Pewani Mzimu Wodzikonda Umene Wafala Masiku Ano
MOSAKAIKILA mumaona kuti anthu masiku ano amaganiza kuti ndiwo oyenelela kupatsidwa maudindo apadela, komanso kucitilidwa zinthu m’njila yapadela kuposa ena. Ngakhale kuti iwo ali ndi zambili, amaganiza kuti akufunikilabe zoculuka kuposa zimene ali nazo kale. Anthu amene amaganiza mwa njila imeneyi ndi odzikonda ndipo sayamikila zimene ali nazo. Ndipo Baibulo limakamba kuti ndi mmene anthu adzakhalila m’masiku otsiliza.—2 Tim. 3:2.
Komabe, kudzikonda sikunayambe lelo ayi. Mwacitsanzo, Adamu ndi Hava anasankha kukhala ndi ufulu wodzisankhila zabwino ndi zoipa. Conco tonsefe timavutika cifukwa ca cisankho cawo coipa. Pambuyo pa zaka zambili, Mfumu Uziya ya Yuda anaganiza kuti anali wololeka kufukiza nsembe pakacisi. Koma umenewu sunali udindo wake. (2 Mbiri 26:18, 19) Mofananamo, Afarisi ndi Asaduki anali kuganiza kuti anali oyenelela kucitilidwa zinthu mwapadela ndi Mulungu cifukwa anali mbadwa za Abulahamu.—Mat. 3:9.
Tikukhala m’dziko lodzala ndi anthu odzikonda. Conco n’zotheka kwa ife kutengela khalidwe lawoli. (Agal. 5:26) Tingayambe kuganiza kuti tikuyenelela udindo winawake komanso kucitilidwa zinthu mwapadela. Kodi tingapewe bwanji kaganizidwe kameneka? Coyamba, tifunika kudziwa mmene Yehova amakaonela kaganizidwe kameneka. Mfundo ziwili za m’Baibulo zingatithandize pankhaniyi.
Yehova ndi amene amasankha zimene tifunikila. Ganizilani zitsanzo izi:
-
M’banja, mwamuna afunikila kumva kuti amalemekezedwa ndi mkazi wake, ndipo mkazi afunikila kumva kuti amakondedwa ndi mwamuna wake. (Aef. 5:33) Si kulakwa munthu wamuukwati kufuna kuti mnzakeyo azionetsa iye yekha cikondi camuukwati. (1 Akor. 7:3) Makolo amafuna kuti ana awo aziwamvela, ndipo ana ayenela kumakondedwa kwambili, komanso kuthandizidwa ndi makolo awo.—2 Akor. 12:14; Aef. 6:2.
-
Mumpingo, akulu amafunikila kulandila ulemu wathu cifukwa cogwila nchito mwakhama. (1 Ates. 5:12) Komabe, iwo sayenela kulamulila abale ndi alongo awo.—1 Pet. 5:2, 3.
-
Mulungu wapatsa maboma a anthu ufulu wotenga misonkho, komanso wolandila ulemu kwa nzika zawo.—Aroma 13:1, 6, 7.
Yehova mwacikondi amatipatsa zambili kuposa zimene tiyenelela. Popeza ndife ocimwa, tikuyenela kufa basi. (Aroma 6:23) Ngakhale n’telo, Yehova amatipatsa madalitso ambili cifukwa ca cikondi cake cokhulupilika cimene ali naco pa ife. (Sal. 103:10, 11) Dalitso lililonse kapena cinthu ciliconse cabwino cimene tingalandile kwa iye, timalandila cifukwa ca cisomo cake.—Aroma 12:6-8; Aef. 2:8.
MMENE TINGAPEWELE KUKHALA NDI MZIMU WODZIKONDA
Samalani nawo mzimu wa dziko. Ngati sitinasamale, tingayambe kuganiza kuti tikuyenela kulandila zambili kuposa ena. Yesu anaonetsa kuti n’zosavuta munthu kukhala ndi kaganizidwe kameneka. Anatelo mwa kufotokoza fanizo la anchito amene analandila dinari imodzi. Anchito ena anayamba kugwila nchito m’mawa kwambili kwa tsiku lonse pa dzuwa lotentha, pomwe ena anangogwila nchito kwa ola limodzi. Anchito oyambililawo anaona kuti anayenela kulandila malipilo oculukilapo kuposa ena cifukwa ca nchito imene anagwila. (Mat. 20:1-16) Yesu, pofotokoza fanizo limeneli, anaonetsa kuti ophunzila ake ayenela kukhala okhutila ndi zimene Mulungu wasankha kuwapatsa.
Khalani oyamikila, ndipo pewani mzimu woumiliza ena kukucitilani zinthu. (1 Ates. 5:18) Tengelani citsanzo ca mtumwi Paulo amene sanapemphe thandizo la zinthu zakuthupi kwa abale a ku Korinto ngakhale kuti anali ndi ufulu wocita zimenezi. (1 Akor. 9:11-14) Tiyenela kuyamikila zinthu zilizonse zimene ena atipatsa, ndipo tiyenela kupewa kuumiliza ena kuticitila zinthu.
Kulitsani khalidwe la kudzicepetsa. Ngati munthu amadziganizila kuposa mmene ayenela kudziganizila, angayambe kuona kuti ndi woyenela kulandila zinazake kuposa ena. Kudzicepetsa ndiko kungathandize munthu kupewa kaganizidwe kolakwika kameneka.
Mneneli Danieli anaonetsa citsanzo cabwino pankhani ya kudzicepetsa. N’kutheka kuti cifukwa ca banja kumene anacokela, maonekedwe ake abwino, kumvetsa zinthu kwake, komanso maluso ake akanamupangitsa kuona kuti anali woyenela kulandila zinthu zapadela komanso maudindo amene anapatsidwa. (Dan. 1:3, 4, 19, 20) Komabe, Danieli anakhalabe wodzicepetsa, ndipo izi zinamupangitsa kukhala wamtengo wapatali kwa Yehova.—Dan. 2:30; 10:11, 12.
Tiyeni tikanize mzimu wodzikonda umene wafala masiku ano. M’malomwake, tipitilize kupeza cimwemwe pa zimene Yehova amatipatsa mwa cisomo cake.