Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

Khalani Osatekeseka Ndipo Dalilani Yehova

Khalani Osatekeseka Ndipo Dalilani Yehova

LEMBA LA CAKA CA 2021:“Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo. ”​—YES. 30:15.

NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Mofanana na Mfumu Davide, kodi ena a ife tingafunse mafunso ati?

TONSEFE, timafuna kukhala na mtendele wa mumtima. Palibe amene amafuna kukhala na nkhawa. Koma nthawi zina nkhawa timakhala nazo. Ndipo atumiki a Yehova ena angafunse mafunso monga amene Mfumu Davide anafunsa Yehova akuti: “Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikila liti? Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi cisoni kufikila liti?”—Sal. 13:2.

2. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Ngakhale kuti n’zosatheka kupewelatu nkhawa, pali zambili zimene tingacite kuti tizicepetse. M’nkhani ino, tiyamba na kuona zina mwa zinthu zimene zingatibweletsele nkhawa. Ndiyeno tikambilane njila 6 zimene zingatithandize kukhala osatekeseka polimbana na mavuto.

KODI N’CIANI CINGATIBWELETSELE NKHAWA?

3. Kodi n’zotani zimene zingatibweletsele nkhawa? Nanga kodi tingaletse zinthu zimenezo?

3 Pali zinthu zambili zimene zingatibweletsele nkhawa. Ndipo nthawi zina, palibe zimene tingacite kuti zimenezo zisacitike. Mwacitsanzo, sitingaletse kuti anthu asakweze mitengo ya zakudya, zovala, kapena ya nyumba za lendi. Komanso, sitingapeweletu kuyesedwa na anzathu a kunchito kapena a kusukulu kuti ticite zinthu zosakhulupilika, kapena za ciwelewele. Ndipo palibe zimene tingacite kuti tiletse anthu kucita zaupandu m’dela lathu. Timakumana na mavuto amenewa cifukwa tikukhala m’dziko limene maganizo a anthu ambili si ogwilizana na mfundo za m’Baibo. Satana, mulungu wa dzikoli, adziŵa kuti anthu ena adzalola “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino” kuwalepheletsa kutumikila Yehova. (Mat. 13:22; 1 Yoh. 5:19) Ndiye cifukwa cake dzikoli ni lodzala na zinthu zobweletsa nkhawa!

4. Kodi n’ciani cingacitike ngati timadela nkhawa kwambili za mavuto athu?

4 Tingakhale na nkhawa kwambili mpaka kulephela kuganizila zinthu zina. Mwacitsanzo, tingade nkhawa kuti sitidzakhala na ndalama zokwanila zogulila zofunikila, kapena kuti tidzalephela kugwila nchito tikadwala, kapena kucotsedwa nchito kumene. Mwina tingakhalenso na nkhawa kuti sitidzakhala okhulupilika tikayesedwa kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Posacedwa, Satana adzapangitsa anthu amene amawalamulila kuukila anthu a Mulungu. Conco, tingakhale na nkhawa kuti tidzacita ciani panthawiyo. Koma mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi n’kulakwa kuda nkhawa pa zinthu zimenezi?’

5. Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati: “Lekani kudela nkhawa?”

5 Tidziŵa kuti Yesu anauza otsatila ake kuti: “Lekani kudela nkhawa.” (Mat. 6:25) Kodi izi zitanthauza kuti iye amatiyembekezela kukhala opanda nkhawa iliyonse? Kutalitali! Ndi iko komwe, atumiki a Yehova ena akale okhulupilika anavutikapo na nkhawa, koma Yehova sanaleke kuwakonda. * (1 Maf. 19:4; Sal. 6:3) Conco, pokamba mawu amenewa, Yesu anali kutilimbikitsa kuti tisamade nkhawa kwambili posakila zofunikila mu umoyo cakuti n’kulephela kutumikila bwino Mulungu. Nanga tingacite ciani kuti ticepetse nkhawa?—Onani bokosi lakuti “ Zimene Mungacite.”

ZINTHU 6 ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUKHALA OSATEKESEKA

Onani ndime 6 *

6. Malinga na Afilipi 4:6, 7, n’ciani cingatithandize kucepetsa nkhawa zathu?

6 (1) Pemphelani nthawi zonse. Akhristu amene ali na nkhawa angapeze thandizo mwa kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima. (1 Pet. 5:7) Yehova poyankha mapemphelo anu, adzakupatsani ‘mtendele wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse’ kwa anthu. (Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.) Yehova amatithandiza kucepetsa nkhawa tikakumana na mavuto, kupitila mwa mzimu wake woyela wamphamvu.—Agal. 5:22.

7. Kodi tiyenela kukumbukila ciani popemphela kwa Mulungu?

7 Pamene mukamba na Yehova m’pemphelo, muuzeni nkhawa zanu zonse. Chulani zinthu mwacindunji. Muuzeni vuto lanu, ndipo m’fotokozeleni mmene mukumvelela. Ngati n’zotheka kuthetsa vutolo, m’pempheni kuti akupatseni nzelu zokuthandizani kudziwa zimene mungacite na kuti akupatseni mphamvu zocitila zimenezo. Ngati palibe zimene mungacite pothetsa vutolo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusadela nkhawa kwambili za vutolo. Ngati muchula mwacindunji mavuto anu m’pemphelo, n’kupita kwa nthawi mudzaona mosavuta mmene Yehova akuyankhila mapemphelo amenewo. Ngati mwakhala mukupemphela ndipo pemphelo lanu silinayankhidwe mwamsanga, musagwe mphwayi. Kuwonjezela pa kuchula zinthu mwacindunji m’pemphelo, Yehova amafunanso kuti muzipemphela mosalekeza.—Luka 11:8-10.

8. Kodi tiyenela kuchula zotani m’mapemphelo athu?

8 Pamene mutulila Yehova nkhawa zanu m’pemphelo, muziphatikizamo mawu oyamikila. Tiyenela kuganizila za madalitso amene tili nawo, ngakhale pamene zinthu n’zovuta kwambili. Ngati nthawi zina mumasowa mawu oyenelela pofotokoza nkhawa zanu, kumbukilani kuti Yehova amayankha mapemphelo ngakhale a mawu ocepa akuti ‘Conde n’thandizeni!’—2 Mbiri 18:31; Aroma 8:26.

Onani ndime 9 *

9. Kodi tingapeze bwanji citetezo ceni-ceni?

9 (2) Dalilani nzelu za Yehova osati zanu. Kalekale, ca m’ma 700 B.C.E.; Ayuda anacita mantha atamva kuti Asuri adzawaukila. Cifukwa ca nkhawa yakuti adzagonjetsedwa na Asuri, iwo anapempha Aiguputo kuti awathandize. (Yes. 30:1, 2) Yehova anawacenjeza kuti kudalila Aiguputo kudzawabweletsela mavuto aakulu. (Yes. 30:7, 12, 13) Kupitila mwa mneneli Yesaya, Yehova anauza anthuwo mmene akanapezela citetezo ceni-ceni. Mneneliyo anati: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo “ mwa Yehova.—Yes. 30:15b.

10. Kodi ni pa zocitika zina ziti pamene tingaonetse kuti timadalila Yehova?

10 Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’dalila Yehova? Ganizilani zitsanzo izi: Tiyelekeze kuti mwapatsidwa mwayi wa nchito ya malipilo ambili imene izikutengeleni nthawi yoculuka komanso kusokoneza pulogilamu yanu yauzimu. Kapena mwina wina ku nchito kwanu amakukopani kuti mukhale naye pa cibwenzi, koma munthuyo si mtumiki wa Mulungu wobatizika. Kapenanso mwina wa m’banja lanu angakuuzeni kuti: “Usankhepo pali ine kapena Mulungu wako.” Pa zocitika zimenezi, cingakhale covuta kupanga cosankha. Koma Yehova adzakupatsani citsogozo cofunikila pa cocitika ciliconse. (Mat. 6:33; 10:37; 1 Akor. 7:39) Ndiye funso n’lakuti, Kodi mudzadaliladi citsogozo cimeneco na kuseŵenzetsa malangizo ake?

Onani ndime 11 *

11. Kodi tingaŵelenge nkhani zotani za m’Baibo kuti tikhale osatekeseka tikamatsutsidwa?

11 (3) Phunzilani pa zitsanzo zabwino komanso zoipa. M’Baibo, muli nkhani zambili zoonetsa kufunika kokhala osatekeseka, komanso kuika cidalilo cathu mwa Yehova. Pamene muŵelenga nkhani zimenezi, muziona zimene zinathandiza atumiki a Mulungu kukhala osatekeseka pamene anali kutsutsidwa kwambili. Mwacitsanzo, khoti lalikulu la Ayuda litagamula kuti atumwi aleke kulalikila, iwo sanacite mantha. M’malomwake, anakamba molimba mtima kuti: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29) Ngakhale pambuyo pokwapulidwa, atumwiwo sanacite mantha. Cifukwa ciani? Cifukwa anadziŵa kuti Yehova anali ku mbali yawo. Iye anali kukondwela nawo. Conco, iwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino. (Mac. 5:40-42) Mofananamo, pamene wophunzila Sitefano anatsala pang’ono kuphedwa, iye anakhalabe na mtendele wa mumtima ndipo “nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.” (Mac. 6:12-15) Cifukwa ciani? Cifukwa anadziŵa kuti anali woyanjidwa na Yehova.

12. Malinga na 1 Petulo 3:14, komanso 4:14, n’ciani cingatipangitse kukhala acimwemwe ngakhale pamene tikuzunzidwa?

12 Atumwiwo, anali na umboni wonse wakuti Yehova anali nawo. Iye anawapatsa mphamvu yocita zozizwitsa. (Mac. 5:12-16; 6:8) Koma umu si mmene zilili kwa ife masiku ano. Ngakhale conco, mwacikondi Yehova kupitila m’Mawu ake amatitsimikizila kuti tikamavutika cifukwa ca cilungamo, iye amakondwela nafe ndipo mzimu wake umakhala pa ife. (Ŵelengani 1 Petulo 3:14; 4:14.) Conco m’malo modela nkhawa kwambili kuti tidzacita ciani tikadzakumana na mazunzo oculuka kutsogolo, tiyenela kusumika maganizo athu pa zimene tingacite palipano kuti tikulitse cidalilo cathu mwa Yehova kuti adzaticilikiza na kutipulumutsa. Monga ophunzila oyambilila anacitila, nafenso tiyenela kudalila lonjezo la Yesu lakuti: “Ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzelu, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.” Yesu anati: ‘Ngati mudzapilila mudzapeza moyo.’ (Luka 21:12-19) Komanso, musaiŵale kuti Yehova amakumbukila zonse zokhudza atumiki ake amene amafa ali okhulupilika kwa iye. Popeza kuti amadziŵa zonse zokhudza iwo, iye adzawaukitsa.

13. Kodi tingapindule bwanji na zitsanzo za amene analephela kukhala osatekeseka na kudalila Yehova?

13 Tingaphunzilenso ku zitsanzo za amene analephela kukhala osatekeseka na kudalila Yehova. Kuphunzila zitsanzo zoticenjeza zimenezo, kungatithandize kupewa kucitanso zolakwa zimene iwo anacita. Mwacitsanzo, kumayambililo kwa ulamulilo wake, Mfumu Asa ya Yuda inadalila Yehova itayang’anizana na gulu lalikulu lankhondo. Ndipo Yehova anadalitsa Mfumuyo kuti ipambane. (2 Mbiri 14:9-12) Patapita nthawi, Mfumu Asa anayang’anizana na gulu lankhondo locepa la Mfumu Basa ya Isiraeli. Koma panthawiyi, iye anapeleka ndalama kwa Asiriya kuti am’thandize pa nkhondoyo, m’malo modalila Yehova kaamba ka cipulumutso, monga anacitila kumbuyoko. (2 Mbiri 16:1-3) Ndipo kumapeto kwa moyo wake, iye atadwala kwambili sanadalile Yehova kuti am’thandize.—2 Mbiri 16:12.

14. Tingaphunzile ciani pa zimene Asa analakwitsa?

14 Poyamba, Asa anayang’ana kwa Yehova atakumana na mavuto. Koma patapita nthawi, analephela kutembenukila kwa Mulungu kaamba ka thandizo, ndipo anasankha kuthetsa yekha mavuto amene anakumana nawo. Poyamba, zimene Asa anasankha kucita popempha thandizo kwa Asiriya kuti agonjetse Aisiraeli zinaoneka ngati zothandiza kwambili. Koma Ayuda sanakhale pamtendele kwa nthawi yaitali. Yehova kupitila kwa mneneli anauza Asa kuti: “Cifukwa cakuti munadalila mfumu ya Siriya, osadalila Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” (2 Mbiri 16:7) Tifunika kusamala kuti tisamadzidalile na kuganiza kuti tingathetse mavuto athu mwa ife tekha popanda kudalila citsogozo ca Yehova kupitila m’Mawu ake. Ngakhale pamene tifunika kupanga cosankha mwamsanga, tiyenela kudekha na kudalila Yehova, ndipo iye adzatithandiza kuti zinthu zitiyendele bwino.

Onani ndime 15 *

15. Kodi tingacite ciani pamene tiŵelenga Baibo?

15 (4) Loŵezani mavesi a m’Baibo pamtima. Mukapeza mavesi a m’Baibo oonetsa kuti timapeza mphamvu mwa kukhala osatekeseka na kudalila Yehova, yesani kuloweza pamtima mavesiwo. Kuti muloweze mavesiwo, zingakhale zothandiza kuwaŵelenga motulutsa mawu kapena kuwalemba pena pake na kumawaŵelenga kaŵili-kaŵili. Yoswa analamulidwa kuŵelenga buku la Cilamulo nthawi zonse na kusinkha-sinkhapo kuti acite zinthu mwanzelu. Zimene anali kuŵelenga m’cilamuloco, zinali kudzam’thandizanso kugonjetsa mantha amene akanakhala nawo potsogolela anthu a Mulungu. (Yos. 1:8, 9) Mavesi ambili opezeka m’Mawu a Mulungu angakupatseni mtendele wamaganizo pa zocitika zimene zingakupangitseni kukhala na nkhawa kapena kucita mantha.—Sal. 27:1-3; Miy. 3:25, 26.

Onani ndime 16 *

16. Kodi Yehova amaseŵenzetsa bwanji mpingo potithandiza kukhala osatekeseka na kum’dalila?

16 (5) Yanjanani na anthu a Mulungu. Yehova amaseŵenzetsa abale na alongo athu potithandiza kukhala osatekeseka na kum’dalila. Ku misonkhano yathu, timapindula na malangizo opelekedwa kupitila m’nkhani zimene zimakambidwa, ndemanga za abale na alongo, komanso mayanjano athu olimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25) Tingalimbikitsidwenso kwambili mwa kuuzako mabwenzi athu odalilika a mu mpingo za nkhawa zathu. “Mawu abwino” ocokela kwa mnzathu angatithandize kucepetsa nkhawa.—Miy. 12:25.

Onani ndime 17 *

17. Malinga na Aheberi 6:19, kodi ciyembekezo cathu ca Ufumu cingatithandize bwanji kukhalabe olimba pa mikhalidwe yovuta?

17 (6) Ciyembekezo canu cikhalebe colimba. Ciyembekezo cathu ca Ufumu “cili ngati nangula wa miyoyo yathu,” ndipo cimatithandiza kukhalabe olimba ngakhale pa mikhalidwe yovuta kapena tikakhala na nkhawa.(Ŵelengani Aheberi 6:19.) Sinkha-sinkhani pa lonjezo la Yehova lakuti kutsogolo maganizo olefula adzathelatu. (Yes. 65:17) Yelekezani kuti muli m’dziko latsopano la mtendele, mmene simudzakhalanso zinthu zobweletsa nkhawa. (Mika. 4:4) Mudzalimbitsanso ciyembekezo canu pamene muuzako ena za ciyembekezo cimeneci. Conco, citani zonse zotheka pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila. Mukatelo, ‘ciyembekezo canu cidzakhala cotsimikizika mpaka mapeto.’—Aheb. 6:11.

18. Kodi tingakumane na mavuto otani kutsogolo? Nanga n’ciani cingadzatithandize pa mavutowo?

18 Pamene mapeto a dongosolo lino akuyandikila, tidzakumana na mavuto ambili amene angatibweletsele nkhawa. Lemba la caka ca 2021 lingatithandize kukhala osatekeseka pamene tikumana na mavuto, osati mwa mphamvu zathu, koma mwa kudalila kwathu Yehova. M’caka cino, tiyeni tionetse mwa zocita zathu kuti timakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.”Yes. 30:15.

NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵila Pathu

^ ndime 5 Lemba la caka ca 2021 ligogomeza kufunika kodalila Yehova pamene tikulimbana na mavuto odetsa nkhawa palipano, komanso kutsogolo. M’nkhani ino, tikambilane njila za mmene tingaseŵenzetsele uphungu wa m’lemba lathu la caka.

^ ndime 5 Abale na alongo ena okhulupilika ali na vuto lokhala na nkhawa kwambili, kapena la kupanikizika maganizo. Vuto limenelo ni matenda aakulu ndipo si ndiyo nkhawa imene Yesu anali kufotokoza.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (1) Pa zocitika zosiyana-siyana patsiku, mlongo akufotokoza nkhawa zake m’pemphelo locokela pansi pamtima.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (2) Panthawi yopumula ku nchito, akuŵelenga Mawu a Mulungu kuti apeze nzelu.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (3) Akusinkha-sinkha pa zitsanzo zabwino na zoipa zopezeka m’Baibo.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (4) Akumatika kapepala ku filiji kolembapo lemba lolimbikitsa limene afuna kuliloŵeza.

^ ndime 71 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (5) Akusangalala kukhala na mnzake pamene ali mu ulaliki.

^ ndime 73 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (6) Akulimbitsa ciyembekezo cake mwa kuganizila za kutsogolo.