Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ndine Mulungu Wako”

“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ndine Mulungu Wako”

Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—YES. 41:10.

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

ZA M’NKHANI INO *

1-2. (a) Kodi uthenga wa pa Yesaya 41:10 unam’tonthoza bwanji mlongo Yoshiko? (b) Kodi Yehova anauzila uthenga umenewu kuti udzatonthoze ndani?

MLONGO wina, dzina lake Yoshiko, anauzidwa mawu odandaulitsa. Adokotala anamuuza kuti pakapita miyezi yocepa cabe, adzamwalila. Kodi iye anacita ciani? Anakumbukila lemba lake la pamtima, la Yesaya 41:10. (Ŵelengani.) Ndiyeno modekha, Mlongoyo anauza adokotala kuti sanali kuyopa kufa, cifukwa Yehova anali atagwila dzanja lake. * Uthenga wacitonthozo wa m’lembali, unathandiza mlongo wathu ameneyu kudalila Yehova na mtima wake wonse. Na ife, lembali lingatitonthoze pamene takumana na mavuto aakulu. Kuti tidziŵe mmene mfundo za palembali zingatitonthozele, coyamba tiyeni tikambilane cifukwa cake Mulungu anauzila Yesaya kulemba uthenga wa pa lembali.

2 Yehova anauzila mneneli Yesaya kulemba uthenga wa pa lembali, pofuna kutonthoza Ayuda amene anali kudzatengewa kupita ku ukapolo ku Babulo. Ngakhale n’conco, Yehova anadziŵa kuti uthengawu udzatonthozanso atumiki ake a kutsogolo. (Yes. 40:8; Aroma 15:4) Masiku ano, tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta.’ Conco, kuposa kale lonse, uthenga wolimbikitsa wa m’buku la Yesaya ni wofunika kwambili kwa ife.—2 Tim. 3:1.

3. (a) Kodi pa Yesaya 41:10 pali malonjezo ati? (b) Nanga n’cifukwa ciani malonjezo amenewa ni ofunika kwa ife?

3 M’nkhani ino, tidzakambilana malonjezo atatu a Yehova olimbitsa cikhulupililo, a pa Yesaya 41:10, limene ni lemba lathu la caka ca 2019. Malonjezo ake ni awa: (1) Yehova adzakhala nafe, (2) iye ni Mulungu wathu, na (3) adzatithandiza. Malonjezo * amenewa ni ofunika kwambili kwa ife, cifukwa mofanana ndi mlongo Yoshiko, na ife timakumana na mavuto mu umoyo wathu. Komanso, timakumana na mavuto cifukwa ca zinthu zoipa zimene zikucitika m’dzikoli. Ena a ife tikuzunzidwa na maboma amphamvu. Tsopano tiyeni tikambilane malonjezo atatu amenewa.

“NDILI NAWE”

4. (a) Ni lonjezo liti loyamba limene tidzakambilana? (Onaninso mawu amunsi.) (b) Kodi Yehova anakamba ciani poonetsa kuti amatikonda? (c) Nanga mawu ake amenewa amakukhudzani bwanji?

4 Coyamba, Yehova akutitonthoza na mawu akuti: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe.” * Yehova amaonetsa kuti ali nafe mwa kutisamalila na kutikonda. Onani zimene iye anakamba poonetsa kuti amatikonda kwambili. Anati: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4) Palibe ciliconse m’cilengedwe cimene cingapangitse Yehova kuleka kukonda atumiki ake. Iye amacita nafe zinthu mokhulupilika kwambili. (Yes. 54:10) Kudziŵa kuti Yehova ni bwenzi lathu, komanso kuti amatikonda, kumatithandiza kukhala olimba mtima kwambili. Timadziŵa kuti adzatiteteza pa mavuto monga mmene anatetezela Abulamu (Abulahamu) bwenzi lake. Yehova anamuuza kuti: “Usaope Abulamu. Ine ndine cishango cako.”—Gen. 15:1.

Mwa thandizo la Yehova, sitidzakokoloka na mavuto okhala ngati mitsinje, kapena kugonja ku mayeselo okhala ngati laŵi la moto (Onani palagilafu 5-6) *

5-6. (a) Timadziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kutithandiza tikakumana na mavuto? (b) Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo Yoshiko?

5 Tidziŵa kuti Yehova amafuna kutithandiza tikakumana na mavuto, cifukwa iye anatilonjeza kuti: “Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe. Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza. Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.” (Yes. 43:2) Kodi mawu amenewa atanthauza ciani?

6 Yehova amalola kuti tikumane na mavuto. Komabe, iye watilonjeza kuti sadzalola kuti tikokoloke, kapena kuti kugonjetsedwa na mavuto okhala ngati “mitsinje.” Walonjezanso kuti sadzalola mayeselo onga “laŵi la moto” kutiwononga kothelatu. Iye watitsimikizila kuti adzakhala nafe, na kutithandiza kupilila mavuto na mayeselo. Kodi Yehova adzatithandiza bwanji? Adzatithandiza kukhala olimba mtima, n’colinga cakuti tikhalebe okhulupilika kwa iye, olo pamene tayang’anizana na imfa. (Yes. 41:13) Mlongo Yoshiko, amene tam’chula kuciyambi, anadzionela yekha kuti mfundo imeneyi ni yoona. Mwana wake wamkazi anati: “Tinacita cidwi kuona mmene amayi anaonetsela kudekha. Yehova anawathandiza kukhala na mtendele wa m’maganizo. Mpaka pa tsiku limene anamwalila, iwo anali kuuzako manesi na odwala anzawo zokhudza Yehova na malonjezo ake.” Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo Yoshiko? Tiphunzilapo kuti ngati tikhulupilila lonjezo la Mulungu lakuti: “Ndili nawe,” na ife tidzakhala olimba pokumana na mayeselo.

“INE NDINE MULUNGU WAKO”

7-8. (a) Ni lonjezo laciŵili liti limene tidzakambilana? Nanga lonjezo limeneli litanthauza ciani? (b) N’cifukwa ciani Yehova anauza Ayuda amene anali ku ukapolo kuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha”? (c) Ni mawu ati a pa Yesaya 46:3, 4 amene ayenela kuti anathandiza Ayuda kuti asacite mantha?

7 Lonjezo laciŵili limene Yehova anauzila Yesaya kulemba n’lakuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” Kodi mawu amenewa atanthauza ciani? M’citundu coyambilila, mawu amene anamasulidwa kuti, ‘kuyang’ana uku ndi uku mwamantha,’ amatanthauza “kuceuka-ceuka monga mmene munthu amacitila akadzidzimutsidwa” kapena “cifukwa coopa cinacake.”

8 N’cifukwa ciani Yehova anauza Ayuda amene anali kudzatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo kuti ‘asacite mantha’? Cifukwa iye anadziŵa kuti panthawi ina, anthu a ku Babulo adzacita mantha. N’ciani cikanawacititsa kukhala na mantha? Cakumapeto kwa zaka 70 za ukapolo wa Ayuda, mzinda wa Babulo unali kudzaukilidwa na asilikali amphamvu a Mediya ndi Perisiya. Yehova anakambilatu kuti adzaseŵenzetsa asilikali amenewa kuti amasule anthu ake ku ukapolo ku Babulo. (Yes. 41:2-4) Pamene Ababulo ndi anthu a mitundu ina anadziŵa kuti adani awo akubwela, anayesa kulimbikitsana mwa kuuzana kuti: “Limba mtima.” Iwo anapanganso mafano ambili, poganiza kuti adzawateteza. (Yes. 41:5-7) Koma Yehova analimbikitsa Ayuda amene anali ku ukapolo, mwa kuwauza kuti: “Iwe Isiraeli, [osati mitundu ina] ndiwe mtumiki wanga . . . Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” (Yes. 41:8-10) Onani kuti Yehova anati: “Ine ndine Mulungu wako.” Mawu a Yehova amenewa anathandiza atumiki ake okhulupilika kudziŵa kuti iye sanawaiŵale. Anawatsimikizila kuti iye akali Mulungu wawo, ndiponso kuti iwo akali anthu ake. Anawauza kuti, ‘adzawatenga ndi kuwapulumutsa.’ Mwacionekele, mawu otonthoza amenewa anawalimbikitsa ngako Ayuda amene anali ku ukapolo.—Ŵelengani Yesaya 46:3, 4.

9-10. N’cifukwa ciani sitifunika kuyopa tikakumana na mavuto? Fotokozani citsanzo.

9 Kuposa kale lonse, anthu ambili masiku ano ali na mantha cifukwa cakuti mavuto akuculukila-culukila m’dzikoli. N’zoona kuti na ife timakumana na mavuto amenewa. Koma sitiyenela kuyopa, cifukwa Yehova akutiuza kuti: “Ine ndine Mulungu wako.” N’cifukwa ciani mfundo imeneyi ni yolimbikitsa kwambili?

10 Tiyelekeze motele: Anthu aŵili, Ben na Jim, ali m’ndeke imene iwombedwa na cimphepo camphamvu. Pamene ndekeyo indenguma uku na uku cifukwa ca cimphepo camphamvu, iwo amva mawu ocokela kwa woyendetsa ndeke. Iye akamba kuti: “Mangani malamba anu. Cifukwa tidzapita m’dela lacimphepo kwa kanthawi.” Jim acita mantha kwambili. Koma kenako woyendetsa ndekeyo akamba mawu olimbikitsa, amvekele: “Ndine pailoti wanu. Musataye mtima, cifukwa zonse zili m’malo.” Koma cifukwa ca nkhawa, Jim akayikila zimenezi. Akuti: “Sinikhulupilila kuti tikafika bwino.” Kenako pamene ayang’ana Ben, akudabwa kuona kuti iye sacita mantha ngakhale pang’ono. Ndiyeno, Jim afunsa Ben kuti: “N’cifukwa ciani sucita mantha?” Ben amwetulila na kumuyankha kuti: “Cifukwa amene ayendetsa ndeke niŵadziŵa bwino. Ni atate anga!” Ndiyeno Ben auza Jim kuti: “Leka nikuuze zambili zokhudza atate na maluso awo oyendetsa ndeke. Nikhulupilila kuti ukawadziŵa bwino, nawenso sudzacita mantha.”

11. Kodi titengapo phunzilo lanji pa citsanzo ca anthu aŵili amene anakwela ndeke?

11 Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo cimeneci? Mofanana na Ben, na ife siticita mantha tikakumana na mavuto, cifukwa timawadziŵa bwino kwambili Atate wathu wakumwamba, Yehova. Tidziŵa kuti iye adzatithandiza kupilila ngakhale mavuto aakulu amene timakumana nawo masiku ano otsiliza. (Yes. 35:4) Popeza kuti timadalila Yehova, tingakhalebe opanda mantha, ngakhale pamene anthu m’dzikoli ali na mantha aakulu. (Yes. 30:15) Mofanana na Ben, timauzako anzathu cifukwa cake timadalila Mulungu. Izi zingawathandize kuti nawonso asamakayikile kuti Yehova adzawacilikiza, olo akumane na mavuto aakulu bwanji.

“NDIKULIMBITSA [KOMANSO] NDIKUTHANDIZA”

12. (a) Ni lonjezo lacitatu liti limene tidzakambilana? (b) Kodi mawu akuti “mkono” wa Yehova atikumbutsa mfundo yanji?

12 Tsopano, ganizilani lonjezo lacitatu limene Mulungu anakamba kupitila mwa Yesaya. Anati: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” Pofotokoza mmene Yehova adzalimbitsila anthu ake, Yesaya anati: “Yehova. . .adzabwela ngati wamphamvu ndipo [“mkono,” NW-E] wake uzidzalamulila m’malo mwa iyeyo.” (Yes. 40:10) Kaŵili-kaŵili, Baibo imaseŵenzetsa liwu lakuti “mkono” kuphiphilitsila mphamvu. Conco, mawu akuti “mkono wa [Yehova] udzalamulila” atikumbutsa zakuti Yehova ni Mfumu yamphamvu. Iye anaseŵenzetsa mphamvu zake zopanda malile polimbitsa atumiki ake akale na kuwateteza. Ndipo masiku anonso, amalimbitsa na kuteteza atumiki ake amene amam’dalila.—Deut. 1:30, 31; Yes. 43:10.

Palibe cida ciliconse cimene cingagonjetse mkono wamphamvu wa Yehova, umene umatiteteza (Onani palagilafu 12-16) *

13. (a) Ni panthawi iti maka-maka pamene Yehova amasunga lonjezo lake lakuti adzatilimbitsa? (b) Ni lonjezo liti limene limatilimbikitsa kwambili?

13 Yehova amasunga lonjezo lake lakuti: “Ndikulimbitsa,” maka-maka pamene adani athu akutizunza. M’maiko ena, adani athu akuyesetsa mwamphamvu kuletsa nchito yathu yolalikila kapena kutseka maofesi athu. Ngakhale n’conco, sititaya mtima na zimenezi, cifukwa zimene Yehova watilonjeza zimatilimbikitsa kwambili. Iye akuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.” (Yes. 54:17) Lonjezo limeneli litikumbutsa mfundo zitatu zofunika.

14. N’cifukwa ciani n’zosadabwitsa kuti adani a Mulungu amatiukila?

14 Mfundo yoyamba ni yakuti, monga otsatila a Yesu, timayembekezela kuzondewa. (Mat. 10:22) Yesu anakambilatu kuti ophunzila ake adzazunzidwa kwambili m’masiku otsiliza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Yaciŵili, zimene Yesaya analosela zionetsa kuti kuwonjezela pa kutizonda, adani athu adzaseŵenzetsa zida zosiyana-siyana polimbana nafe. Zida zimenezo, ni cinyengo camacenjela, mabodza amkunkhuniza, cizunzo coopsa, na zina zotelo. (Mat. 5:11) N’zoona kuti Yehova sadzaletsa adani athu kuseŵenzetsa zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitifunika kucita mantha. Cifukwa ciani?

15-16. (a) Ni mfundo iti yacitatu imene tiyenela kukumbukila? Nanga Yesaya 25:4, 5 imatsimikizila bwanji mfundo imeneyi? (b) Kodi Yesaya 41:11, 12 imakamba kuti n’ciani cidzacitikila adani athu amene amalimbana nafe?

15 Onani mfundo yacitatu imene tiyenela kukumbukila. Yehova anakamba kuti, “Cida ciliconse” cimene cidzaseŵenzetsedwa kuti citivulaze “sicidzapambana.” Monga mmene cipupa cingatitetezele ku mvula yoopsa yamkuntho, nayenso Yehova amatiteteza kwa “anthu ankhanza” amene amazunza anzawo. (Ŵelengani Yesaya 25:4, 5.) Ndithudi, adani athu sadzakwanitsa kutiwononga kothelatu!—Yes. 65:17.

16 Kuwonjezela apo, Yehova amatilimbikitsa mwa kutifotokozela zimene adzacita kwa anthu ‘onse otipsela mtima.’ (Ŵelengani Yesaya 41:11, 12.) Olo adani athu amenewa alimbane nafe bwanji, zotulukapo zake n’zodziŵikilatu: Adani onse a anthu a Mulungu “sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.”

ZIMENE TINGACITE KUTI TIZIDALILA KWAMBILI YEHOVA

Cimene cingatithandize kuti tiyambe kudalila kwambili Yehova, ni kuŵelenga za iye m’Baibo nthawi zonse. (Onani palagilafu 17-18) *

17-18. (a) Kodi kuŵelenga Baibo kungatithandize bwanji kuti tizidalila kwambili Mulungu? Fotokozani citsanzo. (b) Kodi kusinkha-sinkha lemba la caka ca 2019 kudzatithandiza bwanji?

17 Kuti tiyambe kudalila kwambili Yehova, tifunika kum’dziŵa bwino. Ndipo njila imodzi yokha imene tingam’dziwile bwino, ni mwa kuŵelenga Baibo n’colinga cofuna kuimvetsetsa, komanso kusinkha-sinkha pa zimene timaŵelenga. M’Baibo, muli nkhani zofotokoza mmene Yehova anatetezela atumiki ake akale. Nkhani zimenezi, zimatithandiza kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila.

18 Ganizilani za mawu ofanizila ogwila mtima, amene Yesaya anaseŵenzetsa poonetsa mmene Yehova amatitetezela. Iye anayelekezela Yehova na mbusa, komanso atumiki ake na nkhosa. Pokamba za Yehova, Yesaya anati: “Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi [“mkono,” NW-E] wake, ndipo adzawanyamulila pacifuwa pake.” (Yes. 40:11) Tikaona mmene Yehova amatitetezela na mkono wake wamphamvu, sitikhalanso na mantha. Pofuna kutithandiza kuti tisacite mantha ngakhale tikumana na mavuto, kapolo wokhulupilika na wanzelu wasankha Yesaya 41:10 kukhala lemba la caka ca 2019. Lembali limati: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” Muzisinkha-sinkha mawu olimbikitsa amenewa. Adzakuthandizani kukhala olimba mukadzakumana na mavuto kutsogolo.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

^ ndime 5 M’lemba la caka ca 2019, muli mfundo zitatu zimene zingatithandize kukhalabe odekha pamene zinthu zoipa zikucitika m’dziko, kapena pamene takumana na mavuto. M’nkhani ino, tidzakambilana mfundo zimenezo. Kucita izi kudzatithandiza kuti tisamakhale na nkhawa kwambili, koma kuti tizidalila Yehova. Muzisinkha-sinkha lemba la caka limeneli. Liloŵezeni pa mtima ngati n’kotheka. Mukatelo, lidzakuthandizani kupilila mavuto amene mudzakumana nawo kutsogolo.

^ ndime 1 Onani Nsanja ya Mlonda ya July 2016, peji 18.

^ ndime 3 MAWU OFOTOKOZEDWA: Malonjezo ni mawu otsimikizila kuti cinacake cidzacitikadi. Malonjezo amene Yehova anapeleka, angatithandize kucepetsa nkhawa imene timakhala nayo cifukwa ca mavuto amene timakumana nawo.

^ ndime 4 MAWU AMUNSI: Mawu akuti “Usacite mantha” amachulidwa maulendo atatu pa Yesaya 41:10, 13, 14. Mavesi amenewa amachulanso mobweleza-bweleza mawu akuti ‘ine’ (kutanthauza Yehova). N’cifukwa ciani Yehova anauzila Yesaya kulemba mobweleza-bweleza mawu akuti ‘ine’? Cifukwa anafuna kugogomeza mfundo yofunika yakuti tingacepetse mantha kokha ngati tidalila Yehova.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 3: A m’banja limodzi akukumana na mavuto osiyana-siyana; ku nchito, mu ulaliki, na ku sukulu, ndipo wina akudwala.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 5: Pamene abale na alongo akucita msonkhano m’nyumba, apolisi abwela kudzawagwila. Koma iwo sakucita mantha.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 6: Kucita Kulambila kwa Pabanja mokhazikika kumatithandiza kuti tipilile.