MBILI YANGA
Sin’nasiye Kuphunzila
NIMAYAMIKILA Yehova pokhala “Mlangizi [wanga] wamkulu.” (Yes. 30:20) Amaphunzitsa alambili ake kudzela m’Mawu ake Baibo, m’cilengedwe cake codabwitsa, komanso gulu lake. Ndipo amaseŵenzetsanso abale na alongo athu potithandiza. Ngakhale kuti nili na zaka 97, nikupitilizabe kupindula na malangizo a Yehova m’njila zosiyanasiyana. Lekani nikufotokozeleni cifukwa cake zili conco.
N’nabadwa m’caka ca 1927 m’tauni yaing’ono ya Illinois, yomwe ili pafupi na mzinda wa Chicago ku America. M’banja mwathu tilimo ana asanu—Jetha, Don, ine, Karl, na Joy. Tonse tinali ofunitsitsa kutumikila Yehova na mtima wathu wonse. Jetha analoŵa nawo kalasi ya nambala 2 ya Giliyadi mu 1943. Don anapita kukatumikila ku Beteli ya ku Brooklyn, New York mu 1944. Karl anatsatilapo mu 1947, ndipo Joy anapita mu 1951. Citsanzo cawo cabwino komanso ca makolo anga cinanilimbikitsa kufuna kucita zambili potumikila Yehova.
MMENE BANJA LATHU LINAPHUNZILILA COONADI
Atate na amayi anali kuŵelenga kwambili Baibo, ndipo anali kumukonda Mulungu. Iwo anaphunzitsanso ife ana kumukonda. Komabe atate anasiya kulemekeza machalichi pambuyo potumikila monga msilikali wa ku Europe pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Amayi anayamikila kwambili Mulungu cifukwa cakuti atate anabwelako amoyo ku nkhondo. Conco iwo anati kwa atate: “A Karl, tiyeni tipite ku chalichi mmene tinali kucitila kale.” Atate anayankha kuti: “Nidzakupelekezani kumeneko, koma ine sinidzaloŵa.” Amayi anafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani simudzaloŵa?” Atate anayankha kuti: “Atsogoleli acipembedzo cofanana a maiko olimbanawo, anali kudalitsa asilikali a dziko lawo pa nkhondoyo. Kodi Mulungu anali kucilikiza asilikali a mbali zonse ziŵili?”
Tsiku lina pomwe amayi anali kuchalichi, amuna aŵili a Mboni za Yehova anafika panyumba yathu. Iwo anapatsa atate mabuku aŵili othandiza kuphunzila Baibo ochedwa Light, omwe anali kufotokoza za m’buku la Chivumbulutso. Atate anacita cidwi na mabukuwo ndipo anayalandila. Amayi ataona mabukuwo, anayamba kuwaŵelenga. Kenako tsiku lina, amayi anaona cilengezo m’nyuzipepala inayake yopempha amene angakonde kukaphunzila Baibo poseŵenzetsa mabuku a Light. Conco, iwo anapita. Atafika kumalo okumanako, mayi wacikalambile anatsegula citseko. Amayi anatulutsa imodzi mwa mabukuwo, ndipo anafunsa mzimayiyo kuti, “Kodi maphunzilo a mabukuwa mucitila kuno?” Mzimayiyo anayankha kuti: “Inde okondedwa, loŵani.” Mlungu wotsatila, amayi anatenga ana tonse popita kumeneko, ndipo kuyambila nthawiyo tinayamba kupezekapo nthawi zonse.
Pa msonkhano wina, wotsogoza ananipempha kuŵelenga lemba la Salimo 144:15, limene limati osangalala ni anthu amene amalambila Yehova. Mawu a pa lembali ananifika pamtima, monga mmene zinalili na 1 Timoteyo 1:11, imene imati Yehova ni “Mulungu wacimwemwe,” komanso Aefeso 5:1, imene inanilimbikitsa kuti ‘nizitsanzila Mulungu.’ N’nazindikila kuti niyenela kukhala wacimwemwe pa zomwe ningakwanitse kucitila Mlengi wanga, komanso kumuyamikila pa mwayi womutumikila. Mfundo zimenezi za coonadi, zakhala mbali yofunika kwambili ya umoyo wanga.
Mpingo wapafupi na kumene n’nali kukhala, unali pa mtunda wa makilomita 32 kucokela ku Chicago. Ngakhale n’telo, tinali kupezeka ku misonkhano, ndipo cidziŵitso canga pa Baibo cinakulilako. Nikumbukila kuti panthawi ina, wotsogoza anapatsa mwayi Jetha kuti apelekepo ndemanga. Pomwe n’nali kumvetsela Jetha akupeleka ndemanga, mumtima mwanga n’nati: ‘N’nali kulidziŵa yankho limeneli. Nikanakweza dzanja kuti nipelekepo ndemanga.’ Kuyambila nthawi imeneyo, n’nayamba kukonzekela misonkhano komanso kuyankhapo m’mawu anga-anga. Koma cofunika kwambili n’cakuti monga mmene zinalili na azibale anga komanso azilongo anga, n’nakula kuuzimu. Conco n’nabatizika mu 1941.
KUPHUNZILA ZA YEHOVA PA MISONKHANO IKULU-IKULU
Nimakumbukila kwambili za msonkhano umene unacitikila ku Cleveland, Ohio mu 1942. Abale na alongo a m’mizinda yoposa 50 ya ku America analumikiza kudzela pa foni kuti amvetsele msonkhanowo. Banja lathu linali kukhala m’matenti pamodzi na mabanja ena pafupi na malo a msonkhanowo. Nkhondo yaciŵili ya padziko lonse inali mkati, ndipo a Mboni za Yehova anali kutsutsidwa kwambili. Madzulo n’nali kuona gulu la abale likuimika magalimoto awo, ndipo nyale za magalimotowo zinali kupenya kunja kwa malo a msonkhano. Onse anagwilizana kuti azisiya munthu m’motoka iliyonse kuti azilondela usiku wonse. Ngati abalewo azindikila kuti pakufika mdani, anafunika kuyatsa nyale zamagalimotozo na kuunika adaniwo kuti awatowe m’maso, kenako kuliza mahuta amagalimotowo. Ndipo abale ena anali kufunika kuthamangilako kuti akathandize abale athu. Zimenezi zinanipangitsa kuganizila kuti, ‘Anthu a Yehova amakhala okonzeka pa ciliconse!’ Makonzedwe amenewa ananitsimikizila kuti tinali otetezeka. Conco n’nali kugona mwamtendele ndipo palibe ciliconse coipa cinacitika.
Patapita zaka zambili n’takumbukila za msonkhano uja, n’nazindikila kuti amayi anga sanaonetse mantha alionse kapena nkhawa. Iwo anali kudalila Yehova na gulu lake. Sin’dzaiŵala citsanzo cawo cabwino.
Pasanapite nthawi yaitali kucokela pa msonkhano uja, amayi anakhala mpainiya wa nthawi zonse. Iwo anali kumvetsela mwachelu ku nkhani zokamba za utumiki wa nthawi zonse. Pomwe tinali kubwelela kunyumba, amayi anakamba kuti, “Ningakonde kupitiliza kucita upainiya, koma siningakwanitse kutelo cifukwa nifunikila kusamalila nyumba yathu.” Conco anatipempha ngati tingawathandize. Titavomela, anagaŵila aliyense wa ife cipinda cimodzi kapena ziŵili kuti tiziyeletsa tisanadye cakudya cam’mawa. Tikapita kusukulu, iwo anali kuona ngati zonse zinali bwino panyumba, kenako anali kupita mu ulaliki. Anali mayi wotangwanika, koma sanatinyalanyaze ife ana. Tikabwela kunyumba kuti tidye cakudya camasana komanso tikaweluka kusukulu, iwo nthawi zonse anali kuceza nafe. Masiku ena tikaweluka kusukulu, tinali kupita nawo mu ulaliki. Izi zinatithandiza kumvetsa zimene kukhala mpainiya kumalowetsamo.
KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
N’nayamba kucita upainiya nili na zaka 16. Ngakhale kuti atate anali asanakhale Mboni, iwo anali na cidwi cofuna kudziŵa mmene zinthu zinali kuyendela mu utumiki wanga. Tsiku lina usiku, ninawauza kuti mosasamala kanthu za khama limene nacita, nalephela kupeza munthu woti niziphunzitsa Baibo. N’naima pang’ono, kenako n’nawafunsa kuti, “Kodi mungakonde kuti nizikuphunzitsani Baibo?” Ataganizilapo pang’ono ananiyankha kuti, “Niona kuti palibe cifukwa cingalepheletse kuti uziniphunzitsa Baibo.” Conco phunzilo langa loyamba la Baibo linali atate. Cimeneci cinali cinthu capadela kwambili kwa ine!
Tinayamba kuphunzila buku lakuti “The Truth Shall Make You Free.” M’kupita kwa nthawi, n’nazindikila kuti atate anali kunithandiza kukhala wophunzila wabwino komanso mphunzitsi wabwino. Mwacitsanzo, tsiku lina usiku titaŵelenga ndime, iwo anati: “Namva zimene ndime iyi ikukamba. Koma kodi udziŵa bwanji kuti bukuli likukamba zoona?” Sin’nali wokonzeka kuwayankha. Conco n’nawauza kuti, “Palipano nilibe yankho, koma pa phunzilo lotsatila nidzakupatsani yankho.” Ndipo ninakwanitsadi kuwayankha. N’napeza mavesi amene anali kugwilizana kwambili na mfundo zimene tinali kuphunzila. Kuyambila nthawiyo, n’nayamba kukonzekela bwino phunzilo lathu, ndipo n’naphunzila kufufuza. Izi zinanithandiza kuti nikule kuuzimu, ndiponso zinathandiza atate kucita cimodzimodzi. Iwo anali kuseŵenzetsa zimene anali kuphunzila, ndipo anabatizika mu 1952.
N’NAKHALA NA COLINGA CATSOPANO COFUNA KUWONJEZELA MAPHUNZILO
N’nacoka panyumba nili na zaka 17. Jetha a anakhala mmishonale, ndipo Don anapita kukatumikila ku Beteli. Onse anali kuwakonda mautumiki awo, ndipo izi zinanilimbikitsa kwambili. Conco, n’nafunsila zonse ziŵili, utumiki wa pa Beteli komanso kukaloŵa Sukulu ya Giliyadi. Nitatelo, n’nasiya nkhani yonse m’manja mwa Yehova. Ndipo zotulukapo zake n’zakuti, n’naitanidwa kukatumikila ku Beteli mu 1946.
Kwa zaka, nacitako mautumiki osiyanasiyana pa Beteli, ndipo naphunzila zinthu zambili. Kwa zaka 75 zimene natumikila pa Beteli, naphunzila nchito yopulinta mabuku komanso ya maakaunti. Naphunzilanso kugula katundu amene tingaseŵenzetse pa Beteli, komanso kutumiza katundu wofunika ku malo ena. Koposa zonse, nimapindula kwambili na maphunzilo akuuzimu amene Beteli limapeleka kupitila m’pulogilamu ya kulambila kwa m’mawa, komanso m’mapulogilamu ena.
Naphunzilanso zambili kwa mng’ono wanga Karl, amene anayamba utumiki wa pa Beteli mu 1947. Iye anali wophunzila Baibo wakhama komanso mphunzitsi waluso wa Baibo. Panthawi ina n’namupempha kuti anithandize pomwe n’napatsidwa
nkhani. N’namufotokozela kuti napeza zofalitsa zambili koma sinidziŵa mmene ningaziseŵenzetsele m’nkhani yanga. Ananipatsa yankho ponifunsa funso limodzi lakuti, “Joel, kodi mutu wa nkhani yako ni wotani?” Nthawi yomweyo ninamvetsa mfundo yake yakuti niyenela kuseŵenzetsa zofalitsa zimene zigwilizana na mutu wa nkhani yanga na kusiya zinazo. Sinidzaiŵala mfundo imeneyo.Kuti tikhale acimwemwe pomwe tikutumikila pa Beteli, tiyenela kulalikila mokwanila, ndipo izi zingacititse kuti tikhale na zokumana nazo zolimbikitsa. Cocitika cosangalatsa cimene nikumbukila cinacitika madzulo enaake mumzinda wa New York. Ine na m’bale wina, tinayendela mayi wina amene kumbuyoko analandila magazini yathu ya Nsanja ya Mlonda na Galamuka! Tinadzidziwikitsa ndipo tinamuuza kuti, “Madzulo ano tikuthandiza anthu kuphunzila mfundo zolimbikitsa za m’Baibo.” Mzimayiyo anayankha kuti, “Ngati nkhani yake ni ya Baibo, loŵani.” Tinaŵelenga na kukambilana naye Malemba angapo ofotokoza Ufumu wa Mulungu, komanso dziko latsopano limene likubwela. Zimenezi ziyenela kuti zinam’fika pamtima cifukwa mlungu wotsatila anaitana mabwenzi ake angapo kuti adzakhale nafe pamakambilanowo. Pambuyo pake, iye na mwamuna wake anakhala atumiki okhulupilika a Yehova.
N’NAPHUNZILA ZAMBILI KWA MKAZI WANGA
N’taganiza zokwatila, panapita zaka ngati 10 kuti nipeze munthu woniyenelela. N’ciyani cinanithandiza kupeza mkazi woniyenelela? Ninapemphela kwa Yehova, ndipo ninaganizila zimene n’nali kufuna kucita pamodzi na mkazi wanga tikadzakwatilana.
Pamsonkhano wa mu 1953 umene unacitikila mu Yankee Stadium, ninakumana na mlongo wina dzina lake Mary Aniol. Iye na Jetha anali ataloŵela limodzi kalasi ya nambala 2 ya Giliyadi, ndipo anali kugwilila limodzi nchito yaumishonale. Mary ananifotokozela mwacimwemwe utumiki wake waumishonale ku Caribbean, komanso za maphunzilo a Baibo amene anali kutsogoza. Pamene tinali kuyendelana, tinazindikila kuti tinali na zolinga zauzimu zofanana. Cikondi cathu cinakula ndipo tinakwatilana mu April 1955. Mary anaonetsa m’njila zambili kuti anali mphatso yocokela kwa Yehova, ndiponso kuti anali citsanzo cabwino coyenela kutengela. Anali wacimwemwe na utumiki uliwonse umene anapatsidwa. Iye anali wakhama, anali kuika zofuna za ena patsogolo, ndipo anali kutsogoza za Ufumu paumoyo wake. (Mat. 6:33) Tinagwila nchito ya m’dela kwa zaka zitatu, ndipo mu 1958 tinaitanidwa kukatumikila ku Beteli.
N’naphunzila zambili kwa Mary. Mwacitsanzo, kuciyambi kwa ukwati wathu, tinasankha kuti tiziŵelengela pamodzi Baibo. Tinasankha kuti tsiku lililonse tiziŵelenga mavesi 15. Mmodzi wa ife akaŵelenga cigawo ca lemba, tinali kukambilana cigawo cimeneco na kuona mmene tingaseŵenzetsele mfundozo paumoyo wathu. Nthawi zambili Mary anali kuniuza zinthu zimene anaphunzila ku Giliyadi kapena mu utumiki wake waumishonale. Makambilano amenewa ananithandiza kukhala wozindikila, kukulitsa luso langa la kuphunzitsa m’nkhani zimene n’nali kukamba, komanso kudziŵa mopelekela cilimbikitso kwa alongo.—Miy. 25:11.
Mkazi wanga wokondeka Mary anamwalila mu 2013. Nikuyembekezela mwacidwi kudzamuona m’dziko latsopano! Koma palipano ndine wofunitsitsa kupitiliza kuphunzila komanso kudalila Yehova na mtima wanga wonse. (Miy. 3:5, 6) Nimalimbikitsidwa komanso kupeza cimwemwe nikaganizila zimene anthu a Yehova azidzacita m’dziko latsopano. Izi zidzaphatikizapo kuphunzila zinthu zatsopano zocokela kwa Mlangizi wathu wamkulu zokhudza iye! Inde, siningathe kumuyamikila mokwanila Yehova cifukwa ca zonse zimene waniphunzitsa kufika pano, komanso pa cisomo cake cacikulu.
a Onani mbili ya Jetha Sunal mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2003, tsa. 23-29.