Kodi Mukukumbukila?
Kodi munaŵelenga mosamala magazini a Nsanja ya Mlonda a caka cino? Ngati n’telo, yesani kupeza mayankho pa mafunso otsatilawa:
Kodi Yehova anapeleka citsanzo cotani ca mmene tingacitile nawo akazi?
Iye amacita nawo mopanda tsankho, ndipo sakonda kwambili amuna kuposa akazi. Mulungu amamvetsela kwa akazi, ndipo amasamala za mmene amamvela komanso nkhawa zimene ali nazo. Ndipo iye amawadalila kuti adzagwila nchito yake.—w24.01, mas. 15-16.
Kodi tingaseŵenzetse bwanji Aefeso 5:7, imene imati: “Conco musamacite zimene iwo amacita”?
Mtumwi Paulo anali kuticenjeza kuti tizipewa kuceza na anthu amene angatilepheletse kutsatila miyeso ya Yehova. Anthu amenewa si okhawo amene timaceza nawo pamaso-m’pamaso ayi, koma amaphatikizapo ngakhale aja amene timaceza nawo pa masamba amcezo.—w24.03, mas. 22-23.
Kodi tiyenela kupewa nkhani zabodza ziti?
Tiyenela kukhala osamala na nkhani zopanda umboni zocokela kwa abale na alongo, komanso mauthenga abodza ocokela kwa anthu amene sitiwadziŵa. Tiyenelanso kusamala na ampatuko amene amadzipanga kukhala na cidwi pa uthenga wathu.—w24.04, tsa. 12.
Kodi tidziŵa ciyani komanso sitidziŵa ciyani ponena za mmene Yehova adzaweluzila Mfumu Solomo, ndiponso aja amene anawonongedwa mumzinda wa Sodomu na Gomora, komanso amene anaphedwa pa Cigumula?
Sitinganene mwatsimitsimi kuti Yehova sadzakawaukitsa m’tsogolo. Ngakhale n’telo, tidziŵa kuti Yehova ndiye adziŵa zonse ndipo ali na cifundo cacikulu.—w24.05, mas. 3-4.
Mulungu pokhala “Thanthwe,” kodi amatitsimikizila ciyani? (Deut. 32:4)
Tingapeze malo othaŵilapo acitetezo kwa Yehova. Iye ni wodalilika ndipo amasunga malonjezo ake. Yehova sasintha, ndipo makhalidwe ake na colinga cake sizisintha.—w24.06, mas. 26-28.
N’ciyani cingakuthandizeni mukasamukila mu mpingo watsopano?
Khalani na cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani mmene anathandizila atumiki ake a m’nthawi zakale. Pewani kuyelekezela mpingo wanu watsopano na mpingo wanu wakale. Muzitengamo mbali m’zocitika za mpingo wanu watsopano, ndipo muziyesetsa kupanga mabwenzi atsopano.—w24.07, mas. 26-28.
Kodi timapezamo maphunzilo ati m’mafanizo atatu opezeka mu Mateyo caputala 25?
Fanizo la nkhosa na mbuzi limagogomeza kufunika kokhala okhulupilika. Fanizo la anamwali ocenjela na anamwali opusa lifotokoza kufunika kokhala okonzeka komanso achelu. Ndipo fanizo la matalente lionetsa kufunika kocita zinthu mwakhama komanso kokhalabe maso.—w24.09, mas. 20-24.
Kodi khonde la kacisi wa Solomo linali lotalika motani?
Pa 2 Mbiri 3:4, mipukutu ina yakale imati khondelo linali lalitali “mikono 120,” zomwe zitanthauza kuti khondelo linali lalitali mamita 53. Pomwe Mabaibo ena amati linali lalitali “mikono 20,” zomwe zitanthauza kuti linali lotalika mamita 9. Mfundo yakuti khondeli linali lalitali mamita 9, ifanana na kucindikala (mtiga) kwa zipupa za kacisi ameneyu.—w24.10, tsa. 31.
Kodi zitanthauza ciyani mtumiki wothandiza kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi”? (1 Tim. 3:12)
Izi zitanthauza kuti anakwatila mkazi mmodzi cabe, ndipo sayenela kucita ciwelewele. Kuwonjezela apo, sayenela kukopana na akazi ena.—w24.11, tsa. 19.
N’cifukwa ciyani tingati Yohane 6:53 sifotokoza dongosolo la mmene Mgonelo wa Ambuye uyenela kucitikila?
Yohane 6:53 imakamba za kufunika kodya mnofu wa Yesu na kumwa magazi ake. Yesu anakamba mawu amenewa mu 32 C.E., ku Galileya kwa Ayuda amene anali kufunikila kuonetsa cikhulupililo cawo mwa iye. Komabe, dongosolo la mmene mwambo wa Mgonelo wa Ambuye uyenela kucitikila linakhazikitsidwa caka cotsatila ku Yerusalemu. Pa mwambowu, Yesu anakamba na aja amene adzalamulila naye kumwamba.—w24.12, mas. 10-11.