Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

N’napeza Cinthu Cabwino Kuposa Kukhala Dokotala

N’napeza Cinthu Cabwino Kuposa Kukhala Dokotala

“ZIMENE mukuniuza n’zimene nakhala nikulakalaka kuyambila nili mwana!” Izi n’zimene n’nauza banja lina kumbuyoku mu 1971, apo n’kuti nangotsegula cipatala canga-canga monga dokotala. Banjalo linali lodwala, ndipo linabwela kudzalandila cithandizo ca mankhwala. Kodi banjalo linali ndani? Nanga n’ciani cimene n’nali kulakalaka? Lekani nikusimbilenkoni mmene makambilanowo anasinthila zolinga zanga pa umoyo, komanso cifukwa cake n’nakhala wotsimikiza kuti zimene n’nali kulakalaka nili mwana zidzakwanilitsidwa posacedwa.

N’nabadwa mu 1941, mu mzinda wa Paris ku France. N’nali kukonda maphunzilo anga, koma n’zacisoni kuti n’tafika zaka 10, n’nadwala TB. Conco, n’nasiya kupita kusukulu. Madokotala ananilimbikitsa kuti nikhalebe kunyumba cifukwa mapapo anga sanali kugwila bwino nchito. Motelo, kwa miyezi ingapo imene n’nali pa nyumba, n’nayamba kuŵelenga dikishonale ina yake, komanso kumvetsela mapulogilamu a pa wailesi oulutsidwa na yunivesiti ya ku Paris. N’nakondwela ngako adokotala ataniuza kuti nacila ku matenda anga, komanso kuti nikhoza kubwelela ku sukulu. Mumtima n’nati; ‘Madokotala amagwila nchito yabwino kwambili.’ Kungoyambila nthawi imeneyo, n’nali kulakalaka kugwila nchito yocilitsa anthu matenda awo. Nthawi zonse atate akanifunsa zimene nifuna kukacita pa umoyo, n’nali kuwayankha kuti; “Nifuna kukakhala dokotala.” Conco, umu ni mmene zinayambila kuti nikhale na colinga codzakhala dokotala.

KUPHUNZILA ZASAYANSI KUNANITHANDIZA KUYANDIKILA MULUNGU

M’banja mwathu, tonse tinali akatolika. Ngakhale conco, sin’nali kudziŵa zambili za Mulungu, ndipo n’nali na mafunso ambili. Koma n’tayamba kuphunzila za udokotala pa yunivesiti, m’pamene n’nakhulupilila kuti moyo unacita kulengedwa.

N’nacita cidwi kwambili n’tayang’anitsitsa maselo a zomela poseŵenzetsa maikulosikopu. N’napeza kuti maselo amenewo, amadziteteza okha kukatentha komanso kukazizila. N’naona kuti mbali ya madzi-madzi ya selo (cytoplasm), imakhwinyata ngati aiika mu mcele, komanso imakula ngati aiika m’madzi. Izi zimapangitsa kuti zomela zipitilize kukhala na moyo ngakhale nyengo yasintha. N’naona kuti kucolowana kwa selo iliyonse ni umboni wakuti moyo sunangokhalako wokha.

Nili m’caka caciŵili ca maphunzilo anga a zaudokotala, n’napeza umboni wina woonetsa kuti Mulungu alikodi. Pamene tinali kuphunzila za thupi la munthu, tinaona kuti mmene mkono anaupangila zimathandiza kuti zala zathu zizibenda na kuwongoka. N’zocititsa cidwi kuona mmene minofu, komanso minyewa zimene n’zolumikizika ku mafupa zimagwilila bwino nchito capamodzi. Mwacitsanzo, n’naphunzila kuti minyewa yolumikizika ku minofu ya kumkono yopita ku fupa la ciŵili la zala zathu imagaŵika paŵili. Izi zimapangitsa kuti zala zathu zizigwila bwino nchito yake. Nayonso minyewa yolimba imathandiza kuti minyewa ina ikhalebe yolumikizika ku mafupa a zala zathu. Ngati zala zathu sizinapangidwe mwanjila imeneyi, cikanakhala covuta kuti zalazo zizigwila bwino nchito. Zonsezi zinanithandiza kukhala na umboni wamphamvu wakuti pali wina wake wanzelu kwambili amene analenga thupi la munthu.

Cidwi canga cofuna kudziŵa amene analenga munthu cinakula pamene n’nali kuphunzila zimene zimacitika mwana asanabadwe. N’naphunzila kuti mwana asanabadwe, amalandila mpweya wa oxygen kwa amayi ake kupitila mu cingwe ca pamucombo. Koma tumatumba twatung’ono twa mwanayo tosunga mpweya mkati mwa mapapo, tumakhala kuti situnadzale mpweya. Kukatsala milungu yocepa kuti mwana abadwe, madzi ena ake apadela ocedwa surfactant amaloŵa m’tumatumba twa mpweya tumeneto. Ndiyeno mwana akabadwa na kuyamba kudzipumila payekha, pamacitika zinthu zina zocititsa cidwi. M’boowo wa ku mtima kwa mwana umatsekeka, ndipo izi zimapangitsa magazi kuyamba kupita kumapapo. Pa nthawi yovutayi, madzi apadela aja amathandiza kuti tumatumba twa mpweya tuja tusagwilane pamene tudzala na mpweya. Nthawi yomweyo, mwanayo amayamba kudzipumila payekha.

N’nali kufuna kudziŵa uyo amene analenga zinthu zocititsa cidwi zimenezo. Conco, n’nayamba kuŵelenga Baibo mwakhama. N’nacita cidwi na malamulo okamba zaukhondo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli zaka zoposa 3,000 zapitazo. Mulungu analamula Aisiraeli kuti azifocela zonyansa zawo, kusamba m’manja kaŵili-kaŵili na madzi, komanso kubindikilitsa aliyense amene ali na zizindikilo za matenda oyambukila. (Lev. 13:50; 15:11; Deut. 23:13) Baibo inali itakambilatu mmene matenda amafalikila zimene a sayansi azitulukila posacedwa. Cina, n’naona kuti malamulo okamba za ciyelo pa nkhani ya kugonana opezeka m’buku la Levitiko, anathandiza mtundu wa Aisiraeli kupewa kupatsilana matenda. (Lev. 12:1-6; 15:16-24) N’nafika pozindikila kuti Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulowo kuti iwo apindule, komanso kuti anadalitsa anthu amene anamvela malamulo ake. N’nayamba kukhulupilila kuti Baibo inauzilidwa na Mulungu—Mulungu amene panthawiyo sin’nali kumudziŵa dzina lake.

MMENE N’NAPEZELA MKAZI WANGA KOMANSO YEHOVA

Ine na Lydie pa tsiku la ukwati wathu pa April 3, 1965

Pamene n’nali kucita maphunzilo a zaudokotala pa yunivesiti, n’nakumana na mtsikana wina dzina lake Lydie, amene n’nam’konda kwambili. Tinakwatilana mu 1965 apo n’kuti nili pakati pa maphunzilo anga. Podzafika mu 1971, tinali kale na ŵana atatu pa ana 6 amene tili nawo. Mkazi wanga wakhala akunicilikiza pa nchito yanga ya udokotala, komanso m’banja mwathu.

N’naseŵenza m’cipatala cina kwa zaka zitatu nisanatsegule cipatala canga-canga. Pasanapite nthawi yaitali, banja lina lodwala limene nachula kuciyambi kwa nkhani ino, linabwela kudzafuna cithandizo ca mankhwala. Nili pafupi kuwalembela mankhwala akuti akagule, mkazi wake anati: “Pepani adokotala, mulembe mankhwala amene alibe magazi.” Modabwa n’nati: “Cifukwa ciani?” Mayiyo anati: “Ndife Mboni za Yehova.” N’nali nisanamvelepo za Mboni za Yehova kapena mmene amaonela magazi. Mayiyo anatenga Baibo yake na kunionetsa cifukwa ca m’Malemba cimene amakanila kuikidwa magazi. (Mac. 15:28, 29) Kenako, iye pamodzi na mwamuna wake ananionetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacita, kuti udzathetsa imfa, matenda na kuvutika. (Chiv. 21:3, 4) Mwacimwemwe n’nati: “Zimene mukuniuza n’zimene nakhala nikulakalaka kuyambila nili mwana! N’nakhala dokotala kuti nithetse mavuto.” N’nakondwela kwambili cakuti tinakambilana kwa ola limodzi na hafu. Pamene banjalo linacoka, mu mtima sin’nalinso katolika ayi. N’naphunzila kuti Mlengi amene n’nali kufunitsitsa kumudziŵa, dzina lake ni Yehova!

Banjalo linabwela ku cipatala canga maulendo atatu, ndipo nthawi iliyonse likabwela tinali kukambilana kupitilila ola limodzi. N’naŵaitanila kunyumba kwanga n’colinga cakuti tikhale na nthawi yoculuka yokambilana za m’Baibo. Ngakhale kuti mkazi wanga anali kupezeka pa phunzilo la Baibo, iye sanagwilizane nazo zakuti ziphunzitso zina za akatolika zimene tinaphunzila zinali zabodza. Conco, n’naitanila m’busa wina kunyumba kwathu. Poseŵenzetsa cabe Baibo, tinakambilana ziphunzitso za m’Baibo mpaka usiku kwambili. Makambilano amenewo, anathandiza mkazi wanga kukhulupilila kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa coonadi. Kenako, cikondi cathu pa Yehova Mulungu cinakula cakuti mu 1974 tinabatizika.

KUIKA YEHOVA PATSOGOLO

Zimene n’naphunzila zokhudza colinga ca Mulungu kwa anthu, zinathandiza kuti cina cake cikhale cofunika kwambili mu umoyo wanga. Kutumikila Yehova ndiko kunakhala kofunika kwambili kwa ine na mkazi wanga. Tinayesetsa kulela ana athu m’coonadi. Tinaphunzitsa ŵana ŵathu kukonda Mulungu komanso anthu ŵena. Izi zinapangitsa kuti banja lathu likhale logwilizana kwambili.—Mat. 22:37-39.

Tikayang’ana kumbuyo, ine na mkazi wanga timakondwela kuona kuti ŵana ŵathu anaona kuti ndife ogwilizana pokhala makolo. Iwo anali kudziŵa kuti mawu a Yesu akuti, ‘Inde wanu akhaledi ‘inde,’ ‘Ayi’ wanu akhaledi ayi,’ linali lamulo m’banja mwathu. (Mat. 5:37) Mwacitsanzo, pamene mwana wathu wamkazi anafika zaka 17, mkazi wanga sanamulole kupita kokasangalala na anzake. Ena mwa anzake anauza mwana wathuyo kuti, “Ngati amayi ako akuletsa kupita pempha atate ako!” Koma mwana wathuyo anawayankha kuti: “Sizingathandize olo pang’ono. Iwo amagwilizana nthawi zonse.” Ana athu 6 anaona kuti ndife ogwilizana potsatila mfundo za m’Baibo. Timayamikila Yehova kuti tsopano ambili mwa acibale athu amamutumikila.

Ngakhale kuti coonadi cinasintha zolinga zanga pa umoyo, n’nali kufuna kuseŵenzetsa zimene n’naphunzila monga dokotala pothandiza anthu a Mulungu. Conco, n’nadzipeleka kugwila nchito ya udokotala pa Beteli ku Paris monga woyendela, kenako ninakatumikilanso pa Beteli yatsopano ku Louviers. Nakhala nikutumikila pa Beteli monga woyendela kwa zaka pafupi-fupi 50. Kwa nthawi yonseyi, napanga mabwenzi ambili a m’banja la Beteli, amene ena a iwo ali na zaka za m’ma 90. Tsiku lina n’nadabwa kwambili n’takumana na mtumiki wina wa pa Beteli watsopano. Zinapezeka kuti ndine n’nali dokotala amene anathandiza amayi ake kubeleka iye zaka ngati 20 kumbuyoku.

NAONA MMENE YEHOVA AMASAMALILA ANTHU AKE

M’kupita kwa zaka, cikondi canga pa Yehova cakulilako nikaona mmene iye amatsogolela anthu ake na kuwateteza kupitila m’gulu lake. Kumayambililo kwa 1980, Bungwe Lolamulila linakhazikitsa dongosolo ku America lothandiza madokotala na anthu ena a zacipatala kumvetsa cifukwa cake Mboni za Yehova zimasankha kusaikidwa magazi.

Ndiyeno mu 1988, Bungwe Lolamulila linakhazikitsa dipatimenti yatsopano pa Beteli yochedwa Ofesi Yothandiza pa Zacipatala. Poyamba, dipatimenti imeneyi inali kuyang’anila Komiti Yokambilana na a Zacipatala, imene inakhazikitsidwa ku America yothandiza Mboni zodwala kupeza cithandizo coyenela ca mankhwala cosaloŵetsamo magazi. Makonzedwe amenewa atakhazikitsidwa padziko lonse, makomiti okambilana na a zacipatala anakhazikitsidwa ku France. Nimacita cidwi kwambili nikaona mmene gulu la Yehova mwacikondi limathandizila abale na alongo odwala ofunikila thandizo la okambilana na a zacipatala.

ZIMENE N’NALI KULAKALAKA ZINAKWANILITSIDWA

Tikupitiliza kulalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu

Poyamba n’nali kukonda kwambili nchito ya udokotala. Koma n’taganizilapo mofatsa, n’naona kuti nchito yofunika kwambili pa umoyo wanga ni yocilitsa anthu mwauzimu—kutanthauza kuthandiza anthu kuyanjananso na Yehova Mulungu amene ni Gwelo la moyo. N’tapuma pa nchito yanga, ine na mkazi wanga tinayamba upainiya. Ndipo tinayamba kutaila maola ambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Tikupitiliza kucita zimene tingathe pa nchito yopulumutsa miyoyo imeneyi.

Ine na mkazi wanga mu 2021

Nikali kuthandizabe odwala mmene ningathele. Koma naona kuti ngakhale madokotala ophunzila kwambili, sangakwanitse kucilitsa matenda onse kapena kucinjiliza imfa. Conco, nimayembekezela mwacidwi nthawi pamene zopweteka, matenda, na imfa, sizidzakhalaponso. M’dziko latsopano la Mulungu limene likuyandikila, n’dzapitilizabe kuphunzila zokhudza cilengedwe ca Mulungu, kuphatikizapo mmene analengela thupi la munthu modabwitsa kwambili. Posacedwa, zimene n’nali kulakalaka nili mwana zidzakwanilitsika pa mlingo waukulu. Sinikaikila kuti zabwino zili kutsogolo!