Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Malipilo a ukwati anaphatikizapo kupeleka nyama

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

N’cifukwa ciani Aisiraeli kalelo anali kupeleka malipilo a ukwati?

PA NTHAWI ya anthu ochulidwa m’Baibo, malipilo a ukwati anali kupelekedwa ku banja la mkazi panthawi imene akukonza za ukwati. Malipilowo mwina anaphatikizapo zinthu zamtengo wapatali, nyama, kapena ndalama. Nthawi zina, malipilo a ukwati anali kukhala nchito imene munthu anali kugwilila banja la mkazi, monga zinalili kwa Yakobo. Kuti akwatile, iye anaseŵenzela atate ake Rakele zaka 7. (Gen. 29:17, 18, 20) Nanga n’cifukwa ciani anali kupeleka malipilo a ukwati?

Katswili wina wa Baibo dzina lake Carol Meyers anati: “Malipilo a ukwati anali ngati cipukuta misozi pa nchito zimene mtsikanayo anali kugwila, zomwe zinali zofunika ku mabanja omwe anali alimi.” Malipilowo ayenelanso kuti anali kuthandiza kulimbitsa ubale pakati pa mabanja aŵili—la kucimuna komanso la kucikazi. Cifukwa ca mgwilizano umenewo, mabanjawo anali kudzathandizana panthawi zovuta. Kuwonjezela apo, malipilo a ukwati anali kuonetsa kuti mkaziyo ni wotomeledwa, komanso kuti adzakhala pansi pa cisamalilo ca mwamuna wake, osati atate ake.

Kupeleka malipilo a ukwati sikunatanthauze kuti mkaziyo ni cinthu cakuti ungagule kapena kugulitsa. Buku lakuti Ancient Israel—Its Life and Institutions inati: “Kulipila ndalama kapena kanthu kena kolingana na mtengo wa malipilowo ku banja la mtsikana, mwacionekele kunacititsa ukwati waciisiraeli kuoneka monga ni kumugula mtsikana. Koma zioneka kuti [malipilo] amenewo anali monga cobwezela ku banja la mtsikana, osati mtengo wogulila mtsikanayo.”

Masiku ano, m’maiko ena anthu akali kutsatila mwambo umenewu wopeleka malipilo a ukwati. Makolo acikhristu akafuna kuti malipilo a ukwati apelekedwe, amafuna anthu ‘onse adziŵe kuti [iwo] ni ololela.’ (Afil. 4:5; 1 Akor. 10:32, 33) Akatelo, amaonetsa kuti si anthu “okonda ndalama,” kapena adyela. (2 Tim. 3:2) Kuwonjezela apo, ngati makolo acikhristu sachaja malipilo a ukwati okwela kwambili, zimathandiza kuti mwamuna wofuna kukwatila mwana wawo asakakamizike kusintha tsiku la ukwati, pofuna kuti akapeze ndalama zokwanila zokalipila. Kapena ngati mwamunayo ni mpainiya, sadzakakamizika kuleka upainiyawo, pofuna kuti azigwila nchito masiku onse kuti apeze ndalama zoculuka zimene anamuchaja.

M’maiko enanso, boma ndilo limakhazikitsa malipilo a ukwati. Zikakhala conco, makolo acikhristu ayenela kumvela malamulo amenewo. Cifukwa ciani? Mawu a Mulungu amati Akhristu ayenela ‘kumvela olamulila akulu-akulu,’ na kutsatila malamulo awo malinga ngati sasemphana na mfundo za Mulungu.—Aroma 13:1; Mac. 5:29.