NKHANI YOPHUNZILA 9
Yamikilani Mphatso ya Mulungu ya Moyo
“Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” —MAC. 17:28.
NYIMBO 141 Moyo ni Cozizwitsa
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Kodi Yehova amauona bwanji moyo wathu?
YELEKEZANI kuti mnzanu wakupatsani nyumba. Koma mbali zina za nyumbayo penti yake inatha, ndipo mtenje wake umadontha. Ngakhale kuti mbali zina n’zowonongeka, nyumbayo ni mphatso ya mtengo wapatali kwambili. Mosakaikila, mungayamikile mphatso ya nyumbayo ndipo mungamaisamalile bwino. Mofananamo, Yehova anatipatsa moyo umene ni mphatso ya mtengo wapatali. Ndipo Yehova anaonetsa kuti amaona moyo wathu kukhala wofunika mwa kupeleka mwana wake monga dipo.—Yoh. 3:16.
2. Monga ikambila 2 Akorinto 7:1, kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa ife?
2 Yehova ndiye Gwelo la moyo. (Sal. 36:9) Povomeleza mfundo ya coonadi imeneyi, mtumwi Paulo anati: “Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:25, 28) Conco, mpake kunena kuti moyo umene tili nawo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Iye mwacikondi amatipatsa zimene tifunikila kuti tikhale na moyo. (Mac. 14:15-17) Koma Yehova sateteza miyoyo yathu mozizwitsa. M’malo mwake, iye amayembekezela kuti tizidzisamalila bwino kuthupi komanso kuuzimu. (Ŵelengani 2 Akorinto 7:1.) N’cifukwa ciyani tiyenela kuteteza thanzi lathu na moyo wathu? Nanga tingacite bwanji zimenezo?
ONANI MPHATSO YA MOYO KUKHALA YOFUNIKA
3. N’cifukwa cina citi cimene timayesetsela kukhala na thanzi la bwino?
3 Cifukwa cina coyesetsela kukhala athanzi, n’cakuti m’pamene tingam’tumikile bwino kwambili Yehova. (Maliko 12:30) Timafunitsitsa kupeleka ‘matupi athu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu.’ Conco, timapewa kucita zinthu zimene tidziŵa bwino kuti zingawononge thanzi lathu. (Aroma 12:1) Komabe, ngakhale tiyesetse bwanji kusamalila thanzi lathu, timadwala ndithu. Ngakhale n’telo, timayesetsa kucita zimene tingathe kuti tikhale na thanzi, cifukwa timafuna kuonetsa Atate wathu kuti timayamikila mphatso ya moyo.
4. Kodi Mfumu Davide anafunitsitsa kucita ciyani?
4 Mfumu Davide anafotokoza cifukwa cake anaona mphatso ya Mulungu ya moyo kukhala yofunika pamene anati: “Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji ngati nditatsikila kudzenje la manda? Kodi fumbi lidzakutamandani? Kodi lidzalengeza kuti inu ndinu woona?” (Sal. 30:9) Davide ayenela kuti analemba mawu amenewa kumapeto kwa moyo wake. Ngakhale n’telo, iye anali kufunitsitsa kuti akhalebe na moyo komanso thanzi labwino kuti apitilizebe kutamanda Yehova. Mosakaika konse, tonsefe timafunitsitsa kucita zimenezo.
5. Kaya ndife okalamba kapena tikudwala, kodi n’zotheka kucita ciyani?
5 Matenda na ukalamba zingatiletse kucita zambili monga tinali kucitila kale. Zotulukapo n’zakuti tingalefuke. Koma tisataye mtima na kuleka kusamalila thanzi lathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa kaya ndife okalamba kapena tikudwala, n’zotheka kutamandabe Yehova monga anacitila Mfumu Davide. N’zolimbikitsa kudziŵa kuti ndife amtengo wapatali kwa Mulungu olo kuti ndife opanda ungwilo. (Mat. 10:29-31) Ngati tingamwalile lelo, iye ni wofunitsitsa kudzatiukitsa. (Yobu 14:14, 15) Conco, tifuna kusamalila thanzi lathu na kuteteza moyo wathu tikali moyo mmene tingathele.
PEWANI MACITIDWE OWONONGA THANZI LANU
6. Kodi Yehova amafuna kuti tizicita motani pa nkhani ya cakudya komanso zakumwa?
6 Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala kapena lophunzitsa za thanzi, imafotokoza maganizo a Yehova pa nkhani zimenezi. Mwacitsanzo, iye amatilangiza kuti ticotse zinthu zimene zingawononge thupi lathu. (Mlal. 11:10) Baibo imati tizipewa kudya kwambili na kumwa kwambili, cifukwa zimaika moyo wathu pa ciwopsezo. (Miy. 23:20) Yehova amafuna kuti tizisankha zimene timadya na kumwa, komanso kuculuka kwake.—1 Akor. 6:12; 9:25.
7. Kodi uphungu wa pa Miyambo 2:11, umatithandiza bwanji kupanga zisankho zabwino ponena za thanzi lathu?
7 Mwa kugwilitsa nchito luntha la kuzindikila, tikhoza kupanga zisankho zoonetsa kuti mphatso ya Mulungu ya moyo timailemekeza kwambili. (Sal. 119:99, 100; ŵelengani Miyambo 2:11.) Mwacitsanzo, timakhala osamala kwambili na zakudya zimene timadya. Ngati timakonda cakudya cina cake koma tapeza kuti cimatidwalitsa, nzelu zimatithandiza kucipewa. Cina, timaonetsa kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanila, tikamacita maseŵela olimbitsa thupi nthawi zonse, komanso tikamasunga mathupi athu na nyumba zathu zili zaukhondo.
MUZIYESETSA KUPEWA NGOZI
8. Malinga n’kunena kwa Baibo, kodi nkkhani ya citetezo ni yofunika motani kwa Mulungu?
8 M’cilamulo cimene Yehova anapatsa mtundu wa Isiraeli, munalinso malangizo owathandiza kupewa ngozi zoopsa panyumba komanso akamagwila nchito. (Eks. 21:28, 29; Deut. 22:8) Munthu akapha mnzake mwangozi, anali kupalamulabe mlandu woopsa. (Deut. 19:4, 5) Cilamuloco cinanena kuti ngakhale aja amene mwangozi avulaza mwana ali m’mimba, anayenela kulandila cilango. (Eks. 21:22, 23) Conco, Malemba amaonetsa kuti Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kupewa ngozi.
9. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti tizipewa ngozi? (Onaninso cithunzi.)
9 Timaonetsa kuyamikila mphatso ya Mulungu ya moyo ngati titsatila malangizo acitetezo panyumba, komanso tikamagwila nchito. Mwacitsanzo, potaya zinthu monga tuzitsulo twakuthwa, makemiko oopsa, kapena mankhwala, timasamala kuti zisavulaze anthu ena. Ndipo timaonetsetsa kuti ana asazione zinthu zimenezi. Komanso tikayatsa moto, kapena tikateleka madzi pamoto, tiyenela kukhalapo tikuyang’anila kuopela ana. Ndipo tikamagwilitsa nchito zida zamagetsi tisamazisiye zokha. Cinanso, timapewa kuyendetsa motoka tikamwa moŵa, tikatopa cifukwa cosagona mokwana, kapena ngati tikumwa mankhwala amphamvu amene angapangitse kuti cikhale covuta kuyendetsa motoka. Kuwonjezela apo, timapewa kuyendetsa motoka kwinaku tikuseŵenzetsa foni yam’manja.
TSOKA LIKAGWA
10. Kodi tiyenela kucita ciyani tsoka lisanagwe komanso likagwa?
10 Koma pali zocitika zina zosaletseka zoika moyo pa ciopsezo, monga ngozi zacilengedwe, milili, komanso nkhondo. Ngakhale n’telo, zinthu zimenezi zikacitika, timacita zotheka kuti tidziteteze potsatila malangizo omwe boma limapeleka. (Aroma 13:1, 5-7) Koma matsoka ena n’zotheka ndithu kuwakonzekela pasadakhale. Conco, cingakhale canzelu kutsatila malangizo alionse a boma otithandiza kukonzekela matsokawo. Mwacitsanzo, cingakhale cothandiza kusungilatu madzi na cakudya cosawonongeka msanga, komanso kabokosi ka mankhwala ogwilitsa nchito munthu akadwala mwadzidzidzi.
11. Kodi tiyenela kukhala okonzeka kucita ciyani matenda oyambukila akabuka?
11 Kodi tiyenela kucita ciyani ngati matenda oyambukila akufalikila m’dela lathu? Tiyenela kumvela malangizo a boma amene angapelekedwe, monga okhudza kusamba m’manja, kukhala motalikilana, kuvala mamasiki, na kubindikilitsidwa. Kutsatila malangizo ngati amenewa kumaonetsa kuti timayamikila kwambili mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa.
12. Kodi mfundo ya pa Miyambo 14:15 ingatithandize bwanji kukhala osamala na nkhambakamwa pa nthawi ya tsoka?
12 Matsoka akacitika, nthawi zina timamva nkhambakamwa zambili kwa mabwenzi athu, maneba athu, komanso m’nkhani zofalitsidwa. M’malo mongokhulupilila “mawu alionse” amene tamvela, tingacite bwino kukhulupilila zimene a boma komanso zimene madokotala odalilika anena. (Ŵelengani Miyambo 14:15.) Bungwe Lolamulila na maofesi a nthambi amacita zonse zotheka kuti akhale na cidziŵitso colondola asanapeleke citsogozo pa nkhani yokhudza misonkhano ya mpingo na nchito yolalikila. (Aheb. 13:17) Tikatsatila citsogozo cimene angapeleke, timadziteteza komanso kuteteza ena. Izi zingathandizenso kuti mpingo ukhale na mbili yabwino m’dela lathu.—1 Pet. 2:12.
KONZEKELANI KUPEWA MAGAZI
13. Pa nkhani ya magazi, kodi timaonetsa bwanji kuti timayamikila mphatso ya Mulungu ya moyo?
13 Anthu ambili amadziŵa kuti Mboni za Yehova zimaona magazi kukhala opatulika. Timamvela lamulo la Yehova lokhudza magazi mwa kukana kuikidwa magazi, ngakhale pamene tadwala mwadzidzidzi. (Mac. 15:28, 29) Koma izi sizitanthauza kuti imfa timaifuna ayi. Moyo timaukonda ngako monga mphatso yocokela kwa Mulungu. Timapempha thandizo la madokotala amene ni okonzeka kupeleka cithandizo ca mankhwala cabwino kwambili cosafuna kuikidwa magazi.
14. Kodi tingapewe bwanji kucitidwa opaleshoni?
14 Tikamasamalila thanzi lathu pocita zimene takambilana m’nkhani ino, tingapewe kucitidwa opaleshoni kapena njila zina zoopsa zocilitsila. Tikakhala athanzi, zinthu zimayenda bwino tikamacitidwa opaleshoni, komanso timacila mosavuta pambuyo pake. Ngati titsatila malamulo a pamsewu, kucotsa zinthu zomwe zingapangitse ngozi pakhomo kapena kunchito, tingapewe kucitidwa opaleshoni yadzidzidzi.
15. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kumayenda nayo khadi ya DPA yokonzedwa bwino nthawi zonse? (Onaninso cithunzi.) (b) Malinga na mmene tinaonela mu vidiyo, kodi tingapange bwanji cisankho canzelu pa nkhani yolandila cithandizo ca cipatala cofuna magazi?
15 Cifukwa cakuti timayamikila mphatso ya moyo, timadzaza khadi lopatsa munthu mphamvu yosasinthika yosankhilatu cithandizo ca mankhwala, na kumayenda na khadilo nthawi zonse. b Pa khadi limeneli timalembapo zimene tifuna zokhudza kugwilitsa nchito magazi, na zina zokhudza cithandizo ca mankhwala. Kodi zimene munalemba pa khadi yanu palibe casintha? Ngati mufunika kusaina khadi yatsopano, kapena mukufuna kusinthako zina, conde musazengeleze. Kulembelatu zofuna zathu pa nkhani ya zacipatala, kungathandize kuti tilandile cithandizo mwamsanga. Cina, tidzathandizanso madokotala kupewa kutipatsa cithandizo ca mankhwala cimene sicingatikomele. c
16. Kodi tingacite ciyani ngati sitidziŵa bwino molembedwa khadi ya DPA?
16 Kaya ndife acicepele kapena tili na thanzi labwino, tonsefe tikhoza kukumana na ngozi kapena kudwala. (Mlal. 9:11) Conco, n’cinthu canzelu kulemba khadi ya DPA. Ngati simudziŵa bwino molembela khadi imeneyi, pemphani akulu mu mpingo mwanu kuti akuthandizeni. Iwo amayesetsa kudziŵa bwino molembela khadi imeneyi. Koma sadzakupangila cisankho cokhudza cithandizo ca mankhwala cimene mungalandile. Umenewo ni udindo wanu. (Agal. 6:4, 5) Komabe, angakuthandizeni kumvetsa zolembedwa pa khadiyo, na mmene mungalembele zimene mwasankha.
KHALANI OLOLELA
17. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife ololela komanso oganiza bwino pa nkhani yokhudza thanzi?
17 Zisankho zambili zimene timapanga zokhudza thanzi lathu, na cithandizo ca mankhwala cimene tingalandile, zimadalila cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. (Mac. 24:16; 1 Tim. 3:9) Tikamapanga zisankho na kuzikambilana na anthu ena, tingacite bwino kutsatila uphungu wa pa Afilipi 4:5 wakuti: “Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.” Tikakhala ololela kapena kuti oganiza bwino, sitidzadela nkhawa kwambili za thanzi lathu, kapena kukakamiza ena kuyendela maganizo athu pa zisankho zimene tapanga. Timawakonda na kuwalemekeza abale na alongo athu, olo kuti zisankho zawo zingasiyane na zathu.—Aroma 14:10-12.
18. Kodi tingaonetse bwanji ciyamikilo cathu kaamba ka mphatso ya moyo?
18 Timaonetsa ciyamikilo cathu kwa Yehova, amene ndiye Gwelo la moyo, tikamateteza moyo wathu na kum’tumikila mmene tingathele. (Chiv. 4:11) Palipano, tizidwalabe na kukumana na matsoka. Koma ici sindiye cinali colinga ca Mlengi wathu ayi. Posacedwa, adzatipatsa moyo wosatha wopanda zoŵaŵa na imfa. (Chiv. 21:4) Pamene tikuyembekezela nthawiyo, timayamikila kwambili kukhala na moyo, komanso kutumikila Atate wathu wacikondi wakumwamba Yehova!
NYIMBO 140 Moyo Wosatha Watheka!
a Nkhani ino, itithandize kukulitsa ciyamikilo cathu pa mphatso ya Mulungu ya moyo. Tione zimene tingacite kuti tikhalebe athanzi komanso otetezeka tsoka likagwa, na mmene tingapewele ngozi. Tikambilanenso zimene tiyenela kucita kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kulandila cithandizo ca mankhwala tikadwala mwadzidzidzi.
b Khadili limadziŵikanso kuti DPA.
d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale wacinyamata akulemba khadi ya DPA, ndipo sakuiŵala kuinyamula.