Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu:

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu:

Kodi mumakonda kuŵelenga nkhani zakuti “Mbili Yanga”?

M’maŵa uliwonse, m’bale wina na mkazi wake amaŵelenga nkhani imodzi, pa nkhani zakuti “Mbili Yanga.” Iwo anati: “Nkhani zimenezi zimatibweletsela cimwemwe komanso zimatilimbikitsa kwambili. Zimatikumbutsa kuti nafenso tingakhalebe okhulupilika pa mkhalidwe uliwonse umene tingakumane nawo.” Mlongo wina analemba kuti: “Nkhanizi n’zotonthoza, zolimbikitsa, komanso n’zogwila mtima. Abale na alongo athu amenewo amakhala na umoyo waphindu komanso watanthauzo. Nkhani zawo zimanilimbikitsa kucita zambili mu utumiki, komanso zimanithandiza kulimbikitsa ana anga kutumikila Yehova mwa kucita utumiki wa nthawi zonse.”

Nkhani zakuti “Mbili Yanga” zingakulimbikitseni kudziikila zolinga zabwino m’gulu la Mulungu, kugonjetsa zifooko, komanso kupilila mayeso aakulu mwacimwemwe. Kodi nkhani zimenezi mungazipeze kuti?

  • Pitani pa jw.org na kufufuza nkhani zakuti “Mbili Yanga.

  • Kapena mungazifufuze pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower.