Anadzipeleka na Mtima Wonse
PA MBONI zacangu zimene zikutumikila ku malo kumene kuli ofalitsa Ufumu ocepa, ambili ni alongo amene ni mbeta. Ena atumikila ku maiko acilendo kwa zaka zambili. N’ciani cinawalimbikitsa kusamukila ku maiko acilendo? Nanga aphunzila ciani potumikila ku maikowo? Kodi umoyo wawo wakhala bwanji? Tinafunsako alongo angapo amene anatumikilapo ku maiko acilendo. Ngati ndimwe mlongo wosakwatiwa, ndipo mufunitsitsa kucitako utumiki wokhutilitsa umenewu, tikhulupilila mudzapindula na zimene iwo anakamba. Ndipo atumiki a Mulungu onse angapidule ndi citsanzo ca alongo amenewa.
KUTHETSA ZIKAIKO
Kodi inu mumakaika ngati mungakwanitse kukatumikila monga mpainiya ku dziko lacilendo? Mlongo Anita amene lomba ali m’zaka za m’ma 70, anali kukaikila ngako ngati angakwanitse. Anakulila ku England kumene anayambila upainiya ali na zaka 18. Iye anati “Nimakonda kuphunzitsa anthu za Yehova. Koma sin’naganizilepo kuti ningakwanitse kukatumikila kudziko lina. Sin’naphunzilepo citundu cina, ndipo n’nali kuona kuti siningakwanitse. Conco, pamene n’nanitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi, n’nadabwa kwambili. Sin’nayembekezele kuti munthu wamba monga ine ningaitanidwe ku Giliyadi. Koma n’naganiza kuti, ‘Ngati Yehova aona kuti ningakwanitse, n’dzayesako.’ Papita zaka zoposa 50 lomba. Mpaka pano nikali kutumikila monga mmishonale ku Japan.” Anita anawonjezela kuti: “Nthawi zina, mokondwela nimauza alongo acicepele kuti, ‘Iwenso nyamula cola cako, ukatumikile kudziko lacilendo.’ Ndine wokondwa kuti ambili acitadi zimenezo.”
CIMENE CINAWALIMBITSA MTIMA
Alongo ambili amene anatumikilapo ku dziko lina, poyamba anacita mantha kupita ku dziko lacilendo. Kodi n’ciani cinawalimbitsa mtima?
Maureen, wa zaka za m’ma 60, anakamba kuti: “Pamene n’nali kukula, n’nali kulakalaka kukhala na umoyo wa colinga, umoyo wothandiza ena.” Atafika zaka 20, anapita ku Quebec ku Canada, kumene apainiya anali ocepa kwambili. Anatinso, “pambuyo pake, n’naitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi. Koma n’nali kuopa kupita kudziko lacilendo kumene kunalibe anzanga.” Anatinso: “N’nali kudelanso nkhawa kusiya amayi amene anali kusamalila atate anga odwala. Nthawi zambili sin’nali kugona usiku, ndipo n’nali kupemphela uku nikugwetsa misozi, kucondelela Yehova pa mavuto amenewa. N’tafotokozela
makolo anga nkhawa zanga, iwo ananilimbikitsa kuti nipite. N’naonanso mmene mpingo unacilikizila makolo anga mwacikondi. Kuona cisamalilo ca Yehova, kunan’thandiza kukhala na cidalilo cakuti inenso adzanisamalila. Apa, n’nali wokonzeka kupita.” Kuyambila mu 1979, Maureen watumikila monga mmishonale ku West Africa, kwa zaka zoposa 30. Lomba, akusamalila amayi ake ku Canada, ndipo akutumikila monga mpainiya wapadela. Pokumbukila utumiki wake pa zaka zonsezo ku maiko acilendo, iye anati: “Nthawi zonse, Yehova ananipatsa zofunikila panthawi yake.”Mlongo Wendy wa zaka za m’ma 60, anayamba upainiya ali wacicepele ku Australia. Iye anati: “N’nali kucita manyazi ndi mantha kukamba ndi anthu acilendo. Koma upainiya unaniphunzitsa kukamba ndi anthu a mitundu yonse. M’kupita kwa nthawi, mantha anayamba kutha ndipo n’nakhala na cidalilo. Upainiya unaniphunzitsa kudalila Yehova, ndipo mantha oopa kukatumikila kudziko lacilendo anatha. Cinanso, mlongo wina mmishonale amene anatumikila ku Japan kwa zaka zoposa 30, ananiitana kuti tikalalikile pamodzi m‘dzikolo kwa miyezi itatu. Kugwila naye nchito kunakulitsa cikhumbo canga cokatumikila kudziko lina.” Ca m’ma 1980, mlongo Wendy anapita ku dziko lacisumbu la Vanuatu, pamtunda wa makilomita 1,770 kum’maŵa kwa Australia.
Mlongo Wendy akali ku Vanuatu, ndipo akutumikila pa ofesi yomasulila mabuku. Iye anati, “Kuona mmene mipingo na tumagulu tukuculukila m’madela akutali, kumanipatsa cimwemwe cacikulu. Kucitako mbali yaing’ono m’nchito ya Yehova pa zisumbuzi ni dalitso losakambika.”
Mlongo Kumiko, wa zaka za m’ma 60, anali mpainiya wathawi zonse ku Japan. Ali kumeneko, mpainiya mnzake anam’pempha kuti asamukile ku Nepal. Kumiko anati: “Anayesa kunilimbikitsa kuti tipite, koma ine n’nali kukana. N’nali kuopa za kuphunzila citundu cina, na kuyamba kujailanso umoyo watsopano. Panalinso vuto lopeza ndalama zoyendela kuti tisamukile ku dziko lina. Pamene n’nali kusinkha-sinkha pa zimenezi, n’napezeka m’ngozi ya honda moti anan’cita adimiti ku cipatala. Nili kumeneko, n’naganiza kuti: ‘Kaya n’dzacila kaya? Mwina matenda adzakula ndi kuphonya mwayi wokatumikila ku dziko lina. Ningakonde kukatumikilako ngakhale caka cimodzi cabe.’ Conco, n’nacondelela Yehova m’pemphelo kuti anithandize.” Atacoka m’cipatala, Kumiko anapita kukaonako ku dziko la Nepal.
Pambuyo pake iye ndi mpainiya mnzake anakukila ku Nepal.Kumiko atayang’ana kumbuyo zaka monga 10 za utumiki wake Nepal, anati: “Mavuto onidetsa nkhawa anagaŵikana ngati Nyanja Yofiila. Ndine wokondwa kuti n’napita kukatumikila ku malo osoŵa. Nthawi zambili, polalikila pa nyumba imodzi uthenga wa m’Baibo, anthu 5 kapena 6 apafupi amabwela kudzamvetsela. Ngakhale ana anali kupempha mwaulemu tumapepa twa uthenga. Gawo yaconde imeneyi ni yokondwelatsa kwambili kuseŵenzelamo.”
KUPILILA ZOVUTA ZINA
Mosakaikila, alongo olimba mtima amene tinafunsa anakumana na mavuto. Koma kodi analimbana nawo bwanji?
Mlongo Diane wa ku Canada anati: “Poyamba cinanivuta kukhala kutali na acibanja.” Ali na zaka za m’ma 60, anali atatumikila monga mmishonale ku Ivory Coast (Lomba lochedwa Côte d’Ivoire) kwa zaka 20. Anatinso: “Ninapempha Yehova kuti anithandize kukonda anthu a m’gawo langa. Mlangizi wathu wina ku Sukulu ya Giliyadi, m’bale Jack Redford, anatiuza kuti poyamba tingadabwe, ngakhale kukhumudwa ndi malo amene tidzatumikilako, maka-maka poona umphawi wa anthu. Ndiyeno anati: ‘Koma inu osayang’ana umphawiwo. Yang’anani anthu, yang’anani nkhope zawo. Onani mmene akulabadilila coonadi ca m’Baibo.’ Izi n’zimene ninacita, ndipo zinanipindulitsa kwambili! Polalikila uthenga wotonthoza wa Ufumu, n’nali kuona nkhope za anthu zikuwala.” N’cianinso cinathandiza Diane kujaila utumiki wa ku dziko lacilendo? Iye anati: “N’nayamba kukonda kwambili anthu amene n’nali kuphunzila nawo Baibo, ndipo n’nali kumva bwino kuwaona akukhala atumiki okhulupilika a Yehova. Kumene n’nali kutumikila kunakhala kwathu. N’napeza amayi, atate, abale na alongo anga auzimu, monga mmene Yesu analonjezela.”—Maliko 10:29, 30.
Anne wa zaka za m’ma 40, amatumikila ku Asia m’dziko lina limene nchito yathu ni yoletsedwa. Iye anati: “Kwa zaka zambili zimene natumikila m’madela osiyana-siyana, n’nakhala na alongo a zikhalidwe ndi zibadwa zosiyana ndi ine. Mwa ici, tinali kusiyana maganizo na kukhumudwitsana nthawi zina. Izi zikacitika, n’nali kuyesetsa kugwilizana nawo kuti nimvetse bwino cikhalidwe cawo. N’nali kuyesetsa kuwakonda ndi kuwaganizila. Ndine wokondwa kuti zoyesa-yesa zanga zinabala zipatso. Napeza mabwenzi odalilika, amene amanithandiza kupitiliza utumiki wanga.
Mlongo Ute wa ku Germany, wa zaka za m’ma 50, anatumizidwa kukatumikila monga mmishonale ku Madagascar mu 1993. Iye anati: “Poyamba zinanivuta kuphunzila citundu ca m’dzikolo, na kuzoŵelela nyengo. N’nali kudwala-dwalanso maleliya, matenda a amoeba, na njoka za m’mimba. Koma abale ananithandiza kwambili. Alongo, ana awo, ndi ophunzila Baibo anga, ananithandiza moleza mtima kuti niphunzile citundu cawo. Mmishonale mnzanga, anali kunisamalila nikadwala. Koma Yehova ndiye ananithandiza kwambili. N’nali kum’tulila nkhawa zanga m’pemphelo. Ndiyeno n’nali kuyembekezela moleza mtima kuti aniyankhe, mwina kwa masiku angapo, olo kwa miyezi. Yehova anan’thandiza pa vuto iliyonse.” Mlongo Ute watumikila ku Madagascar kwa zaka pafupifupi 23.
ANADALITSIKA KWAMBILI
Alongo athu amene akutumikila kumalo osoŵa ku maiko acilendo amati kutumikila m’maiko ena kwawapatsa madalitso ambili. Kodi ena a madalitsowo ni abwanji?
Mlongo Heidi, wa ku Germany, wa zaka za m’ma 70, watumikila ku Ivory Coast (lomba lochedwa Côte d’Ivoire) kucokela mu 1968. Iye anati, “Cinthu cokondweletsa ngako kwa ine ni kuona ana anga auzimu ‘akupitirizabe kuyenda m’coonadi.’ Ophunzila Baibo anga ena, lomba ni apainiya ndi akulu mumpingo. Ambili amaniitana kuti Amama kapena Ambuya. Mkulu wina, mkazi wake na ana ake, anangonitenga monga wa m’banja mwawo weni-weni. Conco, Yehova wanipatsa mwana mwamuna, mpongozi, na adzukulu atatu.”—3 Yoh. 4.
Mlongo Karen wa ku Canada, wa zaka za m’ma 70, watumikila kwa zaka zoposa 20 ku West Africa. Anakamba kuti: “Umishonale waniphunzitsa kukhala wodzimana, wacikondi ndi woleza mtima. Ndiponso, atumiki anzanga a ku maiko ena anithandiza kukhala woganiza bwino. N’naphunzila kuti pali njila zambili zocitila zinthu. Ndipo lomba, ndili ndi anzanga kuzungulila dziko lapansi. Ngakhale kuti umoyo ndi mautumiki athu asintha, ubwenzi wathu sunasinthe.”
Mlongo Margaret wa ku England, amene lomba ali m’zaka za m’ma 70, anatumikila monga mmishonale ku Laos. Iye anasimba kuti: “Kutumikila ku dziko lina kwanipatsa mwayi wodzionela nekha mmene Yehova akukopela anthu a mafuko ndi zikhalidwe zonse kubwela m’gulu lake. Izi zinalimbitsa ngako cikhulupililo canga. Zimanipatsa cidalilo cakuti Yehova amatsogoleladi gulu lake, ndipo zolinga zake zidzacitika.”
Kukamba zoona, alongo osakwatiwa amene akutumikila kumaiko acilendo akhala na mbili yabwino ngako mu utumiki wawo wacikhiristu. Timawayamikila kwambili. (Ower. 11:40) Komanso, ciŵelengelo cawo cikulila-kulila. (Sal. 68:11) Kodi mungasinthe zinthu zina kuti mutsatile mapazi a alongo acangu amene anafunsidwa mafunso m’nkhani ino? Ngati mwacita zimenezi, mosakaika ‘mudzalaŵa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’—Sal. 34:8.