Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

“Ofuna-funa Yehova Sadzasoŵa Ciliconse Cabwino”

“Ofuna-funa Yehova Sadzasoŵa Ciliconse Cabwino”

LEMBA LA CAKA CA 2022: “Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.”—SAL. 34:10.

NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’

ZIMENE TIKAMBILANE *

Davide anaona kuti ‘sanasoŵe ciliconse cabwino’ ngakhale panthawi zovuta (Onani ndime 1-3) *

1. Kodi Davide anapezeka mu mkhalidwe wovuta uti?

DAVIDE anali kuthaŵa-thaŵa kuti apulumutse moyo wake. Sauli, mfumu yamphamvu ya Isiraeli, anali kufunitsitsa kumupha. Pamene Davide anali kufuna zakudya, anafika mu mzinda wa Nobu, mmene anapempha mitanda isanu ya mkate. (1 Sam. 21:1, 3) Patapita nthawi, iye na asilikali ake anabisala m’phanga kuti atetezeke. (1 Sam. 22:1) Kodi Davide anapezeka bwanji mu mkhalidwe wovuta umenewu?

2. Kodi Sauli anaika motani moyo wake pa ciwopsezo? (1 Samueli 23:16, 17)

2 Sauli anali kucitila nsanje kwambili Davide cifukwa anachuka, komanso cifukwa anapambana nkhondo zambili. Sauli anadziŵa kuti kusamvela kwake, n’kumene kunapangitsa kuti Yehova amukane kukhala mfumu ya Isiraeli, komanso kuti anali atasankha Davide kukhala mfumu ya m’tsogolo. (Ŵelengani 1 Samueli 23:16, 17.) Koma pokhalabe mfumu ya Isiraeli, Sauli anali na asilikali ambili, na ŵanthu ambili om’cilikiza. N’cifukwa cake, Davide anathaŵa kuti apulumutse moyo wake. Kodi n’kutheka kuti Sauli anali kuona kuti angakwanitse kulepheletsa colinga ca Mulungu pa Davide? (Yes. 55:11) Baibo siikamba, koma cimene tidziŵa n’cakuti: Sauli anaika moyo wake pa ciwopsezo. Anthu otsutsana na Mulungu sapambana konse!

3. Kodi Davide anamva bwanji mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta?

3 Davide anali munthu wodzicepetsa. Iye sanasankhe yekha kuti akhale mfumu ya Isiraeli, koma Yehova ndiye anacita kumusankha. (1 Sam. 16:1, 12, 13) Sauli anayamba kuona Davide kukhala mdani wake woopsa. Davide sanaimbe mlandu Yehova cifukwa cakuti moyo wake unali pa ciwopsezo, kapena kudandaula cifukwa cokhala na zakudya zocepa komanso kubisala m’phanga. M’malo mwake, zioneka kuti pa nthawi imene iye anabisala m’phanga, m’pamene analemba nyimbo yokoma yacitamando imene mawu ake ena ni lemba la mutu wa nkhani ino. Iye anati: “Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.”—Sal. 34:10.

4. Tikambilane mafunso ati? Nanga n’cifukwa ciani mafunsowa ni ofunika?

4 Masiku ano, atumiki a Yehova ambili akumana na vuto la kucepekela kwa cakudya, na zofunikila zina pa umoyo. * Ndipo izi zakhala conco maka-maka m’nthawi ino ya mlili. Ndipo pa “cisautso cacikulu” cimene catsala pan’gono kuyamba, tingadzakumane na mavuto aakulu kuposa amenewa. (Mat. 24:21) Tili na mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni tiyankhe mafunso anayi aya: Kodi Davide ‘sanasoŵe ciliconse cabwino’ m’lingalilo lotani? N’cifukwa ciani tiyenela kukhala okhutila? N’cifukwa ciani tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila? Nanga tingakonzekele bwanji zam’tsogolo pali pano?

“SINDIDZASOŴA KANTHU”

5-6. Kodi Salimo 23:1-6, imatithandiza bwanji kumvetsa zimene Davide anatanthauza pokamba kuti atumiki a Mulungu “sadzasoŵa ciliconse cabwino”?

5 Kodi Davide anatanthauza ciani pokamba kuti atumiki a Yehova “sadzasoŵa ciliconse cabwino”? Tingamvetse tanthauzo lake tikaona mawu ofananako pa Salimo 23. (Ŵelengani Salimo 23:1-6.) Davide anayamba salimoli na mawu akuti: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasoŵa kanthu.” Mu salimo lonselo, Davide anachula zinthu zokhalitsa, zimene ni madalitso oculuka auzimu amene analandila cifukwa colola Yehova kukhala M’busa wake. Yehova anam’tsogolela “m’tinjila tacilungamo,” ndipo iye anacilikiza Davide mokhulupilika pa nthawi zabwino komanso zovuta. Davide anadziŵa kuti umoyo wake “m’mabusa a msipu wambili” a Yehova udzakhala na mavuto. Nthawi zina, iye anali kulefulidwa, monga kuti akuyenda “m’cigwa ca mdima wandiweyani,” komanso kuti adzakhala na adani. Koma cifukwa Yehova anali M’busa wake, Davide ‘sanaope kanthu.’

6 Conco, tapeza yankho la funso lathu lakuti: Kodi Davide ‘sanasoŵe ciliconse cabwino’ m’lingalilo lotani? Mwauzimu tingakambe kuti, iye anali na zonse zofunikila. Cimwemwe cake sicinadalile zinthu zakuthupi. Davide anakhutila na zimene Yehova anam’patsa. Cinali cofunika ngako kwa iye cinali madalitso na citetezo ca Mulungu wake.

7. Malinga n’kunena kwa Luka 21:20-24, kodi Akhristu oyambilila ku Yudeya anakumana na vuto lotani?

7 Malinga na mawu a Davide, tiona kuti n’kofunika kwambili kukhala na maganizo oyenela pa zinthu zakuthupi. Tingakhale na zinthu zambili zakuthupi, koma sitiyenela kuona zinthuzo kukhala zofunika ngako pa umoyo wathu. Iyi ni mfundo yofunika kwambili imene Akhristu oyambilila a ku Yudeya anafika poimvetsa. (Ŵelengani Luka 21:20-24.) Yesu anawacenjeza kuti nthawi ikadzafika, ‘magulu ankhondo azazungulila’ mzinda wa Yerusalemu. Izi zikadzacitika, iwo anayenela ‘kuthaŵila kumapili.’ Kuthaŵa kumeneko kukanapulumutsa miyoyo yawo, koma anafunika kusiya zinthu zawo zambili. Zaka zambili kumbuyoko, Nsanja ya Mlonda ina inati: “Iwo anasiya minda, nyumba, osatenga ngakhale katundu wawo m’nyumba zawo. Pokhala na cidalilo cakuti Yehova adzawateteza na kuwathandiza, iwo anaika kulambila Mulungu patsogolo pa cina ciliconse cooneka ngati cofunika kwambili.”

8. Kodi pali phunzilo lofunika liti pa zimene zinacitikila Akhristu oyambilila ku Yudeya?

8 Kodi pali phunzilo lofunika liti pa zimene zinacitikila Akhristu oyambilila ku Yudeya? Nsanja imene tachula inati: “M’tsogolomu tingadzakumane na mayeso okhudza mmene timaonela zinthu zakuthupi. Kodi zinthuzo ndiye zofunika kwambili, kapena kodi cipulumutso ndiye cofunika koposa cifukwa cakuti tili ku mbali ya Mulungu? Inde, mapeto akadzafika, tingafunike kukapilila mavuto na kukhala odzimana. Tidzayenela kukhala okonzeka kucita zonse zotheka, monga anacitila Akhristu anzathu a m’zaka za zana loyamba amene anathaŵa ku Yudeya.” *

9. Kodi malangizo amene Paulo anapatsa Akhristu aciheberi amakulimbikitsani bwanji?

9 Tangoganizilani mmene zinalili zovuta kwa Akhristu amenewo kusiya pafupifupi zonse anali nazo, na kukayamba umoyo watsopano kumalo acilendo. Zinafuna kuti iwo akhale na cikhulupililo mwa Yehova kuti iye adzawapatsa zofunikila zakuthupi. Onani cinawathandiza. Kukali zaka zisanu kuti Aroma azungulile Yerusalemu, mtumwi Paulo anapeleka malangizo ofunika kwa Akhristu aciheberi akuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’” (Aheb. 13:5, 6) Mosakayikila, aja amene anatsatila malangizo a Paulo Aroma asanaukile mzindawo, cinakhala cosavuta kwa iwo kuzoloŵela umoyo wosalila zambili kumalo awo atsopano. Iwo anali na cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila kuthupi. Mawu a Paulo amenewa amatilimbikitsa nafenso kukhala na cidalilo cofananaco.

“TIKHALE OKHUTILA NDI ZINTHU ZIMENEZI”

10. Kodi Paulo anatiuza “cinsinsi” cotani?

10 Paulo anapeleka malangizo ofananawo kwa Timoteyo, ndipo ni othandizanso kwa ife masiku ano. Iye anati: “Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:8) Kodi izi zitanthauza kuti sitingakhale na cakudya cabwino, nyumba yokongola, kapena kugula zovala zatsopano nthawi na nthawi? Ayi, izi si zimene Paulo anali kutanthauza. Iye anali kukamba kuti tiyenela kukhutila na zinthu zakuthupi zimene tili nazo. (Afil. 4:12) Ici ndiye cinali “cinsinsi” ca Paulo. Cinthu camtengo wapatali kwa ife ni ubale wathu na Mulungu, osati zinthu zakuthupi zimene tili nazo.—Hab. 3:17, 18.

Aisiraeli ‘sanasoŵe ciliconse cabwino’ pa zaka 40 zimene anali m’cipululu. Tizikhala okhutila na zimene tili nazo (Onani ndime 11) *

11. Pa nkhani yokhala okhutila, kodi tiphunzilapo ciani pa zimene Mose anauza Aisiraeli?

11 Kaonedwe kathu pa zofunikila zakuthupi, kangakhale kosiyana na mmene Yehova amaonela. Ganizilani zimene Mose anauza Aisiraeli atakhala zaka 40 m’cipululu. Iye anati: “Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa ciliconse cimene dzanja lanu likucita. Iye akudziŵa za kuyenda kwanu kudutsa m’cipululu cacikulu ici. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi, ndipo simunasoŵe kanthu.” (Deut. 2:7) Pa zaka 40 zonsezo, Yehova anapatsa Aisiraeli mana monga cakudya. Zovala zawo zimene anacoka nazo ku Iguputo sizinathe. (Deut. 8:3, 4) Ngakhale kuti ena anaona kuti zimene anali nazo n’zosakwanila, Mose anakumbutsa Aisiraeli kuti iwo anali na zonse zofunikila. Yehova amakondwela kwambili tikakhala okhutila, ngakhale pa zocepa zimene angatipatse. Tiziona zinthuzo kuti ni mphatso, ndipo tiziyamikila.

KHALANI NA CIDALILO CAKUTI YEHOVA ADZAKUSAMALILANI

12. N’ciani cionetsa kuti Davide anali kudalila Yehova?

12 Davide anadziŵa kuti Yehova ni wokhulupilika, komanso kuti amasamala kwambili za anthu amene amam’konda. Olo kuti moyo wake unali pa ciwopsezo pamene analemba Salimo 34, na maso a cikhulupililo, Davide anaona “mngelo wa Yehova” akumanga msasa “mozungulila” iye. (Sal. 34:7) N’kutheka kuti Davide anayelekezela mngelo wa Yehova na msilikali amene ali chelu kwa adani amene angaukile. Ngakhale kuti iye anali msilikali wamphamvu pa nkhondo, komanso Yehova anali atamulonjeza ufumu, Davide sanadalile luso lake loponya mwala na gulaye, kapena loseŵenzetsa lupanga pogonjetsa adani. (1 Sam. 16:13; 24:12) Iye anakhulupilila Mulungu, ali na cidalilo cakuti mngelo wa Yehova ‘amapulumutsa onse oopa Mulungu.’ Masiku ano, sitingayembekezele Mulugu kutiteteza mozizwitsa. Koma tidziŵa kuti aliyense amene amakhulupilila Yehova sadzawonongedwa kothelatu.

Pa cisautso cacikulu, gulu la nkhondo la Gogi wa Magogi lidzatiukila m’nyumba zathu. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yesu na angelo ake adzaona zimenezo, ndipo adzatithandiza (Onani ndime 13)

13. Gogi wa Magogi akadzatiukila, kodi tidzaoneka anthu otani? Koma kodi n’cifukwa ciani panthawiyo sitidzaopa? (Onani cithunzi pacikuto.)

13 M’tsogolomu, cikhulupililo cathu cakuti Yehova adzatiteteza cidzayesedwa. Pamene Gogi wa Magogi, kutanthauza mgwilizano wa mitundu, adzaukila anthu a Mulungu, miyoyo yathu idzaoneka kukhala yosatetezeka. Panthawiyo, tidzayenela kukhala otsimikiza kuti Yehova adzatipulumutsa. Kwa a mitundu, tidzaoneka monga nkhosa zopanda wodziteteza. (Ezek. 38:10-12) Tidzakhala tilibe zida zankhondo, komanso osadziŵa kumenya nkhondo. Mitunduyo idzaona kuti n’zosavuta kutigonjetsa. Iyo sidzaona zimene ife timaona na maso athu a cikhulupililo—gulu la angelo lozungulila anthu onse a Mulungu, lokonzeka kuwateteza. Mitundu ya anthu ilibe maso auzimu. Idzadzidzimuka ikadzaona gulu lankhondo lakumwamba likutsika kudzatiteteza.—Chiv. 19:11, 14, 15.

KONZEKELANI PALI PANO ZAM’TSOGOLO

14. Tingacite ciani pali pano pokonzekela zam’tsogolo?

14 Tingacite ciani pali pano pokonzekela zam’tsogolo? Coyamba, tiziona zinthu zakuthupi moyenela, podziŵa kuti tsiku lina tidzasiya zonsezo. Cina, tizikhala okhutila komanso acimwemwe cifukwa cokhala pa ubale na Yehova. Tikafika pom’dziŵa bwino Mulungu wathu, m’pamenenso tidzakulitsa cidalilo cathu cakuti iye adzatiteteza pamene Gogi wa Magogi adzatiukila.

15. Kodi n’zocitika ziti za pa unyamata wake zinathandiza Davide kutsimikiza kuti Yehova sangamusiye konse?

15 Onani cina cinathandiza Davide, cimene nafenso cingatithandize kukonzekela mayeso. Davide anati: “Talaŵani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathaŵila kwa iye.” (Sal. 34:8) Mawuwa amaonetsa cifukwa cake Davide anali kudalila thandizo la Yehova. Iye anali kudalila Yehova nthawi zonse, ndipo Mulungu wake sanamgwilitse mwala. Ali wacinyamata, Davide anayang’anizana na Goliyati, ciphona coopsa cacifilisiti, na kuciuza kuti: “Lelo Yehova akupeleka m’manja mwanga.” (1 Sam. 17:46) Pambuyo pake, Davide anayamba kutumikila mfumu Sauli, imene kangapo konse inafuna kumupha. Koma “Yehova anali ndi” Davide. (1 Sam. 18:12) Cifukwa coona mmene Yehova anam’thandizila m’mbuyomu, Davide anadziŵa kuti Mulungu adzam’thandizanso pa mayeso amene anali kukumana nawo.

16. Kodi ‘tingalaŵe’ ubwino wa Yehova m’njila ziti?

16 Tikamadalila kwambili citsogozo ca Yehova pali pano, m’pamenenso tidzakulitsa cidalilo cathu cakuti iye adzatipulumutsa m’tsogolomu. Zimafuna cikhulupililo komanso kukhala okonzeka kudalila Yehova, kuti tipemphe abwana athu masiku akuti tikacite msonkhano wadela kapena wacigawo. Kapenanso kuwapempha kuti tiziweluka mwamsanga, n’colinga cakuti tikapezeke ku misonkhano yampingo na mu ulaliki. Bwanji ngati abwana akana pempho lathu, ndipo aticotsa nchito. Kodi timakhala na cikhulupililo kuti Yehova sadzatisiya kapena kutitaya, komanso kuti nthawi zonse adzatipatsa zofunikila pa umoyo? (Aheb. 13:5) Ambili amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, angafotokozeko zocitika zoonetsa mmene Yehova anawathandizila pa nthawi zovuta kwambili. Kukamba zoona, iye ni wokhulupilika.

17. Kodi lemba la caka ca 2022 n’liti? Nanga n’cifukwa ciani n’loyenelela?

17 PopezaYehova ali kumbali yathu, palibe cifukwa coopela za kutsogolo. Mulungu wathu sadzatisiya m’pang’ono pomwe, malinga ngati tiika cifunilo cake patsogolo. Pofuna kutithandiza kukonzekela nthawi zovuta m’tsogolo, komanso kufunika kokhulupilila kuti Yehova sadzatisiya konse, Bungwe Lolamulila linasankha Salimo 34:10 kukhala lemba lathu la caka ca 2022. Limati: “Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.”

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Lemba la caka ca 2022 lacokela pa Salimo 34:10. Limati: “Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.” Atumiki ambili a Yehova okhulupilika alibe zinthu zambili zakuthupi. Nanga n’cifukwa ciani tikamba kuti iwo ‘sasoŵa ciliconse cabwino’? Kodi kumvetsetsa tanthauzo la vesiyi, kungatithandize bwanji kukonzekela nthawi zovuta m’tsogolomu?

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti, “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Mlonda ya September 15, 2014.

^ ndime 8 Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1999, tsa. 19.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Ngakhale pamene anali kubisala m’phanga pothaŵa Mfumu Sauli, Davide anayamikila zimene Yehova anali kum’patsa.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Aisiraeli atacoka ku Iguputo, Yehova anali kuwapatsa mana monga cakudya, ndipo zovala zawo sizinathe.