Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

Cifukwa Cake Timayamikila Kuti Yehova Amatikhululukila

Cifukwa Cake Timayamikila Kuti Yehova Amatikhululukila

“Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.”​—YOH. 3:16.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kukulitsa ciyamikilo cathu pa kukhululuka kwa Yehova. Tidzacita zimenezi mwa kuona zimene Yehova anacita kuti macimo athu akhululukidwe.

1-2. Kodi mkhalidwe wathu ulingana motani ndi wa mnyamata amene tam’chula m’ndime 1?

 TIYELEKEZE motele: Mnyamata wokulila m’banja lolemela akusangalala ndi umoyo wawofuwofu. Kenako tsoka likugwa m’banja mwawo. Kwabwela uthenga wakuti makolo ake onse awili amwalila pangozi yapamsewu. Nkhani imeneyi ikumubweletsela cisoni cacikulu. Ali ndi cisonico, akumvanso zakuti makolo akewo anawononga cuma conse ca banjalo, ndipo asiya nkhongole zosaneneka. Tangoganizani! M’malo momusiyila cuma ca banjalo monga colowa cake, makolo akewo amusiyila colowa ca nkhongole zothetsa nzelu. Eni ake ndalamazo akuzifuna zivute zitani! Koma iye sangakwanitse kuzibweza nkhongolezo.

2 Mwa njila ina, mkhalidwe wathu ukulingana ndi wa mnyamata uja. Makolo athu oyambilila, Adamu ndi Hava, anali angwilo ndipo anali kukhala m’paradaiso wokongola. (Gen. 1:27; 2:​7-9) Anali ndi mwayi wokhala ndi moyo wacimwemwe kwamuyaya, koma zinthu zinasintha iwo atacimwa. Anataya mwayi wokhala m’Paradaiso, komanso wokhala ndi moyo wosatha. Kodi ana awo am’tsogolo anali kudzalandila ciyani monga colowa? Baibulo limatiuza kuti: “Ucimo unalowa mʼdziko kudzela mwa munthu mmodzi ndipo ucimowo unabweletsa imfa. Conco imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) Colowa cimene tinalandila kwa Adamu ndi ucimo umene umabweletsa imfa. Ucimo umenewu uli ngati nkhongole yaikulu imene palibe aliyense wa ife angakwanitse kuibweza.​—Sal. 49:8.

3. N’cifukwa ciyani macimo athu tingawafananitse ndi nkhongole?

3 Baibulo limafananitsa ucimo ndi nkhongole. (Mat. 18:​32-35) Conco, tikacimwa zimakhala ngati takhala ndi nkhongole kwa Yehova, ndipo timafunika kuibweza. Ngati sitinaibweze, nkhongoleyo imafafanizidwa kokha tikamwalila.​—Aroma 6:​7, 23.

4. (a) Popanda thandizo, n’ciyani cikanacitika kwa ocimwa onse? (Salimo 49:​7-9) (b) Kodi mawu akuti “chimo” amatanthauza ciyani m’Baibulo? (Onani danga lakuti “ Chimo.”)

4 Pa ife tokha, n’zosatheka kupezanso zabwino zonse zimene Adamu ndi Hava anataya. (Welengani Salimo 49:​7-9.) Popanda thandizo, tikanakhala tilibe ciyembekezo codzakhala ndi moyo m’tsogolo kapena codzaukitsidwa. Tikanakhala opanda ciyembekezo monga mmene zimakhalila nyama ikafa.​—Mlal. 3:19; 2 Pet. 2:12.

5. Kodi Atate wathu wacikondi anatithandiza bwanji pa nkhongole ya ucimo imene tinalandila monga colowa? (Onani cithunzi pa )

5 Ganizilani za mnyamata amene tam’chula m’ndime 1. Muganiza akanamva bwanji ngati munthu wina wacuma akanadzipeleka kuti abweze nkhongole zake zonse? Mosakaikila, mnyamatayo akanayamikila kwambili kuwolowa manja kwa munthuyo ndipo akanavomela thandizo lake. Mofananamo, Atate wathu wacikondi Yehova, watipatsa mphatso imene imabweza nkhongole zonse za ucimo zimene tinalandila monga colowa kwa Adamu. Pokamba za mphatso imeneyi, Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupilila asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Kuwonjezela apo, mphatso imeneyi imatipatsa mwayi wokhala paubwenzi wabwino ndi Yehova.

Yesu analalikila uthenga wabwino wonena za kukhululukidwa ndi Yehova pa maziko a nsembe ya dipo. (Yoh. 3:16) Mofunitsitsa, iye anapeleka moyo wake monga dipo (Onani ndime 5)


6. Kodi tikambilane mawu ati a m’Baibulo m’nkhani ino? Nanga n’cifukwa ciyani?

6 Timapindula motani ndi mphatso yabwino imeneyi, yomwe imacititsa kuti macimo athu akhululukidwe? Tiyankhe funso limeneli mwa kukambilana mawu amene Baibulo limagwilitsa nchito pankhani imeneyi. Mawuwa ndi akuti kuyanjananso, kuphimba macimo, kugwilizananso, dipo, kuwombola, komanso kuonedwa kukhala olungama. Pokambilana mawu amenewa, tidzamvetsetsa ndi kuyamikila kwambili zimene Yehova anacita kuti macimo athu akhululukidwe.

YEHOVA ANAFUNA KUTI TIYANJANENSO NAYE

7. (a) N’ciyaninso cina cimene Adamu ndi Hava anataya? (b) Monga mbadwa za Adamu ndi Hava, timafunikila kwambili ciyani? (Aroma 5:​10, 11)

7 Adamu ndi Hava sanangotaya mwayi wokhala ndi moyo wosatha, koma anatayanso mwayi wamtengo wapatali wokhala paubale wabwino ndi Atate wawo, Yehova. Paciyambi, Adamu ndi Hava anali m’banja la Mulungu. (Luka 3:38) Koma pomwe sanamvele Yehova, anacotsedwa m’banja limenelo asanayambe kubeleka ana. (Gen. 3:​23, 24; 4:1) Ifeyo monga mbadwa zawo, tinafunikila kuyanjananso ndi Yehova. (Welengani Aroma 5:​10, 11.) M’mawu ena, tifunikila kupanga ubale wabwino ndi iye. Malinga ndi buku lina lofotokozela Baibulo, mawu a Cigiriki akuti “kuyanjana” omwe ali pa Aroma 5:​10, 11, amagwilitsidwa nchito pofotokoza “za anthu awili amene akhalanso mabwenzi pambuyo pokhala paudani.” N’zocititsa cidwi kuti Yehova ndiye anayamba kucitapo kanthu kuti zimenezi zitheke. Anacita bwanji zimenezi?

ANAKHAZIKITSA MAKONZEDWE OPHIMBA MACIMO

8. (a) Kodi kuphimba macimo n’kutani? (b) Nanga kugwilizananso kutanthauza ciyani?

8 Kuphimba macimo ndi makonzedwe amene Yehova anakhazikitsa kuti abwezeletse ubale wabwino pakati pa iye ndi anthu ocimwa. Izi zimaphatikizapo kusinthanitsa zinthu ziwili zolingana mtengo. Mwa njila imeneyi, cinthu cimene catayika, kapena cimene cawonongeka, cingabwezeletsedwe. Malemba a Cigiriki a Cikhristu amagwilitsa nchito mawu ofananako tanthauzo ndi mawu akuti “kuphimba macimo” omwe ndi kugwilizananso. (Aroma 3:25) Munthu akagwilizananso ndi Mulungu amakhala naye pa mtendele, ndipo amakhala paubale wabwino ndi iye.

9. Ndi makonzedwe ati apakanthawi amene Yehova anapanga kuti macimo a Aisiraeli azikhululukidwa?

9 Yehova anapanga makonzedwe apakanthawi akuti macimo a Aisiraeli azikhululukidwa kuti akhale paubale wabwino ndi iye. M’nthawi ya Aisiraeli, Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo linali kukhalako kamodzi pa caka. Patsiku limenelo, mkulu wa ansembe anali kupeleka nsembe yanyama moimilako anthu onse. Ngakhale n’telo, nsembe zanyama sizinali kuphimbilatu macimo a anthu, cifukwa nyama ndi zamoyo zotsika poziyelekezela ndi anthu. Komabe, Yehova anali wokonzeka kukhululuka macimo a Aisiraeliwo ngati apeleka nsembe mogwilizana ndi zimene iye anali kufuna. (Aheb. 10:​1-4) Makonzedwe akuti azipeleka nsembe nthawi zonse akacimwa anali kuwakumbutsa kuti analidi anthu ocimwa. Anali kuwakumbutsanso kuti anafunikila makonzedwe acikhalile owakhululukila macimo.

10. Ndi makonzedwe acikhalile ati okhululuka macimo amene Yehova anakhazikitsa?

10 Yehova anali nawo kale m’maganizo mwake makonzedwe acikhalile odzathandiza anthu kukhululukidwa macimo awo. Iye anapanga makonzedwe akuti Mwana wake wokondeka apelekedwe “nsembe kamodzi kokha kuti anyamule macimo a anthu ambili.” (Aheb. 9:28) Yesu anabwela “kudzapeleka moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.” (Mat. 20:28) Kodi dipo n’ciyani?

ANALIPILA MTENGO WA DIPO

11. (a) Malinga n’kunena kwa Baibulo, kodi dipo n’ciyani? (b) Ndi munthu wotani amene anali woyenelela kupeleka dipo?

11 Malinga n’kunena kwa Baibulo, dipo ndi malipilo amene amapelekedwa kuti aphimbe macimo, komanso kuti anthu ayanjanitsidwe kwa Mulungu. a M’maso mwa Yehova, dipo ndi maziko obwezeletsa zimene zinatayika. M’lingalilo lotani? Kumbukilani kuti Adamu ndi Hava anataya moyo wangwilo limodzi ndi ciyembekezo cokhala ndi moyo kwamuyaya. Cotelo, dipo linafunika kukhala lolingana ndendende ndi zomwe zinatayika. (1 Tim. 2:6) Dipo linayenela kupelekedwa kokha ndi mwamuna wamkulu msinkhu (1) wangwilo, (2) amene akanatha kukhala kwamuyaya padziko lapansi, komanso (3) amene anali wokonzeka kupeleka moyo wake nsembe kaamba ka ife. Moyo wa munthu ameneyo ndi wokhawo umene ukanakwanitsa kulowa m’malo kapena kubwezeletsa moyo umene unatayika.

12. N’ciyani cinayeneleza Yesu kupeleka mtengo wa dipo?

12 Tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene zinayeneleza Yesu kupeleka mtengo wa dipo. (1) Iye anali wangwilo​—“sanacite chimo” lililonse. (1 Pet. 2:22) (2) Pa cifukwa cimeneci, iye akanakwanitsa kukhala ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi. (3) Iye anali wokonzeka kutifela ndi kupeleka moyo wake kaamba ka ife. (Aheb. 10:​9, 10) Monga munthu wangwilo, Yesu anali wofanana ndi munthu woyambilila, Adamu, asanacimwe. (1 Akor. 15:45) Conco, imfa ya Yesu inaphimba macimo a Adamu, kutanthauza kuti inakwanitsa kubwezeletsa zimene Adamu anataya. (Aroma 5:19) Mwa kutelo, Yesu anakhala “Adamu womalizila.” Cotelo, sipafunikilanso munthu wina wangwilo kuti abwele kudzalipila zimene Adamu anataya. Yesu anafa “kamodzi kokha kuti akhale nsembe yothandiza anthu mpaka kalekale.”​—Aheb. 7:27; 10:12.

13. Pali kusiyana kotani pakati pa makonzedwe ophimba macimo ndi dipo?

13 Kodi pali kusiyana kotani pakati pa makonzedwe ophimba macimo ndi dipo? Makonzedwe ophimba macimo ndi zimene Mulungu amacita kuti abwezeletse ubale wabwino pakati pa iye ndi anthu. Dipo ndi mtengo umene unalipilidwa kuti macimo athu aphimbidwe. Mtengo umenewu umaimilidwa ndi magazi amtengo wapatali a Yesu omwe anakhetsedwa kaamba ka ife.​—Aef. 1:7; Aheb. 9:14.

YEHOVA ANATIWOMBOLA NDIPO AMATIONA KUKHALA OLUNGAMA

14. Kodi tsopano tikambilane ciyani? Ndipo n’cifukwa ciyani?

14 Kodi pakhala zotulukapo zotani cifukwa ca makonzedwe ophimba macimo? Baibulo limagwilitsa nchito mawu angapo pofotokoza mapindu amene akhalapo. Ngakhale kuti tanthauzo la mawu amenewa limamveka lofanana, alionse a mawuwo amagogomeza zinazake zimene Yehova anacita pa makonzedwe ophimba macimo, zimene zinatsegulila njila kuti iye azitikhululukila. Pamene tikambilana mawu amenewa, tidzaonanso mmene aliyense wa ife amapindulila ndi kukhululuka kwa Yehova.

15-16. (a) Kodi mawu akuti “kuwombola” amatanthauza ciyani m’Baibulo? (b) Kodi kudziwa kuti tinamasulidwa ku ucimo ndi imfa kumatilimbikitsa kucita ciyani?

15 M’Baibulo, mawu akuti kuwombola amatanthauza kumasula, kapena kuthetsa mlandu winawake komwe kumacitika dipo likapelekedwa. Mtumwi Petulo anafotokoza mfundo imeneyi motele: “Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani [m’cilankhulo coyambilila “zinakuwombolani”] ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengela kucokela kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Khristu, omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda cilema komanso yopanda mawanga.”​—1 Pet. 1:​18, 19; mawu a m’munsi.

16 Cifukwa ca nsembe ya dipo, tinamasulidwa ku ulamulilo wopondeleza wa ucimo ndi imfa. (Aroma 5:21) Conco, timayamikila kwambili Yehova ndi Yesu kaamba kotiwombola pogwilitsa nchito magazi a Yesu amtengo wapatali.​—1 Akor. 15:22.

17-18. (a) Kodi kuonedwa kukhala olungama kumatanthauza ciyani? (b) Ndipo timapindula bwanji kaamba ka zimenezi?

17 Kuonedwa kukhala olungama kumatanthauza kuti mlandu wathu unakhululukidwa, komanso kuti zolakwa zathu zinafafanizidwa. Sikuti Yehova amanyalanyaza mfundo zake zolungama pocita zimenezi. Sationa kukhala olungama cifukwa ca nchito zathu, ndipo sizitanthauza kuti amakondwela ndi macimo athu. Yehova amakhululuka nkhongole yathu ya ucimo ngati timakhulupilila makonzedwe a kuphimba macimo, komanso mtengo wa dipo umene anapeleka.​—Aroma 3:24; Agal. 2:16.

18 Kodi zimenezi zimatipindulila motani? Ena mwa anthu amene amaonedwa kukhala olungama, amasankhidwa kuti akalamulile limodzi ndi Khristu kumwamba, ndipo amakhala ana a Mulungu. (Tito 3:7; 1 Yoh. 3:1) Iye amawakhululukila macimo awo. Zimakhala ngati sanacitepo chimo lililonse. Conco, amayenelela kukakhala mu Ufumu. (Aroma 8:​1, 2, 30) Enanso omwe amaonedwa kukhala olungama ali ndi ciyembekezo codzakhala pa dziko lapansi. Iwo amakhala mabwenzi a Mulungu, ndipo iye amakhululuka macimo awo. (Yak. 2:​21-23) A khamu lalikulu amene adzapulumuke Aramagedo, ali ndi ciyembekezo cokhala ndi moyo kwamuyaya. (Yoh. 11:26) Ndipo “olungama” komanso “osalungama” amene anamwalila adzaukitsidwa m’tsogolo. (Mac. 24:15; Yoh. 5:​28, 29) Pamapeto pake, atumiki onse omvela a Yehova apadziko lapansi adzakhala ndi “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Timapeza dalitso lalikulu zedi cifukwa ca makonzedwe ophimba macimo, lomwe ndi kuyanjananso ndi Atate wathu, Yehova!

19. Kodi mkhalidwe wathu unasintha motani cifukwa ca zimene Yehova ndi Yesu anaticitila? (Onaninso bokosi lakuti “ Kukhululukidwa Macimo.”)

19 Poyamba, mkhalidwe wathu unali monga wa mnyamata uja amene anatayikilidwa cuma conse ndi kulandila colowa ca nkhongole imene sakanakwanitsa kuibweza. Koma ndife oyamikila kwambili kuti Yehova anatithandiza. Mkhalidwe wathu unasintha cifukwa ca makonzedwe a kuphimba macimo, komanso cifukwa ca kulipilidwa kwa dipo. Kukhulupilila Yesu Khristu kumacititsa kuti tiwomboledwe, kapena kuti timasulidwe ku ucimo ndi imfa. Macimo athu amafafanizidwa, ndipo zimakhala ngati sitinacitepo macimo alionse. Koma koposa zonse, tsopano zimakhala zotheka kukhala paubale wabwino ndi Atate wathu wacikondi wakumwamba, Yehova.

20. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

20 Tikamasinkhasinkha zimene Yehova ndi Yesu anaticitila, mitima yathu imadzaza ndi ciyamikilo. (2 Akor. 5:15) Popanda thandizo lawo, tikanakhala opanda ciyembekezo! Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene kukhululuka kwa Yehova kumatipindulila.

NYIMBO 10 Tamandani Yehova, Mulungu Wathu!

a M’zilankhulo zina, mawu akuti “dipo” amamasulidwa ndi mawu ofotokozela akuti “mtengo wa moyo” kapena “malipilo amene anapelekedwa.”