Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 8

“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”

“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”

“Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.”—1 PET. 5:8.

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi Yesu anawauza ciyani ophunzila ake za “mapeto”? Nanga anawalimbikitsa kucita ciyani?

 KUTATSALA masiku ocepa kuti Yesu aphedwe, ophunzila ake anayi anam’funsa kuti: “Cizindikilo . . . ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciyani?” (Mat. 24:3) Ophunzila a Yesu amenewo anafunsa kuti adziŵe codzawaonetsa kuti mapeto a dongosolo la Ayuda ali pafupi. Powayankha, Yesu sanakambe cabe za mapeto a dongosolo la Ayuda limenelo, koma anakambanso za “mapeto a nthawi” imene tikukhalamoyi. Zakuti mapeto adzafika liti, Yesu anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.” Kenako, iye analimbikitsa ophunzila ake onse kuti ‘akhalebe chelu’ komanso ‘akhalebe maso.’—Maliko 13:32-37.

2. N’cifukwa ciyani Akhristu a m’zaka za zana loyamba anayenela kukhalabe maso?

2 Akhristu aciyuda a m’zaka za zana loyamba anayenela kukhalabe maso, cifukwa kupulumuka kwawo kunadalila kucita zimenezi. Yesu anafotokozela otsatila ake zocitika zodzaonetsa kuti mapeto a dongosolo la Ayuda ayandikila. Iye anati: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulila Yerusalemu, mudzadziŵe kuti ciwonongeko cake cayandikila.” Pa nthawi imeneyo, iwo anayenela kumvela cenjezo la Yesu na ‘kuyamba kuthaŵila kumapili.’ (Luka 21:20, 21) Aja amene anamvela cenjezo limeneli anapulumuka Aroma atawononga Yerusalemu.

3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Masiku anonso, tikukhala m’nthawi ya mapeto a dongosolo lino loipa la zinthu. Conco, nafenso tiyenela kukhala oganiza bwino, komanso kukhala maso. M’nkhani ino, tikambilane zimene zingatithandize kuti tikhalebe oganiza bwino pamene tikuona zocitika za m’dzikoli, mmene tingakhalile osamala m’zocita zathu, na mmene tingagwilitsile nchito bwino nthawi yotsalayi.

KHALANI OGANIZA BWINO MUKAMAONA ZOCITIKA ZA M’DZIKOLI

4. N’cifukwa ciyani tiyenela kucita cidwi poona mmene zocitika padzikoli zikukwanilitsila maulosi a m’Baibo?

4 Pa zifukwa zabwino, timacita cidwi kuona mmene zocitika m’dzikoli zikukwanilitsila maulosi a m’Baibo. Mwacitsanzo, Yesu anachula zocitika zotithandiza kudziŵa kuti mapeto a dongosolo la Satana ayandikila. (Mat. 24:3-14) Mtumwi Petulo anatilimbikitsa kukhala na cidwi pa kukwanilitsika kwa maulosi, kuti cikhulupililo cathu cikhalebe colimba. (2 Pet. 1:19-21) Buku lothela m’Baibo limayamba na mawu akuti: “Civumbulutso copelekedwa ndi Yesu Khristu, cimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chiv. 1:1) Conco, timacita cidwi kwambili na zocitika za m’dzikoli, kuti tidziŵe mmene zingakwanilitsile maulosi a m’Baibo. Ndipo tingakhale ofunitsitsa kukambilana zocitikazo pakati pathu.

Pokambilana maulosi a m’Baibo, kodi tiyenela kupewa ciyani? Nanga tiyenela kucita ciyani? (Onani ndime 5) b

5. Kodi tiyenela kupewa ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Onaninso zithunzi.)

5 Komabe, tikamakambilana maulosi a m’Baibo, tizipewa kukamba zongoganizila. Cifukwa ciyani? Cifukwa sitifuna kulankhula zinthu zimene zingasokoneze mgwilizano mumpingo. Mwacitsanzo, tingamve atsogoleli andale akukambilana mmene angathetsele mkangano wina wake kuti abweletse bata na mtendele. M’malo molankhula zongoganizila kuti mawu amenewo akukwanilitsa ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3, tiyenela kukhala na kamvedwe katsopano pa nkhani ngati zimenezi. Ngati makambilano athu azikika m’zofalitsa za gulu la Yehova, tidzathandiza mpingo kukhalabe wogwilizana pa “maganizo amodzi.”—1 Akor. 1:10; 4:6.

6. Kodi tiphunzilapo ciyani pa 2 Petulo 3:11-13?

6 Ŵelengani 2 Petulo 3:11-13. Mtumwi Petulo akutithandiza kukhala na maganizo oyenela tikamasanthula maulosi a m’Baibo. Iye anatilimbikitsa kuti ‘tizikumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Cifukwa ciyani? Osati kuti tidziŵe “tsiku na ola” limene Yehova adzabweletse Aramagedo ayi. Koma cifukwa timafuna kugwilitsa nchito bwino nthawi yotsalayi kuti ‘ticite nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’ (Mat. 24:36; Luka 12:40) M’mawu ena, timafuna kukhala oyela m’makhalidwe athu, na kuonetsetsa kuti zocita zathu potumikila Yehova zikuonetsa kuti timam’konda kwambili. Kuti izi zitheke, tiyenela kukhala osamala m’zocita zathu.

KODI TIYENELA KUCITA CIYANI POONETSA KUSAMALA PA ZOCITA ZATHU?

7. Kodi timaonetsa bwanji kuti tikusamala m’zocita zathu? (Luka 21:34)

7 Yesu sanangouza ophunzila ake kuyang’ana zocitika za m’dzikoli, koma anawauzanso kuti akhale osamala m’zocita zawo. Mfundo imeneyo ikumveketsedwa bwino m’cenjezo lili pa Luka 21:34. (Ŵelengani.) Yesu anatilimbikitsa kukhala osamala m’zocita zathu. Munthu amene amakhala wosamala, amakhala maso ku zilizonse zingawononge ubale wake na Yehova, ndipo amayesetsa kuzipewa. Mwa kutelo, iye amakhalabe m’cikondi ca Mulungu.—Miy. 22:3; Yuda 20, 21.

8. Kodi mtumwi Paulo analangiza Akhristu kucita ciyani?

8 Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azisamala m’zocita zawo. Mwacitsanzo, iye anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu.” (Aef. 5:15, 16) Uzimu wathu umakhala pa ciwopsezo nthawi zonse. N’cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti ‘tipitilize kuzindikila cifunilo ca Yehova,’ kuti tigonjetse mayeso alionse amene angawononge ubwenzi wathu na iye.—Aef. 5:17.

9. Kodi timadziŵa bwanji zimene Yehova afuna kuti tizicita?

9 Baibo siitiuza zonse zimene zingawononge ubwenzi wathu na Yehova. Nthawi zambili timafunika kupanga zisankho pa nkhani zimene sizichulidwa mwacindunji m’Malemba. Koma kuti tipange zisankho zanzelu, tiyenela kuzindikila “cifunilo ca Yehova.” Tingatelo mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse na kuwasinkhasinkha. Tikafika pocimvetsa bwino cifunilo ca Yehova, n’kukhala na “maganizo a Khristu,” cidzakhala capafupi kuyenda “ngati anzelu,” ngakhale pamene palibe lamulo lacindunji lotiuza zoyenela kucita. (1 Akor. 2:14-16) Zinthu zina zimene zingawononge ubwenzi wathu na Yehova n’zosavuta kuzizindikila, koma zina n’zovutilapo.

10. Kodi zina mwa zoopsa zoyenela kupewa ni ziti?

10 Zina mwa zoopsa zimene tiyenela kupewa ni kuceza mokopana, kumwa kwambili, kudya kwambili, mawu okhumudwitsa ena, kuonelela zaciwawa, zamalisece, na zina zotelo. (Sal. 101:3) Mdani wathu Mdyerekezi nthawi zonse amafunafuna mipata kuti awononge ubwenzi wathu na Yehova. (1 Pet. 5:8) Tikapanda kusamala, m’maganizo na mumtima mwathu Satana angabzalemo mbewu za kaduka, kusaona mtima, dyela, cidani, kudzikuza, komanso kusunga cakukhosi. (Agal. 5:19-21) Poyamba makhalidwe amenewa sangaoneke oopsa kwenikweni. Koma ngati siticitapo kanthu mwamsanga kuti tiwazule, adzapitiliza kukula monga comela cokhala na poizoni na kutibweletsela mavuto.—Yak. 1:14, 15.

11. Kodi cina coopsa covuta kucizindikila cimene tiyenela kupewa n’ciyani? Ndipo n’cifukwa ciyani?

11 Cina coopsa covuta kucizindikila ni mayanjano oipa. Onani citsanzo ici. Tinene kuti mumagwila nchito na munthu amene si Mboni. Ndipo mumafuna kuti mnzanu wa kunchitoyo akhale na kapenyedwe kabwino ka Mboni za Yehova. Conco, mukucita naye zinthu mokoma mtima, ndipo mumam’thandiza. Cinanso, mukuvomela kumadya naye cakudya camasana panthawi yopuma mwa apa na apo. Koma posakhalitsa, mukuyamba kudya naye nthawi zonse. Kenako, mukamaceza naye, iye nthawi zina amalankhula nkhani zoipa zimene poyamba simukugwilizana nazo. Koma m’kupita kwa nthawi, mukuyamba kuzoloŵela kumva nkhani zotelozo, moti mukuyamba kuona kuti zilibe vuto. Ndiyeno tsiku lina, mnzanuyo akukupemphani kuti mukamwe naye moŵa, ndipo mukuvomela. Pang’ono-m’pang’ono, mukuyambanso kutengela maganizo ake. N’zosacita kufunsa kuti posakhalitsa mudzayamba kutengela makhalidwe ake. N’zoona kuti tiyenela kucita zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu kwa aliyense. Koma tizikumbukila kuti timatengela kwambili khalidwe la anthu amene timagwilizana nawo. (1 Akor. 15:33) Tikamasamala m’zocita zathu monga mmene Yesu anatilimbikitsila, tidzapewa kugwilizana na anthu osatsatila malamulo a Yehova. (2 Akor. 6:15) Inde, tidzatha kuona tsoka, na kulipewa.

MUZIGWILITSA NCHITO BWINO NTHAWI YANU

12. Kodi ophunzila a Yesu anayenela kucita ciyani poyembekezela mapeto a dongosolo la zinthu?

12 Ophunzila a Yesu sanafunikile kukhala manja lende poyembekezela mapeto a dongosolo la zinthu. Yesu anawapatsa nchito. Iye anawalamula kuti azilalikila uthenga wabwino “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Iyi inali nchito yaikulu kwambili imene otsatila a Yesu anapatsidwa! Podzipeleka kuti acite utumiki umenewu, iwo anagwilitsa nchito bwino nthawi yawo.

13. N’cifukwa ciyani tiyenela kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu? (Akolose 4:5)

13 Ŵelengani Akolose 4:5. Kuti tizisamala m’zocita zathu, tiyenela kuganizila kwambili mmene timagwilitsila nchito nthawi yathu. Cifukwa n’cakuti “zinthu zosayembekezeleka” zingagwele aliyense wa ife. (Mlaliki 9:11) Mwadzidzidzi tingamwalile.

Kodi nthawi yathu tingaiseŵenzetse bwanji mwanzelu? (Onani ndime 14-15)

14-15. Kodi nthawi yathu tingaiseŵenzetse bwanji mwanzelu? (Aheberi 6:11, 12) (Onaninso cithunzi.)

14 Tingagwilitse nchito bwino nthawi yathu pocita cifunilo ca Yehova, na kulimbitsa ubwenzi wathu na iye. (Yoh. 14:21) Tiyenela kukhala “olimba, osasunthika, okhala ndi zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) Ndiyeno mapeto akadzafika, kaya adzakhale mapeto a moyo wathu kapena a dziko loipali, tidzaona kuti sitinasankhe molakwika.—Mat. 24:13; Aroma 14:8.

15 Masiku ano, Yesu akupitiliza kutsogolela otsatila ake pa nchito yolalikila za Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Iye wakhala akucita mbali yake. Kudzela m’gulu la Yehova, Yesu watiphunzitsa molalikilila, komanso watipatsa zida zotithandiza kufalitsa uthenga wabwino. (Mat. 28:18-20) Ifenso timacita mbali yathu tikamakangalika pa nchito yolalikila na kuphunzila, komanso tikamakhalabe maso pomwe tikuyembekezela Yehova kuthetsa dongosolo lino la zinthu. Ndipo tikatsatila uphungu wa pa Aheberi 6:11, 12, tidzagwilitsitsa ciyembekezo cathu “mpaka mapeto.”—Ŵelengani.

16. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani?

16 Yehova anaikilatu tsiku komanso ola limene adzawononge dziko la Satanali. Tsikulo likadzafika, Yehova mosalephela konse adzakwanilitsa maulosi onse opezeka m’Mawu ake. Koma nthawi zina tingaone monga mapeto akucedwa. Komabe, tsiku la Yehova ‘silidzacedwa.’ (Hab. 2:3) Conco, tiyeni tiyesetse ‘kudikila Yehova,’ inde ‘kuyembekezela moleza mtima Mulungu wa cipulumutso cathu.’—Mika 7:7.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

a M’nkhani ino, tikambilane zimene tingacite kuti tikhalebe oganiza bwino pamene tikuona zocitika za m’dzikoli. Cina, tione mmene tingakhalile osamala m’zocita zathu, komanso mmene tingaseŵenzetsele bwino nthawi yathu.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: (Pamwamba) Banja likumvetsela nyuzi. Ndiyeno pambuyo pa msonkhano wa mpingo, iwo akuuzako ena maganizo awo pa tanthauzo la zocitika zimene anaona pa nyuzi. (Pansi) Banja likuonelela ciunikilo ca Bungwe Lolamulila kuti liziyendela kamvedwe katsopano pa maulosi a m’Baibo. Iwo akugaŵila zofalitsa zozikika pa Baibo zokonzedwa na kapolo wokhulupilika.