yehova. Mwala umenewo uli ku miziyamu yochedwa Louvre mumzinda wa Paris, m’dziko la France. Kope la mwala umenewu limapezekanso mu miziyamu yakuti “Baibo na Dzina la Mulungu” ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova ku Warwick, m’dziko la America. Mwala wolembedwa na Amowabu umenewu umaonetsa kuti Mfumu Mesa wa ku Mowabu anapandukila Aisiraeli. Zimenezi n’zogwilizana na zimene Baibo imakamba. (2 Maf. 3:4, 5) Mwana wanu akadzionela yekha umboni wakuti Baibo imakamba zoona komanso wakuti ni yodalilika, cikhulupililo cake cidzalimbilako.—Yelekezelani na 2 Mbiri 9:6.
7-8. (a) Timaphunzila ciyani tikaona kukongola komanso mpangidwe wa zinthu zacilengedwe? Pelekani citsanzo. (Onaninso cithunzi.) (b) Ni mafunso ati angathandize mwana wanu kulimbitsa cikhulupililo cake mwa Mlengi?
7 Limbikitsani mwana wanu kukhala na cidwi comaganizila pa zinthu zacilengedwe. Pamene mukuyenda na mwana wanu ku malo akuminda kapena cakuthengo, muthandizeni kuona mapatani a mpangidwe wa zinthu omwe timaona pa zacilengedwe zocititsa cidwi. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciyani? Cifukwa mapatani amenewo amaonetsa luso komanso nzelu zimene Yehova ali nazo zopanga zinthu. Mwacitsanzo, titenge mapatani ooneka ozungulila monga mwa makulungidwe a nkhata. Kwa zaka zambili, asayansi akhala akuwafufuza mapatani amenewo n’kuwaunika kuti awamvetsetse. Wasayansi wina dzina lake Nicola Fameli, anafotokoza kuti mukaŵelenga mizele ya mapatani azungulizunguli amenewo, mumapeza kuti ali mu dongosolo linalake la ziŵelengelo. Mapatani azungulizunguli amenewo timawaona mu zinthu zambili, monga mu mlalang’amba, zigoba za nkhono, m’masamba a zomela zina, komanso kumutu wa mpenyadzuwa. a
8 Pamene mwana wanu akuphunzila zambili m’kalasi ya sayansi ku sukulu, iye angamvetse kuti zinthu zacilengedwe zimatsatila malamulo enaake. Mwacitsanzo, m’cilengedwe muli mphamvu yokoka. Mphamvu imeneyi yokoka zinthu kuti zigwe pansi, imapangitsa cifungadziko (atmosphere) kufungatila dziko lapansi, kukhalitsa bata mafunde a panyanja, komanso kucilikiza zamoyo padziko. Koma kodi ndani amene analenga mphamvu yokoka imeneyi? Kodi ndani analinganiza kuti zinthu zikhale mwadongosolo conci? Mwana wanu akamaganizila kwambili za mafunso ngati amenewa, n’kutheka kuti zidzamuthandiza kukhala na cikhulupililo colimba cakuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. (Aheb. 3:4) Pamene mwana akusinkhuka, mungaone kuti m’pofunika kumuthandiza kumvetsa cifukwa cake tiyenela kumvela malamulo a Mulungu. Mungatelo mwa kumufunsa kuti, “Popeza Mulungu ndiye anatilenga, kodi si poyenela kunena kuti iye ndiye woyenela kutipatsa mfundo za makhalidwe abwino zimene zingatithandize kukhala acimwemwe?” Kenako mungamufotokozele kuti mfundo zothandiza zimenezo zipezeka m’Baibo.
MUTHANDIZENI KUMVETSA CIFUKWA CAKE AYENELA KUTSATILA MFUNDO ZA M’BAIBO ZA MAKHALIDWE ABWINO
9. N’ciyani cingacititse mwana wanu kufunsa mafunso okhudza mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino?
9 Mwana wanu akamafunsa ngati kulidi kwa phindu kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino, yesani kumvetsa cifukwa cake ali na mafunso amenewo. Kodi iye amafunsa mafunsowo cifukwa sagwilizana na mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino? Kapena kodi sadziŵa mmene angakhalile kumbuyo mfundo za Cikhristu akafunsidwa? Mulimonsemo, mungathandize mwana wanu kumvetsa cifukwa cake tiyenela kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino. Mungatelo mwa kuphunzila naye buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! b
10. Mungathandize bwanji mwana wanu kuti aziona ubwenzi wake na Yehova kukhala wofunika?
10 Limbikitsani mwana wanu kuti aziona ubwenzi wake na Yehova kukhala wofunika. Pamene mukuphunzila Baibo na mwana wanu, yesani kuseŵenzetsa mafunso, komanso zitsanzo zopezeka m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! kuti mumvetse mmene amaonela zinthu. (Miy. 20:5) Mwacitsanzo, mu phunzilo 8, Yehova amayelekezeledwa na mnzathu amene amasamala za ife, yemwe amatikumbutsa mfundo zimene zingatiteteze komanso kutipindulila. Pambuyo pokambilana 1 Yohane 5:3, mungamufunse kuti, “Podziŵa kuti Yehova ni Bwenzi labwino kwambili, kodi tiyenela kuziona motani zimene amatiuza kucita?” Funsoli lingaoneke losavuta, koma kulifunsa kwa mwana wanu, n’kutheka kuti lingamuthandize kuti aziona malamulo a Mulungu kuti ni umboni wakuti iye amatikonda.—Yes. 48:17, 18.
11. Mungathandize motani mwana wanu kumvetsa ubwino wotsatila mfundo za m’Baibo? (Miyambo 2:10, 11)
11 Kambilanani naye mmene timapindulila tikaseŵenzetsa mfundo za m’Baibo. Mukamaŵelenga Baibo kapena lemba la tsiku pamodzi, kambilanani mmene mfundo za m’Baibo zathandizila banja lanu. Mwacitsanzo, kodi mwana wanu amaona mapindu amene amabwela cifukwa cokhala wakhama pa nchito komanso woona mtima m’zocita? (Aheb. 13:18) Mungamufotokozelenso kuti kutsatila mfundo za m’Baibo kumaticititsa kukhala otetezeka mwakuthupi komanso acimwemwe. (Miy. 14:29, 30) Mwana wanu akamvetsa ubwino umene umakhalapo tikamatsatila ziphunzitso za m’Baibo, angafune kumaseŵenzetsa mfundozo paumoyo wake.—Ŵelengani Miyambo 2:10, 11.
12. Kodi tate wina amathandiza bwanji mwana wake kumvetsa mapindu amene amabwela kaamba kotsatila mfundo za m’Baibo?
12 Tate wina wa ku France dzina lake Steve, anafotokoza mmene iye na mkazi wake amathandizila mwana wawo wa zaka 16 dzina lake Ethane, kuona malamulo a Yehova ngati njila imene iye amaonetsela kuti amatikonda. Steve anakamba kuti: “Timamufunsa mafunso monga akuti, ‘N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizitsatila mfundo imeneyi? Kodi mfundoyi ionetsa bwanji kuti iye amatikonda? N’ciyani cingacitike ngati sungatsatile mfundo imeneyi paumoyo wako?’” Makambilano amenewa athandiza Ethane kuti azitsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Steve anawonjezela kuti: “Colinga cathu ni kuthandiza Ethane kuona kuti nzelu zopezeka m’Baibo n’zapamwamba kwambili kuposa nzelu za anthu.”
13. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo? Pelekani citsanzo.
13 Phunzitsani mwana wanu kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo. Mpata umodzi umene mungaseŵenzetse m’pamene mwana wanu wapatsidwa buku la kusukulu kuti aŵelenge. Anthu ochulidwa m’bukulo angakhale anthu ocita zaciwelewele komanso aukali kwambili. Ndipo bukulo lingakhale kuti linalembedwa m’njila imene ionetsa kuti tiyenela kutengela makhalidwe ya anthu amenewo. Mungafunse mwana wanu mmene Yehova amaonela anthu ochulidwa m’bukulo. (Miy. 22:24, 25; 1 Akor. 15:33; Afil. 4:8) Kucita izi kungathandize mwana wanu kuti akakwanitse kulalikila aphunzitsi ake komanso anzake amukalasi pamene akukambilana za m’bukulo.
THANDIZANI MWANA WANU KUKHALA WOKONZEKA KUKHALILA KUMBUYO ZIMENE AMAKHULUPILILA
14. Ni nkhani iti ingacititse mantha Mkhristu wacinyamata kukambilana na ena? Ndipo cifukwa ciyani?
14 Nthawi zina, Akhristu acinyamata angamaope kukhalila kumbuyo zimene amakhulupilila. Mwacitsanzo, iwo angacite mantha kufotokoza cifukwa cake sakhulupilila ciphunzitso ca cisanduliko. Cifukwa ciyani? Aphunzitsi awo angafotokoze kuti nkhani ya cisanduliko si maloto cabe ayi koma kuti inacitikadi. Ngati ndinu kholo, mungathandize bwanji mwana wanu kukhala wotsimikiza kuti zimene amakhulupilila n’zoona?
15. N’ciyani cingathandize Mkhristu wacinyamata kukhala wotsimikiza kuti zimene amakhulupilila n’zoona?
15 Thandizani mwana wanu kukhala wotsimikiza kuti zimene amakhulupilila n’zoona. Mwana wanu sayenela kucita naco manyazi cikhulupililo cakuti kuli Mlengi. (2 Tim. 1:8) Cifukwa ciyani? Zili conco cifukwa cakuti ngakhale asayansi ambili amakhulupilila kuti zamoyo sizinakhalepo mwa ngozi. Asayansi amenewo amakhulupilila kuti winawake wanzelu, ayenela kuti ndiye analenga zamoyo zonse zomwe ni zogometsa. Kaamba ka ici, iwo sakhulupilila ciphunzitso ca cisanduliko comwe n’cofala m’masukulu padziko lonse. Mwana wanu angalimbitse cikhulupililo cake mwa kuganizila zifukwa zimene zinapangitsa abale na alongo ena kukhulupilila kuti moyo unacita kulengedwa. c
16. Kodi makolo angamuthandize bwanji mwana wawo kukhalila kumbuyo cikhulupililo cakuti kuli Mlengi? (1 Petulo 3:15) (Onaninso cithunzi.)
16 Konzekeletsani mwana wanu kukhalila kumbuyo cikhulupililo cakuti kuli Mlengi. (Ŵelengeni 1 Petulo 3:15.) Cimodzi cingakuthandizeni ni kukambilana naye nkhani za pa jw.org ku Chichewa pa mpambo wa nkhani wakuti “Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa” Kenako yesezani na mwana wanu mmene angafotokozele kwa ena mfundo za m’nkhani imene mwasankha powathandiza kumvetsa coonadi ponena za Mlengi. Mukumbutseni kuti pocita zimenezo sayenela kukangana na ena. Mulimbikitseni kufotokoza zinthu m’njila yosavuta kumva ena akalola kukamba naye. Mwacitsanzo, mnzake wa kusukulu angakambe kuti: “Ine nimangokhulupilila zinthu zooneka. Conco sinikhulupilila mwa Mulungu cifukwa sin’namuonepo.” Mkhristu wacinyamatayo angayankhe kuti: “Yelekeza kuti ukuyenda m’chile komwe nikutali kwambili na kumene kumakhala anthu, ndipo wapeza citsime comangidwa na miyala. Kodi ungaganize ciyani? Mwacionekele, munthu winawake ndiye anamanga citsimeco. N’cimodzimodzi na pulaneti yathu komanso zamoyo zonse zili m’menemo. Payenela kuti pali winawake amene anazilenga.”
17. Kodi makolo angalimbikitse bwanji mwana wawo kufunafuna mipata youzilako ena coonadi ca m’Baibo? Pelekani citsanzo.
17 Limbikitsani mwana wanu kufunafuna mipata youzilako ena coonadi ca m’Baibo. (Aroma 10:10) Mungauuze mwana wanu kuti kuuzako ena zimene amakhulupilila kuli monga mmene zimakhalila munthu akamaphunzila kuliza cida coimbila. Cakumayambililo, munthuyo angamayeseze kuliza nyimbo zosavuta ndipo m’kupita kwa nthawi iye angazolowele kuliza cipangizoco. Mofananamo, Mkhristu akangoyamba kulalikila, angaseŵenzetse njila yosavuta pouzako ena zimene amakhulupilila. Mwacitsanzo, iye angafunse mnzake wakusukulu kuti: “Kodi udziŵa kuti akatswili a zopangapanga amakopela cilengedwe popanga zinthu zawo? Leka nikuonetseko vidiyo yocititsa cidwi.” Pambuyo poonetsa mnzakeyo vidiyo yopezeka pa mpambo wa nkhani wakuti Kodi Zinangocitika Zokha? wacicepeleyo angafunse mnzakeyo kuti: “Ngati asayansi amapezelapo citamando pa zomwe akopela m’cilengedwe, kodi ndani ayenela kutamandidwa pa zomwe timaona m’cilengedwe?” Kufotokoza zinthu m’njila yosavuta imeneyi, kungadzutse cidwi mwa mnzake wa kusukuluyo ndipo angafune kuphunzila zambili.
PITILIZANI KUTHANDIZA MWANA WANU KULIMBITSA CIKHULUPILILO CAKE
18. Kodi makolo angapitilize bwanji kuthandiza mwana wawo kulimbitsa cikhulupillilo cake mwa Mulungu?
18 Tikukhala m’dziko limene anthu ambili sakhulupilila Yehova. (2 Pet. 3:3) Conco makolonu, pamene mukuphunzila Baibo na mwana wanu, mulimbikitseni kuti azifufuza nkhani zimene zingam’thandize kuti azilemekeza kwambili Mawu a Mulungu komanso malamulo ake. M’thandizeni kuganizila mozamilapo za Yehova, komanso kulimbitsa cikhulupililo cake mwa iye. Mungatelo mwa kukambilana naye zacilengedwe ca Yehova cocititsa cidwi. M’thandizeni kumvetsa maulosi ocititsa cidwi a m’Baibo amene akukwanilitsidwa komanso amene anakwanilitsidwa kale. Koposa zonse, muzipemphela naye mwana wanu, ndipo muzimupemphelela. Mukatelo, dziŵani kuti Yehova adzadalitsa khama lanu pamene mukuthandiza mwana wanu kulimbitsa cikhulupililo cake mwa iye.—2 Mbiri 15:7.
NYIMBO 133 Lambila Yehova Ukali Wacicepele
a Kuti mudziŵe zambili, onani vidiyo yacingelezi yakuti The Wonders of Creation Reveal God’s Glory—Patterns pa jw.org.
b Ngati mwana wanu anamaliza kuphunzila buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mungakambilane naye ena mwa maphunzilo a m’cigawo 3 na 4 omwe amakamba za miyeso ya m’Baibo ya makhalidwe abwino.
c Onani nkhani yakuti “Chifukwa Chimene Timakhulupirira Kuti Kuli Mlengi,” mu Galamukani! ya September 2006, komanso bulosha yakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri. Kuti mupeze zitsanzo zina, tambani mavidiyo akuti Zokhudza Mmene Moyo Unayambira pa jw.org ku Chichewa.
d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mboni yacicepele ikuonetsa mnzake wa kusukulu vidiyo yopezeka pa mpambo wa nkhani wakuti Kodi Zinangocitika Zokha?