Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi “angelo ocita kusankhidwa” ochulidwa pa 1 Timoteyo 5:21 ndani?

Mtumwi Paulo analembela mkulu mnzake Timoteyo kuti: “Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu ndiponso angelo ocita kusankhidwa, kuti uzitsatila malangizo amenewa popanda tsankho kapena kukondela.”​—1 Tim. 5:21.

Coyamba, tiyeni tikambilane za amene sali pa gulu la angelo amenewa. Mwacionekele, si gulu la 144,000. Panthawi imene Paulo anali kulembela Timoteyo, Akhristu odzozedwa anali asanayambe kuukitsidwa kupita kumwamba. Atumwi komanso odzozedwa ena anali asanakhale zolengedwa zauzimu. Conco iwo sanali “angelo ocita kusankhidwa” amene akuchulidwa pa lembali.​—1 Akor. 15:50-54; 1 Ates. 4:​13-17; 1 Yoh. 3:2.

Cinanso, “angelo ocita kusankhidwa” amenewa si angelo amene anapanduka panthawi ya Cigumula. Angelo amenewo anali ku mbali ya Satana, ndipo anakhala ziŵanda. Conco anali adani a Yesu. (Gen. 6:2; Luka 8:​30, 31; 2 Pet. 2:4) M’tsogolo, iwo adzaponyedwa mumdima wandiweyani kwa zaka 1,000. Ndipo pambuyo pake, adzawonongedwa pamodzi na Satana Mdyelekezi.​—Yuda 6; Chiv. 20:1-3, 10.

“Angelo ocita kusankhidwa” amene Paulo anachula pa lembali ayenela kuti ni angelo okhulupilika amene amagwila nchito pamodzi na “Mulungu ndi Khristu Yesu.”

Pali angelo okhulupilika masauzande ambili. (Aheb. 12:22, 23) Sitiyenela kuganiza kuti angelo onse amagwila nchito yofanana panthawi imodzi. (Chiv. 14:17, 18) Kumbukilani kuti panthawi ina, mngelo mmodzi anapatsidwa nchito yakupha asilikali 185,000 a Asuri. (2 Maf. 19:35) Payenela kuti pali angelo ambili amene anapatsidwa nchito ‘yocotsa mu Ufumu wa [Yesu] zinthu zonse zopunthwitsa kuphatikizapo anthu osamvela malamulo.’ (Mat. 13:39-41) N’kuthekanso kuti angelo ena anapatsidwa nchito ‘yosonkhanitsa osankhidwa ake’ pamodzi kupita nawo kumwamba. (Mat. 24:31) Ndipo ena amalamulidwa kuti ‘atiteteze m’njila zathu zonse.’​—Sal. 91:11; Mat. 18:10; yelekezelani na Mateyo 4:11; Luka 22:43.

“Angelo ocita kusankhidwa” ochulidwa pa 1 Timoteyo 5:21, ayenela kuti ni angelo amene anapatsidwa udindo wapadela wothandiza kusamalila mipingo. Nkhani yonse imene Paulo anali kukamba ionetsa kuti iye anali kupeleka uphungu kwa akulu wa mmene angasamalilile maudindo awo. Anapelekanso uphungu kwa abale na alongo mumpingo wakuti ayenela kuonetsa akulu ulemu. Kumbali yawo, akulu ayenela kusamalila maudindo awo “popanda tsankho kapena kukondela,” ndipo sayenela kupanga cisankho kapena kupeleka cigamulo asanaganizilepo mosamala. Paulo anapeleka cifukwa comveka cimene akulu anayenela kutsatilila malangizo ake ouzilidwa. Iye anati akulu anali kutumikila abale awo “pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu ndiponso angelo ocita kusankhidwa.” Mawuwa aonetsa kuti Yehova, Yesu, komanso “angelo ocita kusankhidwa,” amaona mmene akulu amasamalilila mpingo. Conco, n’zoonekelatu kuti angelo ena ali na udindo wosamalila mpingo. Zina mwa zimene amacita ni kuteteza atumiki a Mulungu, kuwathandiza pa nchito yolalikila, komanso kuuza Yehova zimene amaona.​—Mat. 18:10; Chiv. 14:6.