Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

‘Cikondi Cimene Khristu Ali Naco Cimatilimbikitsa’

‘Cikondi Cimene Khristu Ali Naco Cimatilimbikitsa’

“Cikondi cimene Khristu ali naco cimatikakamiza [cimatilimbikitsa] . . . kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha.”—2 AKOR. 5:14, 15.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. (a) Kodi timamva bwanji tikaganizila za umoyo na utumiki wa Yesu? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

 MUNTHU amene timam’konda akamwalila, timamuyewa kwambili! Poyamba, cimatiŵaŵa kwambili tikaganizila masiku amene tinali naye atatsala pang’ono kumwalila, maka-maka ngati munthuyo anavutika kwambili. Koma m’kupita kwa nthawi, timapezanso cimwemwe tikaganizila zimene munthuyo anatiphunzitsa, anaticitila, zimene anali kukamba potilimbikitsa kapena kutiseketsa.

2 Mofananamo, timamva cisoni tikaŵelenga za imfa ya Yesu ndiponso mmene anavutikila. Pa nyengo ya Cikumbutso, timaganizila kwambili za kufunika kwa nsembe yake ya dipo. (1 Akor. 11:24, 25) Komabe, timakhalanso na cimwemwe cacikulu tikaganizila zonse zimene Yesu anakamba na kucita ali padziko lapansi. Cina, timalimbikitsidwa tikaganizila zimene akucita palipano, komanso zimene adzaticitila kutsogolo. Kuganizila zinthu zimenezi na cikondi cake pa ife, kungatilimbikitse kuti tionetse ciyamikilo cathu, monga tionele m’nkhani ino.

KUYAMIKILA KUMATILIMBIKITSA KUTSATILA YESU

3. Kodi tili na zifukwa ziti zoyamikila dipo?

3 Timakhala oyamikila tikaganizila za umoyo wa Yesu na imfa yake. Pa utumiki wake wonse ali padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa anthu za madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa. Timayamikila kwambili madalitso a Ufumu amenewo. Ndife othokoza kaamba ka dipo, cifukwa linatitsegulila njila kuti tikhale pa ubwenzi wolimba na Yehova komanso Yesu. Aja amene amaika cikhulupililo cawo mwa Yesu alinso na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya, na kuonanso okondedwa awo amene anamwalila. (Yoh. 5:28, 29; Aroma 6:23) Sitinacite kalikonse kuti tiyenelele madalitso amenewa. Ndipo palibe cimene tingalipile Mulungu na Yesu pa zimene iwo anaticitila. (Aroma 5:8, 20, 21) Koma tingawaonetse kuzama kwa cikondi cathu pa iwo. Motani?

Kodi kusinkhasinkha citsanzo ca Mariya Mmagadala kungakulimbikitseni bwanji kuonetsa kuyamikila? (Onani ndime 4-5)

4. Kodi Mariya Mmagadala anaonetsa bwanji kuyamikila pa zimene Yesu anam’citila? (Onani cithunzi.)

4 Ganizilani citsanzo ca mayi wina waciyuda dzina lake Mariya Mmagadala. Mayiyu anali na vuto lalikulu, cifukwa ziŵanda 7 zinali kumuvutitsa koopsa. Ayenela kuti anaona kuti palibe angam’thandize. Ndiyeno ganizilani mmene anakhalila woyamikila Yesu atam’tulutsa ziŵandazo n’kumasuka! Kuyamikila kunam’limbikitsa kukhala wophunzila wake, kuseŵenzetsa nthawi, mphamvu, na zinthu zake kuti athandize Yesu pa utumiki wake. (Luka 8:1-3) Ngakhale kuti Mariya anayamikila kwambili zimene Yesu anam’citila, ayenela kuti sanadziŵe kuti Yesu anali kudzam’citila zazikulu koposa m’tsogolo. Iye anali kudzapeleka moyo wake kaamba ka anthu, “kuti aliyense wokhulupilila iye” akasangalale na moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Ngakhale n’telo, Mariya anaonetsa ciyamikilo cake kwa Yesu mwa kukhala wokhulupilika. Pamene Yesu anali kuvutika pamtengo wozunzikilapo, Mariya anaima capafupi kuti amulimbikitse na kutonthoza ena. (Yoh. 19:25) Yesu atafa, Mariya na azimayi ena aŵili anapeleka zonunkhila ku manda a Yesu kuti akapake thupi lake. (Maliko 16:1, 2) Mariya anadalitsidwa cifukwa ca kukhulupilika kwake. Iye anakondwela kuona Yesu atangoukitsidwa kumene komanso kulankhula naye. Uwu unali mwayi umene ophunzila ambili sanakhale nawo.—Yoh. 20:11-18.

5. Tingaonetse bwanji kuyamikila pa zonse zimene Yehova na Yesu aticitila?

5 Ifenso tingaonetse ciyamikilo cathu pa zonse zimene Yehova na Yesu aticitila, mwa kugwilitsa nchito nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu kuti tipititse patsogolo nchito ya Ufumu. Mwacitsanzo, tingadzipeleke kuti tithandize pa nchito zomanga malo olambilila Yehova, komanso kusamalila malowo.

KUKONDA YEHOVA NA YESU KUMATILIMBIKITSA KUKONDA ENA

6. N’cifukwa ciyani tingati dipo ni mphatso ya munthu aliyense payekha?

6 Tikaganizila mmene Yehova na Yesu amatikondela, ifenso timalimbikitsidwa kuwakonda. (1 Yoh. 4:10, 19) Timawakonda kwambili tikaganizilanso zakuti Yesu anafela aliyense wa ife payekha. Mtumwi Paulo anavomeleza mfundoyi, ndipo anaonetsa ciyamikilo cake m’kalata imene analembela Agalatiya. Iye anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agal. 2:20) Pa maziko a dipo limenelo, Yehova anakukokelani kwa iye kuti mukhale bwenzi lake. (Yoh. 6:44) Kodi sizikulimbikitsani kudziŵa kuti Yehova anaona cina cake cabwino mwa inu, ndipo anapeleka malipilo okwela kwambili kuti mukhale bwenzi lake? Kodi izi sizikupangitsani kukulitsa cikondi canu pa Yehova na Yesu? Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi cikondico cidzanilimbikitsa kucita ciyani?’

Cikondi cathu pa Mulungu na Khristu cimatilimbikitsa kuuzako munthu aliyense uthenga wabwino wa Ufumu (Onani ndime 7))

7. Monga tikuonela pa cithunzi, kodi tonsefe tingaonetse bwanji cikondi cathu pa Yehova na Yesu? (2 Akorinto 5:14, 15; 6:1, 2)

7 Cikondi cathu pa Mulungu na Khristu cimatilimbikitsa kuonetsa ena cikondi. (Ŵelengani 2 Akorinto 5:14, 15; 6:1, 2.) Imodzi mwa njila zimene tingaonetsele cikondi cathu ni kukangalika pa nchito yolalikila. Timalalikila aliyense amene takumana naye. Polalikila siticita tsankho. Timakamba na aliyense mosayang’ana khungu, mtundu, cuma, kapena maphunzilo. Mwa ici, timacita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Yehova “cakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.”—1 Tim. 2:4.

8. Tingaonetse motani cikondi kwa abale na alongo athu?

8 Timaonetsanso cikondi cathu pa Mulungu na Khristu mwa kukonda abale na alongo athu. (1 Yoh. 4:21) Timasamala kwambili za iwo, ndipo timawathandiza akakumana na mavuto. Cina, timawatonthoza munthu amene amam’konda akamwalila, kupita kukawaona akadwala, komanso kuyesetsa kuwalimbikitsa akalefuka. (2 Akor. 1:3-7; 1 Ates. 5:11, 14) Ndiponso timapitiliza kuwapemphelela, podziŵa kuti “pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.”—Yak. 5:16.

9. Ni njila ina iti imene tingaonetsele cikondi kwa abale na alongo athu?

9 Timaonetsanso cikondi kwa abale na alongo athu mwa kuyesetsa kukhala nawo pa mtendele. Timayesetsa kutengela citsanzo ca Yehova ca kukhululuka. Yehova mofunitsitsa anapeleka Mwana wake kuti afe kaamba ka macimo athu. Conco, nafenso tiyenela kukhala ofunitsitsa kukhululukila abale na alongo athu akatilakwila. Sitifuna kukhala monga kapolo woipa wochulidwa m’fanizo lina la Yesu. Ngakhale kuti mbuye wake anam’khululukila nkhongole yaikulu kwambili, kapoloyo analephela kukhululukila kapolo mnzake nkhongole yaing’ono. (Mat. 18:23-35) Ngati munasemphana maganizo na wina mumpingo, bwanji osayamba ndinu kukhazikitsa mtendele Cikumbutso cisanacitike? (Mat. 5:23, 24) Mukacita izi, mudzaonetsa kuti mumam’konda kwambili Yehova na Yesu.

10-11. Kodi akulu angaonetse motani cikondi cawo pa Yehova na Yesu? (1 Petulo 5:1, 2)

10 Kodi akulu angaonetse bwanji kuti amakonda Yehova na Yesu? Njila imodzi yofunika ni kusamalila zosoŵa za nkhosa za Yesu. (Ŵelengani 1 Petulo 5:1, 2.) Yesu anaimveketsa bwino mfundoyi kwa mtumwi Petulo. Pambuyo pokana Yesu katatu, Petulo ayenela kuti anali kufunitsitsa kuonetsa kuti amam’konda Yesu. Yesu ataukitsidwa, anafunsa Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Sitikayikila kuti Petulo anali wokonzeka kucita ciliconse poonetsa kuti anali kukonda Mbuye wake. Yesu anauza Petulo kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Pa umoyo wake wonse, Petulo anasamalila nkhosa za Ambuye mwacikondi, poonetsa kuti anali kum’konda Yesu.

11 Inu akulu, kodi mungaonetse bwanji kuti mawu amene Yesu anauza Petulo ni ofunika kwa inu pa nyengo ya Cikumbutso? Mungaonetse kuti mumam’konda Yehova na Yesu, mwa kucita maulendo aubusa nthawi zonse, komanso kuyesetsa kuthandiza ozilala kubwelela kwa Yehova. (Ezek. 34:11, 12) Cina, mungaonetse cidwi kwa ophunzila Baibo komanso okondwelela amene adzabwela ku Cikumbutso, mwa kuwalandila mwacimwemwe ophunzila a Yesu a m’tsogolo amenewa.

CIKONDI CATHU PA KHRISTU CIMATILIMBIKITSA KUKHALA OLIMBA MTIMA

12. N’cifukwa ciyani kuganizila mawu amene Yesu anakamba usiku wakuti aphedwa maŵa kungatithandize kukhala olimba mtima? (Yohane 16:32, 33)

12 Usiku wakuti maŵa lake aphedwa, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.” (Ŵelengani Yohane 16:32, 33.) N’ciyani cinathandiza Yesu kulimba mtima adani ake atamuopseza, na kukhalabe wokhulupilika mpaka imfa yake? Anadalila Yehova. Podziŵa kuti otsatila ake adzakumana na mayeso ngati amenewa, Yesu anapempha Yehova kuti awayang’anile. (Yoh. 17:11) N’cifukwa ciyani mfundoyi itithandiza kukhala olimba mtima? Cifukwa Yehova ni wamphamvu kwambili kuposa mdani wathu aliyense. (1 Yoh. 4:4) Ndipo iye amaona zonse. Mwa ici, sitikayikila konse kuti tikam’dalila Yehova, tingathetse mantha athu na kuonetsa kulimba mtima.

13. Kodi Yosefe wa ku Arimateya anaonetsa bwanji kulimba mtima?

13 Ganizilani citsanzo ca Yosefe wa ku Arimateya. Iye anali munthu wolemekezeka kwa Ayuda. Anali mmodzi wa oweluza m’khoti Yapamwamba ya Ayuda. Koma pamene Yesu anali kucita utumiki wake padziko lapansi, Yosefe anali wamantha. Yohane ananena kuti iye anali “wophunzila wa Yesu koma wamseli cifukwa anali kuopa Ayuda.” (Yoh. 19:38) Ngakhale kuti Yosefe anacita cidwi na uthenga wa Ufumu, anali kudzibisa kwa ena kuti asadziŵike kuti anali na cikhulupililo mwa Yesu. Mosakayikila, iye anali kuopa kuti angataye udindo wake ndipo anthu angaleke kum’lemekeza. Koma Baibo imatiuza kuti Yesu atafa, Yosefe tsopano “anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo wa Yesu.” (Maliko 15:42, 43) Apa Yosefe sanadzibisenso kuti anali wophunzila wa Yesu.

14. Kodi muyenela kucita ciyani ngati mumaopa anthu?

14 Kodi nthawi zina mumaopa anthu monga anacitila Yosefe? Kodi mumacita mantha kuuza ena kuti ndinu Mboni ya Yehova kusukulu kapena kunchito? Kodi mukuzengeleza kukhala wofalitsa kapena kubatizika, cifukwa codela nkhawa mmene ena angakuoneleni? Musalole zimenezi kukulepheletsani kucita zimene mudziŵa kuti ndiye zoyenela. Pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. M’pempheni kuti akulimbitseni mtima kuti mucite cifunilo cake. Mukamaona kuti Yehova akuyankha mapemphelo anu, mudzakhala amphamvu ndipo mudzalimba mtima kwambili.—Yes. 41:10, 13.

CIMWEMWE CIMATILIMBIKITSA KUPITILIZA KUTUMIKILA YEHOVA

15. Yesu ataonekela kwa ophunzila ake, kodi cimwemwe cawo cinaŵalimbikitsa kucita ciyani? (Luka 24:52, 53)

15 Yesu atafa, ophunzila ake anali na cisoni kwambili. Yelekezani kuti munali mmodzi wa ophunzilawo. Iwo anatayikilidwa bwenzi lawo lokondeka, ndipo anamva monga kuti ciyembekezo cawo naconso catayika. (Luka 24:17-21) Komabe, Yesu ataonekela kwa iwo anathela nthawi yoculuka powathandiza kumvetsa mmene iye anakwanilitsila maulosi a m’Baibo. Anawapatsanso nchito yofunika kwambili. (Luka 24:26, 27, 45-48) Pambuyo pa masiku 40, Yesu anakwela kupita kumwamba, ndipo ophunzilawo sanakhalenso na cisoni koma cimwemwe cacikulu. Kudziŵa kuti Mbuye wawo ali moyo, ndipo ni wokonzeka kuŵathandiza kugwila nchito yawo yatsopano imene anawapatsa, kunawabweletsela cimwemwe. Cimwemwe cawo cinaŵalimbikitsa kutamanda Mulungu mosalekeza.—Ŵelengani Luka 24:52, 53; Mac. 5:42.

16. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca ophunzila a Yesu?

16 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca ophunzila a Yesu? Ifenso tingapeze cimwemwe polambila Yehova caka conse, osati cabe pa nyengo Cikumbutso. Kuti izi zitheke tiyenela kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, ena amapanga masinthidwe pa magwilidwe awo a nchito kuti azipeza nthawi yolalikila, kupezeka ku misonkhano, na kucita kulambila kwa pa banja mokhazikika. Ena amadzimana zinthu zina zakuthupi zimene ena amaona kuti n’zofunika. Iwo amacita izi kuti akhale na zocita zambili mumpingo, kapena kuti apite kukatumikila kumene kuli alengezi a Ufumu ocepa. Ngakhale kuti tifunikila kupilila kuti tipitilize kutumikila Yehova, iye analonjeza kuti adzatidalitsa kwambili tikamaika Ufumu patsogolo mu umoyo wathu.—Miy. 10:22; Mat. 6:32, 33.

Pa nyengo ya Cikumbutso, patulani nthawi yosinkhasinkha zimene Yehova na Yesu akucitilani inu pacanu (Onani ndime 17)

17. Kodi mudzayesetsa kucita ciyani pa nyengo ino ya Cikumbutso? (Onani cithunzi.)

17 Tiyembekezela mwacidwi kudzacita Cikumbutso pa Ciŵili, April 4. Komabe, musayembekezele mpaka nthawi ya Cikumbutso kuti mudzayambe kuganizila za umoyo wa Yesu na imfa yake, komanso za cikondi cimene iye na Yehova anationetsa. Muzicita zimenezi kaŵili-kaŵili pa nyengo yonse ya Cikumbutso. Mwacitsanzo, muzipatula nthawi yoŵelenga na kusinkhasinkha zocitika za pa umoyo wa Yesu zofotokozedwa m’nkhani yakuti, “Kodi Mudzakonzekela Bwanji Cikumbutso?” yopezeka m’kabuku ka Umoyo na Utumiki ka April, 2019 tsamba 4. Pamene muŵelenga zocitikazo, yesani kupeza mfundo za m’Baibo zokuthandizani kukulitsa ciyamikilo na cikondi canu, kukuwonjezelani cimwemwe, komanso kukulimbitsani mtima. Ndiyeno pezani njila zimene mungaonetsele kuyamikila mocokela pansi pa mtima. Mungakhale otsimikiza kuti Yesu adzayamikila kwambili zonse zimene mudzacita pomukumbikila pa nyengo ino ya Cikumbutso.—Chiv. 2:19.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

a Pa nyengo ya Cikumbutso, timalimbikitsidwa kuganizila za umoyo wa Yesu, imfa yake, komanso cikondi cimene iye na Atate wake anationetsa. Kucita zimenezi kungatilimbikitse kucita zinthu zoonetsa ciyamikilo cathu pa iwo. Nkhani ino, ifotokoze mmene tingaonetsele cikondi cathu pa Yehova na Yesu, komanso kuyamikila dipo. Tionenso cimene cingatilimbikitse kukonda abale na alongo athu, kuonetsa kulimba mtima, komanso kupeza cimwemwe mu utumiki wathu.