Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 2

Zimene Tingaphunzile Kwa “Wophunzila Amene Yesu Anali Kumukonda Kwambili”

Zimene Tingaphunzile Kwa “Wophunzila Amene Yesu Anali Kumukonda Kwambili”

“Tiyeni tipitilize kukondana, cifukwa cikondi cimacokela kwa Mulungu.”—1 YOH. 4:7.

NYIMBO 105 “Mulungu Ndiye Cikondi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi cikondi ca Mulungu cimakupangitsani kumvela bwanji?

MTUMWI Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mawu ocepa amenewa, amatikumbutsa mfundo ya coonadi yofunika kwambili yakuti Mulungu ni Gwelo la moyo komanso Gwelo la cikondi. Yehova amatikonda! Cikondi cimatipangitsa kudzimva otetezeka, acimwemwe, komanso okhutila.

2. Kodi pa Mateyu 22:37-40, pali malamulo aŵili ati aakulu koposa? Nanga n’cifukwa ciani cingakhale covuta kumvela lamulo laciŵili?

2 Kwa Akhristu, kuonetsa cikondi ni lamulo. (Ŵelengani Mateyu 22:37-40.) Tikam’dziŵa bwino Yehova, cingakhale cosavuta kumvela lamulo loyamba. Zili conco cifukwa Yehova ni wangwilo, amasamala za ife komanso amacita nafe zinthu mokoma mtima. Koma mwina zingakhale zovuta kwa ife kumvela lamulo laciŵili. Cifukwa ciani? Cifukwa abale na alongo athu ni opanda ungwilo. Ndipo nthawi zina angakambe kapena kucita zinthu zoonetsa kuti satiganizila komanso satikonda. Yehova anadziŵa kuti zidzakhala zovuta kwa ife kumvela lamulo laciŵili limeneli. Ndiye cifukwa cake anauzila olemba Baibo ena kupeleka uphungu womveka bwino za cifukwa cake tiyenela kuonetsana cikondi na mmene tingacitile zimenezi. Mmodzi mwa olemba amenewo anali Yohane.—1 Yoh. 3:11, 12.

3. Kodi Yohane anagogomeza za ciani?

3 M’zimene Yohane analemba, anagogomeza kuti Akhristu afunika kuonetsa cikondi. Ndipo polemba za umoyo wa Yesu, Yohane anakamba kwambili za cikondi kuposa zimene Mateyu, Maliko, na Luka analemba. Yohane anali na zaka pafupi-fupi 100 pamene analemba uthenga wake wabwino komanso makalata ake atatu. Mabuku ouzilidwa amenewa aonetsa kuti Akhristu ayenela kucita zinthu zonse mosonkhezeledwa na cikondi. (1 Yoh. 4:10, 11) Komabe, panapita nthawi kuti Yohane aphunzile mfundo imeneyi.

4. Kodi Yohane anali kuonetsa ena cikondi nthawi zonse?

4 Pamene Yohane anali mnyamata, nthawi zina sanali kuonetsa cikondi. Mwacitsanzo, panthawi ina Yesu na ophunzila ake anali kupita ku Yerusalemu ndipo anapitila ku Samariya. Anthu a m’mudzi wina wa ku Samariya, anakana kuwalandila. Kodi Yohane anacita ciani? Iye anapempha Yesu kuti aitane moto kucokela kumwamba na kunyeketsa anthu onse m’mudzi umenewo! (Luka 9:52-56) Panthawi inanso, Yohane analephela kuonetsa cikondi kwa atumwi anzake. Zioneka kuti iye na m’bale wake Yakobo anauza amayi awo kuti apemphe Yesu kuti akawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. Atumwi ena atadziŵa zimene Yakobo na Yohane anacita, anakwiya kwambili! (Mat. 20:20, 21, 24) Ngakhale kuti Yohane analakwitsa zinthu zonsezi, Yesu anali kum’kondabe.—Yoh. 21:7.

5. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

5 M’nkhani ino, tikambilana citsanzo ca Yohane na zinthu zina zimene iye analemba ponena za cikondi. Tiphunzila mmene tingaonetsele cikondi kwa abale na alongo athu. Tiphunzilanso njila yofunika kwambili imene mutu wa banja ungaonetsele kuti umakonda banja lake.

CIKONDI CIMAONEKELA M’ZOCITA

Yehova anaonetsa cikondi cake pa ife mwa kutumiza Mwana wake pa dziko lapansi kudzatifela (Onani ndime 6-7)

6. Kodi Yehova waonetsa bwanji cikondi cake pa ife?

6 Kambili timaganiza kuti cikondi cimatanthauza mmene timamvelela wina akatiuza mawu okoma mtima. Koma cikondi ceni-ceni, cimafunika kuonekelanso m’zocita. (Yelekezelani na Yakobo 2:17, 26) Mwacitsanzo, Yehova amatikonda. (1 Yoh. 4:19) Iye amaonetsa kuti amatikonda kupitila m’mawu abwino opezeka m’Baibo. (Sal. 25:10; Aroma 8:38, 39) Komabe, tidziŵa kuti Mulungu amatikonda, osati cabe cifukwa ca zimene amatiuza, koma kupitilanso m’zocita zake. Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Yehova analola kuti Mwana wake avutike na kutifela. (Yoh. 3:16) Kodi tingakaikile zakuti Yehova amatikonda kwambili?

7. Kodi Yesu anacita ciani poonetsa cikondi cake pa ife?

7 Yesu anatsimikizila ophunzila ake kuti anali kuwakonda kwambili. (Yoh. 13:1; 15:15) Iye anaonetsa ukulu wa cikondi cake pa iwo komanso pa ife osati cabe m’zimene anakamba koma kupitilanso m’zimene anacita. Iye anati: “Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Tikaganizila zimene Yehova na Yesu aticitila, kodi ziyenela kutilimbikitsa kucita ciani?

8. Kodi 1 Yohane 3:18 imakamba kuti tiyenela kucita ciani?

8 Timaonetsa kuti timakonda Yehova na Yesu mwa kuwamvela. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 5:3) Ndipo Yesu anatilamula kuti tizikondana. (Yoh. 13:34, 35) Sitiyenela kuonetsa cabe cikondi kwa abale na alongo athu m’mawu koma tiyenelanso kuonetsa kuti timawakonda mwa zocita zathu. (Ŵelengani 1 Yohane 3:18.) Kodi tingacite ciani poonetsa kuti timawakonda?

MUZIKONDA ABALE NA ALONGO ANU

9. Kodi cikondi cinalimbikitsa Yohane kucita ciani?

9 Yohane akanafuna, akanakhalabe na atate ake n’kumapanga ndalama pa nchito ya banja yopha nsomba. M’malomwake, anaseŵenzetsa moyo wake wautali pothandiza ena kuphunzila coonadi conena za Yehova na Yesu. Umoyo umene Yohane anasankha sunali wopepuka. Iye anazunzidwa ndipo ca mu 96 C.E., anathamangitsidwila kudela lina apo ali wokalamba. (Mac. 3:1; 4:1-3; 5:18; Chiv. 1:9) Ngakhale pamene anali m’ndende kaamba kolalikila za Yesu, Yohane anaonetsa kuti anali kukonda ena. Mwacitsanzo, pamene anali pa cisumbu ca Patimo, iye analemba masomphenya amene analandila na kuwatumiza ku mipingo kuti adziŵe “zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chiv. 1:1) Ndipo zioneka kuti pambuyo potulutsidwa m’ndende pa cisumbu ca Patimo, Yohane analemba uthenga wake wabwino wokamba za umoyo na utumiki wa Yesu. Iye analembanso makalata atatu kuti alimbikitse abale na alongo ake. Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yohane ca kukhala na umoyo wodzimana?

10. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumakonda anthu?

10 Mungaonetse kuti mumakonda anthu mwa zimene musankha kucita na moyo wanu. Dziko la Satana limafuna kuti muthele nthawi yanu yonse na mphamvu zanu pofuna kudzipindulitsa nokha, mwa kufuna-funa ndalama komanso kuyesa kudzipangila dzina. Koma alengezi a Ufumu odzimana padziko lonse lapansi amathela nthawi yawo yoculuka pa kulalikila za uthenga wabwino, na kuthandiza anthu kuyandikila Yehova. Ena asankha ngakhale kucita utumiki wanthawi zonse kuti azilalikila na kuphunzitsa.

Timaonetsa cikondi cathu mwa zimene timacitila abale na alongo athu, komanso banja lathu (Onani ndime 11, 17) *

11. Kodi ofalitsa okhulupilika ambili amaonetsa bwanji kuti amakonda Yehova, komanso abale na alongo awo?

11 Akhristu ambili okhulupilika amagwila nchito nthawi zonse kuti azidzisamalila na kusamalila mabanja awo. Ngakhale n’telo, ofalitsa okhulupilika amenewa, amacilikiza gulu la Mulungu mulimonse mmene angathele. Mwacitsanzo, ena amagwila nchito yopeleka thandizo pakacitika matsoka. Ena amagwila nchito zomanga za gulu, ndipo aliyense ali na mwayi wocita zopeleka zothandiza panchito yapadziko lonse. Amacita zimenezi cifukwa cokonda Mulungu na anthu anzawo. Wiki iliyonse timaonetsa kuti timakonda abale na alongo athu, mwa kupezeka pamisonkhano ya mpingo na kutengako mbali. Ngakhale kuti ndife olema, timapitabe ku misonkhano imeneyi. Ngakhale kuti mwina tingacite mantha, timapelekapo ndemanga. Ngakhale kuti aliyense wa ife ali na mavuto ake, timalimbikitsa ena misonkhano isanayambe kapena pambuyo pake. (Aheb. 10:24, 25) Timayamikila cotani nanga nchito imene ofalitsa anzathu amenewa amagwila!

12. Kodi Yohane anaonetsanso m’njila iti kuti anali kukonda abale na alongo ake?

12 Yohane anaonetsa cikondi cake pa abale na alongo ake, osati cabe mwa kuwayamikila, koma mwa kuwapatsanso uphungu. Mwacitsanzo, m’makalata ake Yohane anayamikila abale na alongo ake cifukwa ca cikhulupililo cawo na nchito zawo zabwino. Koma anawapatsanso uphungu wosapita mbali ponena za macimo. (1 Yoh. 1:8–2:1, 13, 14) Mofananamo, tiyenela kuyamikila abale na alongo athu pa zabwino zimene amacita. Koma ngati wina wayamba kuganiza molakwika kapena wayamba khalidwe loipa, tingamuonetse cikondi mwa kum’thandiza mokoma mtima kuti awongolele. Zimafuna kulimba mtima kupeleka uphungu kwa mnzathu. Koma Baibo imakamba kuti mabwenzi azoona amanolana, kapena kuwongolelana wina na mnzake.—Miy. 27:17.

13. Kodi tiyenela kupewa kucita ciani?

13 Nthawi zina, timaonetsa cikondi cathu pa abale na alongo athu mwa zimene timapewa kucita. Mwacitsanzo, timapewa kukwiya msanga na zimene angakambe. Ganizilani zimene zinacitika cakumapeto kwa umoyo wa Yesu padziko lapansi. Yesu anauza ophunzila ake kuti ngati afuna kukapeza moyo, anayenela kudya mnofu wake na kumwa magazi ake. (Yoh. 6:53-57) Zimene iye anakamba zinali zodabwitsa kwambili, cakuti ophunzila ake ambili anamusiya—koma osati mabwenzi ake eni-eni, kuphatikizapo Yohane. Iwo anamamatila kwa iye mokhulupilika. Sanamvetse zimene Yesu anakamba, ndipo n’kutheka kuti nawonso anali odabwa. Komabe, mabwenzi okhulupilika a Yesu sanaganize kuti zimene anakamba zinali zolakwika na kukhumudwa nazo. M’malomwake, anamukhulupilila, podziŵa kuti amakamba zoona. (Yoh. 6:60, 66-69) Conco, m’pofunika kwambili kupewa kukhumudwa msanga na zimene anzathu angakambe. Koma timawalola kufotokoza zimene akutanthauza.—Miy. 18:13; Mlal. 7:9.

14. N’cifukwa ciani sitiyenela kulola cidani kukula mu mtima mwathu?

14 Yohane anatilimbikitsanso kupewa kuzonda abale kapena alongo athu. Ngati tilephela kumvela uphungu umenewu, Satana angamatiseŵenzetse. (1 Yoh. 2:11; 3:15) Izi n’zimene zinacitika cakumapeto kwa nthawi ya Akhristu oyambilila. Satana anali kucita zonse zotheka kulimbikitsa cidani na magaŵano pakati pa anthu a Mulungu. Panthawi imene Yohane analemba makalata ake, anthu amene anali kuonetsa mzimu monga wa Satana anali ataloŵa mu mpingo. Mwacitsanzo, Diotirefe anayambitsa magaŵano aakulu mu mpingo wina. (3 Yoh. 9, 10) Iye sanali kulemekeza akulu oyendela, oimila bungwe lolamulila. Iye anafika ngakhale pocotsa ena mu mpingo amene anali kuceleza anthu amene iye sanali kuwakonda. Ati kudzikuza kwake ati! Ngakhale masiku ano, Satana akali kuyesa-yesabe kugaŵanitsa na kugonjetsa anthu a Mulungu. Conco, tisalole cidani kutigaŵanitsa.

KONDANI BANJA LANU

Yesu anapeleka udindo kwa Yohane wosamalila amayi ake mwakuthupi komanso mwauzimu. Nayonso mitu ya mabanja masiku ano ifunika kusamalila zofunikila za mabanja awo (Onani ndime 15-16)

15. Kodi mutu wa banja uyenela kukumbukila ciani?

15 Imodzi mwa njila yofunika imene mutu wa banja ungaonetsele kuti umakonda banja lake, ni mwa kulipezela zofunikila zakuthupi. (1 Tim. 5:8) Komabe, ayenela kukumbukila kuti zinthu zakuthupi sizingakhutilitse banja lake kuuzimu. (Mat. 5:3) Onani citsanzo cimene Yesu anapeleka ku mitu ya mabanja. Malinga na buku la uthenga wabwino la Yohane, ngakhale pamene Yesu anali kufa pamtengo wozunzikilapo anali kuganizilabe za banja lake. Yohane anaimilila capafupi na mayi ake a Yesu, Mariya, pamalo amene Yesu anali kuphedwela. Ngakhale kuti anali kumva ululu kwambili, Yesu anakonza zakuti Yohane azisamalila Mariya. (Yoh. 19:26, 27) Yesu anali na azing’ono ake amene akanasamalila Mariya mwakuthupi. Koma zioneka kuti panthawiyo, panalibe aliyense amene anakhala wophunzila wake. Conco Yesu anafuna kutsimikiza kuti Mariya adzasamalidwa mwakuthupi komanso mwauzimu.

16. Kodi Yohane anali na maudindo otani?

16 Yohane anali na maudindo ambili. Monga mmodzi wa atumwi, anali kutsogolela nchito yolalikila. Iye ayenelanso kuti anali wokwatila. Conco, anafunika kugaŵa bwino nthawi kuti asamalile banja lake mwakuthupi komanso mwauzimu. (1 Akor. 9:5) Kodi mitu ya mabanja masiku ano ingaphunzilepo ciani pamenepa?

17. N’cifukwa ciani m’pofunika kuti mutu wa banja uzisamalila zofunikila zauzimu za banja lake?

17 M’bale amene ni mutu wa banja mwina angakhale na maudindo ambili ofunika. Mwacitsanzo, angafunike kugwila nchito yake yakuthupi molimbika kuti khalidwe lake licititse kuti Yehova alemekezeke. (Aef. 6:5, 6; Tito 2:9, 10) Ndipo mwina angakhale na nchito zina mu mpingo, monga kucita ubusa na kutsogolela pa nchito yolalikila. Panthawi imodzi-modzi, m’pofunika kwambili kuti aziphunzila Baibo na mkazi wake komanso ana ake nthawi zonse. Iwo adzayamikila kwambili zoyesa-yesa zake powathandiza kukhala athanzi kuthupi, acimwemwe, komanso olimba kuuzimu.—Aef. 5:28, 29; 6:4.

‘KHALANIBE M’CIKONDI CANGA’

18. Kodi Yohane anali wotsimikiza za ciani?

18 Yohane anakhala moyo wautali komanso wokhala na zocitika zambili zokondweletsa. Iye anakumana na mavuto ambili amene akanafooketsa cikhulupililo cake. Koma nthawi zonse anali kuyesetsa kusunga malamulo a Yesu, kuphatikizapo lamulo la kukonda abale na alongo ake. Cotulukapo cake n’cakuti, Yohane anali wotsimikiza kuti Yehova na Yesu anali kum’konda, na kuti adzam’patsa mphamvu zom’thandiza kupilila vuto lililonse. (Yoh. 14:15-17; 15:10; 1 Yoh. 4:16) Palibe ciliconse cimene Satana na dongosolo lake anacita, cimene cinalepheletsa Yohane kuonetsa cikondi kwa abale na alongo ake mwa zokamba na zocita zake.

19. Kodi 1 Yohane 4:7 itilimbikitsa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

19 Mofanana na Yohane, tikukhala m’dziko lolamulidwa na Satana, amene ni Mulungu wa dongosolo lino wopanda cikondi. (1 Yoh. 3:1, 10) Ngakhale kuti iye amafuna kuti tileke kukonda abale na alongo athu, sangatilepheletse kucita zimenezo kokha ngati tamulola ndife. Tiyeni titsimikize mtima kukonda abale na alongo athu mwa kuwaonetsa cikondico mwa zokamba na zocita zathu. Ndipo tikatelo, tidzakondwela kukhala m’banja la Yehova na kukhala na umoyo wopindulitsa kwambili.—Ŵelengani 1 Yohane 4:7.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

^ ndime 5 Zioneka kuti mtumwi Yohane ndiye “wophunzila amene Yesu anali kumukonda kwambili.” (Yoh. 21:7) Conco, ngakhale kuti anali mnyamata, ayenela kuti anali na makhalidwe ambili abwino. Patapita zaka, Yehova anamuseŵenzetsa kulemba zambili ponena za khalidwe la cikondi. M’nkhani ino, tione zina mwa zimene Yohane analemba, ndipo tikambilane zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mutu wa banja amene ali na zocita zambili, atengako mbali pa nchito yothandiza pakagwa tsoka, acilikiza nchito ya padziko lonse mwa zopeleka zake, komanso waitanila ena kuti akhale nawo pa kulambila kwa pabanja pamodzi na mkazi wake na ana ake.