Mmene Mungakhalile Bwenzi Lenileni
KODI nthawi ina munamvapo kuti muli nokhanokha pamene munali kukumana ndi mavuto? Tikukhala mu “nthawi yapadela komanso yovuta.” Izi zingacititse kuti tilefuke komanso kuti tisungulumwe. (2 Tim. 3:1) Komabe, pali anthu ena amene angatithandize pamene tikukumana ndi mavuto apaumoyo. Baibulo limakamba kufunika kokhala ndi mabwenzi enieni ‘tikagwedwa mavuto.’—Miy. 17:17.
MMENE MABWENZI ENIENI ANGATITHANDIZILE
Mtumwi Paulo anathandizidwa kwambili ndi mabwenzi amene anali kuyenda naye. (Akol. 4:7-11) Pamene Paulo anali m’ndende ku Roma, mabwenzi ake anamuthandiza mwa kumucitila zinthu zimene iyemwini sakanakwanitsa kucita. Mwacitsanzo, Epafurodito anapeleka zinthu kwa Paulo zimene abale ndi alongo a ku Filipi anatumiza. (Afil. 4:18) Tukiko anapeleka makalata a Paulo ku mipingo yosiyanasiyana. (Akol. 4:7) Ngakhale pamene Paulo anali pa ukaidi wosacoka panyumba, kapena pamene anali kwayekha m’ndende, iye anakwanitsa kucita utumiki wake cifukwa ca thandizo la mabwenzi ake. Kodi mungacite ciyani kuti mukhale bwenzi lenileni masiku ano?
Zitsanzo zamakono zimaonetsa kufunika kokhala bwenzi lenileni. Ganizilani za mlongo wina amene anaonetsa kuti ndi bwenzi lenileni kwa Elisabet, mpainiya wokhazikika ku Spain. Pamene amayi ake a Elisabet anawapeza ndi matenda a khansa, mlongoyo anatumizila Elisabet mauthenga olimbikitsa ozikika m’Baibulo. Elisabet anati, “Mauthengawo anandipatsa cimwemwe, ndipo anali kundilimbikitsa kuthana ndi zocitika za tsiku lililonse popanda kumva monga ndili ndekha.”—Miy. 18:24.
Tingalimbitse ubwenzi wathu ndi okhulupilila anzathu mwa kuwathandiza pocita zauzimu. Mwacitsanzo, ngati muli ndi galimoto, mungatengeko m’bale kapena mlongo wacikalambile popita ku misonkhano kapena muulaliki. Kucita izi kudzakupatsani mpata wolimbikitsana cikhulupililo. (Aroma 1:12) Komabe, Akhristu ena sakwanitsa kucoka pakhomo. Kodi tingatani kuti tikhale mabwenzi enieni kwa iwo?
KHALANI BWENZI LENILENI KWA AMENE SAKWANITSA KUCOKA PAKHOMO
Mavuto a thanzi kapena zinthu zina, zimalepheletsa okhulupilila anzathu ena kupezeka kumisonkhano. Ganizilani citsanzo ca David yemwe anamupeza ndi matenda a khansa. Kwa miyezi yoposa 6, anali kulandila cithandizo camankhwala ca kemofelapi. Pa nthawi yonse imene David anali kulandila cithandizo camankhwala, iye ndi mkazi wake Lidia anali kulumikiza ku misonkhano kudzela pa vidiyokomfalensi.
Kodi anzawo mumpingo anawathandiza motani? Pambuyo pa msonkhano ulionse, ena mwa amene anali kupezeka kumisonkhano m’Nyumba ya Ufumu, anali kuyesetsa kukambilana ndi David komanso Lidia pa vidiyokomfalensi. Kuwonjezela apo,
David ndi Lydia akapelekapo ndemanga pamsonkhano, abale ndi alongo anali kuwalembela mauthenga oyamikila ndemanga zawo. Kodi panali kukhala zotulukapo zotani? David ndi Lidia sanali kumva kuti ali okhaokha.Tingasintheko zinthu zina kuti tipange makonzedwe akuti tizilalikilako ndi abale ndi alongo amene sakwanitsa kucoka panyumba. Kucita zimenezi kungaonetse kuti sitinawaiwale abale ndi alongo athu amenewo. (Miy. 3:27) Mungalinganize zakuti muciteko nawo ulaliki wamakalata kapena wapafoni. Abale ndi alongo amene sakwanitsa kucoka panyumba, angalumikize kumsonkhano wautumiki kudzela pa vidiyokomfalensi. David ndi Lidia anayamikila makonzedwe amenewa. David anafotokoza kuti, “Kungokhalako pa makambilano acidule a kagulu kathu kaulaliki, komanso kupemphela nawo pamodzi, kunali kutilimbikitsa kwambili.” Ngati m’poyenela ndipo ngati siziika moyo wa ena pa ciopsezo, mungalinganize zakuti nthawi ndi nthawi muzipita ndi wophunzila wanu kunyumba ya wofalitsa amene sakwanitsa kucoka panyumba kuti nayenso azikhalapo pa phunzilo.
Tikamagwila nchito limodzi ndi abale ndi alongo amene sacoka panyumba, komanso kuona makhalidwe awo abwino, timawayandikila kwambili. Mwacitsanzo, mukamalalikila pamodzi ndi ofalitsa amenewa n’kuwaona akugwilitsa nchito Mawu a Mulungu mwaluso kuti afike munthu pa mtima, cikondi canu pa iwo cimakulilako. Mukamathandiza okhulupilila anzanu pa zinthu zauzimu, mungawonjezele mabwenzi anu.—2 Akor. 6:13.
Paulo anapeza cilimbikitso pokhala ndi mnzake Tito. (2 Akor. 7:5-7) Nkhaniyi ya Paulo ndi Tito imatiphunzitsa kuti tingalimbikitse ena osati cabe mwa kuwamvela cifundo, koma tingawalimbikitsenso mwa kukhala nawo pafupi ndi kucita zimene tingathe powathandiza.—1 Yoh. 3:18.
KHALANI BWENZI LENILENI PA NTHAWI YA MAZUNZO
Abale ndi alongo athu ku Russia aonetsa citsanzo cabwino pankhani yothandizana wina ndi mnzake. Onani zimene zinacitikila Sergey ndi mkazi wake Tatyana. Pambuyo pakuti apolisi afufuza m’nyumba yawo, iwo anatengedwa kukafunsidwa mafunso. Tatyana ndi amene anayambila kumasulidwa, ndipo anabwelela kunyumba. Sergey anati: “Tatyana atafika kunyumba, mlongo mmodzi wolimba mtima anapita kunyumba kwathu kukaona Tatyana. Anzathu ambili anabwela kudzatithandiza kuika zinthu m’malo m’nyumba yathu.”
Sergey anawonjezela kuti: “Ndimakonda Miyambo 17:17, lomwe limati: ‘Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.’ Ndinaona kukwanilitsidwa kwa mawuwa pa nthawi ya mazunzo pomwe sindinali kukwanitsa kucita zinthu pandekha. Yehova wandipatsa mabwenzi omwe molimba mtima akhalabe pa mbali panga.” a
Pamene tikukumana ndi mavuto aakulu, tifunikila mabwenzi amene angatithandize. Iwo adzakhala ofunikila kwambili pa nthawi ya cisautso cacikulu. Conco tiyeni ticite zonse zimene tingathe kuti tikhale bwenzi lenileni palipano!—1 Pet. 4:7, 8.
a Onani nkhani pa jw.org ku Chichewa yakuti “Yehova Wandipatsa Anzanga Opanda Mantha.”