MBILI YANGA
Coloŵa Cauzimu Cimene N’nalandila Cinanithandiza Kupita Patsogolo
TSIKU lina pakati pa usiku, ine na m’bale wina tinaimilila m’mbali mwa mtsinje wa Niger, umene m’mimba mwake ni waukulu pafupi-fupi makilomita 1.6, ndipo madzi ake amathamanga kwambili. Kuwoloka mtsinjewo kunali koopsa, cifukwa panthawiyo mu Nigeria munali nkhondo. Komabe, tinaika miyoyo yathu paciopsezo mwa kuwoloka mtsinjewo kangapo konse. Kodi cinacitika n’ciani kuti nipezeke kumeneko? Lekani nikusimbileni mbili yanga.
Mu 1913, atate, a John Mills anabatizika ku New York, ali na zaka 25. M’bale Russell ndiye anakamba nkhani ya ubatizo. Patapita nthawi yocepa, atate anakukila ku Trinidad. Kumeneko, anakwatila mlongo Constance Farmer, amene anali Wophunzila Baibo wakhama. Atate anali kuthandiza mnzawo, William R. Brown, kutambitsa “Sewelo la Pakanema la Cilengedwe.” Anacita izi mpaka pamene M’bale Brown na mkazi wake anatumizidwa kukatumikila ku West Africa mu 1923. Koma atate na amayi anapitiliza kutumikila ku Trinidad. Onse aŵili anali odzozedwa.
MAKOLO ATHU ANALI KUTIKONDA
M’banja mwathu, tinalimo ana 9. Ndipo woyamba anam’patsa dzina lakuti Rutherford, potengela dzina la pulesidenti wa Watch Tower wa panthawiyo. Ine n’tabadwa, pa December 30, 1922, ananipatsa dzina lakuti Woodworth, potengela dzina la M’bale Woodworth, amene anali mlembi wa magazini ya The Golden Age (imene lomba timaicha Galamuka!). Makolo athu anatiphunzitsa sukulu mpaka giledi 12, koma anali kutilimbikitsa kwambili kukhala na zolinga zauzimu. Amayi anali na luso lapadela lofotokoza Malemba mogwila mtima kwambili. Atate anali kukonda kutisimbila nkhani za m’Baibo, ndipo anali kucita magesica pofuna kutithandiza kuti tiziona nkhanizo kukhala zeni-zeni.
Khama lawo linabala zipatso zabwino. Pa ana awo 5 aamuna, ife atatu tinaloŵa Sukulu ya Giliyadi. Atatu mwa azilongosi athu anacita upainiya kwa zaka zambili ku Trinidad na Tobago. Kaamba ka zimene anali kutiphunzitsa komanso citsanzo cawo cabwino, makolo athu mophiphilitsa anatibyala “m’nyumba ya Yehova.” Ndipo cifukwa ca cilimbikitso cawo, tinakula mosangalala “m’mabwalo a Mulungu wathu.”—Sal. 92:13.
Pa nyumba pathu m’pamene panali malo okumanako kaamba ka nchito yolalikila. Apainiya anali kukumana kwathu, ndipo kaŵili-kaŵili anali kukamba za M’bale George Young, mmishonale wa ku Canada amene anabwela ku Trinidad. Makolo anga anali kukamba monyadila za mabwenzi awo, m’bale
na mlongo Brown, amene panthawiyo anali kutumikila ku West Africa. Izi zonse, zinanisonkhezela kuyamba kulalikila nili na zaka 10 cabe.CIYAMBI CA UTUMIKI WANGA
M’masiku amenewo, magazini athu anali kukhala na nkhani zodzudzula mosapita m’mbali. Nkhanizo zinali kuvumbula cipembedzo conyenga, komanso kudzudzula azamalonda adyela ndi azandale acinyengo. Cifukwa ca izi, mu 1936 atsogoleli a zipembedzo anasonkhezela bwanamkumbwa wa mu Trinidad kuti aletse mabuku a Watch Tower m’dzikolo. Tinali kubisa mabuku athu, koma tinapitiliza kuwagaŵila mobisa mpaka pamene onse anatha. Tinali kucita ndawala za ulaliki, titanyamula zikwangwani na tumapepala twa cidziŵitso kwa anthu. Tinali kulalikila na motoka yokhala na zokuzila mawu kucoka m’tauni ya Tunapuna mpaka ku madela akutali a m’dzikoli. Zinali zokondweletsa ngako! Izi zinanilimbikitsa kubatizika. Ndipo n’nabatizika nili na zaka 16.
Zocitika za muulaliki zimenezi, komanso citsanzo ca makolo na cilimbikitso cawo, zinanicititsa kuyamba kulakalaka kukakhala mmishonale. Cikhumbo cimeneci cinali cikali camphamvu pamene n’napita ku Aruba mu 1944, kukatumikila pamodzi na M’bale Edmund W. Cummings. Tinakondwela kuona kuti anthu 10 amene tinawaitanila ku Cikumbutso ca mu 1945, anapezekapo. M’caka cotsatila, mpingo woyamba unakhazikitsidwa pa cisumbuci.
Posapita nthawi, n’nacita ulaliki wamwayi kwa mnzanga wa kunchito, dzina lake Oris Williams. Oris anayesetsa mwamphamvu kuikila kumbuyo ziphunzitso za ku chechi kwawo. Koma n’tayamba kuphunzila naye Baibo, anamvetsetsa coonadi, ndipo anabatizika pa January 5, 1947. M’kupita kwanthawi, tinakondana, ndipo kenako tinakwatilana. Oris anayamba upainiya mu November 1950. N’takwatila Oris, cimwemwe canga cinawonjezeleka.
UTUMIKI WOKONDWELETSA KU NIGERIA
Mu 1955, tinaitanidwa kuti tikaloŵe Sukulu ya Giliyadi. Pokonzekela Sukuluyi, ine na Oris tinaleka nchito zathu zolembedwa, na kugulitsa nyumba na katundu wathu wina. Kenako, tinanyamuka ku Aruba. Titatsiliza maphunzilo a kilasi namba 27 ya Giliyadi pa July 29, 1956, tinauzidwa kuti tikatumikile ku Nigeria.
Pokumbukila za nthawiyo, Oris anati: “Mzimu wa Yehova umathandiza munthu kusintha, n’colinga cakuti ajaile umoyo wa umishonale. Mosiyana ndi amuna anga, ine n’nalibe cidwi cokhala mmishonale. N’nali kufuna cabe kukhala na nyumba yathu-yathu komanso ana. Koma n’nasintha maganizo n’tazindikila kuti nchito yolalikila uthenga wabwino ifunika kugwilidwa mwamsanga. Pamene tinali kutsiliza maphunzilo a Giliyadi, n’nali wokonzeka kukatumikila monga mmishonale. Ndipo pamene tinali kukwela sitima yochedwa Queen Mary, M’bale Worth Thornton, amene anali kutumikila mu ofesi ya M’bale Knorr, anati ‘Muyende bwino!’ Ndiyeno, anatiuza kuti tidzayamba kutumikila pa Beteli. N’nada nkhawa kwambili. Koma mwamsanga n’nasintha kawonedwe kanga. N’nayamba kuukonda utumiki wa pa Beteli, ndipo kumeneko n’nali kugwila nchito zosiyana-siyana. Nchito imene n’nali kukonda kwambili inali yolandila alendo. Zinali conco, cifukwa nimakonda kwambili anthu, ndipo nchitoyi inali kunipatsa mwayi woonana ndi abale osiyana-siyana a mu Nigeria. Ambili anali kubwela ali ombuwa, olema, aludzu, komanso anjala. N’nali kuona kuti ni mwayi kuwasamalila na kuwalimbikitsa. Kucita izi kunali kunibweletsela cimwemwe coculuka, cifukwa n’nali kudziŵa kuti ni mbali ya kutumikila Yehova.” Zoonadi, utumiki uliwonse umene tinacita, unatithandiza kukula mwauzimu.
Mu 1961, pamene tinali pamaceza na abale ku Trinidad, M’bale Brown anatisimbila zokumana nazo zolimbikitsa za mu utumiki wawo ku Africa. Ndiyeno, ine n’nawafotokozela za kuwonjezeka kwa ofalitsa ku Nigeria. M’bale Brown ananikumbatila mwaubwenzi na kuuza atate kuti: “Johnny, waona ka! Iwe sunafikeko ku Africa, koma Woodworth anafikako!” Atate anayankha kuti: “Pitiliza Worth! Usabwelele m’mbuyo!” Zimene aciyambakale m’coonadi amenewa anakamba, zinanilimbikitsa kwambili kucita utumiki wanga modzipeleka.
Mu 1962, n’napatsidwa mwayi wokacita maphunzilo owonjezeleka a Sukulu ya Giliyadi, kwa miyezi 10. N’naloŵa kilasi ya namba 37. M’bale Wilfred Gooch, amene anali woyang’anila nthambi ku Nigeria, analoŵa kilasi ya namba 38 ya Giliyadi, ndipo anatumizidwa kukatumikila ku England. Conco, ine n’naikidwa kukhala woyang’anila nthambi ku Nigeria. Potengela M’bale Brown, n’nali kuyenda m’madela * (malole opangidwa kukhala basi ku Nigeria.) Nthawi zambili, pa mabasi amenewa panali kulembedwa mawu ocititsa cidwi. Mwacitsanzo, pa basi ina panali mawu akuti: “Pang’ono-pang’ono ni mtolo.”
osiyana-siyana. Izi zinanithandiza kuwadziŵa bwino abale a m’dzikolo na kuyamba kuwakonda. Olo kuti abalewo analibe zinthu zambili zakuthupi monga zimene anthu a m’maiko olemela amakhala nazo, anali kukhala okhutila na zimene anali nazo. Izi zinaonetsa kuti kukhala na umoyo wacimwemwe sikudalila pa cuma kapena zinthu zakuthupi. Ngakhale kuti anali na umoyo wosaukila, zinali zocititsa cidwi kuwaona pa misonkhano atavala zovala zaukhondo, zooneka bwino, komanso zoyenelela. Pobwela ku misonkhano yacigawo, ambili anali kukwela mathilaki na ma bolekajasMawu amenewo analidi oona. Zilizonse zimene timacita popititsa patsogolo nchito yolalikila n’zofunika. Nafenso tinacitako mbali yathu. Pofika mu 1974, pa maiko onse kupatulapo dziko la America, Nigeria ndiyo inali yoyamba kukhala na ciŵelengelo ca ofalitsa 100,000. Nchito yolalikila inapita patsogolo kwambili!
Kuwonjezeleka kumeneku kunacitika panthawi imene m’dzikolo munali nkhondo. Nkhondoyo inacitika kuyambila mu 1967 mpaka mu 1970. Kwa miyezi, abale athu m’dela la Biafra, limene linali ku tsidya lina la mtsinje wa Niger, analibe mwayi wokamba na ofesi ya nthambi. Olo kuti zinali zovuta, tinaona kuti tifunika kupitabe kukawapatsa mabuku. Monga nakambila kuciyambi, mwa pemphelo komanso cifukwa codalila Yehova, tinakwanitsa kuwoloka mtsinje wa Niger kupita ku Biafra maulendo angapo.
Pa nthawiyo, zinali zoika moyo pa ciwopsezo kuwoloka mtsinje wa Niger kupita ku Biafra, cifukwa kunali asilikali olusa, matenda, na zinthu zina zimene zikanativulaza. Zinali zoopsa kudutsa m’dela loyang’anilidwa na asilikali aboma. Koma zinali zoopsa kwambili kudutsa m’dela la Biafra, limene linali m’manja mwa asilikali oukila boma. Tsiku lina usiku, n’nawoloka mtsinje wa Niger pa boti imene inali kucokela ku Asaba kupita ku Onitsha. Kenako, n’napita kukalimbikitsa akulu mu mzinda wa Enugu. Nthawi ina n’napita ku tauni ya Aba kukalimbikitsanso akulu. Pa nthawiyo, anthu kumeneko sanali kuloledwa kuyatsa magetsi usiku kuti adani asawaone. M’tauni ya Port Harcourt, tinatsiliza msonkhano wathu mofulumila na pemphelo, cifukwa asilikali a boma analoŵa m’tauniyo pambuyo pogonjetsa asilikali oukila boma.
Mwa misonkhano imeneyo, abale athu okondedwa anali kuona kuti Yehova amawakonda. Komanso anali kulandila malangizo ofunika kwambili pankhani ya kukhala ogwilizana na kupewa kutenga mbali m’zandale. Abale athu a ku Nigeria anapilila pa nthawi yovutayi. Iwo anali kukondana na kugwilizana, mosasamala kanthu za kusiyana kwa mitundu. Ndithudi, unali mwayi waukulu kulimbikitsa abale athu panthawi yovutayi!
Pa msonkhano wamayiko wakuti, “Mtendele Padziko Lapansi,” umene unacitikila m’sitediyamu ya Yankee ku New York, mu 1969, M’bale Milton G. Henschel ndiye anali cheyamani. N’naphunzila zambili kwa iye cifukwa n’nali kutumikila monga wom’thandizila. Izi zinanithandiza kwambili, cifukwa mu 1970 tinacita msonkhano wa maiko mu mzinda wa Lagos, ku Nigeria. Msonkhanowo unali wa mutu wakuti, “Anthu Amene Mulungu Amakondwela Nawo.” Popeza nkhondo inali itatha kumene, n’zoonekelatu kuti msonkhanowu unatheka cabe ndi thandizo la Yehova. Unali msonkhano wosaiŵalika. Unacitika mu vitundu 17 pa nthawi imodzi, ndipo panapezeka anthu 121,128. Zinali zokondweletsa cotani nanga kuona anthu okwana 3,775 akubatizika! Ici cinali ciŵelengelo cacikulu kwambili ca obatizika kungocokela pa Pentekosite. M’bale Knorr na M’bale Henschel, komanso abale ena ocokela ku America na ku England analipo pa msonkhanowu. Pa nchito yokonzekela msonkhanowu, m’pamene n’natangwanika kwambili mu umoyo wanga. Pa nthawiyi, ciŵelengelo ca ofalitsa cinawonjezeleka modabwitsa!
Pa zaka zoposa 30 zimene n’nali ku Nigeria, nthawi zina n’nali kukhala na mwayi wotumikilako monga woyang’anila woyendela, komanso monga woyendela nthambi ku West Africa. Amishonale anali kuyamikila kwambili tikapita kukawalimbikitsa. Tinaona kuti unali mwayi waukulu kuwathandiza kuona kuti Yehova na gulu lake sanawaiŵale. Nchitoyi inatiphunzitsa kuti kucita zinthu zoonetsa kuti timaganizila abale athu n’kofunika kwambili, cifukwa kumawathandiza kupita patsogolo. Ndipo izi zimathandiza kuti gulu la Yehova likhale lolimba komanso logwilizana.
Popanda thandizo la Yehova, sembe sitinakwanitse kupilila mavuto obwela cifukwa ca nkhondo na matenda. Koma zinali zoonekelatu kuti nthawi zonse, Yehova anali kutidalitsa. Mkazi wanga Oris anati:
“Tonse tinadwalapo maleliya maulendo angapo. Tsiku lina, maleliya anawagwila kwambili amuna anga a Worth, ndipo anawapeleka kucipatala ali cikomokele. Kumeneko, madokotala ananiuza kuti zioneka kuti sadzacila. Koma mwamwayi wanji, anatsitsimuka. Atatsitsimuka, anayamba kulalikila nesi amene anali kuwasamalila. Nesiyo dzina lake anali Nwambiwe. A Worth atacila, tinapita ku nyumba kwa a Nwambiwe kukacita ulendo wobwelelako. Iwo anaphunzila coonadi, ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala mkulu mu mpingo wina ku Aba. Inenso n’nathandizako anthu ambili kukhala atumiki a Yehova, kuphatikizapo Asilamu okangalika. Zinali zokondweletsa kwambili kudziŵana ndi anthu a ku Nigeria, kuwakonda, kuphunzila cikhalidwe cawo, na vitundu vawo.”
Tinaphunzilanso mfundo yofunika yakuti, cimene cingatithandize kukhala acimwemwe potumikila m’dziko lina, ni kukonda abale na alongo athu, ngakhale amene cikhalidwe cawo n’cosiyana kwambili na cathu.
MAUTUMIKI ATSOPANO
Mu 1987, pamene tinali kutumikila pa Beteli ku Nigeria, tinauzidwa kuti tikatumikile monga amishonale pa cisumbu cokongola ca St. Lucia ku Caribbean. Unali utumiki wokondweletsa ngako, koma unali na zopinga zake. Mosiyana na ku Africa, kumene mwamuna mmodzi anali kukwatila akazi ambili, ku St. Lucia kunali vuto lakuti anthu anali kungotengana popanda cikwati covomelezeka. Koma cifukwa ca mphamvu ya Mawu a Mulungu, anthu ambili amene tinali kuphunzila nawo Baibo anasintha umoyo wawo.
Pamene mphamvu zathu zinayamba kutha cifukwa ca ukalamba, mu 2005 Bungwe Lolamulila linatiuza kuti tikayambe kutumikila ku likulu lathu la padziko lonse ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, ku America. Tsiku lililonse, nimam’yamikilabe Yehova cifukwa ca mkazi wanga Oris. Iye anali mnzanga wapamtima. Anali wacikondi, komanso ine n’nali kumukonda kwambili pa zaka zonse 68 zimene tinali limodzi. Iye anamwalila mu 2015, ndipo cimaniŵaŵa kwambili. Pamene tinali limodzi, tinaphunzila kuti cisinsi copezela cimwemwe m’banja na mu mpingo, ni kulemekeza umutu, kukhululukilana na mtima wonse, kukhala odzicepetsa, komanso kukhala na makhalidwe amene mzimu woyela umabala.
Ngati takumana na zokhumudwitsa kapena zolefula, tinali kudalila Yehova kuti atithandize kupitiliza kum’tumikila na mtima wonse. Pamene tinapitiliza kupanga masinthidwe, zinthu zinali kutiyendela bwino nthawi zonse, ndipo zabwino kwambili zili kutsogolo—Yes. 60:17; 2 Akor. 13:11.
Ku Trinidad na Tobago, Yehova anadalitsa utumiki umene makolo anga na abale ena anacita, cakuti lipoti yaposacedwa ionetsa kuti kumeneko tsopano kuli Mboni 9,892. Ku Aruba, abale anagwila nchito yaikulu yolimbitsa mpingo umene n’nalimo poyamba, moti pa cisumbuci lomba pali mipingo 14 yopita patsogolo. Ndipo mu Nigeria, ciŵelengelo ca ofalitsa cawonjezeka kwambili kufika pa 381,398. Komanso pa cisumbu ca St. Lucia, pali ofalitsa uthenga wa Ufumu okwana 783.
Tsopano nili na zaka za m’ma 90. Pokamba za anthu obyalidwa m’nyumba ya Yehova, Salimo 92:14 imati: “Zinthu zidzapitiliza kuwayendela bwino ngakhale atacita imvi, adzakhalabe onenepa ndi athanzi.” Nimakondwela kwambili nikaganizila umoyo wabwino umene nakhala nawo potumikila Yehova. Coloŵa cauzimu cimene n’nalandila kwa makolo anga cinanilimbikitsa kutumikila Yehova mokwanila. Kaamba ka cisomo cake, Yehova wanithandiza kukula mosangalala m’mabwalo ake.—Sal. 92:13.
^ ndime 18 Onani Galamuka! ya Cizungu ya March 8, 1972, map. 24-26.