NKHANI YOPHUNZILA 5
NYIMBO 27 Ana a Mulungu Adzaonekela
“Sindidzakusiyani Kapena Kukutayani Ngakhale Pang’ono”!
“Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’”—AHEB. 13:5b.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Kutsimikizila atumiki a Mulungu pano padziko lapansi kuti sadzasiyidwa osasamalilidwa Akhristu odzozedwa akadzatengeledwa kumwamba.
1. Kodi odzozedwa onse adzatengedwa liti kupita kumwamba?
ZAKA zambili kumbuyoku, atumiki a Yehova anali na funso lakuti, ‘Kodi ni liti pamene Akhristu odzozedwa adzatha kutengeledwa kumwamba?’ Tinali kuganiza kuti mwina pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, odzozedwa ena adzakhalapobe kwa kanthawi m’Paradaiso padziko lapansi. Koma mu Nsanja ya Mlonda ya July 15, 2013, tinaphunzila kuti odzozedwa onse amene alipo adzakhala atatha kutengeledwa kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanabuke.—Mat. 24:31.
2. Ni mafunso otani amene angabuke? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino?
2 Komabe, pangabuke funso lakuti: N’ciyani cidzacitika kwa “nkhosa zina” za Khristu zomwe zizitumikila Yehova mokhulupilika padziko lapansi panthawi ya “cisautso cacikulu”? (Yoh. 10:16; Mat. 24:21) Ena angade nkhawa kuti panthawiyo adzakhala atasiyidwa okha-okha opanda thandizo pamene abale na alongo awo odzozedwa adzatengeledwa kumwamba. Tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili za m’Malemba zimene zimapangitsa ena kumva conco. Pambuyo pake tikambilane zifukwa zimene sitiyenela kudela nkhawa.
ZIMENE SIZIDZACITIKA
3-4. Kodi ena mwa ife angakhale na nkhawa yotani? Cifukwa ciyani?
3 Ena angade nkhawa kuti popanda citsogozo ca abale odzozedwa a m’Bungwe Lolamulila, a nkhosa zina adzasocela n’kusiya coonadi. Mwina zocitika zina za m’Malemba n’zimene zimabweletsa mantha amenewo. Tiyeni tikambilaneko zitsanzo ziŵili. Citsanzo coyamba cikhudza Mkulu wa Ansembe Yehoyada. Anali mtumiki wokhulupilika wa Mulungu. Iye pamodzi na mkazi wake Yehosabati anateteza mnyamata wacicepele dzina lake Yehoasi. Cina, anamuthandiza kukhala mfumu yabwino, komanso yokhulupilika. Ndipo nthawi yonse pomwe Yehoyada anali moyo, Yehoasi anacita zoyenela. Koma Yehoyada atamwalila, posakhalitsa Yehoasi anayamba kucita zoipa. Iye anamvetsela kwa akalonga oipa, ndipo anasiya kutumikila Yehova.—2 Mbiri 24:2, 15-19.
4 Cocitika caciŵili cikhudza Akhristu omwe anakhalako m’zaka za zana laciŵili. Mtumwi Yohane, yemwe anali mtumwi wothela kumwalila, anapeleka cisonkhezelo cabwino kwa Akhristu ambili, na kuwathandiza kupililabe mu utumiki wawo kwa Yehova. (3 Yoh. 4) Yohane pamodzi na atumwi ena okhulupilika a Yesu, anamenyela nkhondo kwa nthawi ndithu kuti ampatuko asaloŵelele mu mpingo. (1 Yoh. 2:18) Komabe, Yohane atamwalila mpatuko unafalikila monga moto walupsa. M’zaka zocepa cabe, ampatuko amenewa anaphunzitsa ziphunzitso zambili zonama mu mpingo wa Cikhristu na kulekelela makhalidwe oipa.
5. Tisakhalepo na maganizo otani pa zitsanzo ziŵili zimenezi?
5 Kodi zitsanzo ziŵili izi za m’Malemba zionetsa kuti zidzakhalanso cimodzi-modzi kwa nkhosa zina za Khristu pamene odzozedwa adzatengedwe kupita kumwamba? Panthawi imeneyo, kodi Akhristu okhulupilika padziko lapansi adzasocela n’kusiya zimene anaphunzitsidwa monga mmene Yehoasi anacitila? Kapena kodi adzakhala ampatuko monga anacitila Akhristu ambili pambuyo pa zaka za zana loyamba? Yankho n’lakuti ayi! Tingakhale otsimikiza kuti pomwe Akhristu odzozedwa adzacoka pa dziko lapansi, a nkhosa zina adzasamalidwa bwino ndipo adzapitilizabe kucita zauzimu. N’ciyani citipangitsa kukhala otsimikiza?
KULAMBILA KOONA SIKUDZADETSEDWA
6. Ni nthawi zitatu ziti zimene tizikambitsilane mwacidule?
6 N’cifukwa ciyani tingakhale otsimikiza kuti kulambila koona sikudzadetsedwa, ngakhale m’nthawi zovuta zomwe zikubwela m’tsogolo? Cifukwa ca zimene taphunzila m’Baibo ponena za nthawi imene tikukhalamo. Nthawi imene tikukhalamoyi isiyana kwambili na nthawi ya mu Isiraeli wakale, komanso nthawi ya zaka za zana laciŵili la Akhristu. Conco, tiyeni tikambilane mwacifatse nthawi zitatu zimenezi: (1) Nthawi ya Aisiraeli, (2) nthawi imene atumwi onse atatha kumwalila, (3) nthawi yathu,— “nthawi za kubwezeletsa zinthu zonse.”—Mac. 3:21.
7. N’cifukwa ciyani Aisiraeli okhulupilika sanataye mtima pamene anthu ena, kuphatikizapo mafumu, anasankha njila yocita zoipa?
7 Nthawi ya Aisiraeli. Mose atatsala pang’ono kumwalila, anauza Aisiraeli kuti: “Pakuti ndikudziŵa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikila mudzacita zinthu zokuwonongetsani ndipo mudzapatuka ndi kusiya njila imene ndakulamulani kuyendamo” (Deut. 31:29) Mose anacenjezanso Aisiraeli kuti akadzapanduka, onse adzatengeledwa ku ukapolo. (Deut. 28:35, 36) Kodi mawu amenewo anakwanilitsidwa? Inde. Kwa zaka zambili, mafumu ambili anasankha kucita zoipa zomwe zinasoceletsa anthu a Mulungu. Cifukwa ca zimenezi, Yehova analanga anthu oipa a mu Isiraeli, ndipo sanalole kuti mafumu aciisiraeli apitilize kuwalamulila. (Ezek. 21:25-27) Komabe Aisiraeli okhulupilika analimbikitsidwa pomwe anaona mawu a Mulungu akukwanilitsidwa.—Yes. 55:10, 11.
8. Kodi tiyenela kudabwa kuti mumpingo wa Cikhristu wa mu zaka za zana laciŵili munaloŵa ampatuko? Fotokozani.
8 Atumwi onse atatha kumwalila. Kodi tiyenela kudabwa kuti mpingo wa m’zaka za zana laciŵili la Cikhristu munaloŵa ampatuko? Ayi. Yesu anali atalosela kuti kudzakhala mpatuko waukulu. (Mat. 7:21-23; 13:24-30, 36-43) Mtumwi Paulo, Petulo, komanso Yohane anatsimikizila kuti ulosi wa Yesu unali utayamba kale kukwanilitsidwa m’zaka za zana loyamba C.E. (2 Ates. 2:3, 7; 2 Pet. 2:1; 1 Yoh. 2:18) Pasanapite nthawi kwambili mtumwi wothela atamwalila, Akhristu ampatuko anakhala mbali ya Babulo Wamkulu, ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conyenga. Apanso, ulosi wouzilidwa unali kukwanilitsidwa.
9. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa nthawi yathu ino, nthawi ya Aisiraeli, komanso nthawi ya zaka za zana laciŵili ya mpingo wa Cikhristu?
9 “Nthawi za kubwezeletsa zinthu zonse.” Nthawi yathu isiyana na nthawi ya Aisiraeli, komanso nthawi pomwe mpatuko waukulu unayamba m’zaka za zana laciŵili. Kodi nthawi imene tikukhalamoyi imachedwa ciyani? Nthawi zambili timaicha “masiku otsiliza” a dongosolo lino loipa la zinthu. (2 Tim. 3:1) Koma Baibo imaonetsa kuti nyengo yaikulu, komanso yaitali inayamba panthawi imodzi-modziyo. Idzapitilizabe mpaka Ufumu wa Mesiya utabwezeletsa anthu ku ungwilo na kupangitsa dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. Nyengo imeneyi imachedwa “nthawi za kubwezeletsa zinthu zonse.” (Mac. 3:21) Nthawi imeneyi inayamba mu 1914 C.E. Kodi n’ciyani comwe cinali kubwezeletsedwa? Yesu anaikidwa pa mpando monga Mfumu kumwamba. Conco, Yehova anakhalanso na wolamulila womuimila, yemwe analoŵa m’malo Mfumu yokhulupilika Davide. Komabe, Yehova sanangobwezeletsa ufumu basi. Patangopita kanthawi kocepa kulambila koona kunayamba kubwezeletsedwa pamapeto pake! (Yes. 2:2-4; Ezek. 11:17-20) Kodi kulambila kumeneku kudzaipitsidwanso?
10. (a) Kodi Baibo inanenelatu ciyani za m’nthawi yathu ino ponena za kulambila koona? (Yesaya 54:17) (b) N’cifukwa ciyani maulosi otelo amatipatsa cidalilo?
10 Ŵelengani Yesaya 54:17. Ulosiwu ukunena kuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana”! Mawu ouzilidwa amenewa akukwanilitsidwa masiku ano. Mawu otonthoza otsatilawa akugwilanso nchito kwa ife m’nthawi yathu: “Ana ako onse adzakhala anthu ophunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendele wa ana ako udzakhala woculuka. Iwe udzakhazikika m’cilungamo. . . . sudzaopa aliyense. Ciliconse coopsa udzatalikilana naco, pakuti sicidzakuyandikila.” (Yes. 54:13, 14) Ngakhale Satana Mdyelekezi, “mulungu wa nthawi ino,” alibe mphamvu zolepheletsa nchito ya maphunzilo imene anthu a Yehova akucita. (2 Akor. 4:4) Kulambila koyela kunabwezeletsedwa, ndipo sikudzaimitsidwanso. Kudzapitilizabe kukhalako mpaka muyaya, kulibe cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti citivulaze comwe cidzapambana!
N’CIYANI CIDZACITIKA?
11. N’ciyani cimatitsimikizila kuti a khamu lalikulu sadzasiyidwa osasamalilidwa odzozedwa akadzapita kumwamba?
11 N’ciyani cidzacitike odzozedwa akadzatengedwa kupita kumwamba? Kumbukilani kuti Yesu ndiye M’busa wathu. Iye ndiye mutu wa Mpingo wa Cikhristu. Yesu ananena momveka bwino kuti: “Mtsogoleli wanu ndi mmodzi, Khristu.” (Mat. 23:10) Mfumu yathu yomwe ikulamulila tsopano, siidzalephela kugwila nchito yake. Pokhala kuti Khristu ndiye akutsogolela, otsatila ake onse pano padziko lapansi sadzaopa ciliconse. Inde, sitidziŵa mfundo zonse za mmene Yesu adzatsogolela anthu ake panthawiyo. Tiyeni tikambilaneko zitsanzo zina za m’Baibo zimene zingatipatse cidalilo.
12. Kodi Yehova anawasamalila motani anthu ake (a) Mose atamwalila? (b) Eliya atalandila utumiki wina? (Onaninso cithunzi.)
12 Mose anamwalila Aisiraeli asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa. N’ciyani cinacitika kwa anthu a Mulungu? Kodi Yehova anasiya kusamalila anthu ake munthu wokhulupilika ameneyu atamwalila? Ayi. Yehova anawasamalilabe maka ngati anthuwo anali okhulupilika kwa iye. Mose asanamwalile, Yehova anamuuza kuti aike Yoswa kukhala mtsogoleli wa anthu ake. Mose anaphunzitsa Yoswa kwa nthawi yaitali. (Eks. 33:11; Deut. 34:9) Kuwonjezela apo, panalinso amuna ena oyenela omwe anali kutsogolela anthuwo—atsogoleli a magulu a anthu 1000, 100, 50, ngakhale atsogoleli a magulu a anthu 10. (Deut. 1:15) Anthu a Mulungu anasamalidwa bwino. Timapezanso citsanzo cofanana na cimeneci kwa Eliya. Kwa zaka zambili iye ndiye anali kutsogolela anthu mu Isiraeli pa kulambila koona. Koma inafika nthawi pomwe Yehova anamusintha utumiki kuti akatumikile kum’mwela kwa Yuda. (2 Maf. 2:1; 2 Mbiri 21:12) Kodi anthu okhulupilika a mu ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli analeka kusamalidwa? Ayi. Eliya anaphunzitsa Elisa kwa zaka 50, ndipo kunalinso “ana a aneneli” amene anali kulandila maphunzilo ena ake a mogwilila nchitoyo. (2 Maf. 2:7) Conco, panali amuna ambili okhulupilika omwe anathandiza kutsogolela anthu a Mulungu. Cifunilo ca Yehova cinapitilizabe kukwanilitsidwa, ndipo anali kusamalilabe alambili ake okhulupilika.
13. Kodi timapeza citsimikizo cotani pa Aheberi 13:5b? (Onaninso cithunzi.)
13 Tili na zitsanzo zimenezi m’maganizo, muganiza n’ciyani cidzacitika pomwe odzozedwa othela adzatengedwa kupita kumwamba? Sitiyenela kuda nkhawa. Baibo imavumbula citsimikizo ici cakuti: Yehova sadzasiya anthu ake a padziko lapansi. (Ŵelengani Aheberi 13:5b.) Monga mmene zinalili na Mose komanso Eliya, kagulu kocepa ka Akhristu odzozedwa komwe kakutsogolela masiku ano, kamamvetsa ubwino wophunzitsako ena nchito. Kwa zaka zambili, abale a m’Bungwe Lolamulila akhala akuphunzitsa amuna a nkhosa zina nchito yotsogolela. Mwacitsanzo, iwo akhazikitsa masukulu ophunzitsa akulu, oyang’anila madela, abale a m’Komiti ya Nthambi, oyang’anila a pa Beteli komanso ena. Bungwe Lolamulila lakhala likuphunzitsa mwacindunji owathandiza m’makomiti awo osiyana-siyana. Abale othandiza amenewa akusenza maudindo akulu-akulu mokhulupilika. Iwo aphunzitsidwa bwino kuti apitilize kugwila nchito yosamalila nkhosa za Khristu.
14. Kodi taphunzila ciyani m’nkhani yathu?
14 Mfundo yaikulu imene takambilana m’nkhani ino ni yakuti: Odzozedwa akadzatha onse kutengedwa kupita kumwamba, cakumapeto kwa cisautso cacikulu, kulambila koyela kudzapitilazabe pano padziko lapansi. Ndife oyamikila kuti utsogoleli wa Khristu udzathandiza kuti olambila Mulungu adzapitilize kumulambila mokhulupilika. N’zoona kuti panthawiyo Gogi wa Magogi adzatiukila, amene ni mgwilizano wankhanza wa mitundu. (Ezek. 38:18-20) Koma kutiukila kwa kanthawi kumeneku sikudzapambana; sikudzalepeletsa anthu a Mulungu kulambila Yehova. Iye adzawapulumutsa ndithu! M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” lomwe ni gulu la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘latuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Inde, iwo adzatetezedwa!
15-16. Malinga na Chivumbulutso 17:14, kodi odzozedwa a Khristu adzacita ciyani pa nkhondo ya Aramagedo? N’cifukwa ciyani zimenezi n’zolimbikitsa?
15 Komabe, ena angafunsebe kuti: ‘Nanga bwanji za odzozedwa? Kodi iwo adzacita ciyani akadzacoka pa dziko lapansi?’ Baibo imafotokoza zimene iwo adzacita. Imavumbula kuti maboma a dzikoli “adzamenyana ndi Mwanawankhosa.” N’zodziŵikilatu kuti iwo adzagonja. Timaŵelenga kuti: “Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.” Kodi ndani adzamuthandiza pa nkhondoyi? Ni awo amene ni “oitanidwa,” “osankhidwa,” komanso “okhulupilika.” (Ŵelengani Chivumbulutso 17:14.) Kodi amenewa ndani? Odzozedwa amene aukitsidwa! Conco, odzozedwa othela akadzatengedwela kumwamba cakumapeto kwa cisautso cacikulu, umodzi wa mautumiki awo oyamba kudzakhala kumenya nkhondo. Umenewu ni utumiki wapadela zedi! Ena mwa odzozedwa anagwilako nchito ya usilikali m’dzikoli. Koma pambuyo pake anakhala Akhristu enieni, ndipo anaphunzila kukhala mwamtendele na ena. (Agal. 5:22; 2 Ates. 3:16) Iwo anasiya kucilikiza nkhondo. Komabe, pambuyo popita kumwamba, adzatumikila limodzi na Khristu komanso angelo ake oyela, pomenya nkhondo yothela yolimbana na adani a Mulungu.
16 Ganizilani mfundo iyi. Padziko lapansi, ena mwa Akhristu odzozedwa ni acikulile ndipo alibe mphamvu. Koma akadzaukitsidwa kukakhala kumwamba, adzakhala zolengedwa zauzimu zamphamvu, komanso zosakhoza kufa. Ndiponso adzatumidwa kukamenya nkhondo pamodzi na Yesu Khristu, Mfumu yawo yacisilikali. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, iwo adzagwila nchito pamodzi na Yesu kuthandiza anthu kufika pa ungwilo. Mosakaikila, iwo akadzakhala kumwamba adzacitila abale na alongo awo zinthu zambili zabwino, zomwe sakanakwanitsa kucita ali anthu opanda ungwilo!
17. Tidziŵa bwanji kuti atumiki a Mulungu adzakhala otetezeka pa nkhondo ya Aramagedo?
17 Kodi ndinu wa nkhosa zina? Ngati n’telo, kodi mudzafunika kucita ciyani nkhondo ya Aramagedo ikadzayamba? Mungacite izi: Kukhulupilila Yehova, na kutsatila citsogozo cake. Kodi zimenezo zidzapatikizapo ciyani? Baibo imanena mawu awa otonthonza: “Inu anthu anga, pitani mukaloŵe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Atumiki onse okhulupilika a Mulungu, kumwamba na padziko lapansi, adzakhala otetezeka panthawiyo. Mofanana na mtumwi Paulo, nafenso ndife otsimikiza kuti “maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwela m’tsogolo . . . sizidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu.” (Aroma 8:38, 39) Nthawi zonse muzikumbukila mfundo iyi: Yehova amakukondani, ndipo sadzakusiyani!
ODZOZEDWA AKADZATHA KUTENGELEDWA KUMWAMBA,
-
n’ciyani comwe sicidzakacitika?
-
n’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti kulambila koyela sikudzadetsedwa?
-
n’cifukwa ciyani tiyenela kudalila kuti Yehova adzawasamalilabe anthu ake?
NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵilapo Pathu