Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 3

Yesu Anagwetsa Misozi—Tiphunzilapo Ciani?

Yesu Anagwetsa Misozi—Tiphunzilapo Ciani?

“Yesu anagwetsa misozi.”—YOH. 11:35.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-3. Ni mavuto otani angapangitse anthu a Yehova kugwetsa misozi?

KODI ni liti pamene munalilapo? Pa zocitika zina, timagwetsa misozi yacisangalalo. Koma nthawi zambili timalila cifukwa coŵaŵidwa mtima. Mwacitsanzo, timalila munthu amene timakonda akamwalila. Mlongo Lorilei wa ku America anakamba kuti: “Nthawi zina mtima unali kuŵaŵa kwambili cifukwa ca imfa ya mwana wanga wamkazi, ndipo n’nali kuona kuti palibe cinali kunitonthoza. Panthawi zimenezo, mtima wanga unali kuswekelatu cifukwa cokhuta cisoni.” *

2 Tingagwetse misozi pa zifukwa zinanso. Mlongo Hiromi, amene ni mpainiya ku Japan, anati: “Nthawi zina, nimalefuka cifukwa coona kuti anthu alibe cidwi nikamawalalikila. Pena nimacita kugwetsa misozi popempha Yehova kuti anithandize kupeza munthu amene akufuna-funa coonadi.”

3 Kodi nthawi zina mumamvela monga mmene alongo tachulawa anamvelela? Ambili a ife timamva conco. (1 Pet. 5:9) Timafuna ‘kutumikila Yehova mokondwela,’ koma tingamam’tumikile na misozi cifukwa ca cisoni, zolefula, kapena cifukwa ca vuto lalikulu limene laika kukhulupilika kwathu kwa Mulungu pa mayeso. (Sal. 6:6; 100:2) Kodi tingacite ciani zaconco zikaticitikila?

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 Tingaphunzile zambili pa citsanzo ca Yesu. Nthawi zina, iye anali kukhudzika mtima kwambili mpaka kufika ‘pogwetsa misozi.’ (Yoh. 11:35; Luka 19:41; 22:44; Aheb. 5:7) Tiyeni tikambilane zocitika zimene zinapangitsa kuti iye agwetse misozi. Pokambilana, tione maphunzilo amene titengapo. Tikambilanenso zimene tingacite tikakumana na mavuto amene amaticititsa kugwetsa misozi.

ANAGWETSA MISOZI KAAMBA KA MABWENZI AKE

Limbikitsani amene akulila, monga Yesu anacitila (Onani ndime 5-9) *

5. Tiphunzilapo ciani za Yesu pa cocitika ca pa Yohane 11:32-36?

5 Mu 32 C.E., Lazaro bwenzi la pamtima la Yesu, anadwala n’kumwalila. (Yoh. 11:3, 14) Iye anali na alongo ake aŵili—Mariya na Marita, ndipo Yesu anali kuwakonda ngako! Akazi amenewa anali na cisoni cacikulu cifukwa ca imfa ya mlongosi wawo. Lazaro atamwalila, Yesu ananyamuka ulendo wopita ku Betaniya, kumene Mariya na Marita anali kukhala. Marita atamva kuti Yesu akubwela, anathamanga kuti akakumane naye. Tangoganizilani cisoni cimene anali naco pamene anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalila.” (Yoh. 11:21) Yesu poona kuti Mariya na ŵanthu ŵena akulila, “anagwetsa misozi.”—Ŵelengani Yohane 11:32-36.

6. N’cifukwa ciani Yesu analila?

6 N’cifukwa ciani Yesu analila? Buku lakuti Insight on the Scriptures limayankha kuti: “Imfa ya bwenzi lake Lazaro, komanso cisoni cimene alongo ake anali naco zinacititsa Yesu ‘kudzuma na kugwetsa misozi.’” * Yesu ayenela kuti anaganizila ululu umene bwenzi lake Lazaro anali kumva cifukwa ca matenda, komanso poganizila mmene Lazaroyo anamvelela poona kuti watsala pang’ono kufa. Cina, iye analila poona mmene Mariya na Marita anakhudzidwila na imfa ya mlongosi wawo. Ngati munataikilidwa bwenzi lanu la pamtima kapena wa m’banja mwanu, mosakayikila nanunso munali na cisoni cacikulu. Tiyeni tione maphunzilo atatu amene titengapo pa cocitika cimeneci.

7. Tiphunzilapo ciani za Yehova pamene Yesu anagwetsa misozi kaamba ka mabwenzi ake?

7Yehova amamvetsa mmene mumvelela. Yesu ni “cithunzi ceniceni” ca Atate wake. (Aheb. 1:3) Pamene iye analila, anaonetsa mmene Atate wake amamvelela munthu amene timakonda akamwalila. (Yoh. 14:9) Ngati mukupilila cisoni cifukwa ca imfa ya wokondedwa wanu, dziŵani kuti Yehova samangoona cisoni canuco, koma amakumvelelani cifundo kwambili. Iye amafuna kucilitsa mtima wanu woswekawo.—Sal. 34:18; 147:3.

8. N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti Yesu adzaukitsa okondedwa athu?

8Yesu afuna kukaukitsa okondedwa anu. Iye ali pafupi kulila, anauza Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anakhulupilila Yesu. (Yoh. 11:23-27) Popeza anali mlambili wa Yehova wokhulupilika, mosakayikila Marita anali kudziŵako anthu amene anaukitsidwapo na mneneli Eliya komanso Elisa, zaka mahandiledi ambili m’mbuyomu. (1 Maf. 17:17-24; 2 Maf. 4:32-37) Ndipo n’kuthekanso kuti iye anamvela zakuti Yesu anali ataukitsapo anthu. (Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56) Inunso khalani na cikhulupililo cakuti mudzawaonanso okondedwa anu amene anamwalila. Kugwetsa misozi kwa Yesu potonthoza mabwenzi ake acisoniwo, ni umboni wakuti iye ni wofunitsitsa kukaukitsa akufa.

9. Mofanana na Yesu, kodi tingawalimbikitse bwanji amene akulila? Fotokozani citsanzo.

9Muzilimbikitsa amene akulila. Yesu sanangolila pamodzi na Marita komanso Mariya, koma anawamvetsela na kuwalimbikitsa. Nafenso tizicita cimodzi-modzi kwa amene akulila. M’bale Dan, amene ni mkulu ku Australia, anati: “Mkazi wanga atamwalila, n’nali kufunikila cilimbikitso. Mabanja angapo anali kubwela usana na usiku kudzanimvetsela. Iwo anali kunilola kulila, ndipo sanacite nane manyazi. Kuwonjezela apo, anadzipeleka kugwila nchito za pakhomo monga kutsuka motoka, kugula zinthu, na kuphika, nikalephela kucita zimenezi panekha. Komanso anali kupemphela nane kaŵili-kaŵili. Iwo anaonetsa kuti ni mabwenzi azoona, komanso abale amene ‘anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”—Miy. 17:17.

ANAGWETSA MISOZI KAAMBA KA ANTHU

10. Fotokozani cocitika ca pa Luka 19:36-40?

10 Pa Nisani 9 mu 33 C.E., Yesu anafika ku Yerusalemu. Atayandikila mzindawu, khamu la anthu linasonkhana, ndipo anthuwo anayala zovala zawo mu msewu povomeleza kuti iye ni Mfumu yawo. Izi zinali zokondweletsa ngako. (Ŵelengani Luka 19:36-40.) Ophunzila ake sanadziŵe zimene zinali kudzatsatilapo. “[Yesu] atayandikila mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo n’kuyamba kuulilila.” Misozi ikulengeza m’maso mwake, Yesu analosela za tsoka lalikulu limene linali kudzagwela anthu okhala mu Yerusalemu.—Luka 19:41-44.

11. N’cifukwa ciani Yesu analilila anthu okhala mu Yerusalemu?

11 Yesu anamva mtima kuŵaŵa cifukwa anadziŵa kuti, mosasamala kanthu kuti anthu anam’landila na manja aŵili, ambili anali ataonetsa kale kuti adzakana kumvetsela uthenga wa Ufumu. Pa cifukwa cimeneci, Yerusalemu anali kudzawonongedwa, ndipo Ayuda opulumuka anali kudzatengedwa ukapolo. (Luka 21:20-24) N’zacisoni kuti anthu ambili anamukana, monga iye anakambila. Kodi anthu amauona motani uthenga wa Ufumu kumene mukhala? Ngati ni ocepa amene amamvetsela mukawalalikila, kodi muphunzilapo ciani pa kugwetsa misozi kwa Yesu? Tiyeni tione maphunzilo enanso atatu.

12. Tiphunzilapo ciani za Yehova pa kugwetsa misozi kwa Yesu kaamba ka anthu?

12Yehova amasamala za anthu. Kugwetsa misozi kwa Yesu, kumatikumbutsa kuti Yehova amasamala kwambili za anthu. Iye “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Masiku ano, timaonetsa kuti timakonda anzathu mwa kuyesetsa kuwauzako uthenga wabwino.—Mat. 22:39.

Muzisinthako nthawi yolalikila, monga Yesu anacitila (Onani ndime 13-14) *

13-14. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cifundo kwa anthu? Nanga tingakulitse motani khalidwe limeneli?

13Yesu anali kugwila nchito yolalikila molimbika. Iye anaonetsa kuti amakonda anthu mwa kulalikila pa mpata uliwonse wapezeka. (Luka 19:47, 48) N’ciani cinamusonkhezela kucita zimenezi? Yesu anali kuwamvelela cifundo. Pa nthawi ina, anthu ambili anali kufuna kumva mawu ake moti iye na ophunzila ake, “sanathe n’komwe kudya cakudya.” (Maliko 3:20) Iye analinso wokonzeka kuphunzitsa anthu usiku—nthawi imene munthu wina anaona kuti ili bwino kwa iye kukamvetsela kwa Yesu. (Yoh. 3:1, 2) Ambili amene poyamba anamvetsela kwa iye sanakhale ophunzila ake, ngakhale kuti anawacitila umboni mokwanila. Nafenso tiyenela kupatsa aliyense mwayi womvetsela uthenga wabwino. (Mac. 10:42) Kuti tikwanilitse zimenezi, tingafunike kusintha mmene timalalikila.

14Khalani okonzeka kusintha. Ngati sitimasinthako nthawi yolalikila, sitingapeze anthu amene angalabadile uthenga wabwino. Mlongo Matilda amene ni mpainiya anati: “Ine na mwamuna wanga timafikila anthu pa nthawi zosiyana-siyana. M’maŵa timalalikila kumalo amalonda. Masana pamene anthu akupitana-pitana, timacita ulaliki wa pa kasitandi. Ndiyeno m’madzulo, timafikila anthu ku nyumba zawo ndipo timawapeza.” M’malo mongotsatila ndandanda yathu, tiyeni tikhale okonzeka kusintha kuti tizilalikila pa nthawi imene tingapeze anthu ambili. Tikatelo, dziŵani kuti Yehova adzakondwela kwambili.

ANAGWETSA MISOZI KAAMBA KA DZINA LA ATATE WAKE

Pemphelani mopembedzela kwa Yehova mukapsinjika maganizo, monga Yesu anacitila (Onani ndime 15-17) *

15. N’ciani cinacitika pa usiku wotsiliza wa Yesu, malinga n’kunena kwa Luka 22:39-44?

15 Usiku wa pa Nisani 14, mu 33 C.E., Yesu anapita ku munda wa Getsemane. Kumeneko, iye anakhuthula za mu mtima mwake kwa Yehova. (Ŵelengani Luka 22:39-44.) Pa nthawi yovuta imeneyi, “anapeleka mapemphelo opembedzela . . . mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Kodi Yesu anapemphelela ciani usiku wotsilizawo asanaphedwe? Iye anapempha mphamvu kuti akhalebe wokhulupilika kwa Yehova, na kucita cifunilo ca Mulungu. Yehova anamva pemphelo locondelela la Mwana wake wopsinjika maganizo, ndipo anatuma mngelo kuti akam’limbikitse.

16. N’cifukwa ciani Yesu anali wopsinjika maganizo popemphela m’munda wa Getsemane?

16 Popemphela m’munda wa Getsemane, Yesu analila cifukwa anali wopsinjika maganizo poganizila mmene anthu anali kumuonela kuti ni wonyoza Mulungu. Cina, anadziŵa kuti ali na udindo waukulu wokweza dzina la Atate wake. Ngati inunso muli mu mkhalidwe wovuta kwambili umene waika kukhulupilika kwanu kwa Yehova pa mayeso, kodi muphunzilapo ciani pa kugwetsa misozi kwa Yesu? Tiyeni tikambilane maphunzilo enanso atatu.

17. Tiphunzilapo ciani za Yehova tikaona mmene anayankhila mapemphelo a Yesu ocokela pansi pa mtima?

17Yehova amamva mapemphelo anu opembedzela. Iye anamvetsela mapemphelo a Yesu ocokela pansi pa mtima. Cifukwa ciani? Cifukwa cofunika kwambili kwa Yesu cinali kukhalabe wokhulupilika kwa Atate wake, na kukweza dzina la Mulungu. Ngati nafenso cofunika kwambili ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, na kukweza dzina lake, iye adzayankha mapemphelo athu.—Sal. 145:18, 19.

18. Kodi Yesu ali ngati bwenzi lokoma mtima komanso lomvetsa m’njila yotani?

18Yesu amamvetsa mmene mumvelela. Tikapsinjika maganizo, timamvela bwino bwenzi lathu limene limamvetsa mmene timvelela likatitonthoza na kutilimbikitsa, maka-maka ngati nalonso linakumanapo na mavuto ofanana na athu. Yesu ni bwenzi lotelo. Iye amadziŵa bwino mmene kukhala wofooka kumamvekela, komanso ukamafunikila thandizo. Amadziŵanso zifooko zathu, ndipo adzaonetsetsa kuti watithandiza “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:15, 16) Monga mmene Yesu analandilila thandizo la mngelo m’munda wa Getsemane, nafenso tizilandila thandizo limene Yehova angapeleke, kaya kupitilila m’zofalitsa, m’mavidiyo, m’nkhani, kapena cilimbikitso ca akulu kapena mnzathu wokhwima kuuzimu.

19. Mungacite ciani kuti mupeze mphamvu mukakumana na vuto lothetsa nzelu, loika kukhulupilika kwanu kwa Mulungu pa mayeso? Fotokozani citsanzo.

19Yehova adzakupatsani ‘mtendele wake.’ Kodi Yehova adzatilimbikitsa motani? Tikamapemphela, tidzalandila “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Mtendele umene Yehova amapeleka umatikhazika mtima pansi, na kutithandiza kukhala oganiza bwino. Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina dzina lake Luz. Iye anati: “Nimalimbana na vuto la kusungulumwa. Nthawi zina, vuto limeneli limanipangitsa kuona kuti Yehova sanikonda. Izi zikacitika, nthawi yomweyo nimauza Yehova mmene nikumvelela. Pemphelo limanithandiza kumvelako bwino.” Citsanzo ca mlongoyu, cionetsa kuti pemphelo limatithandiza kukhala na mtendele wa maganizo.

20. Kodi tatengapo maphunzilo otani pa kugwetsa misozi kwa Yesu?

20 Ni maphunzilo olimbikitsa cotani nanga amene titengapo pa kugwetsa misozi kwa Yesu! Takumbutsidwa kuti tiyenela kulimbikitsa anzathu amene akulila, komanso kukhulupilila Yehova na Yesu kuti adzaticilikiza wokondedwa wathu akamwalila. Talimbikitsidwa kuti tizionetsa cifundo pamene tikulalikila na kuphunzitsa, cifukwa Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni acifundo. Ndipo n’zolimbikitsa kuti Yehova na Mwana wake wokondeka, amamvetsa mmene timvelela, amadziŵa zifooko zathu, ndipo amafuna kutithandiza kupilila. Conco, tiyeni tipitilize kuseŵenzetsa zimene taphunzila mpaka pamene Yehova adzakwanilitse lonjezo lake lokondweletsa lakuti, “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu].”—Chiv. 21:4.

NYIMBO 120 Tengelani Kufatsa kwa Khristu

^ ndime 5 Nthawi zina, Yesu anali kugwetsa misozi cifukwa cokhudzika mtima kwambili. M’nkhani ino, tikambilane zocitika zitatu pamene Yesu anagwetsa misozi, komanso maphunzilo amene titengapo.

^ ndime 1 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu analimbikitsa Mariya na Marita. Nafenso tingacite cimodzimodzi kwa anthu amene wokondedwa wawo anamwalila.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu anadzipeleka kuphunzitsa Nikodemo usiku. Nafenso tiyenela kuphunzila Baibo na ŵanthu pa nthawi imene ingawakomele.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu anapempha mphamvu kuti akhalebe wokhulupilika kwa Yehova. Nafenso tizicita cimodzimodzi tikakumana na mayeso.