Funso Losavuta Limene Lingakhale ndi Zotulukapo Zabwino
Mary ndi mwamuna wake John, a akhala ku malo kumene kuli anchito ambili ocokela ku Philippines. Conco, n’zotheka kuwagawilako uthenga wabwino. Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, Mary anakwanitsa kuyambitsa maphunzilo a Baibulo, osati cabe m’dziko lawo, koma ngakhalenso m’maiko ena. Kodi anakwanitsa bwanji kucita zimenezo?
Mary anali kufunsa anthu amene anali kuwaphunzitsa Baibulo funso losavuta lakuti, “Kodi mudziwako aliyense amene angakonde kuphunzila Baibulo?” Ngati ayankha kuti inde, anali kuwapempha kuti amudziwikitse kwa iye. Nthawi zambili, kufunsa funso losavuta limeneli kumakhala ndi zotulukapo zabwino. N’cifukwa ciyani? N’cifukwa cakuti nthawi zambili, anthu amene amalemekeza Mawu a Mulungu amafuna kuuzako am’banja mwawo, komanso mabwenzi awo zimene aphunzila. Kodi kufunsa funso losavuta limeneli kwakhala ndi zotsatilapo zotani?
Jasmin, amene anali kuphunzila ndi Mary, anamudziwikitsa kwa ophunzila anayi atsopano. Mmodzi mwa ophunzila atsopanowo, Kristine, anali kukonda zimene anali kuphunzila moti anauza Mary kuti aziphunzila naye kawili pa mlungu. Mary atafunsa ngati Kristine anali kudziwakonso ena amene anali kufuna kuphunzila Baibulo, Kristine anayankha kuti, “Inde alipo. Ndidzakudziwikitsani kwa iwo.” M’milungu yocepa cabe, Kristine anadziwikitsa Mary kwa anzake anayi amene anali kufuna kuphunzila Baibulo. Pa nthawi ina, Kristine anadziwikitsa Mary kwa anzake enanso. Ndipo ena a iwo anapatsa Mary maina a anzawo amene akanakonda kuphunzila Baibulo.
Kristine anali kufunanso kuti banja lake limene linali ku Philippines liyambe kuphunzila Baibulo. Conco, analankhula ndi mwana wake wamkazi, Andrea. Poyamba, Andrea anaganiza kuti, ‘Mboni za Yehova ndi cipembedzo cacilendo. Anthu ake sakhulupilila Yesu, ndipo amangogwilitsa nchito Cipangano Cakale.’ Koma atangophunzilako kamodzi kokha, anasintha maganizo ake. Pophunzila, Andrea anali kukamba kuti, “Popeza ndi Baibulo lakamba, ndiye kuti ndi zoona!”
Patapita nthawi, Andrea anadziwikitsa Mary kwa anzake awili komanso kwa mnzake wina wakunchito. Ndipo onsewa anayamba kuphunzila Baibulo. Kuwonjezela apo, Andrea anali ndi mlongosi wa atate ake, Angela, amene sanali kupenya. Angela anali kumvetsela nthawi zonse Mary akamaphunzila ndi Andrea, koma Mary sanadziwe zimenezo. Tsiku lina, Angela anapempha Andrea kuti amudziwikitse kwa Mary, kuti nayenso ayambe kuphunzila Baibulo. Angela anali kuzikonda zimene anali kuphunzila. Pasanathe
mwezi, iye anali ataloweza pa mtima Malemba ambili, ndipo anali kufuna kuphunzila kanayi pa mlungu! Mothandizidwa ndi Andrea, iye anayamba kupezeka pamisonkhano ya pa vidiyokomfalensi mokhazikika.Pomwe Mary anadziwa kuti mwamuna wa Kristine, Joshua, amakhala pafupi akamaphunzila, Mary anamupempha ngati angakonde kumakhalapo pa phunzilo lawo. Joshua anakamba kuti, “Ndidzangomvetsela, koma musandifunse mafunso alionse. Mukandifunsa funso, ndidzacokapo.” M’mphindi zisanu zoyambilila za phunzilolo, iye anafunsa mafunso ambili kuposa Kristine. Ndipo anafuna kupitiliza kukambilana za m’Baibulo.
Funso losavuta la Mary, linapangitsa kuti akhale ndi maphunzilo ambilimbili. Mary anapanga makonzedwe akuti ambili mwa maphunzilo ake aziphunzila ndi abale ndi alongo ena. Cifukwa cofunsa funso losavuta lija, Mary anayambitsa maphunzilo a Baibulo okwanila 28 am’maiko anayi.
Jasmin, wophunzila woyamba amene wachulidwa m’cocitikaci, anabatizika mu April 2021. Kristine anabatizika mu May 2022, ndipo anabwelela ku Philippines kukakhala ndi banja lake. Ophunzila enanso awili aja amene Kristine anawadziwikitsa kwa Mary, nawonso anabatizika. Angela anabatizika patapita miyezi yocepa, ndipo tsopano akutumikila monga mpainiya wokhazikika. Mwamuna wa Kristine, Joshua, komanso mwana wawo, Andrea, kuphatikizapo ophunzila ena, nawonso akupita patsogolo.
M’nthawi ya Yesu komanso ya atumwi, anthu ambili anali kuuzako acibale awo komanso mabwenzi awo uthenga wabwino. (Yoh. 1:41, 42a; Mac. 10:24, 27, 48; 16:25-33) Bwanji osafunsako maphunzilo anu a Baibulo, komanso anthu ena acidwi kuti, “Kodi mudziwako aliyense amene angakonde kuphunzila Baibulo?” Ndani akudziwa kuti ndi maphunzilo angati omwe mungayambitse mukafunsa funso losavutali limene lingakhale ndi zotulukapo zabwino?
a Maina asinthidwa.