Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 7

‘Mvela Mawu a Anthu Anzelu’

‘Mvela Mawu a Anthu Anzelu’

“Chela khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzelu.” —MIY. 22:17.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani timapatsidwa uphungu? Nanga n’cifukwa ciani ni wofunikila kwa ife tonse?

 TONSEFE timafunikila uphungu nthawi na nthawi. Ndipo nthawi zina, tingafunike kuyamba ndife kufunsila uphungu kwa munthu amene timamudalila. Nthawi zinanso, m’bale amene amatikonda angatifikile na kutiuza kuti tayamba “kuloŵela njila yolakwika,” imene pambuyo pake ingatigwilitse fuwa la moto. (Agal. 6:1) Mwinanso, tingapatsidwe uphungu mwa kuongoleledwa tikacita colakwa cacikulu. Kaya uphunguwo taulandila pa zifukwa zotani, tiyenela kuumvela. Kucita zimenezi n’kopindulitsa kwa ife, ndipo kungapulumutse moyo wathu.—Miy. 6:23.

2. Malinga na Miyambo 12:15, n’cifukwa ciani tiyenela kumvela uphungu?

2 Lemba la mutu wa nkhani ino, litilimbikitsa ‘kumvela mawu a anthu anzelu.’ (Miy. 22:17) Palibe munthu adziŵa zonse, ndipo nthawi zambili pamakhala munthu amene amatiposa m’cidziŵitso, komanso maluso. (Ŵelengani Miyambo 12:15.) Conco, kumvela uphungu n’cizindikilo cakuti ndife odzicepetsa. Kumaonetsa kuti timadziŵa bwino zopeleŵela zathu, komanso kuti timafunikila thandizo kuti tikwanilitse zolinga zathu. Mfumu yanzelu Solomo inalemba kuti: “Aphungu akaculuka [zolingalila] zimakwanilitsidwa.”—Miy. 15:22.

Pa mitundu iŵili iyi ya uphungu, ni uti umene umakuvutankoni kuulandila? (Onani ndime 3-4)

3. Kodi tingalandile uphungu m’njila ziti?

3 Tingalandile uphungu wacindunji kapena usali wacindunji. Kodi titanthauza ciani tikati uphungu usali wacindunji? Mwacitsanzo, tingaŵelenga nkhani inayake m’Baibo kapena m’zofalitsa zathu imene ingatipangitse kuima na kusinkhasinkha, kenako n’kusintha maganizo athu na zocita zathu. (Aheb. 4:12) Umenewo ni uphungu usali wacindunji. Nanga uphungu wacindunji utanthauza ciani? Mkulu kapena m’bale wina wofikapo kuuzimu, angatichulile mbali inayake imene tiyenela kuwongolela. Umenewo ni uphungu wacindunji. Ngati munthu amene amatikonda watipatsa uphungu wozikika m’Baibo, tiyenela kuonetsa kuyamikila mwa kumvela uphunguwo na kuuseŵenzetsa.

4. Malinga n’kunena kwa Mlaliki 7:9, kodi tiyenela kupewa ciani tikapatsidwa uphungu?

4 Kukamba zoona, cingativute kulandila uphungu umene wapelekedwa mwacindunji. Tingafike ngakhale pokhumudwa. Cifukwa ciani? Olo kuti timavomeleza kuti ndife opanda ungwilo, cingativute kulandila uphungu munthu akatichulila mbali ina yake imene tinalakwitsa. (Ŵelengani Mlaliki 7:9.) Tingayambe kupeleka zifukwa zodzilungamitsa. Komanso tingakaikile zolinga za wopeleka uphunguyo, kapena tingakhumudwe na mmene waupelekela. Tingafike ngakhale pa kumupeza zifukwa, n’kumadziuza kuti: ‘Ameneyu sanganipatse uphungu, nayenso ali n’zolakwa zake.’ Ndipo ngati tiona kuti uphungu umene tapatsidwa si wotiyenelela, tingaunyalanyaze, kapena tingafunsile kwa ena amene tikudziŵa kuti adzatipatsa uphungu umene tingakonde.

5. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

5 M’nkhani ino, tikambilane zitsanzo za m’malemba za anthu amene anakana uphungu, komanso amene anaulandila. Tikambilanenso cimene cingatithandize kulandila uphungu kuti tipindule nawo.

AMENE ANAKANA UPHUNGU

6. Tiphunzilapo ciani pa zimene Rehobowamu anacita atapatsidwa uphungu wanzelu?

6 Ganizilani citsanzo ca Rehobowamu. Iye atakhala mfumu ya Isiraeli, anthu anabwela kwa iye na kum’pempha kuti awafeŵetseleko goli imene atate wake Solomo anawasenzetsa. Rehobowamu anacita bwino kufunsila nzelu kwa akulu-akulu Aisiraeli kuti adziŵe zimene angayankhe anthuwo. Akuluwo anauza mfumuyo kuti ngati adzacita zinthu zimene anthuwo amupempha, ndiye kuti anthuwo adzam’tumikila nthawi zonse. (1 Maf. 12:3-7) Komabe, Rehobowamu sanakhutile na malangizo amene anapatsidwa. Conco, anapita kukafunsila kwa anthu a msinkhu wake amene anakula naye limodzi. Anthuwo ayenela kuti anali na zaka za m’ma 40, amene mwacionekele anali kudziŵa zambili pa umoyo. (2 Mbiri 12:13) Koma iwo anapatsa Rehobowamu uphungu woipa. Anamuuza kuti aonjezele goli la anthuwo. (1 Maf. 12:8-11) Pokhala na malingalilo aŵili osiyana, Rehobowamu akanacita bwino kufunsila kwa Yehova m’pemphelo kuti amuthandize kudziŵa malangizo amene ayenela kutsatila. Koma iye anamvela anthu a msinkhu wake na kutsatila malangizo awo amene anam’komela. Izi zinabweletsa mavuto aakulu kwa Rehobowamu komanso kwa Aisiraeli. Mofananamo, si nthawi zonse pamene tingakonde malangizo amene tingapatsidwe. Ngakhale n’conco, ngati malangizowo azikika pa mawu a Mulungu, tiyenela kuwatsatila.

7. Kodi citsanzo ca Mfumu Uziya citiphunzitsa ciani?

7 Mfumu Uziya anakana uphungu. Iye analoŵa m’malo ena ake m’kacisi wa Yehova, kumene ansembe okha ndiwo anali kuloledwa kuloŵako, ndipo anafuna kupeleka nsembe yofukiza. Ansembe a Yehova anamuuza kuti: “Mfumu Uziya si nchito yanu kufukiza kwa Yehova, koma nchito yofukizayi ni ya ansembe.” Kodi Uziya anacita ciani? Sembe iye modzicepetsa anamvela uphunguwo na kucoka m’kacisi nthawi yomweyo, mwina Yehova akanam’khululukila. Koma “Uziya anakwiya kwambili.” N’cifukwa ciani iye anakana uphungu? Popeza anali mfumu, n’kutheka kuti anaona kuti ali na mphamvu zocita ciliconse cimene afuna. Koma Yehova sanakondwele na zimene anacita. Cifukwa ca kudzikuza kwake, Uziya anakanthidwa na khate, ndipo ‘anakhalabe wakhate mpaka tsiku limene anamwalila.’ (2 Mbiri 26:16-21) Citsanzo ca Uziya citiphunzitsa kuti kaya ndife munthu wotani, tikakana uphungu wozikika m’Baibo timataya ciyanjo ca Yehova.

AMENE ANAMVELA UPHUNGU

8. Kodi Yobu anacita ciani atapatsidwa uphungu?

8 Mosiyana na zitsanzo zoticenjeza zimene tangokambilana kumene, m’Baibo muli zitsanzo zabwino za anthu amene anadalitsidwa cifukwa comvela uphungu. Ganizilani za Yobu. Olo kuti anali munthu woopa Mulungu, iye sanali wangwilo. Cifukwa ca cipsinjo cake cacikulu, anakamba zinthu mosalingalila bwino. Izi zinapangitsa kuti Elihu, komanso Yehova am’patse uphungu mosapita m’mbali. Kodi Yobu anacita ciani? Modzicepetsa anamvela uphungu. Ndipo anati: “Ndinalankhula, koma sindinali kuzindikila . . . ndikubweza mawu anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Yehova anadalitsa Yobu cifukwa codzicepetsa.—Yobu 42:3-6, 12-17.

9. Kodi Mose anapeleka citsanzo cabwino cotani pankhani yolandila uphungu?

9 Mose ni mmodzi mwa anthu amene anamvela uphungu atacita mlandu waukulu. Panthawi ina, iye anakwiya kwambili ndipo sanalemekeze Yehova. Pa cifukwa cimeneci, Mose anataya mwayi woloŵa M’dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:1-13) Mose atapempha Yehova kuti aganizilenso za cigamulo cake cakuti sadzaloŵa m’dziko lolonjezedwa, iye anamuyankha kuti: “Usachulenso nkhani imeneyi kwa ine.” (Deut. 3:23-27) Mose sanakhumudwe. M’malo mwake, iye anagwilizana na cigamuloco, ndipo Yehova anapitiliza kumuseŵenzetsa potsogolela Aisiraeli. (Deut. 4:1) Yobu na Mose ni zitsanzo zabwino zimene tingatengeleko pa nkhani yomvela uphungu. Yobu anawongolela kaonedwe kake ka zinthu, ndipo sanapeleke zifukwa zodzikhululukila. Mose anaonetsa kuti anamvela uphungu wa Yehova mwa kukhalabe wokhulupilika ngakhale kuti anataya mwayi umene unali wamtengo wapatali kwa iye.

10. (a) Malinga na Miyambo 4:10-13, kodi timapindula bwanji tikalandila uphungu? (b) Kodi ena aonetsa mzimu wotani pamene apatsidwa uphungu?

10 Timapindula tikatengela citsanzo ca amuna okhulupilika monga Yobu na Mose. (Ŵelengani Miyambo 4:10-13.) Izi n’zimene abale na alongo athu ambili acita. Onani zimene anakamba m’bale wina dzina lake Emmanuel, wa ku Congo. Pa cenjezo limene anapatsidwa, iye anati: “Abale okhwima kuuzimu mu mpingo mwathu ataona kuti ubale wanga na Yehova uli pafupi kuwonongeka, ananithandiza kwambili. N’naseŵenzetsa uphungu wawo, ndipo unanithandiza kupewa mavuto ambili.” * Ponena za uphungu, mlongo wina ku Canada amene ni mpainiya anati: “Sinimamvela bwino nikapatsidwa uphungu, koma nimadziŵa kuti nifunikiladi uphunguwo.” Ndipo m’bale wina wa ku Croatia dzina lake Marko anati: “N’nataya mwayi wautumiki, koma nikayang’ana kumbuyo, nimaona kuti uphungu umene n’nalandila unanithandiza kulimbitsanso ubale wanga na Yehova.”

11. Kodi m’bale Karl Klein anati ciani pa nkhani yolandila uphungu?

11 Munthu wina amene anapindula atalandila uphungu ni m’bale Karl Klein, amene anali ciwalo ca Bungwe Lolamulila. M’mbili ya moyo wake, m’bale Klein anafotokoza kuti pa nthawi ina m’bale Joseph F. Rutherford, amene anali kugwilizana naye kwambili, anamupatsa uphungu wamphamvu. M’bale Klein anati poyamba anakhumudwa na uphungu umene anapatsidwa. Iye anati: “Tsiku lina [M’bale Rutherford] ataniona, mwacimwemwe ananipatsa moni kuti, ‘Muli bwanji m’bale Klein?’ Cifukwa cokhumudwabe na uphunguwo, n’nayankhila kukhosi. Iye anati, ‘M’bale Klein samala! Mdyelekezi akukulonda-londa.’ Mwamanyazi n’nayankha kuti, ‘Palibe vuto lililonse m’bale Rutherford.’ Koma iye anadziŵa kuti n’nakhumudwa. Conco, anabwelezanso cenjezo lake kuti, ‘Cabwino, koma samala. Mdyelekezi akukulonda-londa.’ M’bale Rutherford anakambadi zoona. Ngati tisungila m’bale wathu cakukhosi, makamaka ngati m’baleyo ni woyenelela kutipatsa uphungu, tingagwele mu msampha wa Mdyelekezi mosavuta.” * (Aef. 4:25-27) M’bale Klein analandila uphungu umene m’bale Rutherford anam’patsa, ndipo ubale wawo unakhalabe wolimba.

N’CIANI CINGATITHANDIZE KULANDILA UPHUNGU?

12. Kodi kudzicepetsa kungatithandize bwanji kulandila uphungu? (Salimo 141:5)

12 N’ciani cingatithandize kulandila uphungu? Kudzicepetsa. Tizikumbukila kuti ndife anthu opanda ungwilo, ndipo nthawi zina tingacite zinthu mopanda nzelu. Yobu amene tachula uja, anali na maganizo olakwika. Koma pambuyo pake iye anawongolela maganizo ake, ndipo Yehova anam’dalitsa. Cifukwa ciani? Cifukwa Yobu anali wodzicepetsa. Kudzicepetsa kwake kunaonekela pamene analandila uphungu kwa Elihu, ngakhale kuti Elihu anali wocepelepo kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Mofananamo, kudzicepetsa kudzatithandiza nafenso kuseŵenzetsa uphungu ngakhale pamene taona kuti sitinafunikile kupatsidwa uphunguwo, kapena ngati amene watipatsa uphunguwo ni wocepelapo kwa ife. Mkulu wina ku Canada anati: “Popeza sitimadziona mmene ena amationela, tingapite bwanji patsogolo popanda wina wotipatsa uphungu?” Ndani wa ife safuna kupita patsogolo pokulitsa zipatso zimene mzimu woyela umabala, komanso pocita utumiki wathu wacikhristu?—Ŵelengani Salimo 141:5.

13. Kodi tiyenela kuuona bwanji uphungu umene tapatsidwa?

13 Tiziona uphungu kukhala cikondi ca Mulungu pa ife. Yehova amatifunila zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa uphungu kupitila m’Mawu ake, m’zofalitsa zozikika pa Baibo, kapena Mkhristu wokhwima mwauzimu, ndiye kuti amatikonda. Iye “amatilanga kuti tipindule,” malinga n’kunena kwa Aheberi 12:9, 10.

14. Kodi tiyenela kuika maganizo athu pa ciani tikapatsidwa uphungu?

14 Ikani maganizo pa uphunguwo osati mmene aupelekela. Nthawi zina, tingaone kuti uphungu umene tapatsidwa sunapelekedwe m’njila yabwino. N’zoona kuti aliyense wopeleka uphungu, ayenela kuupeleka m’njila yakuti zisakhale zovuta kuulandila. * (Agal. 6:1) Koma ngati ndife tikupatsidwa uphungu, tingacite bwino kusumika maganizo pa phindu la uphunguwo, ngakhale pamene taona kuti sunapelekedwe m’njila yabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sin’nakonde mmene uphungu wapelekedwela, kodi pali cina cake cimene niphunzilapo pa uphunguwo? Kodi sininganyalanyaze zophophonya za wopeleka uphunguwo n’colinga cakuti nipindule nawo?’ N’cinthu canzelu kwa ife kuona mmene tingaseŵenzetsele uphunguwo kuti tipindule.—Miy. 15:31.

FUNSILANI UPHUNGU KUTI MUPINDULE NAWO

15. N’cifukwa ciani tiyenela kufunsila uphungu?

15 Baibo imatilimbikitsa kufunsila uphungu. Miyambo 13:10 imati: “Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambilana [kapena kuti kufunsila uphungu] amakhala ndi nzelu.” Mfundo imeneyi ni yoona. Aja amene amafunsila uphungu m’malo moyembekeza kuti wina acite kuwafikila, amapita msanga patsogolo mwauzimu koposa aja amene safunsila. Conco, yambani ndinu kufunsila uphungu kwa ena.

N’cifukwa ciani mlongo wacitsikanayu akufunsila uphungu kwa mlongo wokhwima kuuzimu? (Onani ndime 16)

16. Ni pa zocitika ziti pamene tingafunsile uphungu?

16 Ni pa zocitika ziti pamene tingafunsile uphungu kwa Akhristu anzathu? Ganizilani zocitika izi. (1) Mlongo wina akupempha wofalitsa waluso kuti akhale naye pa phunzilo la Baibo, ndiyeno pambuyo pake akum’pempha malangizo mmene angakulitsile luso lake la kuphunzitsa. (2) Mlongo amene ni mbeta akufuna kugula zovala. Conco, akupempha mlongo wokhwima mwauzimu kuti akambepo maganizo ake moona mtima pa zovala zimene wasankha. (3) M’bale wapatsidwa nkhani ya anthu onse kwa nthawi yoyamba. Iye akupempha mkambi waluso kuti amvetsele mosamala nkhani yake. Pambuyo pake, mkambiyo akupeleka malangizo othandiza kwa m’baleyo mmene angakulitsile luso lake la kuphunzitsa. Ngakhale m’bale amene ni ciyambakale pa kukamba nkhani, angacite bwino kufunsila malangizo kwa akambi aluso, na kuseŵenzetsa uphungu umene am’patsa.

17. Kodi uphungu ungatipindulile motani?

17 M’milungu kapena m’miyezi ikubwelayi, tonsefe tingadzapatsidwe uphungu, kaya mwacindunji kapena mosakhala mwacindunji. Izi zikacitika, kumbukilani mfundo zimene takambilana. Khalanibe wodzicepetsa. Sumikani maganizo pa uphungu osati mmene aupelekela. Komanso, seŵenzetsani uphungu umene mwapatsidwa. Palibe munthu amabadwa na nzelu. Koma ‘tikamvela uphungu na kutsatila malangizo,’ Mawu a Mulungu amatilonjeza kuti ‘tidzakhala anzelu.’—Miy. 19:20.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

^ ndime 5 Anthu a Yehova amadziŵa kuti kumvela uphungu wozikika m’Baibo n’kopindulitsa. Koma panthawi imodzimodzi, si copepuka kulandila uphungu na kuugwilitsila nchito. N’cifukwa ciani zili conco? Nanga n’ciani cingatithandize kupindula na uphungu umene tapatsidwa?

^ ndime 10 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 11 Onani Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya October 1, 1984, masa. 21-28.

^ ndime 14 M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene awo opeleka uphungu angaupelekele mosamala.