NKHANI YOPHUNZILA 7
Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Mukondweletse Yehova
“Bwelani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi . . . Yesetsani kukhala ofatsa.”—ZEF. 2:3.
NYIMBO 80 ‘Talaŵani, Muone Kuti Yehova ni Wabwino’
ZA M’NKHANI INO *
1-2. (a) Kodi Baibo imati Mose anali munthu wotani? Nanga iye anacita ciani? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kukhala ofatsa?
BAIBO imakamba kuti Mose anali “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Kodi izi zitanthauza kuti anali wofooka, wamantha popanga zosankha, kapena woopa anthu? Ena amaganiza kuti umu ni mmene anthu ofatsa amakhalila. Koma zimenezi si zoona. Mose anali mtumiki wa Mulungu wolimba mtima, wamphamvu, komanso wosazengeleza pocita zinthu. Mwacitsanzo, na thandizo la Yehova, anayang’anizana na mfumu yamphamvu ya Iguputo. Komanso, anatsogolela Aisiraeli mwina okwana 3,000,000 kudutsa m’cipululu, na kuwathandiza kugonjetsa adani awo.
2 Masiku ano, sitikumana na mavuto monga amene Mose anakumana nawo. Koma tsiku lililonse, timakumana ndi anthu ovuta, kapena zocitika zimene zingapangitse kuti cikhale covutilapo kukhala ofatsa. Ngakhale n’conco, pali cifukwa comveka cimene ciyenela kutilimbikitsa kuyesetsa kukhala ofatsa. Cifukwa cake n’cakuti Yehova walonjeza kuti “ofatsa adzalandila dziko lapansi.” (Sal. 37:11) Kodi inu mumadziona kuti ndinu wofatsa? Kodi umu ni mmenenso anthu ena amakuonelani? Tisanayankhe mafunso ofunika amenewa, tiyeni tikambilane zimene kukhala wofatsa kumaphatikizapo.
KODI KUKHALA WOFATSA KUMAPHATIKIZAPO CIANI?
3-4. (a) Kodi khalidwe la kufatsa tingaliyelekezele na ciani? (b) Ni makhalidwe anayi ati amene timafunikila kuti tikhale ofatsa? Nanga n’cifukwa ciani ni ofunika?
3 Khalidwe la kufatsa * tingaliyelekezele na cithunzi cokongola. Motani? Katswili wa zojambula-jambula amasakaniza mitundu yosiyana-siyana kuti ajambule cithunzi cokongola. Mofananamo, kuti munthu akhale wofatsa, pali makhalidwe angapo abwino amene amafunika kukhala nawo. Ena mwa makhalidwe amenewo ni kudzicepetsa, kugonjela, kudekha, na kulimba mtima. N’cifukwa ciani makhalidwe amenewa ni ofunika kuti tikondweletse Yehova?
4 Anthu okhawo amene ali odzicepetsa ndiwo amagonjela Mulungu na kucita zimene iye amafuna. Cimodzi cimene iye amafuna n’cakuti tikhale odekha. (Miy. 29:11; 2 Tim. 2:24) Ngati ticita zimene Mulungu amafuna, Satana amakwiya kwambili. Conco, ngakhale kuti ndife odzicepetsa komanso odekha, anthu ambili m’dziko la Satanali amatizonda. (Yoh. 15:18, 19) Ndiye cifukwa cake tifunika kukhala olimba mtima kuti Satana asatigonjetse.
5-6. (a) N’cifukwa ciani Satana amawazonda anthu ofatsa? (b) Tidzakambilana mafunso ati?
5 Munthu amene si wofatsa amakhala wodzikweza, wa mtima wapacala, ndipo samvela Yehova. Umu ni mmene Satana alili. Conco, n’zosadabwitsa kuti iye amadana ndi anthu ofatsa. Amawazonda cifukwa khalidwe lawo labwino, limavumbula khalidwe lake loipa. Ndipo koposa pamenepa, iwo amapeleka umboni wakuti Satana ni wabodza. Cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa olo Satana atayesa bwanji, sangakwanitse kuletsa anthu ofatsa kutumikila Yehova.—Yobu 2:3-5.
6 Ni nthawi iti pamene kukhala ofatsa kungakhale kovuta? Ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kupitiliza kukhala ofatsa? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tidzakambilana citsanzo ca Mose, Aheberi atatu amene anali ku ukapolo ku Babulo, komanso ca Yesu.
PAMENE KUFATSA KUMAKHALA KOVUTA
7-8. Kodi Mose anacita ciani abale ake atacita zinthu zosamulemekeza?
7 Ngati tili na udindo: Cingakhale covuta kwa munthu waudindo kukhalabe wofatsa, maka-maka ngati munthu wina ali pansi pake wacita zinthu zosamulemekeza, kapena ngati wamunena kuti sacita bwino zinthu zina. Kodi zaconco zinakucitikilamponi? Kodi mungacite bwanji ngati wina m’banja mwanu wacita zinthu mwanjila imeneyi? Ganizilani zimene Mose anacita pamene zaconco zinam’citikila.
8 Yehova anasankha Mose kuti akhale mtsogoleli wa Aisiraeli, ndipo anam’patsa mwayi wolemba malamulo oti mtunduwo uzitsatila. Zinali zoonekelatu kuti Mose anali kutsogoleledwa na Yehova. Olo zinali conco, mlongosi wake wa Mose, Miriamu, na mkulu wake, Aroni, anayamba kum’nena komanso kum’dzudzula Num. 12:1-13) N’cifukwa ciani Mose anacita zinthu mwanjila imeneyi?
cifukwa ca mkazi amene anakwatila. Akanakhala wina, sembe anakwiya na kuwabwezela. Koma Mose sanacite zimenezo. Anaugwila mtima. Ndipo anacondelela Yehova kuti acilitse Miriamu khate limene anam’langa nalo. (9-10. (a) Kodi Yehova anathandiza Mose kudziŵa ciani? (b) Kodi mitu ya mabanja komanso akulu angaphunzile ciani kwa Mose?
9 Mose analola Yehova kum’phunzitsa. Zaka 40 kumbuyoko, pamene anali m’banja lacifumu ku Iguputo, Mose sanali wofatsa. Anali wamtima wapacala, cakuti anapha munthu amene anaona kuti sanali kucita zinthu mwacilungamo. Mose anaganiza kuti zimene anacitazo Yehova anakondwela nazo. Koma kwa zaka 40, Yehova anathandiza Mose kudziŵa kuti kukhala wolimba mtima sikunali kokwanila kuti atsogolele bwino mtundu wa Aisiraeli. Anafunikanso kukhala wofatsa. Ndipo kuti akhale wofatsa, anafunika kukhala wodzicepetsa, wogonjela, komanso wodekha. Mose anaphunziladi makhalidwe amenewa, cakuti anakhala woyanga’nila wabwino kwambili.—Eks. 2:11, 12; Mac. 7:21-30, 36.
10 Masiku ano, mitu ya mabanja komanso akulu ayenela kutengela citsanzo ca Mose. Ngati ena akucitilani zinthu mopanda ulemu, musamafulumile kukwiya. M’malomwake, vomelezani modzicepetsa kuti pali zinthu zina zimene simucita bwino. (Mlal. 7:9, 20) Komanso, muziyesetsa kutsatila malangizo a Yehova pofuna kuthetsa mavuto. Ndipo nthawi zonse, muziyankha modekha. (Miy. 15:1) Mitu ya mabanja komanso akulu amene amacita zinthu mwanjila imeneyi, amakondweletsa Yehova, amalimbikitsa mtendele, ndiponso amapeleka citsanzo cabwino pa nkhani ya kukhala ofatsa.
11-13. Tingatengele bwanji citsanzo ca Aheberi atatu?
11 Pamene tikuzunzidwa: Kuyambila kale-kale, olamulila a dziko akhala akuzunza atumiki a Yehova. Iwo amatiimba milandu yosiyana-siyana. Koma cifukwa cacikulu cimene amatizunzila n’cakuti ‘timamvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.’ (Mac. 5: 29) Tinganyozedwe, kumangidwa, na kumenyedwa. Komabe, ndi thandizo la Yehova, timakhala odekha pamene tikuzunzidwa, ndipo sitibwezela.
12 Ganizilani citsanzo ca Hananiya, Misayeli ndi Azariya, Aheberi atatu amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. * Mfumu ya Babulo inawalamula kuti agwadile fano lalikulu la golide. Koma modekha, iwo anafotokozela mfumuyo cifukwa cake anakana kugwadila fanolo. Aheberiwo anamvelabe Mulungu, ngakhale pamene mfumu inawaopseza kuti adzaponyedwa m’nganjo ya moto. Yehova anawapulumutsa. Koma sikuti iwo anadziŵilatu kuti Mulungu adzawapulumutsa. Anali okonzeka kumvelabe Yehova, mosasamala kanthu zakuti adzawapulumutsa kapena ayi. (Dan. 3:1, 8-28) Zimene Aheberi amenewa anacita, zinaonetsa kuti anthu ofatsa amakhaladi olimba mtima. Inde, palibe ciliconse cingatilepheletse kutumikila Yehova na mtima wosagaŵanika—kaya ni mfumu, ciwopsezo, kapena cizunzo.—Eks. 20:4, 5.
13 Tingatengele bwanji citsanzo ca Aheberi atatu amenewa tikakumana na mayeselo? Tiyenela kucita zinthu modzicepetsa podziŵa kuti Yehova adzatiteteza. (Sal. 118:6, 7) Komanso, ngati anthu atiimba mlandu wabodza, tiyenela kuyankha modekha ndi mwaulemu. (1 Pet. 3:15) Kuwonjezela apo, tifunika kukana kwamtu wagalu kucita zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu na Atate wathu wakumwamba.
14-15. (a) N’ciani cingacitike pamene tivutika maganizo? (b) Kodi Yesaya 53:7, 10, ionetsa bwanji kuti Yesu n’citsanzo cabwino kwambili pankhani yokhala ofatsa pamene tivutika?
14 Pamene tikuvutika maganizo: Tonse timakhala na nkhawa, komanso timavutika maganizo pa zifukwa zosiyana-siyana. Mwina munakhalapo na nkhawa pamene munali kuyembekezela kulemba mayeso kusukulu. Kapena munapanikizika maganizo pamene munauzidwa kugwila nchito inayake. Mwina tingakhalenso na nkhawa poyembekezela kucitidwa opaleshoni inayake, kapena kupimidwa matenda ena ake. Ngati tili na nkhawa kapena tikuvutika maganizo, cimakhala covuta kukhala wofatsa. Tingayambe kukwiya na nkhani za zii. Tingayambenso kukamba mokhadzula, komanso kucita zinthu mopanda cikondi. Conco, ngati mukuvutika maganizo, muziganizila citsanzo ca Yesu.
15 Cakumapeto kwa moyo wake padziko lapansi, Yesu anavutika maganizo kwambili. Iye anali kudziŵa kuti adzazunzidwa kwambili, komanso kuti adzaphedwa. (Yoh. 3:14, 15; Agal. 3:13) Patatsala miyezi ingapo asanaphedwe, Yesu anakamba kuti anavutika kwambili mumtima. (Luka 12:50) Ndipo kutatsala masiku ocepa asanaphedwe, iye anati: “Moyo wanga ukusautsika.” Yesu anaonetsa kuti ni wodzicepetsa komanso wogonjela pamene anakhuthulila Mulungu nkhawa zake m’pemphelo. Iye anati: “Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi. Komabe nthawi imeneyi iyenela kundifikila pakuti ndiye cifukwa cake ndinabwela. Atate lemekezani dzina lanu.” (Yoh. 12:27, 28) Nthawiyo itafika, Yesu molimba mtima anadzipeleka kwa adani a Mulungu, ndipo iwo anamupha mwankhanza ndi momunyazitsa. Ngakhale anavutika maganizo komanso kuzunzidwa kwambili, iye anacitabe cifunilo ca Mulungu. Ndithudi, Yesu n’citsanzo cabwino kwambili pankhani yokhalabe ofatsa pamene tivutika!—Ŵelengani Yesaya 53:7, 10.
16-17. (a) Kodi ophunzila a Yesu anacita ciani cimene cikanapangitsa kuti cikhale covuta kwa iye kucita zinthu mofatsa? (b) Nanga tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu?
16 Usiku wakuti maŵa adzaphedwa, mabwenzi a Yesu, anacita zinthu zimene zikanapangitsa kuti cikhale covuta kwa iye kucita zinthu mofatsa. Ganizilani cabe mmene Yesu anavutikila maganizo pa nthawiyo. Iye anafunika kukhala wokhulupilika mpaka imfa, cifukwa miyoyo ya anthu mabiliyoni ambili inadalila pa kukhulupilika kwake. (Aroma 5:18, 19) Kuwonjezela apo, zocita zake zikanakhudza dzina la Atate ŵake. (Yobu 2:4) Komanso, pamene anali kudya cakudya cothela pamodzi na atumwi ake, pakati pa atumwiwo “panabuka mkangano woopsa.” Iwo anali kukangana za “amene anali kuoneka wamkulu kwambili” pakati pawo. Izi zinacitika olo kuti Yesu anali atawalangizapo mobweleza-bweleza pa nkhaniyi, kuphatikizapo madzulo a tsikulo. N’zocititsa cidwi kuona kuti Yesu sanakwiye. M’malomwake, anacita nawo zinthu modekha. Mokoma mtima, Yesu anawapatsanso malangizo mosapita m’mbali pa nkhaniyo. Ndiyeno, anawayamikila cifukwa coonetsa kukhulupilika mwa kukhalabe naye mu umoyo wake wonse.—Luka 22:24-28; Yoh. 13:1-5, 12-15.
17 Kodi mukanakhala imwe, mukanacita ciani pamenepa? N’zotheka kutengela citsanzo ca Yesu mwa kukhalabe odekha, olo pamene tili Akol. 3:13) Cimene cingatithandize kumvela lamulo limeneli, ni kukumbukila kuti tonsefe timakamba kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Miy. 12:18; Yak. 3:2, 5) Cinanso, tiyenela kukhala na cizoloŵezi coyamikila abale athu pa zabwino zimene amacita.—Aef. 4:29.
opanikizika maganizo. Tiyenela kumvela na mtima wonse lamulo la Yehova lakuti, “pitilizani kulolelana.” (CIFUKWA CAKE TIYENELA KUYESETSA KUKHALA OFATSA
18. Kodi Yehova amawathandiza bwanji anthu ofatsa kupanga zosankha mwanzelu? Nanga n’ciani cimene tifunika kucita?
18 Kudzatithandiza kupanga zosankha mwanzelu. Ngati tifuna kupanga zosankha pa nkhani zovuta, Yehova angatithandize kusankha mwanzelu. Koma kuti izi zitheke, tifunika kukhala ofatsa. Iye walonjeza kuti ‘adzamva kucondelela kwa anthu ofatsa.’ (Sal. 10:17) Ndipo adzacita zoposa pamenepa. Baibo imati: “Adzacititsa ofatsa kutsatila zigamulo zake, ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njila yake.” (Sal. 25:9) Yehova amatitsogolela kupitila m’Baibo, zofalitsa, * mavidiyo, na misonkhano yokonzedwa na “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45-47) Conco, tifunika kukhala odzicepetsa na kuvomeleza kuti tifunika thandizo lake. Tingaonetse kuti ndife odzicepetsa mwa kuŵelenga zofalitsa zimene amatigaŵila kupitila mwa kapolo wake, komanso kuyesetsa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila.
19-21. Ni colakwa canji cimene Mose anacita ku Kadesi? Nanga tiphunzilapo ciani pa zimene anacita?
19 Tidzapewa kucita zolakwa. Ganizilaninso za Mose. Kwa zaka zambili anali wofatsa, ndipo anacita zinthu zokondweletsa Yehova. Koma cakumapeto kwa ulendo wa m’cipululu wa zaka 40, Mose analephela kuonetsa khalidwe la kufatsa. Mlongosi wake, Miriamu, mwacionekele amene anathandiza kupulumutsa moyo wake ku Iguputo anali atafa kumene, ndipo anaikidwa m’manda ku Kadesi. Pa nthawiyo, Aisiraeli anayambanso kudandaula kuti sanali kusamalidwa bwino. Iwo ‘anakangana ndi Mose’ pa nkhani yosoŵa madzi. Ngakhale kuti Yehova anacitila Aisiraeli zozizwitsa zambili kupitila mwa Mose, ndipo Mose anawatsogolela bwino kwa zaka zambili, iwo anapitiliza kudandaula. Sanadandaule cabe za kusoŵa kwa madzi, koma anakwiyilanso Mose, monga kuti iye ndiye anacititsa kuti asoŵe madzi.—Num. 20:1-5, 9-11.
20 Mose anakwiya kwambili, cakuti anacita zinthu mosadekha. M’malo mokamba na thanthwe, monga mmene Yehova anam’lamulila, iye anakamba mokwiya kwa anthu. Komanso, anakamba Sal. 106:32, 33) Olo kuti Mose analephela kuonetsa khalidwe la kufatsa kwa kanthawi kocepa cabe, Mulungu sanamulole kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 20:12.
mawu oonetsa ngati kuti iye ndiye adzatulutsa madzi. Ndiyeno, anamenya thanthwelo kaŵili, ndipo munatuluka madzi ambili. Kunyada na mkwiyo zinam’pangitsa kucita colakwa cacikulu. (21 Pa nkhani imeneyi, tiphunzilapo mfundo zofunika kwambili. Yoyamba, nthawi zonse tifunika kuyesetsa kukhala ofatsa. Tikalephela kukhala ofatsa, ngakhale kwa nthawi yocepa, mzimu wonyada ukhoza kutiloŵa na kutipangitsa kukamba, kapena kucita zinthu zolakwika. Yaciŵili, tifunika kuyesetsa kucita zinthu mofatsa, ngakhale pamene takwiya kapena kupanikizika maganizo.
22-23. (a) N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kukhala ofatsa? (b) Kodi mawu a pa Zefaniya 2:3 aonetsa ciani?
22 Tidzatetezedwa. Posacedwa, Yehova adzawononga anthu onse oipa pa dzikoli, ndipo padzakhala ofatsa okha-okha. Pa dziko padzakhala mtendele weni-weni. (Sal. 37:10, 11) Kodi imwe mudzakhala mmodzi wa anthu ofatsa amenewo? Tingakakhale na mwayi umenewo ngati ticita zimene mneneli Zefaniya anakamba.—Ŵelengani Zefaniya 2:3.
23 N’cifukwa ciani Zefaniya 2:3 imakamba kuti, “Mwina mungadzabisike”? Mawu amenewa satanthauza kuti Yehova angalephele kupulumutsa anthu amene amawakonda, komanso amene amafuna kum’kondweletsa. Koma atanthauza kuti cipulumutso cidzadalila pa zocita zathu. Ngati tiyesetsa kukhala ofatsa kuti tikondweletse Yehova, tonse tingakhale na mwayi wokapulumuka “tsiku la mkwiyo wa Yehova,” n’kukakhala na moyo wosatha.
NYIMBO 120 Tengelani Kufatsa kwa Khristu
^ ndime 5 Tonsefe sitinabadwe na khalidwe la kufatsa. Timacita kuliphunzila. Cimakhala copepuka kukhala ofatsa ngati ticita zinthu ndi anthu amtendele. Koma ngati ticita zinthu ndi anthu onyada, kukhala ofatsa kungakhale kovuta. M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zina zimene tiyenela kusamala nazo, kuti tikhalebe na khalidwe labwino limeneli la kufatsa.
^ ndime 3 MAWU OFOTOKOZEDWA: Kufatsa. Munthu wofatsa amakhala wokoma mtima pocita zinthu ndi ena, ndipo amakhalabe wodekha ngakhale pamene ena amukhumudwitsa. Kudzicepetsa. Munthu wodzicepetsa sakhala wonyada kapena wodzikuza. Koma amaona ena kukhala om’posa. Yehova ni wodzicepetsa m’lingalilo lakuti, ngakhale ni wapamwamba kwambili, amacita zinthu mwacikondi komanso mwacifundo ndi anthu komanso angelo.
^ ndime 12 Ababulo anapatsa Aheberi atatu amenewa maina akuti Sadirake, Mesake, na Abedinego.—Dan. 1:7.
^ ndime 18 Mwacitsanzo, onani nkhani yakuti, “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2011.
^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Yesu akuonetsabe khalidwe lofatsa mwa kulangiza ophunzila ake modekha pambuyo pakuti akangana pa nkhani yofuna kukhala wamkulu.