NKHANI YOPHUNZILA 1
Khalani Otsimikiza Kuti ‘Mawu a Mulungu Ndi Coonadi’
LEMBA LA CAKA CA 2023: “Mawu anu onse ndi coonadi cokha-cokha.”—SAL. 119:160.
NYIMBO 96 Buku Lake la Mulungu Ni Cuma
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. N’cifukwa ciyani anthu ambili masiku ano saikhulupilila Baibo?
ANTHU ambili masiku ano zimawavuta kukhulupilila anthu ena. Iwo amakayikila ngati andale, asayansi, komanso amalonda amawafuniladi zabwino. Kuwonjezela apo, iwo sawadalila atsogoleli acipembedzo acikhristu. Conco, n’zosadabwitsa kuti saikhulupilila Baibo, buku limene atsogoleli acipembedzowo amati amatsatila.
2. Malinga na Salimo 119:160, kodi tiyenela kukhala otsimikiza za ciyani?
2 Pokhala atumiki a Yehova, ndife otsimikiza kuti iye ni “Mulungu wa coonadi,” ndipo nthawi zonse amatifunila zabwino. (Sal. 31:5; Yes. 48:17) Timakhulupilila zimene timaŵelenga m’Baibo, cifukwa tidziŵa kuti: “Mawu onse [a Mulungu] ndi coonadi cokha-cokha.” b (Ŵelengani Salimo 119:160.) Tingagwilizane naye katswili wina wa Baibo pa zimene analemba. Iye anati: “Pa ciliconse cimene Mulungu angakambe kuti adzacita, sipakhala bodza lililonse kapena kulephela kulikonse ayi. Anthu a Mulungu amakhulupilila zimene iye wanena, cifukwa amakhulupilila Mulungu amene wanena zimenezo.”
3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Tingawathandize bwanji anthu ena kukhulupilila Mawu a Mulungu mmene ife timacitila? Tiyeni tikambilane zifukwa zitatu zimene zimatipangitsa kuikhulupilila Baibo. Tikambilane za kulondola kwa mawu ake, kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo, komanso mphamvu ya Baibo yosintha anthu.
UTHENGA WA M’BAIBO NI WOLONDOLA NDIPO SUNASINTHE
4. N’cifukwa ciyani anthu ena amakaikila kuti uthenga wa m’Baibo ni wolondola?
4 Yehova Mulungu anagwilitsa nchito amuna okhulupilika pafupifupi 40 kuti alembe mabuku a m’Baibo. Komabe, palibe mipukutu yoyambilila imene yapulumuka mpaka masiku athu ano. Onse amene tili nawo masiku ano ni makope a makope ena. Izi zimapangitsa anthu ena kukayikila ngati zimene timaŵelenga m’Baibo masiku ano, n’zogwilizana molondola na uthenga wake woyambilila. Tingatsimikize bwanji masiku ano kuti zimene Baibo imakamba n’zoonadi?
5. Kodi Malemba Aciheberi anakopeledwa motani? (Onani cithunzi pacikuto.)
5 Pofuna kuteteza uthenga wake wouzilidwa, Yehova anauza anthu ake kuti aziukopela uthengawo. Iye analamula mafumu aciisiraeli kukopela mabuku awo-awo a Cilamulo, komanso anaika a Levi kuti aziphunzitsa anthu Cilamuloco. (Deut. 17:18; 31:24-26; Neh. 8:7) Ayuda atatengeledwa ku ukapolo ku Babulo, kagulu ka akatswili okopela zolembedwa kanayamba kupanga makope ambili a Malemba Aciheberi. (Ezara 7:6) Amuna amenewa anali kukopela zolembedwa mosamala. M’kupita kwa nthawi, akatswiliwa sanali kungoŵelenga cabe mawu amene anawakopelawo, koma anali kuŵelenganso cilembo ciliconse pofuna kutsimikiza kuti zonse zimene anakopelazo zinali zolondola. Ngakhale n’telo, cifukwa ca kupanda ungwilo, twina n’twina tunalakwika pokopela Malemba. Komabe, panapangidwa makope ambili a Malemba amenewa. Conco tolakwikato tunadziŵika pambuyo pake. Motani?
6. Kodi zolakwika za m’makope a Baibo zinadziŵika bwanji?
6 Akatswili a Baibo amakono anapeza njila ya bwino yodziŵila zolakwika zimene zinakhalapo pokopela malemba a m’Baibo. Mwacitsanzo: Tiyelekeze kuti anthu 100 auzidwa kuti akopolole mawu onse a tsamba limodzi la buku, ndiyeno mmodzi wa iwo walakwitsa kambali kocepa pokopolola. Njila imodzi tingadziŵile kambali kolakwikako, ni kuyelekezela kope la munthuyo na makope a anzake. Mofananamo, poyelekezela mipukutu yambili ya Baibo, akatswili a Baibo amatha kudziŵa zolakwika zimene wokopela mmodzi anapanga.
7. N’cifukwa ciyani tinganene kuti okopela Baibo ambili anakopela Malemba molondola?
7 Amene anali kukopela mipukutu ya Baibo anayesetsa kucita zimenezo molondola kwambili. Onani citsanzo ici cotsimikizila mfundoyi. Mpukutu wakale kwambili wathunthu wa olemba Aciheberi, unakopololedwa mu 1008 kapena mu 1009 C.E. Mpukutuwo umachedwa Leningrad Codex. Komabe, m’zaka zaposacedwa apeza mipukutu ya Baibo komanso mbali zake zimene zakhalapo zaka pafupi-fupi 1,000 kuposa mpukutu wa Leningrad Codex. Ena angaganize kuti popeza mipukutu imeneyi inajambulidwa-jambulidwa kwambili pa nyengo ya zaka 1,000, ndiye kuti mawu a mu Leningrad Codex safanana kwenikweni na mipukutu yamakedzana. Koma zimenezi si zoona. Akatswili a Baibo amene anali kuyelekezela mabuku amakedzana na mipukutu yamakono anapeza kuti, ngakhale kuti pali kusiyana kocepa m’kalembedwe, uthenga wa m’Baibo sunasinthe.
8. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa makope a Malemba Acigiriki Acikhristu na makope ena amakedzana?
8 Nawonso Akhristu oyambilila anatengela citsanzo ca akatswili okopolola Malemba Aciheberi. Iwo anakopolola mabuku 27 a Malemba Acigiriki, amene anali kugwilitsa nchito pa misonkhano yawo komanso mu ulaliki. Katswili wina wa Baibo atayelekezela mipukutu ya Malemba Acigiriki na zolemba zina za panthawi imene mipukutuyo inalembedwa anati: “Mwacidule, pali mipukutu yambili komanso yathunthu ya [Malemba Acigiriki], . . . kuposa mabuku ena akale.” Buku lakuti Anatomy of the New Testament limati: “Tingakhale otsimikiza kuti zimene timaŵelenga m’Baibo yamakono ya [Malemba Acigiriki], n’zimenenso analemba olemba oyambilila.”
9. Kodi pa Yesaya 40:8, pali mfundo yanji yosatsutsika yokhudza uthenga wa m’Baibo?
9 Khama na luso la anthu ambili odziŵa kukopolola zolembedwa panyengo ya zaka mahandiledi, linapangitsa kuti Baibo imene timaŵelenga na kuphunzila masiku ano ikhale yolondola kwambili. c Mosakayika konse, ni Yehova amene anaonetsetsa kuti uthenga wake kwa anthu usasinthe ndipo ukhalebe wolondola. (Ŵelengani Yesaya 40:8.) Koma ena anganene kuti ngakhale kuti uthenga wa m’Baibo sunasinthe, izi sizitanthauza kuti uthengawo unauzilidwa na Mulungu. Tsopano tiyeni tione ena mwa maumboni otsimikizila kuti Mulungu ndiye anauziladi Baibo.
MAULOSI A M’BAIBO NI ODALILIKA
10. Fotokozani citsanzo ca ulosi umene unakwanilitsika, zimene zitsimikizila kuti mawu a pa 2 Petulo 1:21 ni oona. (Onani zithunzi.)
10 M’Baibo muli maulosi ambili amene anakwanilitsika. Ena mwa maulosiwo anakwanilitsika patapita zaka mahandiledi pambuyo polembedwa. Mbili yakale imatsimikizila kuti maulosi amenewa anakwanilitsikadi. Izi sitidabwa nazo cifukwa tidziŵa kuti maulosi a m’Baibo amacokela kwa Yehova. (Ŵelengani 2 Petulo 1:21.) Ganizilani za maulosi okhudza kugwa kwa mzinda wamakedzana wa Babulo. Capakati pa zaka za 778 B.C.E komanso 732 B.C.E., mneneli Yesaya mouzilidwa analosela kuti mzinda wamphamvu wamakedzana umenewo wa Babulo udzagonjetsedwa. Iye anachula ngakhale dzina la amene adzaugonjetse kuti adzakhala Koresi, ndipo anakambilatu mwatsatanetsane mmene mzindawo udzagonjetsedwele. (Yes. 44:27–45:2) Cina, Yesaya analoselanso kuti Babulo adzawonongedwa, ndipo adzasiyidwa ali bwinja mpaka kale-kale. (Yes. 13:19, 20) izi n’zimene zinacitikadi. Mu 539 B.C.E., mzinda wa Babulo unagonjetsedwa na Amedi komanso Aperisiya. Pamalo pamene panali mzinda wamphamvu umenewo, lelo ni matongwe okha-okha.—Onani vidiyo yakuti Baibo Inalosela za Kuwonongedwa kwa Babulo m’buku la pacipangizo lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! m’phunzilo 03 mfundo 5.
11. Fotokozani mmene Danieli 2:41-43 likukwanilitsikila masiku ano.
11 Maulosi a m’Baibo sanangokwanilitsika kalelo ayi, koma akukwanilitsikanso masiku ano. Mwacitsanzo, ganizilani za kukwanilitsika kocititsa cidwi kwa ulosi wa Danieli wokhudza ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America. (Ŵelengani Danieli 2:41-43.) Ulosi umenewo unakambilatu bwino-bwino kuti ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America, pa zinthu zina udzakhala wolimba ‘ngati citsulo,’ koma pa zina udzakhala wosalimba ngati “dongo,” kapena kuti [dothi]. Ndipo izi tikuzionadi masiku ano. Ulamulilo wa Britain na America wakhala wamphamvu ngati citsulo. Iwo ndiwo anali patsogolo pa kupambana nkhondo zonse ziŵili za padziko lonse, ndipo akupitilizabe kukhala amphamvu pa nkhondo. Ngakhale n’telo, nzika zawo zikucepetsa mphamvu za ulamulilo wawo. Nzika zawozo zimacita makampeni osiyana-siyana omenyela maufulu a anthu. Katswili wina wa zandale caposacedwa anati: “Dziko la America n’lotsogola pa nkhani ya ulamulilo wa demokalase. Koma n’logaŵikana kwambili pa zandale kuposa dziko lina lililonse.” Ndipo dziko la Britain, mbali ina ya ulamulilo wamphamvu padziko lonse, m’zaka zaposacedwapa lagaŵikana cifukwa cakuti nzika zake zikutsutsana ponena za mgwilizano, umene dziko lawo liyenela kukhala nawo na maiko a m’bungwe la European Union. Magaŵano amenewa apangitsa kuti cikhale covuta ngako ulamulilo wa Britain na America kucita zinthu mwamphamvu kwambili.
12. Kodi maulosi a m’Baibo amatitsimikizila ciyani?
12 Maulosi ambili a m’Baibo amene akwanilitsika kale amalimbitsa cidalilo cathu kuti malonjezo a Mulungu okhudza tsogolo lathu adzakwanilitsika. Timamva mmene anamvela wamasalimo amene anapemphela kwa Yehova kuti: ‘Ndikulakalaka cipulumutso canu, pakuti ndayembekezela mawu anu.’ (Sal. 119:81) Kupyolela m’Baibo, Yehova mokoma mtima watipatsa “ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Ciyembekezo cathu ca za mtsogolo sicidalila zoyesa-yesa za anthu koma pa malonjezo a Yehova. Tiyeni tipitilize kulimbitsa cikhulupililo cathu m’Mawu a Mulungu mwa kuphunzila maulosi a m’Baibo mwakhama.
ULANGIZI WA M’BAIBO UKUTHANDIZA ANTHU MAMILIYONI
13. Malinga na Salimo 119:66, 138, ni umboni wina uti umene umatitsimikizila kuti Baibo ni yodalilika?
13 Umboni wina umene watithandiza kuikhulupilila Baibo, ni zotulukapo zabwino zimene zimakhalapo anthu akamaseŵenzetsa uphungu wake. (Ŵelengani Salimo 119:66, 138.) Mwacitsanzo, okwatilana amene panthawi ina anatsala pang’ono kusudzulana, tsopano ni ogwilizana ndipo ni acimwemwe. Ana awo lomba amakondwela kukhala m’banja lacikhristu mmene makolo awo amawasamalila bwino na kuwakonda.—Aef. 5:22-29.
14. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene kuseŵenzetsa mfundo za coonadi ca m’Baibo kumasinthila anthu kukhala abwino.
14 Kuseŵenzetsa nzelu zothandiza za m’Baibo kwathandiza ngakhale zigaŵenga zoopsa kusinthilatu umoyo wawo. Onani mmene uphungu wake unathandizila mkaidi wina dzina lake Jack. d Iye anali cigananga cankhanza, ndipo anali mmodzi wa akaidi oopsa kwambili amene anagamulidwa kuti anyongedwe. Koma tsiku lina, Jack anapezekapo pamene Mboni zinali kuphunzitsa Baibo. Kukoma mtima kumene abale anaonetsa potsogoza phunzilolo kunam’khudza mtima kwambili Jack, ndipo nayenso anayamba kuphunzila nawo. Pomwe anayamba kuseŵenzetsa mfundo za coonadi ca m’Baibo mu umoyo wake, khalidwe lake na umunthu wake zinayamba kusinthila kwabwino. M’kupita kwa nthawi, iye anayenelela kukhala wofalitsa wosabatizika, ndipo pambuyo pake anabatizika. Anayamba kulalikila mokangalika za Ufumu wa Mulungu kwa akaidi anzake, ndipo anathandiza anayi mwa iwo kuphunzila coonadi. Pamene tsiku la kunyongedwa kwake linafika, Jack anali atasintha kwambili. Mmodzi wa maloya ake anati: “Jack lomba wasintha kwambili kusiyana na mmene n’nali kumudziŵila zaka 20 kumbuyoku. Zimene anali kuphunzila kwa Mboni za Yehova zasintha umoyo wake.” Ngakhale kuti Jack ananyongedwa ndithu, citsanzo cake cionetsa kuti tingawakhulupilile Mawu a Mulungu, ndiponso kuti ali na mphamvu yosintha anthu kukhala abwino.—Yes. 11:6-9.
15. Kodi kugwilitsa nchito mfundo za coonadi ca m’Baibo kumawasiyanitsa bwanji anthu a Mulungu masiku ano na anthu a m’dzikoli? (Onani cithunzi.)
15 Anthu a Yehova ni ogwilizana, cifukwa amagwilitsa nchito mfundo za coonadi ca m’Baibo. (Yoh. 13:35; 1 Akor. 1:10) Mtendele na mgwilizano wathu zimaonekela bwino kwambili cifukwa anthu m’dzikoli ni ogaŵikana pa zandale, amasankhana mitundu, komanso amasalana cifukwa cosiyana mapezedwe. Mnyamata wina dzina lake Jean, anakopeka mtima kwambili ataona mgwilizano pakati pathu. Iye anakulila mu Africa. Nkhondo ya paciweniweni itabuka m’dziko lawo analoŵa usilikali. Koma pambuyo pake anathaŵila ku dziko lina lapafupi. Kumeneko anakumana na Mboni za Yehova. Jean anati: “N’naphunzila kuti anthu a m’cipembedzo coona satengako mbali m’zandale ndipo si ogaŵikana. M’malo mwake, iwo amakondana.” Iye anapitiliza kuti: “N’nadzipeleka kuloŵa usilikali kuti niteteze dziko lathu. Koma coonadi ca m’Baibo cimene n’naphunzila cinanilimbikitsa kupatulila moyo wanga kwa Yehova.” Jean anasinthilatu. M’malo mocita nkhondo na anthu osiyana na mtundu wake, iye amauzako aliyense uthenga wa coonadi wogwilizanitsa anthu. Kudziŵa kuti mfundo za m’Baibo n’zothandiza kwambili ku mitundu yosiyana-siyana, ni umboni wamphamvu wakuti Mawu a Mulungu tingawakhulupililedi.
PITILIZANI KUKHULUPILILA MAWU A MULUNGU A COONADI
16. N’cifukwa ciyani n’kofunika kwambili kuti tilimbitse cikhulupililo cathu m’Mawu a Mulungu?
16 Pamene dzikoli likuipilaipila, kukhulupilila kwathu mawu a coonadi kudzayesedwa. Anthu angayese kubyala mbewu za cikayiko mumtima mwathu. Iwo angafune kuti tizikayikila zakuti Baibo ni yolondola, kapena kukayikila ngati Yehova anaikadi kapolo wokhulupilika ndi wanzelu kutsogolela alambili ake masiku ano. Koma tikakhala otsimikiza kuti nthawi zonse Mawu a Yehova ni oona, tidzatha kukana mayeso ngati amenewo ofooketsa cikhulupililo cathu. M’malo mwake, ‘tidzatsimikiza mtima kutsatila malangizo a [Yehova], mpaka kale-kale, ndithu kwa moyo wathu wonse.’ (Sal. 119:112) ‘Sitidzacita manyazi’ kuuzako ena mfundo za coonadi ca m’Baibo na kukhala umoyo wogwilizana na mfundozo. (Sal. 119:46) Kuwonjezela apo, tidzatha kupilila mavuto aakulu kuphatikizapo mazunzo, ‘moleza mtima komanso mwacimwemwe.’—Akol. 1:11; Sal. 119:143, 157.
17. Kodi lemba la caka cino lizitikumbutsa ciyani?
17 Tikuthokoza cotani nanga kuti Yehova watiphunzitsa coonadi! Coonadi cimeneci cimatithandiza kukhala osatekeseka komanso acidalilo. Ndiponso cimatithandiza mmene tingakhalile m’dzikoli limene cipwilikiti na mipungwepungwe zikuwonjezekabe. Cimatipatsanso ciyembekezo ca tsogolo labwino pansi pa ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu. Lekani kuti lemba la caka ca 2023 litithandize kuima zolimba pa citsimikizo cathu cakuti Mawu onse a Mulungu ni coonadi cokha-cokha!—Sal. 119:160.
NYIMBO 94 Tiyamikila Mau a Mulungu
a Lemba la caka ca 2023 n’lolimbitsa cikhulupililo. N’lakuti: “Mawu anu onse ndi coonadi cokha-cokha.” (Sal. 119:160) Mosakayika, mukuvomeleza mfundoyi. Koma anthu ambili sakhulupilila kuti Baibo ili na coonadi, ndiponso kuti lingatipatse citsogozo codalilika. M’nkhani ino, tikambilane maumboni atatu amene tingaseŵenzetse potsimikizila anthu oona mtima, kuti angaikhulupililedi Baibo na upangili wake.
b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Liwu la Ciheberi limene analimasulila kuti “onse” pa vesili litanthauza thunthu la cinthu.
c Kuti mudziŵe zambili za mmene uthenga wa m’Baibo unatetezekela, pitani pa jw.org na kulemba m’danga lofufuzila kuti, “Kodi Baibo anaisintha kapena anangoisinthako zina?”
d Maina ena asinthidwa.