NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA January 2020

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya March 2–April 5, 2020.

‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’

Lemba la caka ca 2020 lidzatithandiza kuganizila mmene tingakulitsile luso pa nchito yathu yopanga ophunzila.

Mungathe Kulimbikitsa Ena Kwambili

Onani makhalidwe atatu amene angakuthandizeni kucita bwino kwambili polimbikitsa na kuthandiza ena.

Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika

Tikakhala na nkhawa cifukwa ca matenda, mavuto a zacuma, kapena ukalamba, tifunika kukumbukila kuti palibe cimene cingatilekanitse na cikondi ca Atate wathu wakumwamba.

‘Mzimu Umacitila Umboni Limodzi Ndi Mzimu Wathu’

Kodi munthu amadziŵa bwanji kuti wadzozedwa na mzimu woyela? Nanga n’ciani cimacitika munthu akaitanidwa kuti akapite kumwamba?

Tipita Nanu Limodzi

Kodi anthu amene adzadya mkate kapena kumwa vinyo pa Cikumbutso tidzafunika kuwaona bwanji? Kodi tiyenela kuda nkhawa tikaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso cikukwela?