Kodi Mudziŵa?
Kodi zofukula za m’matongwe zimaonetsa bwanji kuti Belisazara wa ku Babulo anali mfumu?
KWA zaka zambili, anthu otsutsa Baibo anali kukamba kuti Mfumu Belisazara yochulidwa m’buku la Danieli ni munthu wongopeka, sanakhaleko. (Dan. 5:1) Anali kukamba conco cifukwa akatswili ofukula za m’matongwe anali asanapeze umboni uliwonse wakuti iye anakhalakodi. Koma zimenezi zinasintha mu 1854. Cifukwa ciani?
M’caka cimeneco, kazembe wina wa dziko la Britain, dzina lake J. G. Taylor anafukula m’matongwe a mzinda wakale wa Uri, kum’mwela kwa dziko limene manje limachedwa Iraq. Kumeneko, m’nsanja inayake yaitali, anapezamo zolembapo zingapo zoumbidwa na dothi. Ciliconse mwa zolembapo zimenezo ni cacitali masentimita 10, ndipo pali zilembo zacikale zocita kuzokota. Pa cimodzi mwa zolembapo zimenezo panalembedwa pemphelo lopempha kuti Mfumu Nabonidasi ya Babulo na mwana wake wamkulu, Belisazara, akhale na moyo wautali. Ngakhale anthu otsutsa Baibo anavomeleza kuti zimene anapezazo ni umboni wakuti Belisazara anakhalakodi.
Komabe, Baibo siikamba cabe kuti Belisazara analiko, koma imakambanso kuti anali mfumu. Otsutsa anali kukayikilanso mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, wasayansi wina wa ku England wa m’ma 1800, dzina lake William Talbot, analemba kuti anthu ena amati “Bel-sar-ussur [Belisazara] anali kulamulila monga mfumu pamodzi ndi Nabonidasi, atate wake. Koma zimenezi zilibe umboni ngakhale pang’ono.”
Koma mtsutso umenewu unatha pamene akatswili ena ofukula zinthu zakale anapeza zolembapo zina zoumbidwa na dothi, zimene zili na mawu oonetsa kuti nthawi zina atate wake Belisazara, Mfumu Nabonidasi, anali kucoka mu mzinda waukulu wa Babulo n’kukakhala kwina kwa zaka. Kodi anali kulamulila n’ndani pa nthawiyo? Buku lakuti Encyclopaedia Britannica limati: “Nabonidasi akacokapo, anali kusiyila Belisazara ufumu komanso udindo woyang’anila mbali yaikulu ya gulu lake la asilikali.” Telo tingakambe kuti pa nthawiyo, Belisazara anali kutumikila monga mfumu ya Babulo pamodzi na atate wake. Pa cifukwa ici, katswili wofukula za m’matongwe komanso wa zinenelo, dzina lake Alan Millard, anakamba kuti m’pomveka kuti “Buku la Danieli limachula Belisazara kuti ‘mfumu.’”
Kwa ife atumiki a Mulungu, cifukwa cacikulu cimene timakhulupilila kuti buku la Danieli ni lodalilika, ndipo ni mawu ouzilidwa na Mulungu, cili m’Baibo momwemo.—2 Tim. 3:16.