Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 4

Zimene Mwambo Wosalila Zambili Umatiphunzitsa Ponena za Mfumu Yathu

Zimene Mwambo Wosalila Zambili Umatiphunzitsa Ponena za Mfumu Yathu

“Mkate uwu ukuimila thupi langa. . . . Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a pangano.’”—MAT. 26:26-28.

NYIMBO 16 Tamandani Mwana Wodzozedwa wa Ya

ZA M’NKHANI INO *

1-2. (a) N’cifukwa ciani n’zosadabwitsa kuti Yesu anationetsa njila yosavuta yokumbukilila imfa yake? (b) Kodi tidzakambilana makhalidwe ati a Yesu?

KODI mungakwanitse kufotokoza zimene zimacitika pa mwambo wa pacaka wa Cikumbutso ca imfa ya Khristu? Mwacionekele, ambili a ife tikumbukila zimene zimacitika pa mwambowu. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti mwambo umenewu suloŵetsamo zambili, kapena kuti siwocolowana. Ngakhale n’conco, cocitika cimeneci n’capadela kwambili. Conco, tingafunse kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciani mwambowu suloŵetsamo zambili?’

2 Pa utumiki wake wa pa dziko lapansi, Yesu anali kudziŵika kwambili cifukwa ca luso lophunzitsa mfundo zofunika za coonadi m’njila yosavuta kumva. (Mat. 7:28, 29) Mofananamo, iye anationetsa njila yosavuta komanso yabwino yocitila Cikumbutso * ca imfa yake. Lomba tiyeni tikambilane zambili zokhudza mwambo wa Cikumbutso, komanso zinthu zina zimene Yesu anakamba na kucita. Kukambilana izi, kudzatithandiza kuona kuti Yesu anali wodzicepetsa kwambili, wolimba mtima, komanso wacikondi. Tidzaphunzilanso zimene tingacite kuti titengele kwambili makhalidwe ake amenewa.

YESU NI WODZICEPETSA

Ziphiphilitso za pa Cikumbutso, mkate na vinyo, zimatikumbutsa kuti Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka ife, komanso kuti lomba akulamulila monga Mfumu kumwamba (Onani palagilafu 3-5)

3. Malinga n’zimene Mateyu 26:26-28 imakamba, n’ciani cionetsa kuti mwambo wa Cikumbutso umene Yesu anayambitsa unali wosalila zambili? Nanga zinthu ziŵili zimene anaseŵenzetsa ziimila ciani?

3 Yesu anayambitsa mwambo wokumbukila imfa yake ali na atumwi ake 11 okhulupilika. Poyambitsa mwambowo, iye anaseŵenzetsa zakudya zimene zinatsala pa mwambo wa Pasika. (Ŵelengani Mateyu 26:26-28.) Anangoseŵenzetsa mkate wopanda cofufumitsa komanso vinyo. Yesu anauza atumwi ake kuti mkate na vinyo zinali kuimila thupi lake langwilo na magazi ake, amene anali kudzawapeleka cifukwa ca iwo. Atumwi ayenela kuti sanadabwe kuona kuti mwambo wapadela umene Yesu anayambitsa unali wosalila zambili. Cifukwa ciani takamba conco?

4. Kodi uphungu umene Yesu anapatsa Marita utithandiza bwanji kumvetsa cifukwa cake Yesu anayambitsa mwambo wa Cikumbutso wosalila zambili?

4 Ganizilani zimene zinacitika miyezi ingapo kumbuyoko, Yesu asanayambitse mwambo wa Cikumbutso. Umu munali m’caka cacitatu ca utumiki wake. Iye anapita kukaceza ku nyumba kwa mabwenzi ake, Lazaro, Marita, na Mariya. Pa nthawiyo, Yesu anayamba kuphunzitsa. Koma Marita anatangwanika na kukonzela Yesu zakudya zambili, monga mlendo wawo wolemekezeka. Yesu ataona zimenezo, mwacikondi anam’patsa uphungu Marita. Anamuuza kuti si nthawi zonse pamene kukonza zakudya zambili kumakhala kofunikila. (Luka 10:40-42) Pambuyo pake, atatsala pang’ono kupeleka moyo wake monga nsembe, Yesu anacita zinthu mogwilizana na malangizo ake amenewa. Anacita zimenezi mwa kuyambitsa mwambo wa Cikumbutso wosalila zambili. Kodi izi zitiphunzitsa ciani za Yesu?

5. Yesu anayambitsa mwambo wosalila zambili wokumbukila imfa yake. Kodi izi zitiphunzitsa ciani ponena za iye? Nanga zigwilizana bwanji na mfundo ya pa Afilipi 2:5-8 ?

5 Yesu anali wodzicepetsa nthawi zonse m’zocita zake na zokamba zake. Conco, n’zosadabwitsa kuti pa tsiku lothela la moyo wake padziko lapansi, iye anacita zinthu zoonetsa kudzicepetsa kwambili. (Mat. 11:29) Yesu anadziŵa kuti anali atatsala pang’ono kupeleka moyo wake, monga nsembe yofunika koposa m’mbili yonse ya anthu. Anali kudziŵanso kuti Yehova adzamuukitsa kuti akakhale mfumu kumwamba. Ngakhale kuti anali kudziŵa zimenezi, iye sanadzifunile yekha ulemu mwa kuyambitsa mwambo wapamwamba wokumbukila imfa yake. M’malomwake, anauza ophunzila ake kuti azim’kumbukila kamodzi pa caka mwa kucita mwambo wa cikumbutso wosalila zambili. (Yoh. 13:15; 1 Akor. 11:23-25) Ndithudi, Yesu anaonetsa kuti ni wodzicepetsa mwa kuyambitsa mwambo wosalila zambili koma woyenelela. N’zokondweletsa kudziŵa kuti kudzicepetsa, ni limodzi mwa makhalidwe aakulu a Mfumu yathu yakumwamba.—Ŵelengani Afilipi 2:5-8.

6. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa pamene takumana na mavuto?

6 Kodi tingatengele bwanji khalidwe la Yesu la kudzicepetsa? Tingacite izi mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu. (Afil. 2:3, 4) Ganizilaninso zimene zinacitika madzulo pa tsiku lothela la moyo wa Yesu pa dziko lapansi. Yesu anali kudziŵa kuti watsala pang’ono kufa imfa yoŵaŵa. Koma anali kudela nkhawa kwambili atumwi ake okhulupilika, poganizila za cisoni cimene adzakhala naco cifukwa ca imfa yake. Conco, madzulo amenewo, iye anathela nthawi yoculuka kulangiza ophunzila ake na kuwalimbikitsa. (Yoh. 14:25-31) Yesu anaonetsa kudzicepetsa mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zake. Ndithudi, iye anatisiila citsanzo cabwino kwambili cimene tiyenela kutengela!

YESU NI WOLIMBA MTIMA

7. Atangoyambitsa Mgonelo wa Ambuye, kodi Yesu anaonetsa bwanji kulimba mtima kwakukulu?

7 Atangoyambitsa Mgonelo wa Ambuye, Yesu anaonetsa kulimba mtima kwakukulu. Motani? Iye anadzipeleka kucita cifunilo ca Atate wake, olo kuti anali kudziŵa kuti kucita izi, kudzapangitsa kuti aphedwe pa mlandu wocititsa manyazi wakuti ananyoza Mulungu. (Mat. 26:65, 66; Luka 22:41, 42.) Yesu anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa yake, n’colinga cakuti alemekeze dzina la Yehova na kukweza ucifumu wake, ndiponso kuti atsegulile anthu omvela njila yokapeza moyo wosatha. Panthawi imodzi-modziyo, Yesu anakonzekeletsa ophunzila ake kaamba ka mayeselo amene anatsala pang’ono kukumana nawo.

8. (a) Kodi Yesu anawauza zinthu ziti atumwi ake okhulupilika? (b) Kodi ophunzila a Yesu anatsatila bwanji citsanzo cake ca kulimba mtima pambuyo pa imfa yake?

8 Yesu anaonetsanso kulimba mtima mwa kupewa kumangodela nkhawa za mavuto amene anali pafupi kukumana nawo. M’malomwake, anaika mtima wake pa kuthandiza na kulimbikitsa atumwi ake okhulupilika. Mwacitsanzo, pambuyo potulutsa Yudasi, Yesu anayambitsa mwambo wa Cikumbutso. Mwambowu unali kudzakumbutsa otsatila ake odzozedwa za madalitso amene adzapeza cifukwa ca magazi amene iye adzakhetsa, komanso cifukwa cokhala m’pangano latsopano. (1 Akor. 10:16, 17) Komanso, Yesu anauza otsatila ake zimene iye na Atate wake anali kufuna kuti iwo azicita. Anawauza izi pofuna kuwathandiza kuti akhale oyenelela kukalandila mphoto yawo ya kumwamba. (Yoh. 15:12-15) Kuwonjezela apo, anaŵauza za mavuto amene adzakumana nawo kutsogolo. Pambuyo pake, anawalimbikitsa kutengela citsanzo cake ca ‘kulimba mtima.’ (Yoh. 16:1-4a, 33) Kwa zaka zambili, ophunzila a Yesu anapitiliza kutengela citsanzo cake ca kulimba mtima na kudzimana. Iwo analolela kukumana na mavuto aakulu pofuna kuthandiza Akhristu anzawo pa mayeselo osiyana-siyana amene anali kukumana nawo.—Aheb. 10:33, 34.

9. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani yocita zinthu molimba mtima?

9 Masiku anonso, timatengela citsanzo ca Yesu ca kulimba mtima. Mwacitsanzo, pamafunika kulimba mtima kuti tithandize abale athu amene akuzunzidwa cifukwa ca cikhulupililo cawo. Nthawi zina, abale athu amaikiwa m’ndende pa mlandu wa bodza. Ngati izi zacitika, timafunika kuyesetsa kuwathandiza, mwina mwa kuwakambilako pa mlandu. (Afil. 1:14; Aheb. 13:19) Njila ina imene timaonetsela kulimba mtima, ni mwa kupitilizabe kulalikila “molimba mtima.” (Mac. 14:3) Mofanana na Yesu, na ife tatsimikiza mtima kupitilizabe kulalikila uthenga wa Ufumu ngakhale anthu atitsutse kapena kutizunza. Nanga bwanji ngati tiona kuti sindife olimba mtima kweni-kweni? Kodi tingacite ciani?

10. Patatsala mawiki angapo kuti Cikumbutso cicitike, n’ciani cimene tidzafunika kucita? Nanga n’cifukwa ciani tidzafunika kucita zimenezo?

10 Tingakulitse khalidwe la kulimba mtima mwa kuganizila ciyembekezo cimene tili naco cifukwa ca nsembe ya dipo imene Khristu anapeleka. (Yoh. 3:16; Aef. 1:7) Pakatsala mawiki angapo kuti ticite Cikumbutso, timakhala na mwayi wapadela wokulitsa ciyamikilo cathu kaamba ka dipo. Conco, pa nthawiyo, tizikaŵelenga Malemba a pa nyengo ya Cikumbutso, na kusinkha-sinkha mosamala pa zinthu zimene zinacitika panthawi imene Yesu anaphedwa. Ndiyeno, tikadzapezeka pa Mgonelo wa Ambuye, tikamvetsetsa tanthauzo la ziphiphilitso za pa mwambowu, komanso kukula kwa nsembe imene zimaimila. Ngati tamvetsetsa zimene Yesu na Yehova anaticitila, komanso mmene zimapindulitsila ife na okondedwa athu, ciyembekezo cathu cimalimbilako. Komanso, timalimbikitsidwa kupilila molimba mtima mpaka mapeto.—Aheb. 12:3.

11-12. Pofika pano, n’ciani cimene taphunzila?

11 Pofika pano, taphunzila kuti mwambo wa Cikumbutso umatikumbutsa za nsembe yamtengo wapatali ya dipo. Koma taonanso kuti mwambowu umatikumbutsa za makhalidwe abwino a Yesu, monga kudzicepetsa na kulimba mtima. N’zokondweletsa cotani nanga kudziŵa kuti Yesu, Mkulu wa Ansembe amene amaticondelela kwa Yehova, akupitilizabe kuonetsa makhalidwe abwino amenewa! (Aheb. 7:24, 25) Kuti tionetse kuti timayamikila zimenezi mocokela pansi pamtima, nthawi zonse tifunika kumakumbukila imfa ya Yesu mogwilizana na zimene iye anatilamulila. (Luka 22:19, 20) Timacita izi pa deti lofanana ndi tsiku la Nisani 14 pa kalenda ya Ciheberi. Ili ni deti lapadela kwambili m’caka.

12 Cikumbutso cosalila zambili cimene Yesu anayambitsa, cimatiphunzitsanso khalidwe lina limene linam’sonkhezela kuti atifele. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anali kudziŵika kwambili na khalidwe limeneli. Kodi ni khalidwe liti?

YESU NI WACIKONDI

13. Lemba la Yohane 15:9 ndi la 1 Yohane 4:8-10, amafotokoza bwanji cikondi cimene Yehova na Yesu anaonetsa? Nanga n’ndani amapindula na cikondi cimeneci?

13 M’zocita zake zonse, Yesu anaonetsa bwino cikondi cacikulu cimene Yehova ali naco pa ife. (Ŵelengani Yohane 15:9; 1 Yohane 4:8-10) Koposa zonse, Yesu anapeleka moyo wake na mtima wonse monga nsembe yotiwombola ku ucimo na imfa. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” timapindula na cikondi cimene Yehova na Mwana wake anationetsa, mwa kupeleka nsembe imeneyi. (Yoh. 10:16; 1 Yoh. 2:2) Komanso, ganizilani ziphiphilitso za pa Cikumbutso. Ziphiphilitso zimenezi zimaonetsa kuti Yesu ni wacikondi, komanso kuti anali kuganizila ophunzila ake. Motani?

Cifukwa ca cikondi, Yesu anayambitsa mwambo wa Cikumbutso wosalila zambili, umene otsatila ake akwanitsa kuucita kwa zaka zambili, komanso m’mikhalidwe yosiyana-siyana (Onani palagilafu 14-16) *

14. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwakonda ophunzila ake?

14 Yesu anaonetsa cikondi cake kwa otsatila ake odzozedwa, mwa kuyambitsa mwambo wa Mgonelo wosalila zambili, ndi wosacolowana. Otsatila akewo anafunika kupitiliza kucita mwambo wa Cikumbutso caka ciliconse. Ndipo anafunika kucita izi m’mikhalidwe yosiyana-siyana, ngakhale pamene ali m’ndende. (Chiv. 2:10) Kodi iwo anakwanitsa kumvela lamulo la Yesu limeneli? Inde, anatelo.

15-16. Kodi abale na alongo ena anakwanitsa bwanji kucita M’gonelo wa Ambuye m’nthawi zovuta?

15 Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Akhristu oona akhala akuyesetsa kucita Cikumbutso ca Imfa ya Yesu. Iwo akhala akuyesetsa mmene angathele kutsatila dongosolo la kacitidwe ka Mgonelo wa Ambuye, ngakhale pamene zinthu zili zovuta. Ganizilani zitsanzo izi. Pamene M’bale Harold King anali m’cipinda cayekha ca ndende ku China, anacita zonse zotheka kuti akwanitse kucita Cikumbutso. Mosaonetsela, iye anali kukonza ziphiphilitso za pa Cikumbutso, poseŵenzetsa zinthu zimene anali nazo. Komanso, anali kuyesetsa kuŵelengetsela mosamala deti ya Cikumbutso. Ndipo nthawi yocita Cikumbutso ikafika, ali yekha-yekha, anali kuimba, kupemphela, na kukamba nkhani ya Cikumbutso.

16 Citsanzo cina n’ca alongo amene anaikiwa m’ndende yacibalo pa nthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Iwo anaika miyoyo yawo pa ciopsezo n’colinga cakuti acite mwambo wa Cikumbutso. Ndipo anakwanitsa kucita zimenezi mosaonekela, cifukwa mwambowu ni wosalila zambili. Iwo anati: “Tinaimilila moyandikana, komanso mozungulila ka mpando kophimbidwa na nsalu yoyela, kamene tinaikapo ziphiphilitso. Tinaseŵenzetsa kandulo m’malo mwa magetsi, kuti ena asadziŵe zimene tinali kucita. . . . Ndiyeno, tinabwelezanso malumbilo athu ocokela pansi pa mtima kwa Yehova. Tinalonjeza kuti tidzacita zilizonse zotheka pothandiza kuyeletsa dzina lake lopatulika.” Apa, alongowa anaonetsa cikhulupililo colimba kwambili. Ndipo kukamba zoona, Yesu anaonetsa cikondi cacikulu mwa kuyambitsa mwambo wa Cikumbutso wosalila zambili, umene tingathe kuucita ngakhale m’nthawi zovuta.

17. Pamene Cikumbutso cikuyandikila, ni mafunso ati amene tingadzifunse?

17 Pamene Cikumbutso cikuyandikila, tingacite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ningatengele bwanji citsanzo ca Yesu poonetsa cikondi kwa ena? Kodi nimaika zosoŵa za Akhristu anzanga patsogolo pa zosoŵa zanga? Kodi nimayembekezela abale na alongo kucita zambili kuposa zimene angakwanitse, kapena nimazindikila zimene sangakwanitse?’ Tiyeni nthawi zonse titengele citsanzo ca Yesu mwa kumvela ena cisoni.—1 Pet. 3:8.

TENGELANI YESU MWA KUKHALA ODZICEPETSA, OLIMBA MTIMA, NDI ACIKONDI

18-19. (a) Kodi sitili okayikila za ciani? (b) Kodi mudzayesetsa kucita ciani?

18 Posacedwa, tidzaleka kucita Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Yesu ‘akadzafika’ pa cisautso cacikulu, adzasonkhanitsila “osankhidwa ake” kumwamba. Ndipo zikadzakhala conco, sitidzacitanso Cikumbutso.—1 Akor. 11:26; Mat. 24:31.

19 Ngakhale tikadzaleka kucita Cikumbutso, sitikayikila kuti tidzapitiliza kuona mwambo umenewo monga cizindikilo ca kudzicepetsa kwakukulu, kulimba mtima, komanso cikondi cacikulu cimene Yesu anaonetsa. Pa nthawiyo, anthu amene amapezekapo pa mwambo wapadela umenewu, mwacidziŵikile azikasimbilako ena za mwambowu kuti nawonso akaphunzilepo kanthu. Komabe, kuti tipindule na mwambowu panthawi ino, tifunika kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu mwa kukhala odzicepetsa, olimba mtima, ndi acikondi. Tikatelo, tidzakhala na cidalilo cakuti Yehova adzatidalitsa.—2 Pet. 1:10, 11.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

^ ndime 5 Posacedwapa, tidzacita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye pokumbukila imfa ya Yesu Khristu. Mwambo umenewu umakhala wosacolowana, kapena kuti wosalila zambili. Komabe, mwambowu umatiphunzitsa zambili zokhudza kudzicepetsa kwa Yesu, kulimba mtima, komanso cikondi cake. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingacite potengela makhalidwe ake amenewa.

^ ndime 2 MAWU OFOTOKOZEDWA: Cikumbutso ni mwambo wapadela umene umacitika pofuna kulemekeza kapena kukumbukila munthu wina kapena cocitika cinacake cofunika.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Zithunzi zoonetsa mmene atumiki okhulupilika a Yehova anali kucitila Cikumbutso m’nthawi ya atumwi; cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800; m’ndende yacibalo ya Nazi ku Germany; komanso m’Nyumba ya Ufumu yopanda zipupa ya m’nthawi yathu ino, m’dziko linalake la ku South America, kumene nyengo ni yotentha.