Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumaonetsa Kuti Ndife Anthu Otani?

Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumaonetsa Kuti Ndife Anthu Otani?

“Mukulengezabe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.” —1 AKOR. 11:26.

NYIMBO 18 Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

ZA M’NKHANI INO *

1-2. (a) Kodi Yehova amaona ciani pamene anthu mamiliyoni ambili asonkhana kuti acite Mgonelo wa Ambuye? (Onani cithunzi ca pacikuto.) (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

GANIZILANI zimene Yehova amaona pamene anthu mamiliyoni ambili padziko lonse asonkhana kuti acite Mgonelo wa Ambuye. Iye samangoyang’ana kuculuka kwa ciŵelengelo ca anthu amene asonkhana, koma amayang’ana munthu aliyense payekha amene wapezekapo. Mwacitsanzo, amaona anthu amene amayesetsa kupezekapo caka ciliconse. Ena mwa iwo angakhale anthu amene akukumana na cizunzo cacikulu. Komanso ena sapezeka nthawi zonse pa misonkhano ina, koma amaona kuti kupezeka pa Cikumbutso n’kofunika. Yehova amayang’ananso anthu ena amene apezeka pa Cikumbutso mwina kwa nthawi yoyamba. Anthu amenewa amapezekapo mwina cifukwa cofuna kudziŵa mmene mwambowu umacitikila.

2 Mwacionekele, Yehova amakondwela akaona kuti anthu ambili asonkhana kuti acite Cikumbutso. (Luka 22:19) Komabe, sikuti Yehova amakondwela cabe na kuculuka kwa ciŵelengelo ca anthu opezeka pa msonkhano. Koma amacita cidwi na zifukwa zimene zasonkhezela anthu kupezeka pa msonkhanowu. M’nkhani ino, tidzakambilana funso lofunika kwambili lakuti, N’cifukwa ciani timapezeka pa mwambo wa pacaka wokumbukila imfa ya Yesu, komanso pa misonkhano ya mlungu na mlungu imene Yehova amakonzela anthu ake?

Anthu mamiliyoni ambili pa dziko lonse lapansi adzalandilidwa pa Mgonelo wa Ambuye(Onani malagilafu 1-2)

KUDZICEPETSA KUMATISONKHEZELA KUPEZEKA PA MISONKHANO

3-4. (a) N’cifukwa ciani timapezeka pa misonkhano? (b) Nanga kupezekapo kwathu kumaonetsa kuti ndife anthu otani? (c) Malinga n’zimene 1 Akorinto 11:23-26 imakamba, n’cifukwa ciani sitiyenela kuphonya Cikumbutso?

3 Cifukwa cacikulu cimene timapezekela pa misonkhano ya mpingo n’cakuti kusonkhana ni mbali ya kulambila kwathu. Cifukwa cina n’cakuti timafuna kuphunzitsidwa na Yehova. Anthu odzikuza safuna kuphunzitsidwa zinthu na ena. (3 Yoh. 9) Mosiyana na anthu amenewo, ife timafunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso gulu lake.—Yes. 30:20; Yoh. 6:45.

4 Kupezeka kwathu pa misonkhano kumaonetsa kuti ndife odzicepetsa, ndipo timafuna kuphunzitsidwa. Timapezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Yesu cifukwa timadziŵa kuti msonkhanowu ni wofunika kwambili, komanso cifukwa timamvela modzicepetsa lamulo la Yesu, lakuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Ŵelengani 1 Akorinto 11:23-26.) Msonkhanowu umatithandiza kukhala na ciyembekezo colimba, komanso umatikumbutsa za cikondi cacikulu cimene Yehova ali naco pa ife. Komabe, Yehova adziŵa kuti timafunika kulimbikitsidwa nthawi zonse, osati kamodzi cabe pa caka. Mwa ici, iye amatikonzela misonkhano wiki iliyonse, ndipo amatilimbikitsa kuti tizipezekapo. Kudzicepetsa kumatilimbikitsa kumumvela. Ndiye cifukwa cake, wiki iliyonse timathela nthawi yoculuka kukonzekela misonkhano imeneyi komanso kukapezekapo.

5. N’cifukwa ciani anthu odzicepetsa amalabadila ciitano ca Yehova?

5 Caka ciliconse, Yehova amaitana anthu odzicepetsa kuti awaphunzitse. Ndipo ambili amalabadila ciitano cimeneci. (Yes. 50:4) Iwo amakondwela kupezeka pa Cikumbutso, ndipo pambuyo pake, amayamba kupezekanso pa misonkhano ina. (Zek. 8:20-23) Tonse timakondwela kuphunzitsidwa na kutsogoleledwa na Yehova, amene ni ‘thandizo lathu’ komanso Wotipatsa cipulumutso. (Sal. 40:17) Ndithudi, n’zokondweletsa kwambili komanso ni mwayi wa mtengo wapatali kuphunzitsidwa na Yehova ndi Mwana wake wokondedwa kwambili, Yesu.—Mat. 17:5; 18:20; 28:20.

6. Kodi kudzicepetsa kunathandiza bwanji mwamuna wina kupezeka pa Cikumbutso?

6 Caka ciliconse, timayesetsa mmene tingathele kuitanila anthu ambili ku Cikumbutso ca imfa ya Yesu. Anthu ambili odzicepetsa apindula cifukwa colabadila ciitano cimeneco. Ganizilani citsanzo ici. Zaka zapitazo, mwamuna wina anapatsidwa kathilakiti ka ciitano ca ku Cikumbutso. Koma anauza m’bale amene anamupatsa kapepako kuti sadzakwanitsa kufika. Komabe, tsiku la Cikumbutso litafika, m’baleyo anadabwa kuona kuti mwamuna uja wafika pa Nyumba ya Ufumu. Mwamunayo analimbikitsidwa kwambili na mmene abale anamulandilila, cakuti anayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo mokhazikika. Iye anali kusonkhana mokhazikika, moti anangophonyako katatu misonkhano m’caka conse cotsatila. N’ciani cinamulimbikitsa kuti ayambe kupezeka pa misonkhano nthawi zonse? Iye anali wodzicepetsa kwambili, ndipo anali wokonzeka kusintha. M’bale amene anamuitanilayo anati, “Iye ni munthu wodzicepetsa kwambili.” N’zosakayikitsa kuti Yehova ndiye anakokela munthuyo kwa iye kuti ayambe kum’tumikila. Mwamunayo anabatizika tsopano.—2 Sam. 22:28; Yoh. 6:44.

7. Kodi zimene timaphunzila pa misonkhano na zimene timaŵelenga m’Baibo zingatithandize bwanji kukhala odzicepetsa?

7 Zimene timaphunzila pa misonkhano, ndiponso zimene timaŵelenga m’Baibo zingatithandize kukhala odzicepetsa. Kutatsala mawiki angapo kuti ticite Cikumbutso, kaŵili-kaŵili pa misonkhano timaphunzila kwambili za citsanzo ca Yesu, komanso mmene anaonetsela kudzicepetsa popeleka moyo wake monga dipo. Ndipo pamene kwatsala masiku oŵelengeka kuti ticite Cikumbutso, tidzafunika kuŵelenga nkhani za m’Baibo zokhudza zimene zinacitika pa nthawi ya imfa ya Yesu na ciukililo cake. Zimene timaphunzila pa misonkhano imeneyi, komanso zimene timaŵelenga m’nkhani za m’Baibo, zimatithandiza kuyamikila kwambili nsembe imene Yesu anapeleka kaamba ka ife. Izi zimatilimbikitsa kutengela citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa. Zimatilimbikitsanso kucita cifunilo ca Yehova, ngakhale pamene tiona kuti kucita izi n’kovuta.—Luka 22:41, 42.

KULIMBA MTIMA KUMATITHANDIZA KUPEZEKA PA MISONKHANO

8. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kulimba mtima?

8 Timayesetsanso kutengela citsanzo ca Yesu ca kulimba mtima. Ganizilani mmene iye anaonetsela kulimba mtima m’masiku othela a moyo wake. Iye anali kudziŵa bwino kuti posacedwa adani ake adzamucita cipongwe, kumumenya, na kumupha. (Mat. 20:17-19) Ngakhale n’conco, iye sanaope kuphedwa. Nthawi yakuti apelekedwe itafika, Yesu anauza atumwi ake okhulupilika, amene anali naye m’munda wa Getsemane kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipeleka uja ali pafupi.” (Mat. 26:36, 46) Ndiyeno, pamene asilikali ndi anthu ena anabwela kuti amugwile, Yesu anawayandikila na kudzidziŵikitsa. Kenako, anauza asilikaliwo kuti awaleke ophunzila ake apite. (Yoh. 18:3-8) Ndithudi, Yesu anaonetsa kulimba mtima kwakukulu! Masiku ano, Akhristu odzozedwa na a nkhosa zina amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu ca kulimba mtima. Motani?

Kulimba mtima kumene mumaonetsa kuti mupezeke pa misonkhano kumalimbikitsa ena (Onani palagilafu 9) *

9. (a) N’cifukwa ciani timafunika kulimba mtima kuti tizipezeka pa misonkhano nthawi zonse? (b) Kodi citsanzo cathu cingakhudze bwanji abale amene ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo?

9 Kuti tizipezeka pa misonkhano nthawi zonse, timafunika kulimba mtima poyang’anizana na mavuto. Mwacitsanzo, abale na alongo athu ena amayesetsa kupezeka pa misonkhano, mosasamala kanthu za mavuto monga matenda, zofooketsa, na cisoni cacikulu. Palinso ena amene amalimba mtima kupezeka pa misonkhano, ngakhale kuti amatsutsidwa kwambili na a m’banja mwawo, kapena akulu-akulu a boma. Komanso, ganizilani mmene citsanzo cathu cimakhudzila abale amene ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. (Aheb. 13:3) Iwo akamvela kuti tikutumikilabe Yehova olo kuti tikukumana na mayeselo, amalimba mtima, cikhulupililo cawo cimalimbilako, ndiponso amalimbikitsidwa kukhalabe okhulupilika. Mtumwi Paulo analimbikitsidwapo mwanjila imeneyi. Pamene anali m’ndende ku Roma, iye anali kukondwela kwambili akamvela kuti abale ake akutumikila Mulungu mokhulupilika. (Afil. 1:3-5, 12-14) Paulo atatsala pang’ono kumasulidwa kapena atangomasulidwa kumene, analembela kalata Akhristu aciheberi. M’kalatayo, Paulo analimbikitsa Akhristu okhulupilika amenewo kuti apitilize kukondana, komanso kuti asaleke kusonkhana pamodzi.—Aheb. 10:24, 25; 13:1.

10-11. (a) Kodi n’ndani amene tingawaitanile ku Cikumbutso? (b) Nanga pa Aefeso 1:7 pali cifukwa citi cimene timacitila zimenezo?

10 Timaonetsanso kulimba mtima mwa kuitanila ku Cikumbutso abululu athu, anzathu a ku nchito, na maneba athu. N’ciani cimatisonkhezela kuwaitanila? Timayamikila kwambili zimene Yehova na Yesu anaticitila cakuti timafunitsitsa kuitanilako ena ku Cikumbutso. Timafuna kuti iwonso adziŵe mmene angapindulile na ‘kukoma mtima kwakukulu’ kumene Yehova anakuonetsa popeleka dipo.—Ŵelengani Aefeso 1:7;Chiv. 22:17.

11 Pamene tionetsa kulimba mtima mwa kupezeka pa misonkhano, timaonetsanso khalidwe lina lofunika kwambili, limene Yehova na Mwana wake amalionetsa m’njila zambili zapadela.

CIKONDI CIMATISONKHEZELA KUPEZEKA PA MISONKHANO

12. (a) Kodi misonkhano imatithandiza bwanji kukulitsa cikondi cathu pa Yehova na Yesu? (b) Kodi 2 Akorinto 5:14, 15 imatilimbikitsa kucita ciani potengela Yesu?

12 Cikondi cathu pa Yehova na Yesu cimatisonkhezela kupezeka pa misonkhano. Ndipo zimene timaphunzila pa misonkhano, zimatithandiza kukulitsa cikondi cathu pa Yehova na Mwana wake. Zili conco cifukwa nthawi zambili tikapezeka pa misonkhano, timakumbutsidwa zabwino zimene iwo anaticitila. (Aroma 5:8) Maka-maka pa Cikumbutso, m’pamene timakumbutsidwa kwambili za cikondi cacikulu cimene Yehova na Yesu anaonetsa kwa anthu, ngakhale kwa amene sazindikila kufunika kwa dipo. Cifukwa cakuti timayamikila kwambili dipo, timayesetsa nthawi zonse kutengela Yesu pa zocita zathu. (Ŵelengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Kuwonjezela apo, mtima wathu woyamikila umatisonkhezela kutamanda Yehova kaamba ka dipo limene anapeleka. Njila imodzi imene tingam’tamandile ni mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano.

13. Kodi tingaonetse bwanji kuti timakonda kwambili Yehova na Mwana wake? Fotokozani.

13 Tingaonetse kuti timakonda kwambili Yehova na Mwana wake, mwa kukhala okonzeka kudzimana zinthu zina kuti ticite zinthu zowakondweletsa. Nthawi zambili, timafunika kudzimana zinthu zina n’colinga cakuti tikapezeke pa misonkhano. Mwacitsanzo, mipingo yambili imacita msonkhano wa Umoyo na Utumiki mkati mwa wiki madzulo. Pa nthawiyi, ena timakhala kuti tangocoka kumene ku nchito, ndipo ndife olema. Msonkhano wina umacitika kumapeto kwa wiki, pamene ena amaona kuti ndiyo nthawi yopumula. Kodi Yehova amayamikila tikamayesetsa kupezeka pa misonkhano ngakhale pamene tili olema? N’zosacita kufunsa! Yehova amayamikila kwambili ngati ticita zilizonse zotheka kuti tikapezekepo pa misonkhano, poonetsa cikondi cathu pa iye.—Maliko 12:41-44.

14. Kodi Yesu anapeleka bwanji citsanzo cabwino pankhani yoonetsa cikondi codzimana?

14 Yesu anapeleka citsanzo cabwino pankhani yoonetsa cikondi codzimana. Iye anali wokonzeka kufela ophunzila ake, na kuika zofuna zawo patsogolo pa zofuna zake. Mwacitsanzo, ngakhale pamene anali wolema na wopanikizika maganizo, iye sanaleke kulimbikitsa ophunzila ake. (Luka 22:39-46) Cinanso, anali kuganizila kwambili pa zabwino zimene angacitile ena, osati pa zimene anali kufuna kuti ena am’citile. (Mat. 20:28) Ngati timakonda kwambili Yehova na abale athu, tidzacita zonse zotheka kuti tizipezeka pa Mgonelo wa Ambuye, komanso pa misonkhano ina yonse ya mpingo.

15. N’ndani maka-maka amene timafuna kuthandiza?

15 Tili m’gulu lokhalo la Akhristu oona, amene ali pa ubale weni-weni, ndipo timayesetsa kuitanila anthu ena ambili kuti abwele m’gulu limeneli. Koma timafunitsitsa kuthandiza “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo,” amene anazilala mwauzimu. (Agal. 6:10) Timaonetsa kuti timawakonda mwa kuwalimbikitsa kuti azipezeka pa misonkhano, maka-maka pa Cikumbutso. Ndipo mofanana na Yehova na Yesu, timakondwela kwambili pamene Mkhristu wozilala wabwelela kwa Yehova, Atate wathu wacikondi komanso Mbusa wathu.—Mat. 18:14.

16. (a) Tingacite ciani kuti tizilimbikitsana? Nanga misonkhano ingatithandize bwanji?

16 M’mawiki akubwelawa, mukayesetse kuitanila anthu ambili mmene mungathele kuti akapezeke pa Cikumbutso, pa tsiku la Cisanu madzulo, pa April 19, 2019. (Onani bokosi yakuti, “Kodi Mudzaitanilako Ena?”) Conco, tiyeni tiziyesetsa kulimbikitsana mwa kupezeka nthawi zonse pa misonkhano imene Yehova amatikonzela. Ndipo pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, tifunika kumapezeka pa misonkhano, cifukwa idzatithandiza kukhala odzicepetsa, olimba mtima, ndi acikondi. (1 Ates. 5:8-11) Conco, na mtima wathu wonse, tiyeni tizicita zinthu zoonetsa kuti timayamikila kwambili Yehova na Mwana wake, cifukwa ca cikondi cacikulu cimene anationetsa.—Ŵelengani Yohane 3:16.

NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu

^ ndime 5 Cikumbutso ca imfa ya Khristu cimene cidzacitika pa Cisanu madzulo, pa April 19, 2019, cidzakhala cocitika capadela kwambili m’caka cimeneci. Kodi n’ciani cimatisonkhezela kupezeka pa msonkhanowu? Mwacionekele, timapezekapo cifukwa timafuna kukondweletsa Yehova. M’nkhani ino tidzakambilana makhalidwe amene amatisonkhezela kupezeka pa Cikumbutso komanso pa misonkhano ya mlungu na mlungu.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale amene ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cake akulimbikitsidwa na kalata yocokela kwa a m’banja mwake. Iye ni wokondwa kudziŵa kuti a m’banja mwake sanamuiwale komanso kuti iwo akupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika, ngakhale kuti m’dela lawo muli mavuto a zandale na ciwawa.