Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 3

Khamu Lalikulu la Nkhosa Zina Litamanda Mulungu na Khristu

Khamu Lalikulu la Nkhosa Zina Litamanda Mulungu na Khristu

“Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” —CHIV. 7:10.

NYIMBO 14 Tamandani Mfumu Yatsopano Yodzalamulila Dziko

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi nkhani imene inakambidwa pamsonkhano mu 1935 inam’khudza bwanji mnyamata wina?

MU 1926, mnyamata wina anabatizika ali na zaka 18. Makolo ake anali Ophunzila Baibo, monga mmene Mboni za Yehova zinali kudziŵikila panthawiyo. Iwo anali na ana aamuna atatu komanso aakazi aŵili, amene anawaphunzitsa coonadi kuti azitumikila Yehova Mulungu na kutengela citsanzo ca Yesu Khristu. Monga zinalili kwa Ophunzila Baibo onse panthawiyo, mnyamata wokhulupilika ameneyu anali kudya mkate na kumwa vinyo caka ciliconse pa Mgonelo wa Ambuye. Komabe, ciyembekezo cake ca kutsogolo cinasintha atamvetsela nkhani yosaiŵalika yakuti: “Khamu Lalikulu.” Nkhaniyo inakambidwa mu 1935 na m’bale J. F. Rutherford pa msonkhano mu mzinda wa Washington, D.C., ku America. Kodi ni mfundo ya coonadi iti imene inaunikidwa pa msonkhanowo?

2. Ni mfundo yokondweletsa iti ya coonadi imene inaunikidwa m’nkhani ya M’bale Rutherford?

2 M’nkhani yake, M’bale Rutherford anafotokoza amene amapanga “khamu lalikulu” lochulidwa pa Chivumbulutso 7:9. Kumbuyo konseko, Ophunzila Baibo anali kuganiza kuti khamu lalikulu ni gulu laciŵili limene ni losakhulupilika kwambili. M’bale Rutherford anaseŵenzetsa Malemba pofotokoza kuti a khamu lalikulu sanasankhidwe kukakhala kumwamba, koma ni nkhosa zina * za Khristu zimene zidzapulumuka “cisautso cacikulu” na kukhala padziko lapansi kwamuyaya. (Chiv. 7:14) Yesu analonjeza kuti: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenela kuzibweletsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Anthu amene ali monga nkhosa amenewa, ni Mboni za Yehova zokhulupilika zimene zili na ciyembekezo codzakhala kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansi. (Mat. 25:31-33, 46) Tiyeni tione mmene kuwala kwa coonadi kumeneku kunasinthila miyoyo ya anthu a Yehova ambili, kuphatikizapo m’bale uja wacinyamata.—Sal. 97:11; Miy. 4:18.

KAMVEDWE KATSOPANO KAMENE KANASINTHA MIYOYO YA ANTHU MASAUZANDE

3-4. Pa msonkhano wa mu 1935, kodi anthu masauzande anazindikila ciani ponena za ciyembekezo cawo, ndipo n’cifukwa ciani?

3 Zinali zocititsa cidwi kwambili pa msonkhanowo mkambi atauza omvetsela kuti: “Inu nonse amene muli na ciyembekezo codzakhala na moyo padziko lapansi kwamuyaya, conde imililani!” Malinga na mboni zoona na maso, pa anthu pafupi-fupi 20,000 amene anapezeka pa msonkhanowo, anthu opitilila 10,000 anaimilila. Kenako, M’bale Rutherford anati: “Taonani! Khamu lalikulu!” Pambuyo pake, aliyense m’gululo anafuula mwacimwemwe. Amene anaimilila anazindikila kuti sanasankhidwe kukakhala na moyo kumwamba. Iwo anadziŵa kuti sanadzozedwe na mzimu wa Mulungu. Tsiku lotsatila la msonkhanowo, anthu 840 anabatizika kukhala Mboni zatsopano, ndipo ambili a iwo anali a nkhosa zina.

4 Pambuyo pa nkhaniyo, mnyamata uja amene tam’chula kumayambililo na ena masauzande, moyenela analeka kudya mkate na kumwa vinyo pa Mgonelo wa Ambuye. Ambili anamvela monga mmene m’bale wina wodzicepetsa anakambila kuti: “Pa Cikumbutso ca mu 1935, kanali kothela kwa ine kudya ziphiphilitso. N’nazindikila kuti Yehova kupitila mwa mzimu wake woyela sanacitile umboni mwa ine kukhala na ciyembekezo copita kumwamba. M’malomwake, n’nali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi na kudzathandiza pa nchito yopanga dzikoli kukhala paradaiso.” (Aroma 8:16, 17; 2 Akor. 1:21, 22) Kucokela panthawiyo, a khamu lalikulu akhala akuwonjezeka, ndipo amagwila nchito limodzi na otsalila odzozedwa. *

5. Kodi Yehova amawaona bwanji amene analeka kudya ziphiphilitso za Cikumbutso?

5 Kodi Yehova amawaona bwanji aja amene analeka kudya ziphiphilitso za pa Cikumbutso pambuyo pa caka ca 1935? Nanga bwanji ngati Mboni yobatizika masiku ano, moona mtima imadya mkate na kumwa vinyo pa Mgonelo wa Ambuye koma pambuyo pake n’kuzindikila kuti sanadzozedwedi na mzimu woyela? (1 Akor. 11:28) Ena anali kudya ziphiphilitso cifukwa cosadziŵa bwino ciyembekezo cawo. Koma ngati avomeleza moona mtima kuti analakwa na kuleka kudya, ndipo akupitilizabe kutumikila Yehova mokhulupilika, mosakaikila iye adzawalandila kukhala pakati pa nkhosa zina. Ngakhale kuti iwo sakudya mkate na kumwa vinyo, amapezeka pa Cikumbutso cifukwa amayamikila kwambili zimene Yehova na Yesu awacitila.

CIYEMBEKEZO CAPADELA

6. Kodi Yesu analamula angelo kucita ciani?

6 Popeza kuti cisautso cacikulu cili pafupi kwambili, zingakhale zolimbikitsa kwa ife kukambilana zimene Chivumbulutso caputala 7 imakamba ponena za Akhristu odzozedwa komanso khamu lalikulu la nkhosa zina. Yesu analamula angelo kupitiliza kugwila mphepo zinayi za ciwonongeko. Iwo anauzidwa kuti asatailile mphepozo kuti zisawombe dziko lapansi kufikila Akhristu odzozedwa onse atadindidwa cidindo, kutanthauza kuvomelezedwa komaliza na Yehova. (Chiv. 7:1-4) Abale a Khristu adzakhala mafumu ndi ansembe pamodzi naye kumwamba, monga mphoto ya kukhulupilika kwawo. (Chiv. 20:6) Onse amene amapanga gawo lakumwamba la banja la Mulungu, adzakondwela kwambili kuona odzozedwa a 144,000 akulandila mphoto yawo kumwamba.

A khamu lalikulu aimilila pamaso pa Mwanawankhosa komanso ku mpando wacifumu wa Mulungu waulemelelo, atavala mikanjo yoyela komanso atanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo (Onani ndime 7)

7. Mogwilizana na Chivumbulutso 7:9, 10, kodi Yohane anaona ndani m’masomphenya? Nanga iwo anali kucita ciani? (Onani cithunzi pacikuto)

7 Yohane atafotokoza za mafumu na ansembe 144,000 amenewa, anaona cina cocititsa cidwi, “khamu lalikulu” limene linapulumuka Aramagedo. Mosiyana na gulu loyamba, gulu laciŵili limeneli ni lalikulu ndipo lilibe ciŵelengelo coikika. (Ŵelengani Chivumbulutso 7:9, 10.) Iwo ‘anavala mikanjo yoyela,’ kuonetsa kuti ni ‘opanda banga’ locokela m’dziko la Satana, ndipo akhalabe okhulupilika kwa Mulungu komanso kwa Khristu. (Yak. 1:27) Iwo anali kufuula kuti anapulumutsidwa cifukwa ca zimene Yehova na Yesu, Mwanawankhosa wa Mulungu anawacitila. Cina, iwo ananyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo, kuonetsa kuti mwacimwemwe amavomeleza Yesu kukhala Mfumu yosankhidwa na Yehova.—Yelekezelani na Yohane 12:12, 13.

8. Kodi Chivumbulutso 7:11, 12 itiuza ciani za banja lakumwamba la Yehova?

8 Ŵelengani Chivumbulutso 7:11, 12. Ndiyeno n’ciani cinacitika kumwamba? Yohane anaona kuti banja lonse lakumwamba linakondwela kwambili litaona khamu lalikulu ndipo linatamanda Mulungu. Banja lakumwamba la Yehova lidzakondwela kwambili kuona kukwanilitsidwa kwa masomphenya amenewa a khamu lalikulu akadzatuluka mu cisautso cacikulu ali na moyo.

9. Malinga na Chivumbulutso 7:13-15, kodi a khamu lalikulu amacita ciani palipano?

9 Ŵelengani Chivumbulutso 7:13-15. Yohane analemba kuti khamu lalikulu ‘linacapa mikanjo yawo ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.’ Izi zitanthauza kuti iwo ali na cikumbumtima coyela ndiponso ali na kaimidwe kolungama pamaso pa Yehova. (Yes. 1:18) Iwo ni Akhristu obatizika odzipatulila, amene amakhulupilila kwambili nsembe ya Yesu ndipo ali paubale wabwino na Yehova. (Yoh. 3:36; 1 Pet. 3:21) Conco, iwo ni oyenelela kuimilila pamaso pa mpando wacifumu wa Mulungu, kuti azim’citila “utumiki wopatulika usana ndi usiku” m’bwalo la padziko lapansi la kacisi wauzimu. Ngakhale palipano, iwo amacita mbali yaikulu pa nchito yolalikila za Ufumu na kupanga ophunzila, ndipo amaika cifunilo ca Mulungu patsogolo mu umoyo wawo.—Mat. 6:33; 24:14; 28:19, 20.

A khamu lalikulu la nkhosa zina akutuluka mu cisautso cacikulu mwacimwemwe (Onani ndime 10)

10. Kodi a khamu lalikulu ni otsimikiza za ciani? Nanga akuyembekezela kukwanilitsidwa kwa lonjezo liti?

10 A khamu lalikulu amene adzatuluka m’cisautso cacikulu ni otsimikiza kuti Mulungu adzapitilizabe kuwasamalila, cifukwa “wokhala pampando wacifumuyo adzatambasulila hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.” A nkhosa zina adzaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limene akhala akuliyembekezela lakuti: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chiv. 21:3, 4.

11-12. (a) Malinga na Chivumbulutso 7:16, 17, kodi a khamu lalikulu akuyembekezela madalitso otani? (b) Kodi a nkhosa zina angacite ciani pa Cikumbutso, ndipo n’cifukwa ciani?

11 Ŵelengani Chivumbulutso 7:16, 17. Palipano, ena mwa atumiki a Yehova amavutika na njala cifukwa cosoŵa ndalama kapena cifukwa ca mavuto obwela kaamba ka zipolowe komanso nkhondo. Ena ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. Komabe, a khamu lalikulu amalimbikitsidwa kudziŵa kuti akadzapulumuka ciwonongeko ca dongosolo lino loipa, nthawi zonse adzakhala na cakudya ca mwana alilenji cakuthupi komanso cauzimu. Dongosolo la zinthu la Satana likadzawonongedwa, a khamu lalikulu adzapulumuka “kutentha” kwa mkwiyo wa Yehova kumene kudzafikila mtundu wa anthu. Cisautso cacikulu cikadzatha, Yesu adzatsogolela opulumuka padziko lapansi amenewa “ku akasupe amadzi amoyo [wosatha].” Tangoganizilani: Khamu lalikulu lili na ciyembekezo capadela kwambili. Pa mabiliyoni onse a anthu amene anakhalako, pali kuthekela kuti iwo sadzafa!—Yoh. 11:26.

12 A nkhosa zina ali na ciyembekezo cabwino kwambili ndipo amayamikila Yehova na Yesu! Iwo sanasankhidwe kukakhala na moyo kumwamba, koma si kuti ni otsikilapo kwa Yehova. Odzozedwa na a nkhosa zina, onse amatamanda Mulungu na Khristu. Njila imodzi imene amacitila zimenezi ni mwa kupezeka pa Mgonelo wa Ambuye.

TAMANDANI MULUNGU KOMANSO YESU NA MTIMA WANU WONSE PA CIKUMBUTSO

Mkate na vinyo umene umayendetsedwa pa Cikumbutso umatikumbutsa kuti Yesu anatifela kuti tikapeze moyo (Onani ndime 13-15)

13-14. N’cifukwa ciani aliyense ayenela kupezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu?

13 M’zaka zaposacedwa, pa anthu 1,000 aliwonse amene amapezeka pa Cikumbutso munthu mmodzi cabe ndiye amadya mkate na kumwa vinyo. M’mipingo yambili mulibe aliyense amene amadya ziphiphilitso pa Cikumbutso. Ciŵelengelo coculuka ca amene amapezeka pa Cikumbutso ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi. Nanga n’cifukwa ciani amapezeka pa Mgonelo wa Ambuye? Pa cifukwa cofanana na cimene anthu amapezekela ku cikwati ca mnzawo, nawonso amapezeka ku mwambo umenewu. Iwo amapezekapo cifukwa amafuna kuonetsa cikondi cawo kwa amene akukwatilana na kuwacilikiza. Mofananamo, a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso cifukwa amafuna kuonetsa cikondi cawo na kucilikiza Khristu komanso odzozedwa. Komanso, a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso pofuna kuonetsa ciyamikilo cawo kaamba ka nsembe ya Yesu, imene imazipangitsa kukhala zotheka kwa iwo kudzakhala padziko lapansi kwamuyaya.

14 Cifukwa cina cofunika cimene a nkhosa zina amapezekela pa Cikumbutso ni kumvela lamulo la Yesu. Yesu atakhazikitsa Mgonelo wapadela na atumwi ake okhulupilika, iye anawauza kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (1 Akor. 11:23-26) Conco, iwo adzapitilizabe kupezeka pa Mgonelo wa Ambuye nthawi zonse pamene odzozedwa ali na moyo padziko lapansi. Ndipo a nkhosa zina amaitanila aliyense kuti apezeke nawo pa Cikumbutso.

15. Kodi aliyense wa ife angamutamande bwanji Mulungu na Khristu pa Cikumbutso?

15 Pa Cikumbutso, timakhala na mwayi wotamanda Mulungu na Khristu mwa kuimba nyimbo na kupemphela. Nkhani imene idzakambidwa caka cino ili na mutu wakuti, “Muziyamikila Zimene Mulungu na Khristu Akucitilani!” Nkhaniyi idzakulitsa ciyamikilo cathu pa Yehova na Khristu. Pamene ziphiphilitso zikuyendetsedwa, tidzakumbukila kuti zimaimila thupi la Yesu na magazi ake. Tidzakumbukilanso kuti Yehova analola Mwana wake kudzatifela kuti tikapeze moyo. (Mat. 20:28) Aliyense amene amakonda Atate wathu wa kumwamba na Mwana wake adzakhala wofunitsitsa kupezeka pa Cikumbutso.

YAMIKILANI YEHOVA PA CIYEMBEKEZO CIMENE WAKUPATSANI

16. Kodi odzozedwa komanso a nkhosa zina amafanana motani?

16 Mwa njila ina, odzozedwa na a nkhosa zina ni ofanana. Magulu onse aŵili ni ofunika kwambili kwa Mulungu. Malipilo amene iye anapeleka pogula odzozedwa na a nkhosa zina anali ofanana. Inde! Moyo wa Mwana wake wokondeka. Kusiyana kumene kulipo pakati pa magulu aŵili amenewa n’kwakuti ali na ziyembekezo zosiyana. Koma magulu onse aŵili afunika kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu na Khristu. (Sal. 31:23) Ndipo kumbukilani kuti mzimu wa Mulungu ungagwile nchito mofanana pa aliyense wa ife. Izi zitanthauza kuti Yehova angapeleke mzimu wake woyela kwa munthu aliyense payekha malinga na zofunikila zake.

17. Kodi otsalila odzozedwa amayembekezela ciani mwacidwi?

17 Akhristu odzozedwa sabadwa na ciyembekezo copita kumwamba. Mulungu ndiye amaika ciyembekezo cimeneci m’mitima yawo. Iwo amaganizila za ciyembekezo cawo, amapemphelelapo, komanso amakhala ofunitsitsa kukalandila mphoto yawo kumwamba. Iwo sadziŵa mmene matupi awo auzimu adzakhalila kumwamba. (Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Ngakhale n’telo, iwo amayembekezela mwacidwi kukakumana na Yehova, Yesu, angelo, komanso odzozedwa ena onse. Ndipo amalakalaka kukakhala pakati pawo mu Ufumu wakumwamba.

18. N’ciani cimene a nkhosa zina amayembekezela mwacidwi?

18 A nkhosa zina amayembekezela mwacidwi kudzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi. Ici n’ciyembekezo cimene cimabwela mwacibadwa kwa anthu. (Mlal. 3:11) Iwo amayembekezela mwacidwi nthawi imene adzathandiza pa nchito yopanga dziko lonse kukhala paradaiso. Amayembekezela nthawi imene adzamanga nyumba zawo, kulima minda zawo, na kulela ana awo ali na thanzi langwilo. (Yes. 65:21-23) Amayembekezelanso mwacidwi kudzaona zinthu zambili za padziko lapansi—mapili, nkhalango, nyanja na kuphunzila zonse zimene Yehova analenga. Ndipo koposa zonse, iwo amakondwela kudziŵa kuti ubwenzi wawo na Yehova udzalimbilako-limbilako.

19. Kodi Cikumbutso cimapeleka mwayi wotani kwa aliyense wa ife? Nanga caka cino Cikumbutso cidzacitika liti?

19 Yehova anapatsa mtumiki wake aliyense wodzipatulila ciyembekezo cabwino kwambili ca kutsogolo. (Yer. 29:11) Cikumbutso ca imfa ya Khristu cimapatsa aliyense wa ife mwayi waukulu wotamanda Mulungu na Khristu, pa zimene aticitila kuti tikasangalale na moyo wosatha. Mosakaikila, Cikumbutso ni msonkhano wofunika koposa kwa Akhristu oona. Caka cino, Cikumbutso cidzacitika pa Ciŵelu, pa March 27, 2021 dzuŵa litaloŵa. Caka cino, ambili adzakwanitsa kupezeka pa cocitika cofunika kwambili cimeneci mwamtendele. Ena adzapezekapo ngakhale kuti amatsutsidwa. Ndiponso ena, adzacitila mwambo umenewu m’ndende. Pamene Yehova, Yesu, komanso gawo lakumwamba la banja la Mulungu likuyang’ana, lekani kuti mpingo uliwonse, gulu lililonse, komanso wina aliyense akacite bwino mwambo wa Cikumbutso!

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

^ ndime 5 Kwa Mboni za Yehova, tsiku la March 27, 2021, lidzakhala lapadela kwambili. Patsiku limeneli m’madzulo, tidzapezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Unyinji wa amene adzapezeke pa mwambo umenewu, ni a gulu limene Yesu analichula kuti “nkhosa zina.” Kodi ni coonadi cokondweletsa citi cimene cinaunikidwa ponena za gulu limeneli mu 1935? Kodi a nkhosa zina amayembekezela ciani mwacidwi pambuyo pa cisautso cacikulu? Komanso monga openyelela pa Cikumbutso, kodi a nkhosa zina angatamande bwanji Mulungu na Khristu?

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: A nkhosa zina ni aja amene akhala akusonkhanitsidwa m’masiku otsiliza. Iwo amatsatila Khristu, ndipo ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi. Khamu lalikulu ni a nkhosa zina amene adzakhala moyo pamene Khristu adzaweluza mtundu wa anthu pa cisautso cacikulu, ndipo adzapulumuka cisautsoco.

^ ndime 4 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mawu akuti ‘otsalila’ atanthauza Akhristu odzozedwa amene akali na moyo padziko lapansi, ndipo amadya mkate na kumwa vinyo pa Mgonelo wa Ambuye.