Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

“Muzigwilitsa Nchito Bwino Nthawi Yanu”

“Muzigwilitsa Nchito Bwino Nthawi Yanu”

“Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.”—AEF. 5:15, 16.

NYIMBO 8 Yehova Ndiye Pothaŵila Pathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tingathele nthawi na Yehova motani?

TIMAKONDWELA kuceza na ŵanthu amene timakonda. Mwacitsanzo, okwatilana amakonda kwambili kuceza ali aŵili-ŵili. Acicepele amakondwela kukhala pamodzi na anzawo. Ndipo tonsefe timayamikila tikamaceza na alambili anzathu. Koma coposa zonse, timakonda kuthela nthawi yathu na Mulungu. Tingacite zimenezi mwa kupemphela, kuŵelenga Baibo, kusinkha-sinkha colinga cake, komanso makhalidwe ake abwino. Inde, nthawi imene timathela na Yehova ni ya mtengo wapatali kwambili.—Sal. 139:17.

2. Kodi timakumana na zopinga zotani?

2 Ngakhale kuti timakondwela kuthela nthawi na Yehova, timakumana na zopinga. Timakhala umoyo wotangwanika, moti cimativuta kupeza nthawi yocita zauzimu. Nchito ya kuthupi, maudindo a m’banja, na zinthu zina, zingatidyele nthawi yathu cakuti tingamaone kuti tilibenso nthawi yopemphela, yoŵelenga, komanso yosinkha-sinkha.

3. N’ciani cina cingatidyele nthawi yathu?

3 Palinso cina cingatidyele nthawi yathu ife osadziŵa. Ngati sitingasamale, tingamacite zinthu zina zimene mwa izo zokha si zoipa. Koma zinthuzo zingatidyele nthawi yathu imene tikanaiseŵenzetsa kuyandikila kwambili Yehova. Mwacitsanzo, zosangalatsa. Tonsefe timapindula tikamapatula nthawi yosangulukako. Koma ngakhale zosangalatsa zoyenela zingatenge nthawi yathu yambili, cakuti n’kutsala na nthawi yocepa yocita zinthu zauzimu. Conco, tiziika zosangalatsa pa malo ake.—Miy. 25:27; 1 Tim. 4:8.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tiyenela kuika zinthu zofunika patsogolo. Tikambilanenso mmene tingagwilitsile nchito bwino nthawi yathu pa zauzimu, na mmene tingapindulile.

PANGANI ZISANKHO ZANZELU, NDIPO IKANI ZOFUNIKA PATSOGOLO

5. Kodi kutsatila malangizo a pa Aefeso 5:15-17, kungathandize bwanji wacinyamata kusankha umoyo wabwino koposa?

5Sankhani umoyo wabwino koposa. Kambili, acinyamata amadela nkhawa mmene angaseŵenzetsele umoyo wawo m’njila yabwino koposa. Aphunzitsi awo kusukulu komanso acibale awo amene si Mboni, angawalimbikitse kucita maphunzilo a pamwamba kuti akapeze nchito yabwino. Kucita maphunzilowo kungawadyele nthawi yawo yoculuka. Kumbali ina, makolo komanso abale na alongo mu mpingo, angalimbikitse acinyamata kuseŵenzetsa umoyo wawo mu utumiki wa Yehova. N’ciani cingathandize wacinyamata amene amakonda Yehova kupanga cisankho cabwino koposa? Iye angapindule kwambili akaŵelenga Aefeso 5:15-17 na kuisinkha-sinkha. (Ŵelengani.) Pambuyo poŵelenga mavesiwa, wacinyamata angadzifunse kuti: ‘Kodi “cifunilo ca Yehova” n’ciani? N’cisankho cotani cingamusangalatse? N’cisankho citi cidzanithandiza kuseŵenzetsa bwino nthawi yanga?’ Kumbukilani kuti “masikuwa ndi oipa,” ndipo dzikoli lolamulidwa na Satana lidzatha posacedwa. Conco, n’canzelu kuseŵenzetsa umoyo wathu m’njila imene idzapangitsa kuti Yehova atiyanje.

6. Kodi Mariya anapanga cisankho cotani? Nanga n’cifukwa ciani cinali cisankho canzelu?

6Muziika zofunika patsogolo. Nthawi zina, kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu kumafuna kusankha pakati pa zinthu ziŵili zimene pa izo zokha zilibe vuto. Nkhani yodziŵika bwino yokamba za Yesu atapita ku nyumba ya Mariya na Marita, imaonetsa bwino mfundo imeneyi. Marita anakondwela ngako kulandila Yesu monga mlendo wake, ndipo anayamba kuphika zakudya zambili. Koma Mariya m’bale wake anakhala pafupi na Mbuye wake, kuti amvetsela pamene anali kuphunzitsa. Kuphika kumene Marita anacita kunalibe vuto ayi, koma Yesu anati Mariya “wasankha cinthu cabwino kwambili.” (Luka 10:38-42) Patapita nthawi, n’kutheka kuti Mariya anaiŵala zakudya zimene zinaphikidwa pa nthawiyo, koma tingakhale otsimikiza kuti sanaiŵale zimene anaphunzila kwa Yesu. Mariya anaona nthawi imene anali na Yesu kukhala yamtengo wapatali. Nafenso timaona nthawi imene timathela na Yehova kukhala yamtengo wapatali. Kodi tingaseŵenzetse bwanji mwanzelu nthawi yathu?

THELANI NTHAWI YANU BWINO NA YEHOVA

7. N’cifukwa ciani tiyenela kupatula nthawi yopemphela, yoŵelenga Baibo, komanso yosinkha-sinkha?

7Kumbukilani kuti pemphelo, kuŵelenga Baibo, na kusinkha-sinkha, ni mbali ya kulambila Yehova. Tikapemphela, timakhala kuti tikukambilana na Atate wathu wakumwamba amene amatikonda ngako. (Sal. 5:7) Tikamaŵelenga Baibo, timafika ‘pomudziŵadi Mulungu,’ amene ni gwelo la nzelu. (Miy. 2:1-5) Tikamasinkha-sinkha, timakhala kuti tikuganizila makhalidwe abwino a Yehova, komanso colinga cake cokondweletsa cokhudza mtundu wonse wa anthu. Iyi ni njila yabwino koposa imene tingaseŵenzetsele bwino nthawi yathu. Koma kodi n’ciani cingatithandize kupindula kwambili tikamacita zimenezi?

Pezani malo a zii kuti mucite phunzilo la inu mwini (Onani ndime 8-9)

8. Tiphunzilapo ciani tikaona mmene Yesu anaseŵenzetsela nthawi yake m’cipululu?

8Ngati n’zotheka, khalani pamalo a zii. Ganizilani citsanzo ca Yesu. Asanayambe utumiki wake padziko lapansi, iye anakhala masiku 40 m’cipululu. (Luka 4:1, 2) Kumalo a zii amenewo, Yesu anali kupemphela kwa Yehova, na kusinkha-sinkha zimene Atate wake anali kufuna kuti iye acite. Mosakayikila, kucita zimenezo kunamuthandiza kukonzekela mayeso amene anali kudzakumana nawo. Kodi mungapindule bwanji na citsanzo ca Yesu? Ngati pa nyumba pamene mukhala mulipo ambili, cingakhale covuta kupeza malo a zii. Zikakhala conco, mungafunike kupeza malo ena. Izi n’zimene mlongo Julie amacita akafuna kukambilana na Yehova m’pemphelo. Iye na mwamuna wake amakhala m’nyumba yaing’ono ku France, ndipo cimawavuta kukhala paokha-okha popanda cosokoneza. Mlongo Julie anati: “Tsiku lililonse nimapita kokayenda ku paki. Kumeneko nimakhala nekha, ndipo nimakwanitsa kukambilana na Yehova.”

9. Ngakhale anali wotangwanika, kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuona ubale wake na Yehova kukhala wofunika kwambili?

9 Yesu anali kukhala wotangwanika kwambili. Pa utumiki wake wa padziko lapansi, makamu a anthu anali kumutsatila kulikonse kumene wapita. Pa nthawi ina, ‘anthu onse a mumzindawo anasonkhana pakhomo’ kuti aonane naye. Ngakhale anali wotangwanika, Yesu anapatula nthawi yolimbitsa ubale wake na Yehova. M’maŵa kwambili, iye anapita “kumalo kopanda anthu” kumene anatha kukambilana na Atate wake.—Maliko 1:32-35.

10-11. Malinga n’kunena kwa Mateyu 26:40, 41, ni malangizo a pa nthawi yake ati amene Yesu anapatsa ophunzila ake? Koma cinacitika n’ciani?

10 Usiku wothela wa moyo wake padziko lapansi, Yesu anapitanso ku malo a zii kumene anatha kusinkha-sinkha na kupemphela. Iye anapeza malowo m’munda wa Getsemane. (Mat. 26:36) Pa nthawiyo, Yesu anapatsa ophunzila ake malangizo a panthawi yake okamba za pemphelo.

11 Onani zinacitika. Iwo anafika m’munda wa Getsemane usiku kwambili, mwina kudutsa pakati pa usiku. Yesu anauza atumwi ake ‘kukhalabe maso,’ ndipo iye anapita kukapemphela. (Mat. 26:37-39) Koma pamene anali kupemphela, iwo anagona. Atawapeza ali cigonele, Yesu anawauzanso kuti: “Khalani maso ndipo pemphelani kosalekeza.” (Ŵelengani Mateyu 26:40, 41.) Iye anadziŵa kuti ophunzila ake anali opsinjika maganizo kwambili, komanso olema. Yesu anamvetsa kuti “thupi ndi lofooka.” Iye anapitanso maulendo ena aŵili kukapemphela, koma atabwelako anapeza ophunzila ake ali gone m’malo mopemphela.—Mat. 26:42-45.

Muzipemphela pa nthawi imene si muli wolema kwambili (Onani ndime 12)

12. Tingacite ciani ngati nthawi zina timalephela kupemphela cifukwa copanikizika kwambili, kapena cifukwa colema kwambili?

12Sankhani nthawi yabwino. Nthawi zina tingakhale opanikizika kwambili, kapena olema kwambili moti n’kulephela kupemphela. Ngati izi zinakucitikilamponi, dziŵani kuti si ndimwe mwekha. Kodi mungacite ciani? Ena amene anali na cizolowezi copemphela kwa Yehova usiku, aona kuti n’cothandiza ngako kumapemphela madzulo pamene si olema kwambili. Enanso aona kuti kakhalidwe kena kake popemphela kamakhala kothandiza kwambili. Koma bwanji ngati mumalephela kupemphela cifukwa ca kuculuka kwa nkhawa zanu, kapena cifukwa colefuka? Uzani Yehova mmene mumvelela. Mungakhale otsimikiza kuti Atate wathu wacifundo adzakumvetsani.—Sal. 139:4.

Pewani kulemba mauthenga misonkhano ili mkati (Onani ndime 13-14)

13. Kodi zipangizo zathu zingatisokoneze bwanji pamene tikucita zinthu zauzimu?

13Pewani zosokoneza pamene muŵelenga. Pemphelo si njila yokhayo imene tingalimbitsile ubale wathu na Yehova. Kuŵelenga Mawu a Mulungu na kupezeka pa misonkhano yacikhristu, nakonso kungatithandize kumuyandikila kwambili Mulungu. Kodi pali cimene mungacite kuti muziseŵenzetsa bwino nthawi yoŵelenga, komanso yopezeka pa misonkhano ya mpingo? Dzifunseni kuti: ‘N’ciani cimanisokoneza nikakhala pa misonkhano kapena nikamaŵelenga?’ Kodi ni foni kapena mauthenga amene wina angakutumileni pa cipangizo canu? Masiku ano, anthu mabiliyoni amaseŵenzetsa zipangizo zimenezi. Akatswili ena amakamba kuti tikamayesa kuchela khutu ku cina cake, foni yathu ingatisokoneze. Ndipo pulofesa wina wa zamaganizo a anthu anati: “Maganizo ako sakhala pa zimene ukucita, koma amakhala kwina kwake.” Tisanayambe misonkhano yadela kapena yacigawo, kambili timauzidwa kuseting’a zipangizo zathu m’njila yakuti zisasokoneze ena. Kodi tingacitenso cimodzi-modzi ku cipangizo cathu tikakhala tekha, kuti cisatisokoneze na kutidyela nthawi yocita zinthu zauzimu?

14. Malinga na Afilipi 4:6, 7, kodi Yehova amatithandiza bwanji kusumika maganizo athu?

14Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusumika maganizo. Mukazindikila kuti maganizoanu akuyenda-yendapamene muŵelenga, kapena muli pa misonkhano ya mpingo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Ngati muli na nkhawa, cingakhale covuta kuiŵala nkhawazo kuti musumike maganizo anu pa zauzimu. Zikakhala conco, pemphani mtendele umene udzateteza mtima wanu, komanso “maganizo anu.”—Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.

KUTHELA NTHAWI NA YEHOVA N’KOPINDULITSA NGAKO

15. Kodi timapindula bwanji tikamacita zinthu zauzimu?

15 Ngati mupeza nthawi yolankhula na Yehova, kumvetsela kwa iye, komanso kusinkha-sinkha, mudzapindula kwambili. Motani? Coyamba, mudzapanga zisankho zabwino. Baibo imatitsimikizila kuti “munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” (Miy. 13:20) Conco, mukamapatula nthawi yokamba na Yehova amene ni Gwelo la nzelu, nanunso mudzakhala anzelu. Mudzafika podziŵa bwino mmene mungamukondweletsele, na kupewa kucita zinthu zomukhumudwitsa.

16. Kodi kukambilana na Yehova kunganole bwanji luso lathu la kuphunzitsa?

16 Caciŵili, mudzakhala mphunzitsi wabwino. Tikamaphunzila Baibo na munthu, cimodzi mwa zolinga zathu zazikulu ni kumuthandiza kuyandikila Yehova. Tikamakambilana kwambili na Atate wathu wakumwamba, m’pamenenso cikondi cathu pa iye cimakulilako. Komanso m’pamene tingathe kuphunzitsa bwino wophunzila wathu kukonda Mulungu. Ni mmene zinalili kwa Yesu. Iye anafotokoza za Atate wake m’njila imene inapangitsa otsatila ake okhulupilika kuti nawonso azikonda Yehova.—Yoh. 17:25, 26.

17. N’cifukwa ciani pemphelo na kuŵelenga Baibo n’zothandiza polimbitsa cikhulupililo cathu?

17 Cacitatu, cikhulupililo canu cidzalimbilako. Ganizilani zimene zimacitika mukapempha Mulungu kuti akutsogoleleni, kukutonthozani, kapena kukuthandizani. Nthawi iliyonse Yehova akayankha mapemphelo anuwo, cikhulupililo canu cimakulilako. (1 Yoh. 5:15) N’ciani cina cingalimbitse cikhulupililo canu? Ni phunzilo la munthu mwini. Kumbukilani kuti “munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva.” (Aroma 10:17) Komabe, kuwonjezela pa kukhala na cidziŵitso, palinso zina zimene tingacite kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Kodi n’ziti?

18. Fotokozani cifukwa cake tiyenela kusinkhasinkha.

18 Tiyenela kusinkhasinkha zimene tikuphunzila. Ganizilani citsanzo ca wolemba Salimo 77. Iye anapsinjika maganizo cifukwa coona kuti Yehova waleka kumuyanja iye na Aisiraeli anzake. Izi zinali kumusoŵetsa tulo. (Vesi 2-8) Kodi anacita ciani? Anauza Yehova kuti: “Ndidzasinkhasinkha za nchito zanu zonse, ndipo ndiziganizila zocita zanu.” (Vesi 12) Olo kuti wa masalimoyo anali kudziŵa bwino zimene Yehova anacitila anthu ake m’mbuyomu, iye anadzifunsabe kuti: “Kodi Mulungu waiŵala kukhala wokoma mtima, kapena watsekeleza cifundo cake mwaukali?” (Vesi 9) Iye anasinkhasinkha nchito za Yehova, komanso maumboni oonetsa cifundo cimene Mulungu anamuonetsa m’mbuyomu. (Vesi 11) Cotulukapo cake n’cakuti anakhala wotsimikiza kuti Yehova sasiya anthu ake. (Vesi 15) Mofananamo, cikhulupililo canu cidzalimba kwambili mukamasinkhasinkha zimene Yehova wacitila anthu ake, ndiponso zimene wacitila inuyo panokha.

19. Kodi timapindulanso motani tikamakambilana na Yehova?

19 Cacinayi komanso cofunika ngako, cikondi canu pa Yehova cidzakula. Cikondi, cimene cimaposa khalidwe lina lililonse, cidzakusonkhezelani kumvela Yehova, kukhala odzimana kuti mum’kondweletse, na kupilila mayeso. (Mat. 22:37-39; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Yoh. 5:3) Palibe cinthu ca mtengo wapatali kuposa kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova.—Sal. 63:1-8.

20. Kodi mwalinganiza zotani kuti muzikhala na nthawi yocita zauzimu?

20 Kumbukilani kuti pemphelo, kuŵelenga Baibo, na kusinkhasinkha, ni mbali ya kulambila kwathu. Mofanana na Yesu, pezani malo a bata kuti mucite zinthu zauzimu zimenezi. Pewani zosokoneza zilizonse. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusumika maganizo anu mukamacita zauzimu. Ngati mugwilitsila nchito bwino nthawi yanu pali pano, Yehova adzakufupani na moyo wamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu.—Maliko 4:24.

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

^ ndime 5 Yehova ni Bwenzi lathu la pamtima. Ubwenzi wathu na iye ni wamtengo wapatali, ndipo timafuna kumudziŵa bwino. Pamatenga nthawi kuti udziŵe munthu wina. Ni mmenenso zilili ngati tifuna kupitiliza kulimbitsa ubale wathu na Yehova. Popeza timatangwanika kwambili pa umoyo, kodi tingapeze bwanji nthawi yoyandikila Atate wathu wa kumwamba? Nanga tingapindule bwanji tikatelo?