NKHANI YOPHUNZILA 51
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
Misozi Yanu Ni Yamtengo Wapatali kwa Yehova
“Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lacikopa. Kodi misozi yanga sinalembedwe mʼbuku lanu?”—SAL. 56:8.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Yehova amamvetsa bwino ululu wa mumtima mwathu, ndipo adzapeleka thandizo limene tikufunikila kuti tilimbikitsidwe.
1-2. Ni zocitika ziti zingacititse kuti tigwetse misozi?
TONSE tinalilapo panthawi ina. Nthawi zina timagwetsa misozi cifukwa ca cisangalalo. N’kutheka kuti munagwetsapo misozi pamene cinacake cofunika kapena capadela cinakucitikilani. Mwacitsanzo, n’kutheka kuti munagwetsa misozi ya cisangalalo pamene mwana wanu anabadwa, pamene munakumbukila cocitika cimene cinakusangalatsani, kapena pamene munaona mnzanu pambuyo pa zaka zambili.
2 Komabe, nthawi zambili, misozi imaonetsa cisoni cimene tili naco mumtima mwathu. Mwacitsanzo, mwina tingalile munthu wina akatikhumudwitsa kwambili. N’kuthekanso kuti tingagwetse misozi cifukwa covutika na ululu kaamba ka matenda osapolelapo msanga, kapena cifukwa cotaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa. Panthawi ngati zimenezi, tingamve mmene mneneli Yeremiya anamvela pomwe Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu. Iye anati: “Maso anga akungotuluka misozi ngati mitsinje . . . Maso anga akungotuluka misozi mosalekeza.”—Maliro 3:48, 49.
3. Kodi Yehova amamva bwanji akaona ana ake akuvutika? (Yesaya 63:9)
3 Yehova adziŵa kuti talilapo kangati mu umoyo wathu cifukwa ca zovutitsa zimene takumanapo nazo. Baibo imatitsimikizila kuti iye amadziŵa ululu umene atumiki ake amakhala nawo, komanso kuti amamva kufuula kwawo kopempha thandizo. (Sal. 34:15) Koma Yehova amacita zambili kuposa kungoona mavuto amene timakumana nawo, komanso kumva kufuula kwathu kopempha thandizo. Monga kholo lacikondi, Yehova amakhudzika mtima kwambili akaona ana ake akulila, ndipo ni wofunitsitsa kupeleka thandizo.—Ŵelengani Yesaya 63:9.
4. Kodi tikambilane zitsanzo ziti za m’Baibo? Nanga zitsanzo zimenezi zitiphunzitse ciyani ponena za Yehova?
4 M’Mawu ake, Yehova amaonetsa zimene anacita pamene atumiki ake anagwetsa misozi. Tione mfundo imeneyi pamene tikambilana zitsanzo za Hana, Davide, na Mfumu Hezekiya. N’ciyani cinawacititsa kugwetsa misozi? Kodi Yehova anacitapo ciyani pamene iwo anali kufuulila kwa iye popempha thandizo? Kodi zitsanzo zawo zingatilimbikitse bwanji tikagwetsa misozi cifukwa ca cisoni, kukhumudwitsidwa, kapena tikasowa mtengo wogwila?
MUKAGWETSA MISOZI CIFUKWA CA CISONI
5. Kodi Hana anamva bwanji na zimene zinali kumucitikila?
5 Hana anakumanapo na mavuto angapo amene anamupangitsa kugwetsa misozi cifukwa ca cisoni. Limodzi mwa mavuto amene anali nawo linali lakuti anali ku cikwati ca mitala, ndipo mkazi mnzake Penina anali kumuvutitsa kwambili. Kuwonjezela apo, Hana analibe ana koma Penina anali na ana angapo. (1 Sam. 1:1, 2) Penina anali kusautsa Hana mosalekeza cifukwa anali wosabeleka. Kodi inu mukanamva bwanji mukanakhala Hana? Hana anali “wokhumudwa kwambili” moti “ankalila ndipo sankadya.”—1 Sam. 1:6, 7, 10.
6. Kodi Hana anacita ciyani kuti apeze cilimbikitso?
6 Kodi Hana anacita ciyani kuti apeze cilimbikitso? Cimodzi cimene anacita ni kupita kumalo olambilila, ku cihema. Atafika kumeneko, mwina anaimilila pafupi na khomo lolowela m’bwalo la cihema, “ndipo anayamba kupemphela kwa Yehova uku akulila kwambili.” Iye anacondelela Yehova kuti: ‘Onani kuvutika kwa ine kapolo wanu n’kundikumbukila.’ (1 Sam. 1:10b, 11) Hana anakhutulila Yehova za mumtima mwake m’pemphelo. Mosakayikila, Yehova anakhudzika mtima kwambili na misozi ya mwana wake wokondeka ameneyu!
7. Kodi Hana analimbikitsidwa bwanji atakhutulila Yehova za mumtima mwake?
7 Kodi Hana anamva bwanji atakhutulila Yehova za mumtima mwake m’pemphelo, komanso atalimbikitsidwa na Mkulu wa Ansembe Eli? Baibo imati: “[Hana] anacoka n’kupita kukadya ndipo nkhope yake sinkaonekanso ya nkhawa.” (1 Sam. 1:17, 18) Ngakhale kuti mavuto ake anali asanathe, Hana anamvako bwino. Anatulila Yehova nkhawa zake. Yehova anaona kuvutika kwake, anamva kulila kwake, ndipo pambuyo pake anamudalitsa mwa kumupatsa mwana.—1 Sam. 1:19, 20; 2:21.
8-9. Malinga na Aheberi 10:24, 25, n’cifukwa ciyani tifunika kucita zonse zimene tingathe kuti tipezeke pa misonkhano ya Cikhristu? (Onaninso cithunzi.)
8 Zimene tiphunzilapo. Kodi palipano mukukumana na vuto linalake limene limakupangitsani kugwetsa misozi cifukwa ca cisoni? Mwina muli na cisoni cifukwa wa m’banja mwanu kapena mnzanu anamwalila. Panthawi ngati zimenezi, m’pomveka kufuna kukhala kwanokhanokha. Koma kumbukilani kuti Hana anapeza cilimbikitso atapita ku cihema. Inunso mungapeze cilimbikitso mwa kupezeka pa misonkhano ya Cikhristu, ngakhale pamene mukumva kutopa kapena pamene muli acisoni kwambili. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Pamene tikumvetsela Malemba olimbikitsa a m’Baibo pa misonkhano, Yehova angatithandize kucotsa maganizo ofooketsa. Izi zingatithandize kumvako bwino ngakhale pamene vuto lathu silinathe nthawi yomweyo.
9 Pa misonkhano yathu timakhalanso na maceza olimbikitsa na okhulupilila anzathu. Mawu awo acikondi oonetsa kuti amatidela nkhawa angacititse kuti timveko bwino. (1 Ates. 5:11, 14) Mpainiya wina wapadela amene anataikilidwa mkazi wake anati: “Nimagwetsabe misozi mpaka pano. Nthawi zina, nimapita kwanekha n’kuyamba kulila. Koma misonkhano yathu yakhala yonilimbikitsa kwambili. Mawu okoma mtima a abale na alongo komanso ndemanga zawo pa misonkhano zimanitonthoza. Ngakhale n’takhala na nkhawa zoculuka bwanji, nimamvako bwino nikafika pa misonkhano.” Tikakhala pa misonkhano, Yehova angaseŵenzetse abale na alongo athu potithandiza.
10. Tingatengele bwanji citsanzo ca Hana pamene mtima wathu ni wosweka na cisoni?
10 Cinanso cinathandiza Hana kupeza cilimbikitso ni kukhutulila Yehova za mumtima mwake. Inunso ‘mungatulile [Yehova] nkhawa zanu zonse,’ muli na cidalilo cakuti adzakuthandizani. (1 Pet. 5:7) Mlongo wina amene mwamuna wake anaphedwa na acifwamba anafotokoza kuti: “N’nasautsika mtima kwambili moti n’naganiza kuti sinidzakasangalalapo. N’nali kupepukidwa mtima komanso kulimbikitsidwa nikapemphela kwa Atate wanga wacikondi wa kumwamba Yehova. Nthawi zina, n’nali kusoŵa mawu oti ninene m’pemphelo, koma iye anali kudziŵa zimene n’nali kufuna. Nikakhala wokhumudwa komanso wankhawa, n’nali kum’pempha kuti anipatse mtendele wamumtima. Nikacita zimenezo n’nali kupeza mtendele wamumtima, ndipo n’nali kukwanitsa kucita zofunika pa tsikulo.” Mukamukhutulila nkhawa zanu Yehova, iye amakhudzika kwambili na misozi yanu ya cisoni, ndipo amamvetsa ululu umene muli nawo mumtima. Ngakhale pamene nkhawa yanu siinathe nthawi yomweyo, Yehova adzakulimbikitsani ndipo adzakuthandizani kuti mukhaleko na mtendele wamumtima. (Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7) Ndipo adzakudalitsani cifukwa copilila mokhulupilika.—Aheb. 11:6.
MUKAGWETSA MISOZI CIFUKWA COKHUMUDWITSIDWA
11. Kodi Davide anamva bwanji na zoipa zimene zinali kum’citikila?
11 Paumoyo wake, Davide anafunika kupilila mavuto osiyanasiyana amene anamucititsa kuti agwetse misozi. Anacitilidwapo nkhanza na anthu ena komanso kugwilitsidwapo mwala na anthu amene anali kuwadalila. (1 Sam. 19:10, 11; 2 Sam. 15:10-14, 30) Panthawi ina, iye analemba kuti: “Ndafooka cifukwa ca kuusa moyo kwanga. Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi, ndimalila ndipo misozi imadzadza pabedi panga.” N’ciyani cinacititsa Davide kumva conco? Iye analemba kuti: “Cifukwa ca anthu onse amene akundizunza.” (Sal. 6:6, 7) Zocita zoipa za ena zinapangitsa Davide kugwetsa misozi mosalekeza.
12. Malinga na Salimo 56:8, kodi Davide anali wotsimikiza za ciyani?
12 Ngakhale kuti Davide anakumana na mavuto onsewa, iye anali wotsimikiza kuti Yehova amamukonda. Analemba kuti: “Yehova adzamva mawu a kulila kwanga.” (Sal. 6:8) Panthawi ina, Davide analemba mawu ogwila mtima opezeka pa Salimo 56:8. (Ŵelengani.) Mawu amenewa amationetsa kuti Yehova atikonda kwambili komanso kuti amasamala za ife. Davide anakamba kuti zinali monga Yehova akusunga misozi yake m’thumba kapena kuyalemba m’buku. Davide anali wotsimikiza kuti Yehova anali kuona mavuto amene anali kukumana nawo, komanso kuti anali kukumbukila ululu umene anali kumvela. Iye sanali kukaikila kuti Atate wake wacikondi wa kumwamba anali kudziŵa mavuto amene anali kukumana nawo komanso mmene anali kumukhudzila.
13. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani anthu ena akatikhumudwitsa? (Onaninso cithunzi.)
13 Zimene tiphunzilapo. Kodi palipano mtima wanu ni wosweka cifukwa munakhumudwitsidwa kapena munagwilitsidwa mwala na munthu amene munali kumukhulupilila? Mwina mtima wanu ukupweteka cifukwa citomelo canu kapena cikwati canu cinatha mosayembekezeleka. Mwinanso munthu amene mumakonda anasiya kutumikila Yehova. M’bale wina amene mkazi wake anacita cigololo n’kumusiya anati: “Zinanivuta kukhulupilila kuti zimenezi zanicitikiladi. N’nadzimva wacabecabe, wokhumudwa, komanso wacisoni.” Ngati winawake anakugwilitsam’poni mwala kapena kukukhumudwitsani kwambili, mungalimbikitsidwe kudziŵa kuti Yehova sadzakusiyani. M’bale amene tam’chulayu anawonjezela kuti: “Si nthawi zonse pamene anthu angakhale okhulupilika kwa ife, koma Yehova ni wokhulupilika nthawi zonse. Mulimonse mmene zingakhalile, Yehova amatithandiza. Sadzasiya atumiki ake okhulupilika.” (Sal. 37:28) Nthawi zonse muzikumbukila kuti Yehova amakukondani kwambili kuposa mmene munthu wina aliyense angakukondeleni. Ngakhale kuti kugwilitsidwa mwala kumapweteka kwambili, sikungapangitse Yehova kuleka kukukondani. (Aroma 8:38, 39) Mfundo ni yakuti: Mosasamala kanthu zoipa zimene munthu anakucitilani, Atate wanu wa kumwamba amakukondani.
14. Kodi Salimo 34:18 limatitsimikizila ciyani?
14 Cinanso cingatilimbikitse ni mawu a Davide opezeka pa Salimo 34:18. (Ŵelengani.) Buku lina lofotokozela mawu a m’Baibo linakamba kuti mawu a pa lembali akuti “anthu amene akudzimvela cisoni mumtima mwawo,” angatanthauze “awo amene alibe ciyembekezo ca zabwino zilizonse.” Kodi Yehova amawathandiza bwanji awo amene amamva conco cifukwa cogwilitsidwa mwala? Monga mmene kholo lacikondi limagwilila dzanja mwana wake na kum’tonthoza, Yehova nayenso “ali pafupi” na aliyense wa ife. Tikamavutika cifukwa munthu winawake anatigwilitsa mwala kapena kutisiya, Yehova saleka kutimvela cifundo ndipo saleka kutithandiza. Ni wofunitsitsa kutitonthoza komanso kutikhazika mtima pansi tikamamva ululu mumtima. Ndipo watilonjeza zinthu zambili zimene tikuyembekezela m’tsogolo. Zinthu zimenezo zimatithandiza kupilila mavuto athu palipano.—Yes. 65:17.
MUKAGWETSA MISOZI CIFUKWA COSOWA MTENGO WOGWILA
15. N’ciyani cinapangitsa Hezekiya kulila?
15 Ali na zaka 39, Mfumu Hezekiya wa ku Yuda anayamba kudwala mwakayakaya. Mneneli Yesaya atatumidwa na Yehova, anapita kukauza Hezekiya kuti adzamwalila na matenda akewo. (2 Maf. 20:1) Hezekiya atamva uthengawo, anamva cisoni cofa naco moti analila mosaneneka. Hezekiya anapemphela kwa Yehova mocondelela.—2 Maf. 20:2, 3.
16. Kodi Yehova anacitapo ciyani pa kulila kocondelela kwa Hezekiya kopempha thandizo?
16 Yehova anakhudzika mtima na misozi ya Hezekiya, ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Ndamva pemphelo lako ndipo ndaona misozi yako. Ndikucilitsa.” Kudzela mwa Yesaya, Yehova mwacifundo cake analonjeza Hezekiya kuti adzatalikitsa moyo wake, komanso kuti adzapulumutsa Yerusalemu m’manja mwa Asuri.—2 Maf. 20:4-6.
17. Kodi Yehova amatithandiza bwanji tikamakumana na mavuto aakulu a thanzi? (Salimo 41:3) (Onaninso cithunzi.)
17 Zimene tiphunzilapo. Kodi muli na vuto la thanzi limene likuoneka ngati lilibe mankhwala? Uzani Yehova mmene mukumvela, ndipo iye adzakumvetselani ngakhale kuti mukulila pamene mukukamba naye. Baibo imatitsimikizila kuti “Bambo wacifundo cacikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” adzatitonthoza m’masautso athu onse. (2 Akor. 1:3, 4) Masiku ano, sitiyembekezela Yehova kuticotsela mavuto athu onse, koma tingamudalile kuti atithandize. (Ŵelengani Salimo 41:3.) Pogwilitsa nchito mzimu wake woyela, Yehova amatipatsa nyonga, nzelu, komanso mtendele wamumtima kuti tipilile. (Miy. 18:14; Afil. 4:13) Amatilimbikitsanso mwa kutipatsa ciyembekezo cozikika m’Baibo cakuti m’tsogolo adzacotsapo matenda a mtundu uliwonse.—Yes. 33:24.
18. Ni lemba liti limene limakulimbikitsani mukakumana na mavuto aakulu? (Onani danga lakuti “ Malemba Amene Angatitonthoze Pamene Tikulila.”)
18 Hezekiya analimbikitsidwa na mawu amene Yehova anamuuza. Nafenso tingapeze cilimbikitso m’Mawu a Mulungu. Tikakumana na mavuto, mawu a Yehova a m’Baibo angatitonthoze na kutithandiza kukhalabe odekha. (Aroma 15:4) Mlongo wina wa ku West Africa atamupeza na matenda a khansa, anali kungokhalila kulila. Iye anati: “Lemba limene limanitonthoza kwambili ni Yesaya 26:3. Ngakhale kuti palipano sitingakwanitse kucotsa mavuto amene tikukumana nawo, vesi limeneli limatitsimikizila kuti Yehova angatipatse mtendele wamumtima umene tikufunikila kuti utithandize kupilila mavutowo.” Kodi pali lemba linalake limene limakulimbikitsani kwambili mukamakumana na mavuto enaake aakulu, mwina okupangitsani kuona ngati palibe ciyembekezo?
19. N’zabwino zotani zimene tikuyembekezela m’tsogolo?
19 Tili pa cimake ca masiku otsiliza, ndipo tikuyembekezela kuti mavuto amene amaticititsa kugwetsa misozi adzawonjezeka. Koma monga taonela ku zitsanzo za Hana, Davide, na Mfumu Hezekiya, Yehova amaona tikamagwetsa misozi ndipo zimam’khudza kwambili. Misozi yathu ni yamtengo wapatali kwa iye. Conco tikakumana na mavuto, tizikhutula za mumtima mwathu kwa iye kudzela m’pemphelo. Tiyenela kupewa kudzipatula kwa abale na alongo athu mumpingo. Ndipo tiyeni tipitilize kupeza cilimbikitso m’mawu otonthoza a m’Baibo. Tisakaikile kuti tikapitiliza kupilila mokhulupilika, Yehova adzatipatsa mphoto. Mphoto imeneyi iphatikizapo lonjezo labwino kwambili lakuti iye adzacotsapo misozi yonse yomwe imabwela cifukwa ca cisoni, kukhumudwitsidwa, komanso cifukwa cosoŵa mtengo wogwila. (Chiv. 21:4) Panthawi imeneyo, tizidzangogwetsa misozi ya cisangalalo.
NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’