Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 8

Mmene Tingakhalilebe Acimwemwe Popilila Mayeso

Mmene Tingakhalilebe Acimwemwe Popilila Mayeso

“Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayeselo osiyanasiyana.”​—YAK. 1:2.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Malinga na Mateyu 5:11, kodi mayeso tiyenela kuwaona motani?

YESU analonjeza otsatila ake kuti adzakhala na cimwemwe ceni-ceni. Iye anacenjezanso anthu amene anali kum’konda kuti adzakumana na mayeso. (Mat. 10:22, 23; Luka 6:20-23) Timakondwela kukhala ophunzila a Khristu. Koma kodi timamvela bwanji tikamatsutsidwa na a m’banja lathu, kuzunzidwa na boma, kapena ngati anzathu kunchito kapena kusukulu amatikakamiza kucita zinthu zoipa? M’pomveka kuda nkhawa na zinthu ngati zimenezi.

2 Ambili saona mazunzo monga cifukwa cokhalila acimwemwe. Koma Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizikondwela. Mwacitsanzo, wophunzila Yakobo analemba kuti m’malo mwa kuda nkhawa tiyenela kukondwela pamene tikukumana na mayeso. (Yak. 1:2, 12) Ndipo Yesu anakamba kuti tiyenela kukondwela ngakhale pamene tikuzunzidwa. (Ŵelengani Mateyu 5:11.) Kodi tingacite ciani kuti tikhalebe acimwemwe ngakhale pamene tikukumana na mayeso? Tingaphunzile zambili mwa kuona zina mwa zimene Yakobo analemba m’kalata yake yopita kwa Akhristu oyambilila. Coyamba, tiyeni tione mavuto amene Akhristu amenewa anakumana nawo.

KODI AKHRISTU OYAMBILILA ANAKUMANA NA MAVUTO OTANI?

3. N’ciani cinacitika Yakobo atangokhala wophunzila wa Yesu?

3 Patangopita nthawi yocepa kucokela pamene Yakobo m’bale wake wa Yesu anakhala wophunzila, Akhristu ku Yerusalemu anayamba kutsutsidwa. (Mac. 1:14; 5:17, 18) Pamene wophunzila Sitefano anaphedwa, Akhristu ambili anathaŵa mu mzindawo ndipo “anabalalikila m’zigawo za Yudeya ndi Samariya,” mpaka kukafika kumadela akutali a Kupuro na Antiokeya. (Mac. 7:58–8:1; 11:19) Ophunzila amenewa anakumana na mavuto ambili. Ngakhale n’telo, iwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino mwakhama kulikonse kumene anapita, ndipo mipingo inakhazikitsidwa mu Ufumu wonse wa Roma. (1 Pet. 1:1) Koma Akhristu oyambilila amenewo, anali kudzakumananso na mavuto ena aakulu kutsogolo.

4. Ni mayeso ena ati amene Akhristu oyambilila anapilila?

4 Akhristu oyambilila anapilila mayeso ambili. Mwacitsanzo, ca mu 50 C.E., Mfumu ya Roma dzina lake Kalaudiyo analamula kuti Ayuda onse acoke m’dziko la Roma. Conco Ayuda amene anakhala Akhristu anakakamizika kusiya nyumba zawo na kukakhala kwina. (Mac. 18:1-3) Ca mu 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu anzake anali kunyozedwa pamaso pa anthu, kuponyedwa m’ndende, komanso kulandidwa zinthu zawo. (Aheb. 10:32-34) Ndipo mofanana na anthu ena, Akhristuwo anali kuvutika na umphawi komanso matenda.—Aroma 15:26; Afil. 2:25-27.

5. Kodi tidzayankha mafunso ati m’nkhani ino?

5 Yakobo analemba kalata yake cisanafike caka ca 62 C.E. Conco, iye anali kudziŵa bwino mayeso amene abale na alongo ake anali kukumana nawo. Yehova anauzila Yakobo kulembela Akhristu amenewa malangizo owathandiza kukhalabe acimwemwe polimbana na mayeso. Tiyeni tikambilane kalata imene Yakobo analemba na kuyankha mafunso aya: Kodi Yakobo analemba za cimwemwe cotani? Kodi n’ciani cingalande Mkhristu cimwemwe cimeneco? Nanga kodi nzelu, cikhulupililo, na kulimba mtima zingatithandize bwanji kukhalabe acimwemwe pa mayeso alionse?

N’CIANI CIMAPANGITSA MKHRISTU KUKHALA WACIMWEMWE?

Monga lawi lotetezeka limene likuyaka mkati mwa nyale ya galasi, cimwemwe cimene Yehova amapeleka cimapitilizabe kuyaka mu mtima mwa Mkhristu (Onani ndime 6)

6. Malinga na Luka 6:22, 23, n’cifukwa ciani Mkhristu angakhale wacimwemwe pamene akumana na mayeso?

6 Anthu angaganize kuti angakhale acimwemwe kokha ngati ali na thanzi labwino, ndalama zankhani-nkhani, komanso ngati m’banja muli mtendele. Koma cimwemwe cimene Yakobo analemba ni mbali ya cipatso cimene mzimu wa Mulungu umabala, ndipo sicidalila mmene zinthu zilili pa umoyo wa munthu. (Agal. 5:22) Mkhristu amapeza cimwemwe ceni-ceni cifukwa codziŵa kuti akukondweletsa Yehova na kutsatila citsanzo ca Yesu. (Ŵelengani Luka 6:22, 23; Akol. 1:10, 11) Monga lawi loyaka mkati mwa nyale ya galasi, Mkhristu amakhalabe wacimwemwe mu mtima. Cimwemweco sicikutha ngati Mkhristuyo wadwala kapena ngati ali na ndalama zocepa. Cimakhalapobe ngakhale pamene akunyozedwa kapena kutsutsidwa na a m’banja lake kapena anthu ena. Cimwemwe cathu cimalimbilako pamene anthu otsutsa akufuna kutilanda cimwemweco. Mayeso amene timakumana nawo cifukwa ca cikhulupililo cathu amatsimikizila kuti ndifedi ophunzila oona a Khristu. (Mat. 10:22; 24:9; Yoh. 15:20) N’cifukwa cake Yakobo analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayeselo osiyanasiyana.”—Yak. 1:2.

N’cifukwa ciani tingayelekezele mayeso na moto umene amaseŵenzetsa posula lupanga? (Onani ndime 7) *

7-8. Kodi pali ubwino wanji cikhulupililo cathu cikamayesedwa?

7 Yakobo anafotokoza cifukwa cina cimene cimapangitsa Akhristu kukhala okonzeka kukumana na mayeso ngakhale aakulu. Anati: “Cikhulupililo canu cikayesedwa, cimabala kupilila.” (Yak. 1:3) Mayeso tingawayelekezele na moto umene amaseŵenzetsa posula lupanga. Lupanga akalicotsa pa moto amaliviika m’madzi, ndipo limalimba kwambili. Mofananamo, tikamapilila mayeso cikhulupililo cathu cimalimba. Ndiye cifukwa cake Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse.” (Yak. 1:4) Tikadziŵa kuti mayeso amene timakumana nawo amalimbitsa cikhulupililo cathu, tingawapilile mwacimwemwe.

8 M’kalata yake, Yakobo anakambanso ena mwa mavuto amene angatilande cimwemwe. Kodi mavutowo ni ati, ndipo tingawagonjetse motani?

KUGONJETSA MAVUTO AMENE ANGATILANDE CIMWEMWE

9. N’cifukwa ciani timafunikila nzelu?

9 Vuto: Kusadziŵa zimene tingacite. Tikakumana na mayeso, tiyenela kuyang’ana kwa Yehova kuti atithandize kupanga zosankha zom’kondweletsa, zopindulitsa abale na alongo athu, komanso zimene zingatithandize kusunga umphumphu wathu. (Yer. 10:23) Timafunikila nzelu kuti tidziŵe zoyenela kucita, komanso zimene tingakambe kwa anthu amene amatitsutsa. Cifukwa ca kusadziŵa zimene tingacite, tingaone kuti tilibe mtengo wogwila pa mavuto athu, ndipo mwamsanga tingataye cimwemwe cathu.

10. Kodi Yakobo 1:5 imatiuza kuti tiyenela kucita ciani kuti tipeze nzelu?

10 Zimene mungacite: Pemphani nzelu kwa Yehova. Kuti tipilile mayeso mwacimwemwe, coyamba tifunika kupempha nzelu kwa Yehova kuti tipange zosankha zabwino. (Ŵelengani Yakobo 1:5.) Kodi tiyenela kucita ciani tikaona kuti Yehova sanayankhe pemphelo lathu mwamsanga? Yakobo anakamba kuti tiyenela kupitilizabe kum’pempha Mulungu. Yehova sakalipa ngati tipitilizabe kum’pempha nzelu. Iye sadzatitonza. Atate wathu wakumwamba “amapeleka mowolowa manja” tikamupempha nzelu zotithandiza kupilila mayeso. (Sal. 25:12, 13) Iye amaona mavuto athu, ni wacifundo, ndipo ni wofunitsitsa kutithandiza. Kudziŵa zimenezi, kumatibweletsela cimwemwe! Koma kodi Yehova amatipatsa bwanji nzelu?

11. N’ciani cina cimene tiyenela kucita kuti tipeze nzelu?

11 Yehova amatipatsa nzelu kupitila m’Mawu ake. (Miy. 2:6) Kuti tipeze nzelu zimenezo, timafunika kuŵelenga Mawu a Mulungu na zofalitsa zozikidwa pa Baibo. Koma palinso zina zimene tiyenela kucita. Tifunika kuseŵenzetsa nzelu za Mulungu mu umoyo wathu mwa kucita zimene iye amatiuza. Yakobo analemba kuti: “Muzicita zimene mawu amanena, osati kungomva cabe.” (Yak. 1:22) Tikamasewenzetsa malangizo a Mulungu, timakhala anthu obweletsa mtendele, ololela, komanso acifundo. (Yak. 3:17) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupilila mayeso alionse popanda kutaya cimwemwe cathu.

12. N’cifukwa ciani m’pofunika kuidziŵa bwino Baibo?

12 Mawu a Mulungu ali ngati galasi lodziyang’anapo. Amatithandiza kudziŵa mbali zimene tifunika kuwongolela. (Yak. 1:23-25) Mwacitsanzo, pambuyo poŵelenga Mawu a Mulungu, tingazindikile kuti tiyenela kulamulila mkwiyo wathu. Na thandizo la Yehova, timadziŵa mmene tingacitile zinthu modekha na anthu amene atikhumudwitsa kapena tikakumana na mavuto. Cifukwa cokhala odekha, timakwanitsa kupilila mavuto amene timakumana nawo. Timakhala oganiza bwino ndipo timapanga zosankha zabwino. (Yak. 3:13) Conco, m’pofunika kwambili kuidziŵa bwino Baibo!

13. N’cifukwa ciani tiyenela kuphunzila nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo?

13 Nthawi zina timaphunzila zofunika kupewa pambuyo pakuti talakwitsa zinthu. Koma kuphunzila mwa njila imeneyi n’koŵaŵa kwambili. Njila yabwino yopezela nzelu ni kuphunzila pa zimene ena anacita bwino, komanso pa zimene ena analakwitsa. Ndiye cifukwa cake Yakobo akutilimbikitsa kuphunzila ku zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo monga Abulahamu, Yobu, Rahabi, komanso Eliya. (Yak. 2:21-26; 5:10, 11, 17, 18) Atumiki a Yehova okhulupilika amenewo, anakwanitsa kupilila mayeso amene akanawalanda cimwemwe. Citsanzo cawo ca kupilila cionetsa kuti na thandizo la Yehova nafenso tingakwanitse kupilila.

14-15. N’cifukwa ciani tifunika kuthetsa zikaikilo zathu?

14 Vuto. Kukaikila zimene timakhulupilila. Nthawi zina cingakhale covuta kumvetsetsa mfundo ina yake m’Mawu a Mulungu. Kapena mwina Yehova sangayankhe mapemphelo athu mmene tinali kuyembekezela. Izi zingatipangitse kuyamba kukaikila. Ngati siticitapo kanthu pa zimene timakaikila, cikhulupililo cathu cingafooke ndipo ubale wathu na Yehova ungawonongeke. (Yak. 1:7, 8) Ndipo kukaikila kungatitaitse ngakhale ciyembekezo cathu ca zakutsogolo.

15 Mtumwi Paulo anayelekezela ciyembekezo cathu ca zakutsogolo na nangula. (Aheb. 6:19) Nangula amathandiza kuti sitima yapamadzi ikhazikike panthawi yacimphepo, kutinso isatengeke n’kukagunda miyala. Komanso nangulayo angakhale wopanda thandizo ngati cheni yake yomangilila ku sitimayo ni yosalimba. Ndipo nguwe nayonso imapangitsa cheni kukhala yofooka. Nakonso kukaikila kumafooketsa cikhulupililo cathu. Munthu wokaikila akayesedwa mwa kutsutsidwa, angataye cikhulupililo cake cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake. Tikataya cikhulupililo cathu, timatayanso ciyembekezo cathu. Monga Yakobo anakambila, munthu “wokayikila ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo ndi lowindukawinduka.” (Yak. 1:6) Munthu wotelo angakhale alibiletu cimwemwe ngakhale pang’ono!

16. Kodi tiyenela kucita ciani ngati pali zimene timakaikila?

16 Zimene mungacite: Citamponi kanthu pa zimene mumakaikila, ndipo limbitsani cikhulupililo canu. Musazengeleze kucitapo kanthu. Paja amati, zengelezu analinda kwawu-kwawu. M’nthawi ya mneneli Eliya, anthu a Yehova anali kulephela kupanga cosankha cifukwa cokaikila. Eliya anawauza kuti: “Kodi mukayikakayika mpaka liti? Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatilani ameneyo.” (1 Maf. 18:21) N’cimodzimodzinso masiku ano. Timafunika kufufuza pa ife tekha kuti titsimikizile kuti Yehova Mulungu alikodi, kuti Baibo ni Mawu akedi, ndipo Mboni za Yehova ni anthu akedi. (1 Ates. 5:21) Kucita zimenezi kudzathetsa zikaikilo zonse zimene tingakhale nazo na kulimbitsa cikhulupililo cathu. Ngati tifuna thandizo kuti tithetse zikaikilo zathu, tingapemphe akulu kuti atithandize. Timafunika kucitapo kanthu mwamsanga kuti tikhalebe acimwemwe potumikila Yehova!

17. N’ciani cidzacitika ngati sitili olimba mtima?

17 Vuto: Zofooketsa. Mawu a Mulungu amati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” (Miy. 24:10) Liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti “ukafooka” lingatanthauze “kusalimba mtima.” Ngati simulinso wolimba mtima, mudzataya cimwemwe canu mwamsanga.

18. Kodi kupilila kumatanthauza ciani?

18 Zimene mungacite: Dalilani Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima kuti mupilile. Tiyenela kukhala olimba mtima kuti tipilile mayeso. (Yak. 5:11) Liwu limene Yakobo anaseŵenzetsa pokamba za “kupilila” limapeleka lingalilo la munthu woima mocilimika pamalo ake. Tingaganizile za msilikali amene waima nji pamalo ake polimbana na mdani. Ngakhale kuti mdani wake alimbane naye moopsa cotani, iye amalimbikilabe osasunthika ngakhale pang’ono.

19. Tingaphunzile ciani pa citsanzo cimene mtumwi Paulo anapeleka?

19 Mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino zedi pankhani ya kulimba mtima na kupilila. Inde, nthawi zina anali kulefuka. Koma anakwanitsa kupilila cifukwa anadalila Yehova kuti am’patse mphamvu zofunikila. (2 Akor. 12:8-10; Afil. 4:13) Nafenso tingakhale amphamvu komanso olimba mtima ngati modzicepetsa tizindikila kuti timafunikila thandizo la Yehova.—Yak. 4:10.

YANDIKILANI MULUNGU NA KUSUNGA CIMWEMWE CANU

20-21. Tingakhale otsimikiza za ciani?

20 Tizikhala otsimikiza kuti mayeso amene timakumana nawo si cilango cocokela kwa Yehova. Yakobo akutitsimikizila kuti: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yak. 1:13) Tikatsimikizila kuti mfundo imeneyi ni ya zoona, timayandikana kwambili na Atate wathu wacikondi wakumwamba.—Yak. 4:8.

21 Yehova “sasintha.” (Yak. 1:17) Anathandiza Akhristu oyambilila pa mayeso awo, ndipo adzathandizanso aliyense wa ife masiku ano. Pemphani Yehova mocokela pansi pamtima kuti akupatseni nzelu, cikhulupililo, na kulimba mtima. Iye adzayankha mapemphelo anu. Conco, mungakhale wotsimikiza kuti iye adzakuthandizani kukhalabe acimwemwe pamene mupilila mayeso!

NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

^ ndime 5 Buku la Yakobo lili na malangizo ambili otithandiza kupilila mayeso. M’nkhani ino, tikambilana ena mwa malangizo amene Yakobo anapeleka. Malangizowo angatithandize kupilila mavuto na kukhalabe acimwemwe potumikila Yehova.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amumanga ku nyumba kwake. Mkazi wake na mwana wake akuona pamene apolisi akum’tenga kupita naye. Pamene m’baleyo ali kundende, abale na alongo apita ku nyumba kwake kukalambila Yehova pamodzi na mkazi wake na mwana wake. Mayiyo na mwana wake amapempha Yehova kaŵili-kaŵili kuti awapatse mphamvu zowathandiza kupilila ciyeso cawo. Yehova amawapatsa mtendele wa mumtima na kuwathandiza kukhala olimba mtima. Zotulukapo zake n’zakuti cikhulupililo cawo cimalimba, ndipo cimawapangitsa kuti apilile mwacimwemwe.