Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Yehova ‘Wawongola Njila Zanga’

Yehova ‘Wawongola Njila Zanga’

PANTHAWI ina, m’bale wina wacinyamata ananifunsa kuti: “Kodi lemba lako la pamtima ni liti?” Mosazengeleza n’nayankha kuti, “Ni Miyambo 3 vesi 5 na 6, imene imati: ‘Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.’” Inde, Yehova wawongoladi njila zanga. Motani?

MAKOLO ANGA ANANITHANDIZA KUYENDA PANJILA YOYENELA

Makolo anga anaphunzila coonadi ca m’ma 1920 asanakwatilane. N’nabadwa mu 1939. Nili wacinyamata ku England, n’nali kupita na makolo anga ku misonkhano ya mpingo, komanso n’nalembetsa mu Sukulu ya Ulaliki. Mpaka pano nimakumbukila mmene n’namvelela n’takwela pa kabokosi kuti nitalimpheko pokamba nkhani yanga yoyamba pa pulatifomu. Apo n’nali na zaka 6, ndipo n’nali na mantha kwambili kuyang’ana anthu akulu-akulu m’gulu.

Ulaliki wa mu msewu na makolo anga

Ponena za ulaliki, atate ananilembela ulaliki wacidule pa khadi kuti niziuseŵenzetsa mu utumiki. Nthawi yoyamba pamene n’napita nekha kukagogoda pakhomo la munthu, n’nali na zaka 8. N’nakondwela ngako mwininyumba ataŵelenga khadi yanga na kulandila buku lakuti “Mulungu Akhale Woona”! N’nathamangila kumsewu kuti nikauze atate. Ulaliki na misonkhano zinanibweletsela cimwemwe, ndipo zinanithandiza kuti nikulitse cikhumbo canga cotumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse.

Coonadi ca m’Baibo cinayamba kunifika pamtima kwambili atate atanilembetsela magazini a Nsanja ya Mlonda kuti nizilandila anga-anga. Nikangolandila kope yatsopano, n’nali kuiŵelenga. Cikhulupililo canga mwa Yehova cinakula, ndipo cinanisonkhezela kuti nidzipatulile kwa iye.

Monga banja, tinakapezeka pa msonkhano wa ku New York wa mu 1950 wa mutu wakuti, “Kuwonjezeka kwa Teokalase.” Pa Cinayi August 3, mutu wa tsikulo unali wakuti “Tsiku la Amishonale.” Patsikulo, M’bale Carey Barber amene pambuyo pake anatumikila m’Bungwe Lolamulila, ndiye anakamba nkhani ya ubatizo. Kumapeto kwa nkhani yake, M’baleyo atafunsa ife opita kuubatizo mafunso aŵili, nanenso n’naimilila na kuyankha kuti, “Inde!” Apo n’nali na zaka 11, koma n’nadziŵa kuti n’nacita cinthu cofunika kwambili. Koma n’nali kuwopa kuloŵa m’madzi cifukwa sin’nali kudziŵa kunyaya. Atate aang’ono ananipelekeza ku dziŵe ndipo ananitsimikizila kuti zonse zidzayenda bwino. Zoonadi, ubatizowo unacitika mofulumila kwambili, cakuti sin’naponde pansi n’komwe m’dziŵemo. N’nayendela m’manja mwa abale. Wina ananibatiza, basi winayo n’kunilandila kunitulutsa m’dziŵelo. Kucokela patsiku lofunika limenelo, Yehova wakhala akuwongola njila zanga.

KUSANKHA KUDALILA YEHOVA

N’tatsiliza sukulu n’nali kufuna kucita upainiya, koma aziphunzitsi anga ananituntha kuti nicite maphunzilo apamwamba. N’nagonja ku cikakamizo cawo, ndipo n’napita ku yunivesiti. Komabe, posapita nthawi n’nazindikila kuti n’zosatheka kukhalabe wolimba m’coonadi, panthawi imodzimodzi kusumika maganizo pa maphunzilo anga. Conco, n’nasankha kuleka maphunzilowo. N’natulila Yehova nkhaniyo m’pemphelo, ndipo n’nalemba kalata yolekela maphunzilowo, na kufotokoza mwaulemu m’kalatayo kuti nidzaleka maphunzilowo kumapeto kwa caka coyamba. Na cidalilo conse mwa Yehova, mwamsanga n’nayamba upainiya wanthawi zonse.

N’nayamba utumiki wanthawi zonse mu July 1957 m’tauni ya Wellingborough. N’napempha abale pa Beteli ya ku London kuti anipezele m’bale mpainiya amene ni ciyambakale kuti nizitumikila naye pamodzi. M’bale Bert Vaisey anakhala citsanzo cabwino kwa ine, ndipo khama lake linanithandiza kukhala na pulogilamu yabwino yolalikila. Mumpingo mmene tinali kutumikila munali ine, M’bale Vaisey, na alongo 6 acikulile. Kukonzekela na kutengako mbali m’misonkhano yonse kunanipatsa mipata yambili yokulitsa cidalilo canga mwa Yehova, na kufotokoza cikhulupililo canga.

Pambuyo pokhala m’ndende kwa nthawi yocepa cifukwa cokana kuloŵa usilikali, n’nakumana na mlongo Barbara mpainiya wapadela. Tinakwatilana mu 1959, ndipo tinali okonzeka kupita kulikonse kumene akanatitumiza. Poyamba tinatumizidwa kudela la Lancashire ca kumpoto koma kumadzulo pang’ono kwa England. Ndiyeno mu January 1961, n’naitanidwa kuti nikaloŵe Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya mwezi umodzi pa Beteli ya London. Kumapeto kwa sukuluyo n’nadabwa kuti ananitumiza m’nchito yadela. Kwa milungu iŵili n’nalandila maphunzilo kucokela kwa woyang’anila dela wina ciyambakale, mu mzinda wa Birmingham, ndipo Barbara analoledwa kuti azitumikila nane pamodzi. Kenako tinanyamuka kupita kumadela a Lancashire na Cheshire kukacita utumiki umene anatipatsa.

KUDALILA YEHOVA NDIYE CINTHU COYENELA KUCITA NTHAWI ZONSE

Tili pa chuti mu August 1962, tinalandila kalata kucokela ku ofesi yanthambi pamodzi na mafomu ofunsila Sukulu ya Giliyadi. Titapemphelela nkhaniyo, ine na Barbara tinasaina mafomuwo na kuwatumiza ku ofesi yanthambi mwamsanga monga mmene anatipemphela. Patapita miyezi isanu, tinanyamuka ulendo wopita ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, kukaloŵa Sukulu ya Giliyadi ya kalasi nambala 38. Sukulu yophunzitsa Baibo imeneyi inatenga miyezi khumi.

Ku Giliyadi tinaphunzila zambili za Mawu a Mulungu, gulu lake, komanso za ubale wathu wa padziko lonse. Tili m’zaka za m’ma 20, ine na Barbara tinaphunzila zambili kwa anzathu a m’kalasi. Unali mwayi wapadela kwa ine tsiku lililonse kuthandizila M’bale Fred Rusk pa nchito yake. Iye anali mmodzi wa alangizi athu. Mfundo imene anagogomeza kwambili pophunzitsa inali ya kufunika kopeleka uphungu mwacilungamo nthawi zonse, kutanthauza kuonetsetsa kuti uphungu wopelekedwa ni wozikidwa pa Malemba basi. Ena mwa alangizi athu anali abale aciyambakale monga Nathan Knorr, Frederick Franz, na M’bale Karl Klein. Ndipo ife ophunzila tinaphunzila zambili pa citsanzo ca kudzicepetsa kwa M’bale A. H. Macmillan, amene anationetsa mmene Yehova anali kutsogolela gulu lake panthawi ya ciyeso kucokela mu 1914 mpaka kumayambililo kwa 1919.

KUSINTHA KWA UTUMIKI WATHU

Cakumapeto kwa maphunzilowo, M’bale Knorr anauza ine na Barbara kuti adzatitumiza ku dziko la Burundi ku Africa. Mwamsanga tinapita ku laibulale ya pa Beteli kuti tikaone mu buku la pa caka, ofalitsa amene anali kutumikila ku Burundi panthawiyo. Tinadabwa kuti munalibe ziŵelengelo zilizonse za dzikolo! Inde, tinali kupita ku gawo la ku Africa limene silinafoledwepo. Ndipo tinali kudziŵa zocepa kwambili ponena za Africa. Tinali na nkhawa kwambili! Koma pemphelo linatikhazika mtima pansi.

Ku utumiki wathu watsopano, zonse zinali zosiyana na zimene tinazoloŵela—nyengo, cikhalidwe, na citundu. Tsopano, tinafunika kuphunzila ci French. Tinakumananso na vuto losoŵa kokhala. Patapita masiku aŵili cifikileni cathu ku Burundi, mmodzi mwa abale amene tinali nawo m’kalasi ya Giliyadi, dzina lake Harry Arnott, anaticezela pamene anali kubwelela kumene anali kutumikila ku Zambia. Iye anatithandiza kupeza nyumba imene inadzakhala nyumba yoyamba ya amishonale. Koma posapita nthawi, tinayamba kutsutsidwa na akulu-akulu a boma amene sanali kudziŵa kalikonse za Mboni za Yehova. Titangoyamba kusangalala na utumiki wathu, akulu-akulu a boma anatiuza kuti sitingapitilize kukhala m’dzikolo popanda cilolezo ca kugwila nchito. N’zomvetsa cisoni kuti tinafunika kucoka na kupita ku dziko lina ku Uganda.

Kudalila Yehova kunatithandiza kucepetsa nkhawa yathu poloŵa m’dziko la Uganda popanda cilolezo cokhalila m’dziko [visa]. M’bale wa ku Canada amene anali kutumikila kudela losoŵa ku Uganda, anafotokozela woona za oloŵa na otuluka m’dzikolo mmene zinthu zinalili kwa ife. Ndipo anatipatsa miyezi ingapo poyembekezela kutenga cilolezo cokhala m’dzikolo. Zimenezo zinationetsa kuti Yehova anali kutithandiza.

Kumene tinapita kukacitila utumiki wathu watsopano, zinthu zinali zosiyana kwambili na ku Burundi. Nchito ya Ufumu ku Uganda inali itakhazikitsidwa kale ngakhale kuti m’dziko lonselo munali cabe Mboni 28. M’dzikolo, munali anthu ambili okamba Cizungu. Koma posapita nthawi, tinazindikila kuti ngati tifuna kuthandiza anthu ambili acidwi kupita patsogolo, tinafunika kuphunzilako ngakhale cinenelo cimodzi pa zinenelo zambili za m’dzikolo. Tinayamba kulalikila m’madela a mu mzinda wa Kampala, kumene anthu ambili anali kukamba ci Luganda. Conco, tinaganiza zophunzila cineneloco. Kuphunzila cinenelo cimeneci kunatitengela zaka. Koma zinatithandiza kwambili kugwila bwino nchito yathu yolalikila. Tinayamba kumvetsa bwino zosoŵa zauzimu za anthu amene tinali kuphunzila nawo Baibo. Iwo anatsegula mitima yawo na kufotokoza mmene anali kumvelela pa zimene anali kuphunzila.

MAULENDO OSIYANA-SIYANA

Pa ulendo wokafuna-funa malo kumene apainiya apadela akanatsegula munda wa ulaliki, ku Uganda

Tinakondwela zedi kuthandiza anthu kuphunzila coonadi. Ndipo tinasangalalanso kwambili atatipatsa nchito yoyendela dziko lonse la Uganda. Motsogoleledwa na nthambi ya Kenya, tinanyamuka ulendo wokafuna-funa malo kumene apainiya apadela akanatsegula munda wa ulaliki. Nthawi zambili anthu amene anali asanamvepo za Mboni za Yehova anali kutilandila bwino kwambili. Anali kutithandiza kukhala omasuka, komanso anali kutikonzela cakudya.

N’nanyamukanso ulendo wina. Kucoka ku Kampala, n’nayenda ulendo wa masiku aŵili pa sitima kupita ku doko la Mombasa ku Kenya. N’napitiliza ulendowo na boti kupita ku Seychelles, cisumbu ca pa nyanja ya Indian Ocean. Pambuyo pake, kucokela mu 1965 mpaka mu 1972, Barbara anali kuyenda nane pa maulendo opita ku Seychelles. Poyamba kunali cabe ofalitsa aŵili. Koma pambuyo pake anakhala kagulu, kenako mpingo unakhazikitsidwa. Pa maulendo ena n’napita kukayendela abale ku Eritrea, Ethiopia, na ku Sudan.

Ku Uganda zandale zinali zitasintha kwambili asilikali atalanda ulamulilo wa boma mwaupandu. Panthawi yoopsa imeneyo, n’nakumbukila kuti n’cinthu canzelu kumvela malangizo akuti “pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” (Maliko 12:17) Panthawi ina, boma linafuna kuti alendo onse ocokela ku maiko ena akalembetse ku polisi ya kufupi na kumene amakhala. Mwamsanga tinamvela lamulolo. Patapita masiku ocepa, tikuyendetsa motoka mu mzinda wa Kampala, apolisi acinsinsi anaimitsa ine na mmishonale wina. Mitima yathu inali pha! pha! pha! kugunda cifukwa ca mantha. Iwo anatiimba mlandu wakuti tinali akazitape. Ndiyeno anatipeleka ku polisi yaikulu, kumene tinafotokoza kuti tinali amishonale amtendele. Tinafotokoza kuti tinalembetsa kale ku polisi. Koma zimenezo sizinaphule kanthu. Apolisiwo anatitengela ku polisi ya kufupi na nyumba ya amishonale. Mitima inakhalako m’malo pamene wapolisi amene tinapeza anatikumbukila kuti tinalembetsa kale. Ndipo anauza apolisi otilondela aja kuti atimasule.

Nthawi zambili tinali kucita mantha kwambili apolisi akatiimitsa pamsewu, maka-maka ngati taimitsidwa na asilikali amene anali kumwa moŵa kwambili. Koma nthawi zonse tinali kupemphela ndipo tinali kupeza mtendele mumtima akatilola kupita. Mwatsoka lanji, mu 1973 boma linalamula kuti amishonale onse ocokela ku maiko ena acoke mu Uganda.

Kupanga makope a Utumiki Wathu wa Ufumu mu mzinda wa Abidjan, pa ofesi yanthambi ya Côte d’Ivoire

Apanso utumiki wathu unasintha, tinapita kukatumikila ku dziko la Côte d’Ivoire, ku West Africa. Amenewa anali masinthidwe aakulu kwa ife. Tinafunika kuphunzila cikhalidwe catsopano, kuyambanso kukamba ci French nthawi zonse, na kuzoloŵela kukhala na amishonale ocokela ku maiko osiyana-siyana. Ngakhale n’telo, tinaonanso kuti Yehova anali kutsogolela nchito yake, cifukwa anthu odzicepetsa komanso oona mtima analandila uthenga wabwino mwamsanga. Tonse tinaona mmene kudalila Yehova kunawongolela njila zathu.

Koma zacisoni n’zakuti mkazi wanga Barbara anamupeza na khansa. Olo kuti tinapita ku maiko osiyana-siyana kukafuna cithandizo, mu 1983 zinaonekelatu kuti sitingapitilize kucita utumiki wathu mu Africa. Izi zinali zolefula kwambili kwa ife.

KUSINTHA KWA ZINTHU PA UMOYO

Matenda a khansa amene Barbara anali kudwala anakula kwambili pamene tinali kutumikila pa Beteli ya London, ndipo m’kupita kwa nthawi anamwalila. Banja la Beteli linanithandiza kwambili. Banja lina linanithandiza kuvomeleza zimene zinacitika na kudalila Yehova. Patapita nthawi, n’nakumana na mlongo wina amene anali kucita utumiki wa pa Beteli woyendela, amenenso anali atatumikilapo monga mpainiya wapadela. Cikondi cake pa Yehova cinaonetsa kuti anali munthu wauzimu. Ine na Ann tinakwatilana mu 1989, ndipo takhala tikutumikila pa Beteli ya London mpaka pano.

Nili na Ann kutsogolo kwa cimango ca nyumba ya Beteli yatsopano ya Britain

Kucokela mu 1995 mpaka mu 2018, nakhala na mwayi wotumikila monga woimila likulu (amene kale anali kuchedwa woyendela nthambi), ndipo nayendela maiko pafupi-fupi 60. Pa maulendo onsewa, naona mmene Yehova amadalitsila atumiki ake m’mikhalidwe yosiyana-siyana.

Mu 2017 n’napitanso ku Africa. N’nakondwela kwambili kupita na Ann ku Burundi, ndipo tinadabwa kuona kuculuka kwa anthu amene anabwela m’coonadi! M’mbali mwa msewu umene n’nali kulalikila nyumba na nyumba mu 1964, tsopano muli nyumba ya Beteli yokongola imene imayang’anila ofalitsa opitilila 15,500.

N’nakondwela kwambili n’talandila mndandanda wa maiko okacezela mu 2018. Pa mndandandawo panali dziko la Côte d’Ivoire. Titafika ku Abidjan, likulu la dzikolo, kwa ine zinali monga nafika kwathu. N’tayang’ana pa manambala a foni a pa Beteli kuti nione ali pafupi na cipinda cathu ca alendo, n’napeza kuti ni m’bale Sossou amene n’namukumbukila dzina lake. N’nakumbukila kuti anatumikilapo monga woyang’anila mzinda pamene n’nali mu mzinda wa Abidjan. Koma sanali m’bale uja amene n’namukumbukila. Anali m’bale Sossou wina, mwana wake.

Yehova wakwanilitsadi mawu ake. Pa mavuto onse amene napitamo, nafika podziŵa kuti tikam’dalila Yehova, amawongoladi njila zathu. Nifuna kupitilizabe kuyenda pa njila ya kuwala kosatha, imene idzawala kwambili m’dziko latsopano.—Miy. 4:18.