Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 3

Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?

Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?

“Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa.”—MIY. 4:23.

NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu

ZA M’NKHANI INO *

1-3. (a) N’cifukwa ciani Yehova anam’konda Solomo? Nanga anam’dalitsa m’njila ziti? (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana mafunso ati?

SOLOMO anakhala mfumu ya Isiraeli ali wacinyamata. Atangoyamba kumene kulamulila, Yehova anaonekela kwa iye m’maloto na kumuuza kuti: “Pempha cimene ukufuna kuti ndikupatse.” Solomo anayankha kuti: “Ndine mwana ndipo sindikudziŵa zinthu zambili. . . . Mupatse mtumiki wanune mtima womvela kuti ndiweluze anthu anu.” (1 Maf. 3:5-10) Solomo anapempha kuti apatsidwe “mtima womvela.” Uku kunali kudzicepetsa kwambili. Ndiye cifukwa cake Yehova anamukonda maningi. (2 Sam. 12:24) Mulungu anakondwela kwambili na pempho la Solomo, cakuti anam’patsa “mtima wanzelu ndi womvetsa zinthu.”—1 Maf. 3:12.

2 Pa nthawi yonse imene Solomo anali wokhulupilika, anadalitsidwa m’njila zambili. Mwacitsanzo, anapatsiwa mwayi womanga kacisi, amene anabweletsa ulemelelo ku “dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (1 Maf. 8:20) Komanso anapatsiwa nzelu na Mulungu, moti anakhala wochuka kwambili. Ndipo mawu amene iye anakamba mouzilidwa na Mulungu, analembewa m’mabuku atatu a m’Baibo. Limodzi mwa mabuku amenewo ni buku la Miyambo.

3 M’buku la Miyambo, liwu lakuti mtima limachulidwa nthawi zoposa 100. Mwacitsanzo, pa Miyambo 4:23 pamati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa.” Kodi pa vesiyi, liwu lakuti “mtima” litanthauza ciani? M’nkhani ino, tidzayankha funso limeneli. Tidzayankhanso mafunso ena aŵili awa: Kodi Satana amacita ciani pofuna kuipitsa mtima wathu? Nanga tingauteteze bwanji? Kuti tikhalebe okhulupilika kwa Mulungu, tifunika kumvetsetsa mayankho pa mafunso ofunika kwambili amenewa.

KODI “MTIMA” UMENE TIYENELA KUUTETEZA N’CIANI?

4-5. (a) Kodi “mtima” wochulidwa pa Miyambo 4:23 n’ciani? (b) Kodi zimene timacita posamalila thanzi lathu zionetsa bwanji kufunika kosamalila umunthu wathu wamkati?

4 Pa Miyambo 4:23, liwu lakuti “mtima” litanthauza umunthu wa mkati. (Sal. 51:6, NWT-E, ftn.) M’mawu ena, “mtima” uphatikizapo zimene timaganiza, mmene timamvelela, zolinga zathu, komanso zimene timalaka-laka. “Mtima” ni umunthu wathu weni-weni wa mkati, osati cabe maonekedwe akunja.

5 Umunthu wa mkati timafunika kuusamalila. Kuti timvetsetse kufunika kocita zimenezi, tiyeni tiyelekezele na thanzi lathu. Coyamba, kuti tikhalebe na thanzi labwino timafunika kudya zakudya zopatsa thanzi, komanso kucita maseŵela olimbitsa thupi kaŵili-kaŵili. Mofananamo, kuti tikhalebe athanzi mwauzimu, timafunika kudya cakudya cauzimu. Cinanso, nthawi zonse timafunika kucita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yehova. Ndipo tingaonetse kuti tili na cikhulupililo mwa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila, komanso kuuzako ena zimene timakhulupilila. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Caciŵili, nthawi zina tingapusitsike na maonekedwe akunja a munthu, n’kuganiza kuti ni wathanzi, pamene m’thupi mwake muli matenda. Mofananamo, tingakhale na pulogilamu yazauzimu, n’kumaganiza kuti tili na cikhulupililo colimba. Koma pa nthawi imodzi-modzi, zilakolako zoipa zingakhale kuti zikukula mu mtima mwathu. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tizikumbukila kuti Satana amafuna kuipitsa mtima wathu mwa kutipangitsa kutengela maganizo ake. Kodi angacite bwanji zimenezo? Nanga tingauteteze bwanji mtima wathu?

ZIMENE SATANA AMACITA KUTI AIPITSE MTIMA WATHU

6. Kodi Satana ali na colinga canji? Nanga amacita ciani pofuna kucikwanilitsa?

6 Satana ni wopanduka, amanyalanyaza miyezo ya Yehova, ndiponso ni wodzikonda. Iye amafuna kuti ife titengele zocita zake. Komabe, Satana sangatikakamize kucita zimenezi. Conco, amaseŵenzetsa njila zina pofuna kukwanilitsa colinga cake cimeneci. Mwacitsanzo, wasoceletsa anthu ambili a m’dzikoli. (1 Yoh. 5:19) Iye amafuna kuti tizigwilizana na anthu oipa amenewo, olo kuti tidziŵa kuti kucita zimenezo ‘kungawononge’ makhalidwe ndi maganizo athu. (1 Akor. 15:33) Mfumu Solomo anasoceletsedwa na msampha umenewu. Iye anakwatila akazi ambili acikunja, amene m’kupita kwa nthawi, “anapotoza mtima” wake na kum’sonkhezela kusiya Yehova.—1 Maf. 11:3.

Mungateteze bwanji mtima wanu kuti Satana asauipitse na maganizo ake oipa? (Onani palagilafu 7) *

7. Kodi Satana amaseŵenzetsanso ciani pofuna kufalitsa maganizo ake? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kukhala osamala?

7 Satana amaseŵenzetsa mafilimu na mapulogalamu a pa TV pofuna kufalitsa maganizo ake. Iye amadziŵa kuti nkhani zopeka zimakondweletsa, ndipo zili na mphamvu yosonkhezela maganizo a munthu, zocita zake, komanso mmene amamvelela. Yesu anali kuseŵenzetsa tunkhani topeka kapena kuti mafanizo pophunzitsa mwaluso. Mwacitsanzo, iye anapeleka fanizo la Msamariya wacifundo, komanso la mwana woloŵelela. (Mat. 13:34; Luka 10:29-37; 15:11-32) Koma anthu amene amatengela maganizo a Satana angaseŵenzetse nkhani zopeka pofuna kutisoceletsa. Conco, tifunika kukhala oganiza bwino. Mafilimu na mapulogalamu ena a pa TV angatiphunzitse na kutisangalatsa popanda kuipitsa maganizo athu. Koma tifunika kukhala osamala. Posankha zosangalatsa, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi filimu kapena pulogalamu iyi ya pa TV imaonetsa kuti kutsatila zilako-lako za thupi kulibe vuto?’ (Agal. 5:19-21; Aef. 2:1-3) Nanga mungacite ciani ngati mwaona kuti pulogilamuyo imalimbikitsa maganizo a Satana? Ipeweni mmene mungapewele matenda oyambukila!

8. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuteteza mtima wawo?

8 Makolo, muli na udindo waukulu woteteza ana anu kuti Satana asaipitse mtima wawo. Mwacionekele, mumacita zonse zotheka kuti muteteze ana anu ku matenda. Mumaonetsetsa kuti pa nyumba ni paukhondo, ndipo mumataya zilizonse zimene muona kuti zingabweletse matenda kwa imwe kapena kwa anawo. Mofanana na zimenezi, mufunika kuteteza ana anu ku zinthu zimene zingalengetse kuti atengele maganizo a Satana. Zinthu zimenezo ni monga mafilimu oipa, mapulogilamu a pa TV na mawebusaiti osayenela, komanso maseŵela oipa a pa kompyuta. Yehova wakupatsani udindo wothandiza ana anu kukhala naye pa ubwenzi wabwino. (Miy. 1:8; Aef. 6:1, 4) Conco, musaope kuika malamulo panyumba, ozikidwa pa mfundo za m’Baibo. Auzeni ana anu aang’ono zinthu zimene angatambe na zimene sayenela kutamba. Ndipo athandizeni kumvetsetsa zifukwa zimene mwaikila malamulowo. (Mat. 5:37) Pamene anawo akukula, aphunzitseni mfundo za Yehova kuti akhale na luso losiyanitsa cabwino na coipa. (Aheb. 5:14) Komanso, kumbukilani kuti ana amaphunzila zambili maka-maka poona zocita zanu kuposa zokamba zanu.—Deut. 6:6, 7; Aroma 2:21.

9. Kodi Satana amalimbikitsa mfundo yotani? Nanga n’cifukwa ciani kuyendela mfundo imeneyo n’koopsa?

9 Satana amafunanso kuipitsa mtima wathu mwa kuticititsa kuyamba kudalila nzelu za anthu m’malo modalila malangizo a Yehova. (Akol. 2:8) Ganizilani mfundo imodzi imene Satana amalimbikitsa. Iye amasonkhezela anthu kukhala na mtima wofunitsitsa kulemela. Ena amene amakhala na maganizo amenewa amalemeladi, koma enanso salemela. Mulimonsemo, zotulukapo zake zimakhala zoipa. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti pofunitsitsa kulemela, amalolela kuika paciopsezo moyo wawo, banja lawo, ngakhale ubwenzi wawo na Mulungu. (1 Tim. 6:10) Koma ife timayamikila kuti Atate wathu wanzelu Yehova, amatiphunzitsa kuona ndalama m’njila yoyenela.—Mlal. 7:12; Luka 12:15.

KODI TINGATETEZE BWANJI MTIMA WATHU?

Mofanana ndi alonda akale, khalani maso, ndipo yesetsani kuteteza mtima wanu kuti musaloŵe zinthu zimene zingauipitse (Onani palagilafu 10-11) *

10-11. (a) Kodi tiyenela kucita ciani kuti tidziteteze? (b) Kodi alonda a m’nthawi yakale anali kucita ciani? Ndipo cikumbumtima cathu cimagwila nchito bwanji monga mlonda?

10 Kuti tikwanitse kuteteza mtima wathu, tifunika kudziŵa zimene zingauwononge na kucitapo kanthu mwamsanga kuti tiucinjilize. Liwu lakuti ‘kuteteza’ pa Miyambo 4:23 litikumbutsa za nchito ya mlonda. M’nthawi yakale, mlonda anali kukhala pamwamba pa mpanda wa mzinda, ndipo akaona kuti kukubwela adani, anali kucenjeza anthu. Kuganizila zimene alonda anali kucita, kungatithandize kudziŵa zimene tifunika kucita kuti tisalole Satana kuipitsa maganizo athu.

11 M’masiku akale, mlonda anali kuseŵenza mothandizana ndi alonda a pa geti ya mzinda. (2 Sam. 18:24-26) Capamodzi, iwo anali kuteteza mzinda wawo mwa kuonetsetsa kuti mageti onse ni otseka ngati kukubwela adani. (Neh. 7:1-3) Cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo * naconso cimagwila nchito ngati mlonda wathu. Cimaticenjeza ngati Satana afuna kuwononga mtima wathu wophiphilitsa. M’mawu ena, cimaticenjeza ngati Satana afuna kutisonkhezela kukhala na maganizo oipa, zolinga, kapena zilakolako zoipa. Conco, nthawi zonse cikumbumtima cathu cikaticenjeza, tifunika kumvetsela na kutseka geti ya mtima wathu, titelo kukamba kwake.

12-13. Kodi tingayesedwe kuti ticite ciani? Koma kodi tiyenela kucita ciani?

12 Onani citsanzo coonetsa mmene tingadzitetezele kuti Satana asaipitse maganizo athu. Yehova anatiphunzitsa kuti, “dama ndi conyansa camtundu uliwonse [siziyenela kuchulidwa] n’komwe pakati [pathu].” (Aef. 5:3) Koma kodi tingacite ciani ngati anzathu ku nchito kapena ku sukulu ayamba kukamba nkhani zosayenela zokhudza kugonana? Tidziŵa kuti tiyenela “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.” (Tito 2:12) Conco, cikumbumtima cathu, cimene cili monga mlonda, cingaticenjeze. (Aroma 2:15) Koma kodi tidzacimvela? Mwina tingakopeke kuti timvetsele zimene akukamba, kapena kuonako zithunzi zoipa zimene akutamba. Koma imeneyi ndiyo nthawi yofunika kutseka mageti a mtima wathu, mwa kusintha nkhani yokambilana kapena kungocokapo.

13 Pamafunika kulimba mtima kuti tikane pamene anzathu akutituntha kuganizila zinthu zosayenela kapena kucita zoipa. Koma Yehova amaona zoyesa-yesa zathu. Ndipo tiyenela kukhala na cidalilo cakuti iye adzatipatsa mphamvu na nzelu kuti tikwanitse kukana maganizo a Satana. (2 Mbiri 16:9; Yes. 40:29; Yak. 1:5) Nanga n’ciani cina cimene tingacite kuti titeteze mtima wathu?

KHALANI CHELU

14, 15. (a) Kodi tifunika kutsegula mtima wathu kuti muloŵe ciani? Nanga tingacite bwanji zimenezi? (b) Kodi malangizo a pa Miyambo 4:20-22, angatithandize bwanji kuti tizipindula mokwanila na zimene timaŵelenga m’Baibo? (Onani mbali yakuti “Kodi Tingasinkhe-sinkhe Bwanji?”)

14 Kuti titeteze mtima wathu, tifunika kuutseka kuti musaloŵe zinthu zimene zingauipitse. Koma nthawi zina tiyenela kumautsegula kuti muloŵe zinthu zabwino. Ganizilaninso za citsanzo ca mzinda wokhala na mpanda. Mlonda wa pa geti anali kutseka geti ya mzinda kuti adani asaloŵe. Koma nthawi zina, anali kuitsegula pofuna kupeleka mpata woloŵetsa zakudya na zinthu zina mu mzindawo. Cikanakhala kuti mageti sanali kutsegulidwa, sembe anthu anali kufa na njala. Mofananamo, tifunika kumatsegula mtima wathu kaŵili-kaŵili kuti maganizo a Mulungu azititsogolela.

15 Baibo ni buku imene ili na maganizo a Yehova. Conco, nthawi zonse tikamaiŵelenga, timayamba kutengela maganizo a Yehova, zocita zake, na mmene amamvelela. Koma kodi tingacite ciani kuti tizipindula mokwanila na zimene timaŵelenga m’Baibo? Cinthu cimodzi cofunika kwambili ni pemphelo. Mlongo wina anati: “Nikalibe kuyamba kuŵelenga Baibo, nimapempha Yehova kuti anithandize ‘kuona zinthu zocititsa cidwi’ za m’Mawu ake.” (Sal. 119:18) Cinanso, tifunika kusinkha-sinkha pa zimene timaŵelenga. Ngati tipemphela, kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha, Mawu a Mulungu amafika “mkati mwa mtima [wathu],” ndipo timayamba kuwakonda kwambili.—Ŵelengani Miyambo 4:20-22; Sal. 119:97.

16. Kodi timapindula bwanji na JW Broadcasting? Fotokozani citsanzo.

16 Njila ina imene timalolela maganizo a Mulungu kutitsogolela ni mwa kutamba mavidiyo a pa JW Broadcasting®. Banja lina linati: “Mapulogilamu apamwezi a JW Broadcasting akhaladi yankho la mapemphelo athu! Mapulogilamu amenewa amatitsitsimula na kutilimbikitsa tikakhala acisoni kapena osungulumwa. Komanso, nthawi zambili tikakhala pa nyumba, timakonda kumvetsela nyimbo za pa JW Broadcasting®. Timaliza nyimbozi pamene tiphika, kuyeletsa pa nyumba, ngakhale pakumwa tiyi.” Mapulogilamu amenewa amatithandiza kuteteza mtima wathu. Amatiphunzitsa kutengela maganizo a Yehova, komanso amatithandiza kukana kutengela maganizo a Satana.

17, 18. (a) Malinga na 1 Mafumu 8:61, timapindula bwanji ngati tiseŵenzetsa zimene Yehova amatiphunzitsa? (b) Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Mfumu Hezekiya? (c) Mogwilizana na pemphelo la Davide pa Salimo 139:23, 24, tingapemphe ciani kwa Yehova?

17 Nthawi iliyonse tikaona mapindu amene amabwela cifukwa cocita zinthu zoyenela, cikhulupililo cathu cimalimbilako. (Yak. 1:2, 3) Timamvela bwino kudziŵa kuti tacita zinthu zokondweletsa Yehova monga ana ake, ndipo cifuno cathu cocita zinthu zom’kondweletsa cimakulila-kulila. (Miy. 27:11) Tikakumana na mayeselo, timaona kuti ni mpata wabwino woonetsela kuti ndife odzipeleka na mtima wonse kutumikila Atate wathu wacikondi, Yehova. (Sal. 119:113) Mwa njila imeneyi, timaonetsa kuti timakonda Yehova na mtima wathu wonse, na kuti ndife ofunitsitsa kumvela malamulo ake na kucita cifunilo cake.—Ŵelengani 1 Mafumu 8:61.

18 Ngakhale n’conco, nthawi zina tingalakwitse zinthu zina cifukwa ndife opanda ungwilo. Ngati talakwitsa, tiziganizila citsanzo ca Mfumu Hezekiya. Iye anacitapo zolakwa. Koma analapa, na kupitiliza kutumikila Yehova “ndi mtima wathunthu.” (Yes. 38:3-6; 2 Mbiri 29:1, 2; 32:25, 26) Conco, tiyenela kukaniza zoyesa-yesa za Satana zofuna kuticititsa kutengela maganizo ake. Tizipemphela kuti tikhale na “mtima womvela.” (1 Maf. 3:9; Ŵelengani Salimo 139:23, 24.) Tingakhalebe okhulupilika kwa Yehova, ngati timateteza mtima wathu, kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa.

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

^ ndime 5 Kodi tidzakhalabe okhulupilika kwa Yehova, kapena tidzalola Satana kutikopa mpaka kusiya kutumikila Mulungu? Ngati tiyesetsa kuteteza mtima wathu, tingakhalebe okhulupilika kwa Mulungu, olo titakumana na mayeselo aakulu bwanji. Koma kodi “mtima” umenewu n’ciani? N’ciani cimene Satana amacita pofuna kuipitsa mtima wathu? Nanga tingauteteze bwanji? M’nkhani ino, tidzakambilana mafunso ofunika kwambili amenewa.

^ ndime 11 MAWU OFOTOKOZEDWA: Yehova anatilenga na luso lotha kupenda maganizo na mtima wathu, komanso zocita zathu, kenako n’kudziweluza tekha. M’Baibo, luso limeneli limachedwa cikumbumtima. (Aroma 2:15; 9:1) Cikumbumtima cophunzitsidwa Baibo ni cimene cimaseŵenzetsa mfundo za Yehova, zopezeka m’Mawu ake, potiweluza kuti kaya zoganiza zathu, zocita na zokamba zathu n’zabwino kapena ayi.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 15: M’bale akutamba TV. Koma mwadzidzidzi payamba kuoneka zinthu zosayenela. Iye afunika kupanga cosankha.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 16: Mlonda wa m’nthawi yakale waona adani akubwela kunja kwa mzinda. Kenako, akukuwila alonda a pa geti, ndipo iwo akutseka geti mwamsanga na kuikhoma.