Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 2

Mungathe Kulimbikitsa Ena Kwambili

Mungathe Kulimbikitsa Ena Kwambili

Okhawa ndiwo anchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa.”​—AKOL. 4:11.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi atumiki ambili a Yehova akukumana na masautso otani?

KUZUNGULILA dziko lonse lapansi, atumiki ambili a Yehova akukumana na masautso osiyana-siyana. Akhristu ena akudwala matenda aakulu. Ndipo ena anafedwa munthu amene anali kumukonda. Enanso ali na cisoni cacikulu cifukwa cakuti m’bululu wawo kapena mnzawo wapamtima anasiya coonadi. Palinso ena amene akuvutika cifukwa ca ngozi zacilengedwe. Kodi mu mpingo mwanu muliko abale na alongo amene akukumana na mavuto ngati amenewa? Akhristu onse amenewa amafunikila cilimbikitso. Kodi tingawalimbikitse bwanji?

2. N’cifukwa ciani nthawi zina mtumwi Paulo anali kufunika kulimbikitsidwa?

2 Mobweleza-bweleza, Mtumwi Paulo anakumana na mavuto oika moyo pa ngozi. (2 Akor. 11:23-28) Analinso kuvutika na “munga m’thupi.” Mwina mungawo unali matenda ena ake. (2 Akor. 12:7) Ndipo pa nthawi ina, iye analefulidwa pamene Dema, m’bale amene anali kutumikila naye limodzi anamusiya “cifukwa cokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Paulo anali Mkhristu wodzozedwa wolimba mtima, amene anali kuyesetsa kulimbikitsa ena. Koma nthawi zina, nayenso anali kulefuka na zinthu zina.—Aroma 9:1, 2.

3. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo na kumulimbikitsa?

3 Paulo anathandizidwa na kulimbikitsidwa pa nthawi imene anali kukumana na mavuto. Yehova anamulimbikitsa poseŵenzetsa mzimu wake woyela. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Komanso anamulimbikitsa kupitila mwa Akhristu anzake. Paulo anakamba kuti anchito anzake ena anali ‘kumuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:11) Iye anachulako Akhristu monga Arisitako, Tukiko, na Maliko. Iwo anamulimbikitsa Paulo, ndipo izi zinamuthandiza kupilila. Kodi ni makhalidwe ati amene anathandiza Akhristu atatu amenewo kucita bwino kwambili polimbikitsa ena? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cawo cabwino pamene tilimbikitsa ena?

KHALANI WOKHULUPILIKA MONGA ARISITAKO

Mofanana na Arisitako, tingaonetse kuti ndife bwenzi lokhulupilika mwa kukhala pafupi na abale na alongo athu pa nthawi ya “mavuto”(Onani ndime 4-5) *

4. Kodi Arisitako anaonetsa bwanji kuti anali mnzake wokhulupilika wa Paulo?

4 Arisitako anali Mmakedoniya wa ku Tesalonika. Iye anali mnzake wokhulupilika wa Paulo. Nthawi yoyamba pamene timaŵelenga za Arisitako m’Baibo ni pamene Paulo anapita ku Aefeso pa ulendo wake wacitatu wa umishonale. Pamene anali kuyenda na Paulo, Arisitako anagwidwa na gulu la anthu aciwawa. (Mac. 19:29) Arisitako atamasulidwa, sanamusiye Paulo pofuna kupewa mavuto. Koma anakhalabe wokhulupilika mwa kupitiliza kuyenda naye. Miyezi ingapo pambuyo pake, Paulo ali ku Girisi, Arisitako anapitiliza kukhala naye, olo kuti otsutsa anali kufunabe kumupha Paulo. (Mac. 20:2-4) Ca m’ma 58 C.E. pamene Paulo anatumizidwa ku Roma monga mkaidi, Arisitako anapita naye pa ulendo wautali umenewo. Iwo anavutikila limodzi pamene ngalawa inawaswekela pa ulendowo. (Mac. 27:1, 2, 41) Komanso, zioneka kuti atafika ku Roma, Arisitako anakhalako m’ndende kwa kanthawi na Paulo. (Akol. 4:10) Mpake kuti Paulo analimbikitsidwa kwambili na mnzake wokhulupilika ameneyu.

5. Malinga na Miyambo 17:17, tingaonetse bwanji kuti ndife bwenzi lokhulupilika?

5 Mofanana na Arisitako, tingaonetse kuti ndife bwenzi lokhulupilika mwa kukhala pafupi na abale na alongo athu, osati cabe pa nthawi imene zinthu zili bwino koma ngakhale pa nthawi ya “mavuto.” (Ŵelengani Miyambo 17:17.) Abale na alongo amafunikilabe cilimbikitso cathu ngakhale pambuyo pakuti vuto limene anali kukumana nalo latha. Mwacitsanzo, atate ake a mlongo Frances * atamwalila na khansa, panapita cabe miyezi itatu amayi ake nawonso anamwalila na matenda amenewa. Mlongoyu anati: “Niona kuti mavuto akakhala aakulu, amatisautsa kwa nthawi yaitali. Ndipo nimayamikila kukhala na mabwenzi okhulupilika amene amazindikila kuti nikali na cisoni, olo kuti papita nthawi yaitali kucokela pamene makolo anga anamwalila.”

6. Kodi mabwenzi okhulupilika amacita ciani?

6 Mabwenzi okhulupilika amadzipeleka kuthandiza abale na alongo awo. Mwacitsanzo, m’bale wina dzina lake Peter anam’peza na matenda ena ake oopsa osacilitsika. Mkazi wake, Kathryn anati: “M’bale wina na mkazi wake mu mpingo mwathu ndiwo anatitenga na kupita nafe ku cipatala, kumene anapeza matenda a amuna anga. Atamvela za matendawo, iwo analonjeza kuti sadzatisiya pa nthawi yovuta imeneyi, ndipo akhaladi akutithandiza nthawi zonse pamene tifunika thandizo.” Ndithudi, n’zolimbikitsa ngako kukhala na anzathu a pamtima amene amatithandiza kuti tipilile mayeselo!

KHALANI WODALILIKA MONGA TUKIKO

Mofanana na Tukiko, tiyenela kukhala bwenzi lodalilika pamene ena akukumana na mavuto (Onani ndime 7-9) *

7-8. Malinga na Akolose 4:7-9, kodi Tukiko anaonetsa bwanji kuti anali wodalilika?

7 Tukiko anali Mkhristu wocokela m’cigawo ca Asia ca ufumu wa Roma. Iye anali mnzake wa Paulo wodalilika kwambili. (Mac. 20:4) Ca m’ma 55 C.E., Paulo anapanga makonzedwe osonkhanitsa ndalama zothandizila Akhristu a ku Yudeya. Ndipo zioneka kuti anauza Tukiko kuti athandizile pa nchito imeneyi. (2 Akor. 8:18-20) Ndiyeno, pamene Paulo anaikidwa m’ndende kwa nthawi yoyamba ku Roma, Tukiko ndiye anali kutumikila Paulo monga mthenga wake. Iye anali kupeleka makalata na mauthenga olimbikitsa a Paulo ku mipingo ya ku Asia.—Akol. 4:7-9.

8 Tukiko anakhalabe mnzake wa Paulo wodalilika. (Tito 3:12) Akhristu ambili ku Asia sanali odalilika ngati Tukiko. Ca m’ma 65 C.E., Paulo ataikidwa m’ndende kaciŵili, analemba kuti Akhristu ambili m’cigawo ca Asia anali kupewa kuceza naye, mwina cifukwa coopa anthu otsutsa. (2 Tim. 1:15) Koma Paulo anali kumudalila Tukiko moti anamupatsa nchito ina. (2 Tim. 4:12) Mwacionekele, Paulo anayamikila kukhala na Tukiko, bwenzi lake labwino.

9. Tingatengele bwanji citsanzo ca Tukiko?

9 Tingatengele citsanzo ca Tukiko mwa kukhala bwenzi lodalilika. Sitiyenela kulonjeza cabe kwa abale na alongo athu kuti tidzawathandiza, koma tiyenela kuyesetsa kucitapo kanthu kuti tiwathandize. (Mat. 5:37; Luka 16:10) Akhristu amene akukumana na vuto linalake akaona kuti ndife odalilika, amatonthozedwa kwambili. Mlongo wina anafotokoza cifukwa cake zimakhala conco. Iye anakamba kuti ngati munthu ni wodalilika, “sukhalanso na nkhawa kuti kaya adzacitadi zimene analonjeza kapena ayi. Umadziŵa kuti adzakuthandiza pa nthawi yake.”

10. Malinga na Miyambo 18:24, kodi Akhristu amene akukumana na mavuto kapena zolefula angapeze kuti cilimbikitso?

10 Akhristu amene akukumana na mayeselo kapena zolefula, kaŵili-kaŵili amapeza citonthozo mwa kufotokozelako bwenzi lodalilika mmene akumvelela. (Ŵelengani Miyambo 18:24.) Mwacitsanzo, mwana wake wamwamuna atacotsedwa mu mpingo, m’bale Bijay anati: “N’nali kufuna kufotokozelako munthu winawake wodalilika mmene n’nali kumvelela.” Citsanzo cina ni m’bale Carlos. Iye analandidwa mwayi wa utumiki winawake umene anali kuukonda kwambili cifukwa cakuti analakwitsa zinazake. M’baleyu anati: “N’nali kufuna munthu amene nikanamufotokozela momasuka mmene n’nali kumvelela, komanso amene akanatha kumvetsela mokoma mtima popanda kuniweluza.” M’bale Carlos anaona kuti akulu anali okoma mtima, ndipo anamulimbikitsa. Iye analimbikitsidwanso kudziŵa kuti akulu amacita zinthu mosamala moti sangauzeko ena zimene anawauza.

11. Kodi tingakhale bwanji bwenzi lodalilika?

11 Kuti tikhale bwenzi lodalilika, tifunika kukhala woleza mtima. Mwacitsanzo, pamene mwamuna wa mlongo Zhanna anamuthaŵa, iye anapeza citonthozo mwa kuuzako mabwenzi ake mmene anali kumvelela. Mlongoyu anati: “Iwo anali kunimvetsela moleza mtima, olo zioneka kuti n’nali kuwauza zinthu zimodzi-modzi mobweleza-bweleza.” Na imwe mungakhale bwenzi labwino mwa kumvetsela moleza mtima pamene ena afotokoza mavuto awo.

KHALANI WODZIPELEKA KUTUMIKILA ENA MONGA MALIKO

Zocita za Maliko zoonetsa kukoma mtima zinathandiza Paulo kupilila, ndipo nafenso tingathandize abale athu pamene akumana na matsoka (Onani ndime 12-14) *

12. Kodi Maliko anali ndani? Nanga anaonetsa bwanji mzimu wodzipeleka?

12 Maliko, wochedwanso Yohane, anali Mkhristu waciyuda wocokela ku Yerusalemu. Iye anali msuweni wa Baranaba, amene anali mmishonale wodziŵika kwambili. (Akol. 4:10) Zioneka kuti Maliko anabadwila m’banja lolemela. Olo zinali telo, iye sanaike zinthu zakuthupi patsogolo. Mu umoyo wake wonse, Maliko anaonetsa mzimu wodzipeleka. Anali kukondwela kutumikila ena. Mwacitsanzo, pa nthawi zosiyana-siyana, iye anatumikilako pamodzi na mtumwi Paulo komanso mtumwi Petulo pamene anali kusamalila maudindo awo. Mwina Maliko anali kuwathandiza kusamalila zosoŵa zawo zakuthupi. (Mac. 13:2-5; 1 Pet. 5:13) Paulo anakamba kuti Maliko anali mmodzi wa “anchito [anzake] pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu,” amene ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’—Akol. 4:10, 11.

13. Kodi 2 Timoteyo 4:11 ionetsa bwanji kuti Paulo anayamikila utumiki wa Maliko umene anacita mokhulupilika?

13 Maliko anali mmodzi wa anzake a Paulo apamtima. Mwacitsanzo, ca m’ma 65 C.E, Paulo anaikidwanso m’ndende ku Roma. Iyi inali nthawi yothela kuikidwa m’ndende. Pa nthawiyo, Paulo analemba kalata yake yaciŵili kwa Timoteyo. M’kalatayo, Paulo anapempha Timoteyo kuti popita kwa iye ku Roma, apite na Maliko. (2 Tim. 4:11) Mwacionekele, Paulo anayamikila utumiki umene Maliko anacita mokhulupilika, ndipo n’cifukwa cake anafuna kuti Maliko adzakhale naye pa nthawi yovuta imeneyo ya moyo wake. Maliko anali kuthandiza Paulo m’njila zosiyana-siyana. Mwina anali kumupezela zakudya kapena mipukutu na inki yolembela. N’zodziŵikilatu kuti thandizo na cilimbikitso cimene Paulo analandila pa nthawiyi, zinamuthandiza kupilila m’masiku otsiliza a moyo wake amenewo, atangotsala pang’ono kuphedwa.

14-15. Kodi lemba la Mateyu 7:12 litiphunzitsa ciani pa nkhani yothandiza ena?

14 Ŵelengani Mateyu 7:12. Pamene takumana na mavuto aakulu, timayamikila kwambili ena akamatithandiza m’njila zosiyana-siyana. M’bale wina dzina lake Ryan, amene atate wake anamwalila mwadzidzidzi pa ngozi yoopsa, anati: “Tikakumana na mavuto, zinthu zambili zimene tinali kucita mosavutikila tsiku na tsiku, zimaoneka kukhala zovuta kwambili. Conco, munthu akakuthandiza, olo thandizolo likhale locepa, umalimbikitsidwa kwambili.”

15 Ngati tikhala chelu, tingaone njila zosiyana-siyana zothandizila abale athu amene akukumana na mavuto. Mwacitsanzo, m’bale Peter na mkazi wake Kathryn, amene tawachula poyamba paja, sanali kukwanitsa kuyendetsa motoka kuti apite ku cipatala kukalandila cithandizo. Mlongo wina anapeza njila yowathandizila. Iye anapanga ndandanda yoti abale odzipeleka a mu mpingo mwawo azipita kukawatenga na kuyenda nawo ku cipatala. Kodi njila imeneyi inathandizadi? Inde, moti mlongo Kathryn anati: “Tinamvela monga atitula cikatundu colemela.” Conco, dziŵani kuti ena amalimbikitsidwa kwambili mukawathandiza, ngakhale thandizo lanu litakhala locepa.

16. Kodi citsanzo ca Maliko citiphunzitsa mfundo yofunika iti pa nkhani yolimbikitsa ena?

16 N’zoonekelatu kuti wophunzila wa Yesu Maliko, anali Mkhristu wokhala na zocita zambili. Iye anapatsidwa mautumiki ambili ofunika, kuphatikizapo nchito yolemba Uthenga Wabwino wa Maliko. Olo zinali conco, Maliko anali kuyesetsa kupeza nthawi yolimbikitsa Paulo, ndipo Paulo anali kumasuka kupempha thandizo kwa iye. Mlongo Angela, amene m’bululu wake anaphedwa, anayamikila abale na alongo amene anali kuyesetsa kumulimbikitsa. Iye anati: “Ngati mabwenzi afunadi kukuthandiza, amakhala ofikilika. Amacita kuonekelatu kuti ni ofunitsitsa kukuthandiza ndipo sazengeleza kucita zimenezo.” Motelo tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimadziŵika monga munthu wokonda kulimbikitsa abale na alongo mwa kuwathandiza m’njila zosiyana-siyana?’

MUZIYESETSA KULIMBIKITSA ENA

17. Kodi kusinkha-sinkha mawu a pa 2 Akorinto 1:3, 4 kungatisonkhezele bwanji kulimbikitsa ena?

17 Abale na alongo ofunikila cilimbikitso ni ambili. Ndipo tingawalimbikitse ngakhale na mawu amene ena anakamba potilimbikitsa. Mwacitsanzo, mlongo Nino amene ambuye ake aakazi anamwalila anati: “Yehova angatiseŵenzetse potonthoza ena ngati tamulola kuti atigwilitsile nchito.” (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Mlongo Frances, amene tamuchula poyamba paja anati: “Mawu a pa 2 Akorinto 1:4 ni a zoona. Tingalimbikitse ena na kuwatonthoza mwa kukamba mawu kapena kucita zinthu zimene anzathu anacita potilimbikitsa.”

18. (a) N’cifukwa ciani ena amayopa kulimbikitsa ena? (b) Tingacite ciani kuti tilimbikitse ena mowafika pa mtima? Fotokozani citsanzo.

18 Tifunika kuyesetsa kuthandiza ena ngakhale tikhale na mantha. N’kutheka kuti timayopa kuti tidzakamba ciani kapena tidzacita ciani pothandiza munthu amene akukumana na mavuto. Mkulu wina dzina lake Paul amakumbukila khama limene ena anaonetsa pomutonthoza pamene atate wake anamwalila. Iye anati: “N’nali kuona kuti sicinali copepuka kuti iwo abwele kudzanilimbikitsa. Anali kusoŵa cokamba. Koma n’nayamikila mtima wawo wofuna kunithandiza na kunilimbikitsa.” Nayenso m’bale Tajon, pambuyo pa civomezi camphamvu anati: “Kukamba moona mtima, sinikumbukila mauthenga onse a pa foni amene anthu ananitumila kwa masiku angapo pambuyo pa civomezico. Koma cimene nimakumbukila ni cikondi cimene ananionetsa mwa kunitumila mauthenga kuti adziŵe mmene zinthu zinalili kwa ine.” Conco, kuti titonthoze kapena kulimbikitsa ena mowafika pa mtima, tifunika kucita zinthu zoonetsa kuti timawakonda.

19. N’cifukwa ciani mwatsimikiza mtima ‘kuthandiza na kulimbikitsa’ ena?

19 Pamene tiyandikila mapeto a dziko loipali, zinthu zipitiliza kuipila-ipila ndipo umoyo udzakhala wovuta kwambili. (2 Tim. 3:13) Kuwonjezela apo, ndife opanda ungwilo ndipo nthawi zina timalakwitsa zinthu na kudzibweletsela mavuto. Cotelo, tidzafunikabe citonthozo. Mtumwi Paulo anakwanitsa kupilila mokhulupilika mpaka mapeto a moyo wake. Cimodzi cimene cinamuthandiza kupilila ni cilimbikitso cimene analandila kucokela kwa Akhristu anzake. Conco, tiyeni tikhale okhulupilika ngati Arisitako, odalilika ngati Tukiko, komanso odzipeleka kutumikila ena ngati Maliko. Tikatelo, tidzathandiza abale na alongo athu kukhalabe olimba m’cikhulupililo.—1 Ates. 3:2, 3.

^ ndime 5 Mtumwi Paulo anakumana na mavuto ambili mu umoyo wake. M’nthawi zovuta zimenezo, abale ena anali kumulimbikitsa kwambili. M’nkhani ino, tidzakambilana makhalidwe atatu amene anathandiza abale amenewo kucita bwino kwambili polimbikitsa ena. Tidzakambilananso mmene tingalimbikitsile ena potengela citsanzo cawo.

^ ndime 5 Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Arisitako anavutikila pamodzi na Paulo pamene ngalawa inawaswekela pa ulendo.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Tukiko anapatsidwa utumiki wopeleka makalata a Paulo ku mipingo.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Maliko anathandiza Paulo mwa kumucitila zinthu zosiyana-siyana.