NKHANI YOPHUNZILA 4
Cifukwa Cake Timapezeka pa Cikumbutso
“Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—LUKA 22:19.
NYIMBO 20 Munapeleka Mwana Wanu Wokondeka
ZIMENE TIKAMBILANE *
1-2. (a) Ni liti maka-maka pamene timaganizila kwambili wokondedwa wathu amene anamwalila? (b) Kodi Yesu anayambitsa ciani usiku wakuti aphedwa maŵa?
KAYA papita zaka zambili motani kucokela pamene okondedwa athu anamwalila, timawakumbukilabe. Timawaganizila kwambili maka-maka likafika tsiku limene anamwalila.
2 Caka ciliconse, timakhala pakati pa anthu ofika m’mamiliyoni, amene amasonkhana pa tsiku lokumbukila imfa ya wina wake amene tima’konda kwambili—Yesu Khristu. (1 Pet. 1:8) Timasonkhana kuti tikumbukile uyo amene anapeleka moyo wake dipo, kuti atipulumutse ku ucimo na imfa. (Mat. 20:28) Ndipo Yesu anafuna kuti otsatila ake azikumbukila imfa yake. Usiku wakuti maŵa aphedwa, iye anayambitsa mgonelo wapadela, na kulamula kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—Luka 22:19.
3. Tikambilane ciani m’nkhani ino?
3 Pa anthu onse opezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Khristu, ni ocepa ali na ciyembekezo cakumwamba. Koma ambili ali na ciyembekezo ca padziko lapansi. M’nkhani ino, tikambilane zifukwa zimene magulu onse aŵili amayembekezela mwacidwi kupezeka pa Cikumbutso. Tikambilanenso mmene timapindulila tikapezekapo. Tiyeni tiyambe mwa kukambilana zifukwa zimene odzozedwa amapezekela pa Cikumbutso.
CIFUKWA CAKE ODZOZEDWA AMAPEZEKA PA CIKUMBUTSO
4. N’cifukwa ciani odzozedwa amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso?
4 Caka ciliconse, odzozedwa amayembekezela mwacidwi * (Luka 22:19, 20, 28-30) Mapangano amenewa anatsegula njila kuti atumwiwo komanso anthu ena oŵelengeka akakhale mafumu ndiponso ansembe kumwamba. (Chiv. 5:10; 14:1) Otsalila odzozedwa okha, * amene ali m’mapangano aŵiliwa, ndiwo amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso.
kukapezeka pa Cikumbutso monga akudya. N’cifukwa ciani iwo ni oyenelela kudya mkate na kumwa vinyo? Kuti tiyankhe funsoli, ganizilani zinacitika usiku wakuti Yesu aphedwa maŵa. Pambuyo pa cakudya ca Pasika, Yesu anayambitsa mwambo umene umadziŵika kuti Mgonelo wa Ambuye. Iye anapatsa atumwi ake 11 okhulupilika mkate na vinyo, na kuwauza kuti adye komanso kumwa. Yesu anawauza za mapangano aŵili—pangano latsopano komanso pangano la Ufumu.5. Kodi odzozedwa amadziŵa ciani ponena za ciyembekezo cimene apatsidwa?
5 Cifukwa cina cimene odzozedwa amapezekela pa Cikumbutso n’cakuti: Amakhala na mwayi wosinkha-sinkha za ciyembekezo cawo. Yehova waapatsa ciyembekezo cabwino ngako—moyo wosafa komanso wosawonongeka kumwamba. Iwo adzalamulila pamodzi na Yesu Khristu waulemelelo, komanso odzozedwa onse a 144,000. Ndipo koposa zonse, iwo adzaima pamaso pa Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:51-53; 1 Yoh. 3:2) Odzozedwa amadziŵa kuti anapatsidwa mwayi wa mautumiki amenewa kumwamba. Koma kuti akatengedwe kupita kumwamba, iwo ayenela kukhalabe okhulupilika mpaka imfa. (2 Tim. 4:7, 8) Odzozedwa amakhala na cimwemwe cacikulu akamasinkha-sinkha za ciyembekezo cawo cakumwamba. (Tito 2:13) Nanga bwanji a “nkhosa zina”? (Yoh. 10:16) Kodi pali zifukwa zotani zimene iwo amapezekela pa Cikumbutso?
CIFUKWA CAKE A NKHOSA ZINA AMAPEZEKA PA CIKUMBUTSO
6. N’cifukwa ciani a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso caka ciliconse?
6 A nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso, osati monga akudya, koma monga openyelela. Mu 1938, anthu okhala na ciyembekezo ca padziko lapansi anapemphedwa kukapezeka pa Cikumbutso kwa nthawi yoyamba. Nsanja ya Mlonda ya March 1, 1938, inati: “M’poyenelela kwambili kuti [a nkhosa zina] azipezeka pa msonkhano umenewu, na kupenyenela zimene zikucitika. . . . Imakhala nthawi yakuti naonso asangalale.” Monga mmene alendo oitanidwa amakondwela kupenyelela mwambo womangitsa cikwati, a nkhosa zina naonso amakondwela kupezeka pa Cikumbutso monga oponyelela.
7. N’cifukwa ciani a nkhosa zina amayembekezela mwacidwi kumvetsela nkhani ya Cikumbutso?
7 Naonso a nkhosa zina amasinkha-sinkha za ciyembekezo cawo. Iwo amayembekezela mwacidwi nkhani ya Cikumbutso, imene imasumika kwambili pa zimene Khristu na olamulila anzake a 144,000 adzacitile mtundu wa anthu okhulupilikila mu ulamulilo wa zaka Cikwi. Motsogoleledwa na Mfumu yawo Yesu Khristu, olamulila akumwamba amenewo adzathandiza posandutsa dziko lapansi kukhala paladaiso, komanso kuthandiza anthu omvela kukhala angwilo. Awo amene amapezeka pa Cikumbutso monga openyelela cabe, amalimbikitsidwa kwambili akaganizila mmene malonjezo a m’Baibo Yesaya 35:5, 6; 65:21-23, komanso pa Chivumbulutso 21:3, 4. Akamayelekezela kuti iwo ali na okondedwa awo m’dziko latsopano, ciyembekezo cawo ca zakutsogolo cimalimbilako, ndipo amakhala ofunitsitsa kupitiliza kutumikila Yehova.—Mat. 24:13; Agal. 6:9.
adzakwanilitsidwila, monga lonjezo la pa8. Kodi n’cifukwa cina citi cimene a nkhosa zina amapezekela pa Cikumbutso?
8 Naci cifukwa cina cimene a nkhosa zina amapezekela pa Cikumbutso. Iwo amafuna kuonetsa cikondi odzozedwa na kuwacilicikiza. Mawu a Mulungu anakambilatu kuti padzakhala mgwilizano wolimba pakati pa odzozedwa komanso aja ali na ciyembekezo ca padziko lapansi. Motani? Tiyeni tioneko zitsanzo zocepa.
9. Kodi ulosi wa pa Zekariya 8:23, umaonetsa bwanji mmene a nkhosa zina amamvelela ponena za odzozedwa?
9 Ŵelengani Zekariya 8:23. Ulosi umenewu umafotokoza momveka bwino mmene a nkhosa zina amamvelela ponena za abale na alongo awo odzozedwa. Mawu akuti “Myuda” komanso “anthu inu” amaimila gulu limodzi-modzi la anthu, limene ni otsalila odzozedwa. (Aroma 2:28, 29) “Amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina,” amaimila a nkhosa zina. Iwo ‘amagwila [mwamphamvu]’ odzozedwa—kutanthauza kuwamamatila mokhulupilika, na kugwilizana nawo pa kulambila koyela. Conco, a nkhosa zina akapezeka pa Cikumbutso, amaonetsa kuti ni ogwilizana kwambili na odzozedwa.
10. Kodi Yehova wacita ciani pokwanilitsa ulosi wa pa Ezekieli 37:15-19, 24, 25?
10 Ŵelengani Ezekieli 37:15-19, 24, 25. Pokwanilitsa ulosi umenewu, Yehova wagwilizanitsa kwambili odzozedwa na a nkhosa zina. Ulosiwu umakamba za ndodo ziŵili. Awo amene ali na ciyembekezo cakumwamba ali ngati ndodo “ya Yuda” (mtundu umene mafumu a Isiraeli anali kusankhidwa). Ndipo aja amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi ali ngati ndodo “ya Efuraimu.” * Yehova anali kudzagwilizanitsa magulu aŵili kuti akhale “ndodo imodzi.” Izi zitanthauza kuti iwo amatumikila pamodzi mogwilizana pansi pa Mfumu yawo, Khristu Yesu. Caka ciliconse, odzozedwa komanso a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso, osati monga magulu aŵii osiyana, koma “gulu limodzi” pansi pa “m’busa mmodzi.”—Yoh. 10:16.
11. Kodi “nkhosa” zochulidwa pa Mateyu 25:31-36, 40, zimaonetsa bwanji kuti zimacilikiza abale a Khristu?
11 Ŵelengani Mateyu 25:31-36, 40. “Nkhosa” za mfanizo ili, zimaimila anthu olungama m’nthawi ino ya mapeto amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi—kutanthauza a nkhosa zina. Iwo amacilikiza mokhulupilika abale a Khristu otsalila odzozedwa, mwa kuwathandiza kukwanilitsa udindo waukulu, umene ni nchito ya padziko lonse yolalikila na kupanga ophunzila.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
12-13. Ni m’njila zinanso ziti zimene a nkhosa zina amacilikizila abale a Khristu?
12 Caka ciliconse, kukangotsala milungu yocepa kuti ticite Cikumbutso, a nkhosa zina amacilikiza abale a Khristu mwa kutengako mbali pa kampeni ya padziko lonse yoitanila anthu ku Cikumbutso. (Onani bokosi lakuti, “ Kodi Mukukonzekela Nyengo ya Cikumbutso?”) Cina, iwo amapanga makonzedwe ofunikila kuti Cikumbutso cicitike m’mipingo padziko lonse, ngakhale kuti m’mipingo yambili mulibe amene amadya ziphiphilitso. A nkhosa zina amakondwela ngako kucilikiza odzozedwa mwa njila imeneyi. Amadziŵa kuti Yesu amaona zimene iwo amacitila abale ake odzozedwa, monga kuti akucitile iye.—Mat. 25:37-40.
13 Ni zifukwanso zina ziti zimene tonsefe timapezekela pa Cikumbutso, mosasamala kanthu za ciyembekezo cathu?
CIFUKWA CAKE TONSEFE TIMAPEZEKA PA CIKUMBUTSO
14. Kodi Yehova na Yesu anationetsa motani cikondi cacikulu?
14Timayamikila cikondi cimene Yehova na Yesu anationetsa. Yehova amationetsa cikondi m’njila zambili. Koma njila yaikulu imene Mulungu wathu anationetsela cikondi, ni kutumiza mwana Mwana wake wokondeka kuti akavutike na kufa kaamba ka ife. (Yoh. 3:16) Nayenso Yesu anaonetsa kuti amatikonda kwambili mwa kupeleka moyo wake kaamba ka ife. (Yoh. 15:13) Palibe cimene tingabwezele Yehova na Yesu pa cikondi cimene iwo anationetsa. Koma tingaonetse kuyamikila mwa zimene timacita pa umoyo wathu. (Akol. 3:15) Ndipo timapezeka pa Cikumbutso kuti tikumbukile cikondi cawo, komanso kuti tionetse kuti nafenso timawakonda.
15. N’cifukwa ciani odzozedwa komanso a nkhosa zina amayamikila kwambili mphatso ya dipo?
15Timayamikila kwambili mphatso ya dipo. (Mat. 20:28) Odzozedwa amayamikila kwambili dipo, cifukwa inapangitsa kuti zikhale zotheka kukhala na ciyembekezo cakumwamba. Cifukwa cokhulupilila nsembe ya Khristu, Yehova amawacha olungama, ndipo waatenga kukhala ana ake. (Aroma 5:1; 8:15-17, 23) Naonso a nkhosa zina amayamikila dipo. Pa maziko a cikhulupililo cawo m’magazi amene Khristu anakhetsa, iwo ali na kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu, amacita utumiki wopatulika, ndipo ali na ciyembekezo ‘codzatuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:13-15) Njila imodzi imene odzozedwa komanso a nkhosa zina amaonetsela kuti amayamikila dipo, ni kupezeka pa Cikumbutso caka ciliconse.
16. N’cifukwa cinanso citi cimene timapezekela pa Cikumbutso?
16 Cifukwa cina cimene timapezekela pa Cikumbutso n’cakuti, timafuna kumvela Yesu. Kaya tili na ciyembekezo cotani, timafuna kumvela lamulo la Yesu limene anapeleka usiku umene anayambitsa mwambo wa Cikumbutso. Iye anati: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—1 Akor. 11:23, 24.
MMENE TONSEFE TIMAPINDULILA TIKAPEZEKAPO
17. Kodi Cikumbutso cimatithandiza bwanji kumuyandikila Yehova?
17Yehova timamuyandikila kwambili. (Yak. 4:8) Monga taphunzilila, Cikumbutso cimatipatsa mpata woganizila ciyembekezo cimene Yehova anatipatsa, komanso kusinkha-sinkha cikondi cacikulu cimene anationetsa. (Yer. 29:11; 1 Yoh. 4:8-10) Tikamaganizila ciyembekezo cathu cotsimikizika ca zakutsogolo, komanso cikondi cosatha ca Mulungu, timalimbitsa cikondi cathu pa Yehova ndiponso ubale wathu na iye.—Aroma 8:38, 39.
18. Kodi kusinkha-sinkha citsanzo ca Yesu kumatilimbikitsa kucita ciani?
18Timalimbikitsidwa kutengela citsanzo ca Yesu. (1 Pet. 2:21) Pakatsala masiku ocepa kuti ticite Cikumbutso, timaŵelenga zocitika pa mlungu womaliza wa Yesu padziko lapansi, imfa yake, na kuukitsidwa kwake. Ndiyeno madzulo pa Cikumbutso, nkhani imene imakambidwa imatikumbutsa cikondi ca Yesu pa ife. (Aef. 5:2; 1 Yoh. 3:16) Tikamaŵelenga za citsanzo ca Yesu ca kudzimana na kucisinkha-sinkha, timalimbikitsidwa “kupitiliza kuyenda mmene iyeyo anayendela.”—1 Yoh. 2:6.
19. Kodi tingakhale bwanji m’cikondi ca Mulungu?
19Timakhala ofunitsitsa kukhalabe m’cikondi ca Mulungu. (Yuda 20, 21) Timakhalabe m’cikondi ca Mulungu ngati tiyesetsa kumumvela, kuyeletsa dzina lake, na kukondweletsa mtima wake. (Miy. 27:11; Mat. 6:9; 1 Yoh. 5:3) Kupezeka pa Cikumbutso kumatisonkhezela kukhala na umoyo woonetsa kuti tifuna kukhalabe m’cikondi ca Mulungu mpaka muyaya.
20. Tili na zifukwa zabwino ziti zopezekela pa Cikumbutso?
20 Kaya ciyembekezo cathu n’cokakhala kwamuyaya kumwamba kapena padziko lapansi, tili na zifukwa zomveka zopezekela pa Cikumbutso. Caka ciliconse tikasonkhana pamodzi pa tsikuli, timakumbukila imfa ya munthu amene tim’konda—Yesu Khristu. Ndipo coposa zonse, timakumbukila njila yaikulu imene Yehova anaonetsela cikondi mwa kupeleka Mwana wake dipo. Caka cino, Cikumbutso cidzakhalako pa Cisanu, April 15, 2022. Timam’konda ngako Yehova na Mwana wake. Motelo, pa mwambo wokumbukila imfa ya Yesu, palibe cingapose kupezekapo kwathu pa Cikumbutso.
NYIMBO 16 Tamandani Ya Kaamba ka Mwana Wake Wodzozedwayo
^ ndime 5 Kaya ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena padziko lapansi la paladaiso, timayembekezela mwacidwi kupezaka pa Cikumbutso caka ciliconse. Nkhani ino, ifotokoza zifukwa za m’Malemba zimene timapezekela pa Cikumbutso, na mmene timapindulila tikatelo.
^ ndime 4 Kuti mudziŵe zambili zokhudza pangano latsopano komanso pangano la Ufumu, onani nkhani yakuti, “Mudzakhala ‘Ufumu wa Ansembe’” mu Nsanja ya Mlonda ya October 15, 2014, mas. 15-17.
^ ndime 4 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mawu akuti otsalila odzozedwa atanthauza Akhristu odzozedwa amene akali na moyo padziko lapansi.
^ ndime 10 Kuti mudziŵe zambili za ulosi wokhudza ndodo ziŵili wa pa Ezekieli caputala 37, onani buku la Cizungu lakuti, Pure Worship of Jehovah—Restored At Last!, mas. 130-135, ndime 3-17.