Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZIMENE MUNGACITE PA KUWELENGA KWANU

Onetsani Kulimba Mtima Mukapanikizika

Onetsani Kulimba Mtima Mukapanikizika

Welengani Yeremiya 38:​1-13 kuti muphunzile mmene mneneli Yeremiya ndi Ebedi-meleki anaonetsela kulimba mtima.

Mvetsani nkhani yonse. Kodi n’cifukwa ciyani Yeremiya anafunika kukhala wolimba mtima polengeza uthenga wa Yehova? (Yer. 27:​12-14; 28:​15-17; 37:​6-10) Kodi anthu anatani atamva uthenga wake?​—Yer. 37:​15, 16.

Kumbani mozamilapo. Kodi anthu anali kukakamiza Yeremiya kucita ciyani? (jr-CN 26-28 ¶20-22) Fufuzani zokhudza zitsime zakale. (it-1-E 471) Kodi muganiza Yeremiya anali kumva bwanji ali m’citsime camatope? Kodi Ebedi-meleki ayenela kuti anali kuopa ciyani?​—w12-CN 5/1 31 ¶2-3.

Onani zimene mwaphunzilapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi nkhaniyi indiphunzitsa ciyani ponena za mmene Yehova amatetezela atumiki ake okhulupilika?’ (Sal. 97:10; Yer. 39:​15-18)

  • ‘Kodi ndi pa zocitika ziti pomwe ndingafunike kukhala wolimba mtima?’

  • ‘Ndingacite bwanji kuti ndiwonjezele kulimba mtima kuti ndizicita zoyenela ndikapanikizika?’ (w11-CN 3/1 30) a

a Kuti mudziwe zowonjezela zokhudza zimene mungacite pa kuwelenga kwanu, onani nkhani yakuti “Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2023.