NKHANI YOPHUNZILA 49
NYIMBO 147 Lonjezo la Moyo Wamuyaya
N’zotheka Kwa Inu Kukakhala na Moyo Wosatha—Motani?
“Aliyense wovomeleza Mwana komanso kumukhulupilila [adzakhala] ndi moyo wosatha.”—YOH. 6:40.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Madalitso amene odzodzedwa komanso a nkhosa zina adzapeze cifukwa ca nsembe ya Yesu Khristu.
1. Kodi ena amaganiza ciyani akamva za kukhala na moyo wosatha?
ANTHU ambili amasamala posankha zimene afuna kudya, ndipo ali na pulogilamu yokhazikika yocita maseŵela olimbitsa thupi. Iwo amacita zimenezo pofuna kukhala athanzi. Ngakhale n’telo, iwo amadziŵa kuti zinthu zimenezo sizingacititse kuti asamakalambe kapenanso kufa. Kwa ena, kukhala na moyo wosatha kungaoneke kosatheka komanso kosakhumbilika maka-maka akaganizila mavuto amene amabwela kaamba ka ukalamba. Koma Yesu anakamba zabwino zokhudza “moyo wosatha,” monga ionetsela Yohane 3:16 na 5:24.
2. Kodi Yohane caputala 6 imakamba zotani zokhudza moyo wosatha? (Yohane 6:39, 40)
2 Tsiku lina, Yesu anadyetsa khamu la anthu lofika m’masauzande pomwe anaculukitsa mikate na nsomba. a Zimenezo zinali zodabwitsa, koma zomwe anakamba tsiku lotsatila zinali zodabwitsa kwambili kuposa cocitikaco. Khamu la anthu linam’tsatila ku Kaperenao. Ndipo ali kumeneko m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya, anawauza kuti iye angadzaukitse anthu amene anamwalila, ndipo anthuwo angadzakhale na moyo wosatha. (Ŵelengani Yohane 6:39, 40.) Malinga na mawuwo, ganizilani za mabwenzi anu komanso okondedwa anu ena amene anamwalila. Mawu a Yesu amenewo aonetsa kuti anthu ambili amene anamwalila angadzaukitsidwe, ndipo inuyo pamodzi na okondedwa anu mungadzakhale na moyo wosatha. Komabe anthu ambili akhala akuvutika kumvetsa mawu a m’mavesi ena opezeka mu Yohane caputala 6 amene Yesu anakamba. Tiyeni tiwakambilane mwacifatse mawu amenewo.
3. Malinga na Yohane 6:51, kodi Yesu anakamba zotani zokhudza iyemwini?
3 Yesu atadyetsa khamulo mozizwitsa, anthuwo anaganizila za mana amene Yehova anali kupeleka kwa makolo awo akale m’cipululu. Ndipo Malemba amanena kuti mana anali “cakudya cocokela kumwamba.” (Sal. 105:40; Yoh. 6:31) Yesu anaseŵenzetsa mana ngati maziko a zinthu zotsatila zimene anawaphunzitsa. Ngakhale kuti mana anali cakudya cozizwitsa cocokela kwa Mulungu, amene anadya cakudyaco mkupita kwa nthawi anafa. (Yoh. 6:49) Koma mosiyana na zimenezi, Yesu anakamba kuti iye anali “cakudya ceniceni cocokela kumwamba,” “cakudya cimene Mulungu wapeleka,” komanso “cakudya copatsa moyo.” (Yoh. 6:32, 33, 35) Yesu anafotokoza kusiyana kwakukulu kumene kunalipo pakati pa iye na mana. Iye anati: “Ine ndine cakudya camoyo cocokela kumwamba. Ngati wina atadya cakudya cimeneci adzakhala ndi moyo wosatha.” (Ŵelengani Yohane 6:51.) Ayudawo anakhumudwa na mawu amenewa. Iwo sanamvetse cifukwa cake Yesu anakamba kuti anali “cakudya” cocokela kumwamba comwe cinali coposa mana amene Mulungu anali kupeleka kwa makolo awo akale mozizwitsa. Pofuna kuwathandiza kumvetsa zimene anali kukamba, iye anawauza kuti: “Cakudya cimene nidzapeleke . . . ndi mnofu wangawu.” Kodi iye anali kutanthauza ciyani? Tiyenela kumvetsa zimene anali kutanthauza cifukwa yankho lake lionetsa zimene zinacititsa kuti zikhale zotheka ifeyo komanso okondedwa athu kukapeza moyo wosatha. Tiyeni tione zimene Yesu anali kutanthauza.
MKATE WOPATSA MOYO KOMANSO THUPI LAKE
4. N’cifukwa ciyani ena anadabwa na zimene Yesu anakamba?
4 Ena mwa anthu amene anali kumumvetsela Yesu, anadabwa pomwe iye anakamba kuti: “Cakudya cimene ndidzapeleke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.” N’kutheka kuti iwo anaganiza kuti Yesu adzawapatsa thupi lake lenileni kuti adye, komwe kukanakhala kudya munthu. (Yoh. 6:52) Onani mfundo inanso imene inawadabwitsa. Yesu anawauza kuti: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo wosatha.”—Yoh. 6:53.
5. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti Yesu sanali kuuza gulu la anthuwo kuti limwe magazi ake enieni?
5 M’masiku a Nowa, Mulungu analetsa anthu kuti asamadye magazi. (Gen. 9:3, 4) Yehova anabwelezanso lamulo limeneli m’Cilamulo cimene anapatsa Aisiraeli. Aliyense wodya magazi anayenela ‘kuphedwa.’ (Lev. 7:27) Yesu anali kulitsatila lamulo limenelo. (Mat. 5:17-19) Conco, zinali zosatheka kuti iye auze khamu la Ayudawo kuti lidye mnofu wake komanso kumwa magazi ake. Koma pokamba mawu amenewo, Yesu anali kungofuna kuphunzitsa anthuwo zimene anayenela kucita kuti akapeze “moyo wosatha.”—Yoh. 6:54.
6. N’cifukwa ciyani tingakambe kuti mawu a Yesu akuti anthuwo anayenela kudya mnofu wake na kumwa magazi ake anali okuluwika?
6 Kodi mfundo ya Yesu inali yotani pamenepa? N’zoonekelatu kuti Yesu anali kulankhula na khamu la anthuwo poseŵenzetsa mawu okuluwika. Iye anali atacitapo zimenezi kumbuyoku pamene anali kulankhula na mkazi wacisamariya, pomwe anati: “Amene adzamwe madzi amene ine ndidzamupatse sadzamvanso ludzu ngakhale pangʼono. Madzi amene ndidzamupatsewo adzasanduka kasupe wa madzi amene akutuluka mwa iye nʼkumupatsa moyo wosatha.” (Yoh. 4:7, 14) b Yesu sanali kutanthauza kuti mayi wacisamariyayo angapeze moyo wosatha ngati wamwa madzi enaake a pacitsime. Mofananamo, iye sanali kutanthauza kuti khamu la anthu limene anakamba nalo ku Kaperenao, lingapeze moyo wosatha ngati lingadye thupi lake lenileni komanso kumwa magazi ake enieni.
ZOCITIKA ZIŴILI ZOSIYANA
7. Kodi anthu ena amanena zotani pa mawu a Yesu a pa Yohane 6:53?
7 Anthu ena acipembedzo amakamba kuti mawu a Yesu a pa Yohane 6:53, onena kuti anthu ayenela kudya mnofu wake komanso kumwa magazi ake, anali kuonetsa zimene anthu ayenela kucita pa Mgonelo wa Ambuye. Iwo amanena zimenezi pokamba kuti Yesu anaseŵenzetsa mawu ofanana poyambitsa Mgonelo wa Ambuye. (Mat. 26:26-28) Iwo amanena kuti aliyense amene wapezeka pa Mgonelo wa Ambuye ayenela kudya mkate komanso kumwa vinyo umene umapelekedwa pa cocitikaco. Koma kodi zimenezi n’zoona? M’pofunika kwambili kuti timvetse bwino nkhani imeneyi cifukwa caka ciliconse, anthu ofika m’mamiliyoni kuzungulila dziko lonse amakhala nafe pa Mgonelo wa Ambuye. Tidzaona mfundo zingapo zimene zimasiyanitsa mawu a Yesu a pa Yohane 6:53 komanso amene iye anakamba pa Mgonelo wa Ambuye.
8. Ni mfundo ziŵili ziti zimasiyanitsa zocitika zimene tachula? (Onaninso zithunzi.)
8 Tiyeni tikambilane mfundo ziŵili zimene zimasiyanitsa zocitika ziŵilizi. Coyamba, ni liti komanso ni kuti kumene Yesu anakambila mawu a pa Yohane 6:53-56? Anakamba mawuwo ku khamu la Ayuda pomwe anali ku Galileya mu 32 C.E. Yesu anakamba mawuwo kutatsala caka pafupifupi cimodzi kuti ayambitse Mgonelo wa Ambuye ku Yerusalemu. Caciŵili, kodi pa zocitikazo anali kulankhula kwa ndani? Pa cocitika ca mu Yohane caputala 6, Yesu anali kulankhula kwa anthu amene anaika kwambili maganizo awo pa kukhutilitsa zosoŵa zawo zakuthupi, zomwe zinali zosakhalitsa, m’malo mokhutilitsa zofuna zawo zauzimu. (Yoh. 6:26) Ni iko komwe, pamene Yesu anakamba zinazake zimene anthuwo sanamvetse, nthawi yomweyo anasiya kumukhulupilila. Ngakhale ena mwa ophunzila ake anasiya kumutsatila. (Yoh. 6:14, 36, 42, 60, 64, 66) Koma zimenezi n’zosiyana na zimene zinacitika patapita caka cimodzi pamene Yesu anali kuyambitsa Mgonelo wa Ambuye mu 33 C.E. Pa cocitika cimeneco, atumwi ake okhulupilika 11 anakhalabe naye ngakhale kuti sanamvetse zonse zimene iye anali kuphunzitsa. Ngakhale n’telo, mosiyana na ambili amene anali ku Galileya, atumwi ake okhulupilika anali otsimikiza kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu komanso kuti anatsika kucokela kumwamba. (Mat. 16:16) Iye anawayamikila powauza kuti: “Inu ndi amene mwakhalabe ndi ine m’mayeselo anga.” (Luka 22:28) Mfundo ziŵili zokhazi zimene takambilana, zionetsa kuti mawu a Yesu a pa Yohane 6:53 saonetsa mmene Mgonelo wa Ambuye uyenela kucitikila. Ndipo pali umboni wina wotsimikizila mfundo imeneyi.
ZIMENE YESU ANAKAMBA INUNSO ZIKUKHUDZANI
9. Kodi mawu amene Yesu anakamba pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye anali kukamba za ndani?
9 Pamene Yesu anali kuyambitsa Mgonelo wa Ambuye, anapatsa ophunzila ake mkate wopanda cofufumitsa ndipo anawauza kuti unali kuimila thupi lake. Kenako atawapatsa kapu ya vinyo, anawauza kuti vinyowo unali kuimila “magazi [ake] a pangano.” (Maliko 14:22-25; Luka 22:20; 1 Akor. 11:24) Mfundo imene Yesu anakamba yokhudza pangano latsopano ni yofunika kwambili. Pangano limeneli limapangidwa na a ‘m’nyumba [yauzimu] ya Isiraeli,’ amene adzalamulila pamodzi na Yesu “mu Ufumu wa Mulungu,” osati mtundu wonse wa anthu. (Aheb. 8:6, 10; 9:15) Atumwiwo anali asanamvetse mfundo imeneyi pa nthawiyo. Koma posakhalitsa, iwo anali kudzadzozedwa na mzimu woyela, na kudzaloŵa m’pangano latsopano kuti akakhale na Yesu kumwamba.—Yoh. 14:2, 3.
10. N’kusiyana kuti komwe kulipo pakati pa zimene Yesu anakamba pomwe anali ku Galileya na zomwe anakamba pa Mgonelo wa Ambuye? (Onaninso cithunzi.)
10 Zimene Yesu anakamba pa Mgonelo wa Ambuye zinali kupita kwa kagulu kocepa kochedwa “kagulu ka nkhosa.” Atumwi ake okhulupilika amene analipo pomwe anali kuyambitsa mwambowo, ndiwo anayambilila kukhala m’kagulu kocepa kameneka. (Luka 12:32) Iwo anayenela kudya mkate komanso kumwa vinyo. Enanso amene anali kudzakhala m’kagulu kameneka, nawonso anayenela kudya mkate komanso kumwa vinyo pocita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye. Anthu amenewa ndiwo adzapita kumwamba kukakhala na Yesu. Conco, uku ndiko kusiyana kwina pakati pa zimene Yesu anauza atumwi ake pa Mgonelo wa Ambuye na zomwe anakamba ku khamu la Ayuda pomwe anali ku Galileya. Zimene iye anakamba pa Mgonelo wa Ambuye zimagwila nchito kokha kwa anthu a m’kagulu kocepa. Koma zimene Yesu anakamba pomwe anali pafupi na mzinda wa Kaperenao, zigwila nchito kwa anthu osaŵelengeka.
11. N’ciyani cimene Yesu anakamba ku Galileya cimene cionetsa kuti sanali kukamba za kagulu kocepa?
11 Ambili mwa anthu amene Yesu anali kukamba nawo ku Galileya mu 32 C.E., anali kungofuna cakudya cina kwa iye. Komabe, Yesu anayesetsa kuwathandiza anthuwo kumvetsa kuti panali cinthu cinacake cofunika kwambili kuposa cakudya. Cinthuco cikanawathandiza kukapeza moyo wosatha. Ndipo Yesu anati anthu amene anamwalila angadzaukitsidwe pa tsiku lomaliza na kudzakhala na moyo wosatha. Pokamba mawu amenewa, Yesu sanali kukamba za anthu ocepa, monga momwe zinalili pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye. M’malomwake, iye anali kukamba za madalitso amene anthu onse adzalandile. Ndiye cifukwa cake iye anakamba kuti: “Ngati wina atadya cakudya cimeneci adzakhala ndi moyo wosatha. Ndipotu cakudya cimene ndidzapeleke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.”—Yoh. 6:51.
12. Kodi munthu ayenela kucita ciyani kuti akalandile dalitso la moyo wosatha limene Yesu anakambapo?
12 Yesu sanauze Ayuda ku Galileya kuti dalitso limeneli la moyo wosatha lidzabwela kwa wina aliyense amene anakhalako na moyo, kapena kwa wina aliyense amene adzabadwe m’tsogolo. Koma kwa okhawo amene ‘amadya cakudya cimeneci,’ kutanthauza amene amakhulupilila Yesu. Anthu ambili masiku ano amakamba kuti amakhulupilila Yesu ndipo amamucha kuti ni mpulumutsi wawo. (Yoh. 6:29) Koma zimenezi si zokwanila. Ayuda ambili a ku Galileya poyamba anamukhulupilila Yesu koma m’kupita kwa nthawi anamusiya. N’cifukwa ciyani anamusiya?
13. Kodi munthu ayenela kucita ciyani kuti akhale wotsatila weniweni wa Khristu?
13 Ambili mwa anthu m’khamulo anali kutsatila Yesu cifukwa ca zinthu zimene anawacitila. Iwo anali kufuna kuti awacilitse mozizwitsa, kuwapatsa cakudya caulele, komanso kuti awaphunzitse zinthu zimene zinali kuwasangalatsa. Koma Yesu anawauza momveka bwino kuti sanangobwela padziko lapansi kudzapatsa anthuwo zimene anali kufuna, koma kuti anabwela kudzawaphunzitsa zimene anayenela kucita kuti akhale otsatila ake enieni. Iwo anafunika “kubwela kwa” iye mwa kumumvela komanso kutsatila zonse zimene anali kuphunzitsa.—Yoh. 5:40; 6:44.
14. Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na mnofu wa Yesu komanso magazi ake?
14 Yesu anaphunzitsa khamu la anthuwo kuti mwa kupeleka thupi lake komanso magazi ake monga nsembe, adzapangitsa kuti zikhale zotheka kwa iwo kukapeza moyo wosatha. Anthuwo anafunika kukhulupilila mfundo ya coonadi imeneyi. Kukhulupilila zimenezi kunali kofunika kwa Ayuda, ndipo kukali kofunikanso kwa ife masiku ano. (Yoh. 6:40) Inde, kuti tikapindule cifukwa ca mnofu wa Yesu komanso magazi ake zochulidwa pa Yohane 6:53, tiyenela kuonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo. N’zotheka anthu osaŵelengeka kukapeza dalitso la moyo wosatha.—Aef. 1:7.
15-16. Kodi taphunzila mfundo zofunika ziti mu Yohane caputala 6?
15 Mu Yohane caputala 6 timaphunzilamo zinthu zambili zomwe ni zofunika komanso zolimbikitsa kwa ife na okondedwa athu. Caputala cimeneci cimaonetsa bwino kuti Yesu amasamala kwambili za anthu. Pomwe iye anali ku Galileya, anacilitsa odwala, kuphunzitsa za Ufumu, ndipo anawapatsa cakudya cimene anali kufunikila. (Luka 9:11; Yoh. 6:2, 11, 12) Koma coposa zonse, anaphunzitsa kuti iye ndiye “cakudya copatsa moyo.”—Yoh. 6:35, 48.
16 A “nkhosa zina” sayenela kudya mkate kapena kumwa vinyo pocita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye. (Yoh. 10:16) Ngakhale n’telo, iwo amapindula na mnofu wa Yesu Khristu komanso magazi ake. Amacita zimenezi poonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo ya Yesu komanso mu madalitso amene nsembeyo imatheketsa. (Yoh. 6:53) Mosiyanako na zimenezi, awo amene amadya mkate komanso kumwa vinyo, amaonetsa kuti analowa m’pangano latsopano ndipo ali na ciyembekezo cokalamulila monga mafumu kumwamba. Conco, kaya ndife a nkhosa zina kapena odzozedwa, nkhani ya mu Yohane caputala 6 ili na mfundo zofunika kwambili kwa tonsefe. Imatiphunzitsa kuti tonsefe tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba mu nsembe ya dipo kuti tikakhale na moyo wosatha.
NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu