NKHANI YOPHUNZILA 3
NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse
Yehova Adzakuthandizani m’Nthawi Zovuta
“Kukhulupilika [kukhazikika mwa Yehova] kudzabweletsa cipulumutso cacikulu.”—YES. 33:6.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zimene tiyenela kucita kuti tipindule na thandizo la Yehova m’nthawi zovuta.
1-2. Ni zovuta ziti zimene atumiki okhulupilika a Yehova angakumane nazo?
MAVUTO aakulu akatigwela, moyo wathu ukhoza kusintha m’kanthawi kocepa. Mwacitsanzo, m’bale wina wokhulupilika dzina lake Luis a anadwala matenda a khansa. Dokotala anamuuza kuti pakapita miyezi yocepa cabe, adzamwalila. Monika na mwamuna wake anali okangalika na zinthu zauzimu. Koma tsiku lina, iye anadziŵa kuti mwamuna wake, yemwe anali mkulu, anali kucita macimo mwamseli kwa zaka zambili. Mlongo Olivia, yemwe ni mbeta, anakakamizika kucoka m’nyumba yake cifukwa kunali kubwela namondwe. Iye atabwelela, anapeza kuti namondweyo waononga nyumba yake. M’kanthawi kocepa, miyoyo ya anthuwa inasinthilatu mwadzidzidzi. Kodi inunso munakumanapo na vuto lina lake limene linasinthilatu moyo wanu mosayembekezela?
2 Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupilika a Yehova, nafenso timakumana na zovuta, komanso kudwala monga mmene zilili na anthu ena. Kuwonjezela apo, timafunikanso kupilila citsutso kapena mazunzo ocokela kwa anthu amene amadana na anthu a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova satiteteza ku mavutowa, iye analonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Na thandizo lake, tingakhalebe acimwemwe, kupanga zisankho zanzelu, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye ngakhale pomwe tikukumana na zinthu zovuta. M’nkhani ino, tikambilane njila zinayi za mmene Yehova amatithandizila tikakumana na zovuta. Tikambilanenso zimene tiyenela kucita kuti tilandile thandizo limene iye amapeleka.
YEHOVA ADZAKUTETEZANI
3. N’ciyani cingativute kucita tikakumana na vuto lalikulu?
3 Vuto. Tikakumana na vuto lalikulu maganizo athu angasokonezeke, ndipo zingakhale zovuta kupanga zisankho zanzelu. Cifukwa ciyani? Mtima wathu ungakhale ukupweteka, komanso kulemedwa na nkhawa. Tingamve monga tasoŵa kopita cifukwa cosaona bwino njila pa tsiku lomwe kwacita khungu. Onani mmene alongo aŵili tachula kumayambililo anamvela pamene anakumana na mavuto. Olivia anati, “Namondwe ataononga nyumba yanga, n’nadzimva wosoŵa, ndipo n’nathedwa nzelu.” Ponena za mwamuna wake, Monika anati: “N’nakhumudwa zedi. N’namva monga munthu wanilasa na mpeni. Zinali zovuta kugwila nchito za tsiku na tsiku. Sin’naganizilepo kuti za conco zinganicitikile.” Kodi Yehova analonjeza kuti adzatithandiza motani tikakumana na mavuto?
4. Malinga na Afilipi 4:6, 7, kodi Yehova anatilonjeza ciyani?
4 Zimene Yehova amacitapo. Analonjeza kutipatsa cimene Baibo imacha “mtendele wa Mulungu.” (Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.) Mtendele umenewu umatithandiza kukhala odekha, komanso a bata mu mtima cifukwa cokhala pa ubale wa mtengo wapatali na iye. Mtendele umenewu “umaposa kuganiza mozama kulikonse”; ndipo ni wapadela kwambili kuposa mmene tingaganizile. Kodi munakhalapo wodekha pambuyo popemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima? Munamva conco cifukwa iye anakupatsani “mtendele wa Mulungu.”
5. Kodi mtendele wa Mulungu umateteza motani maganizo na mitima yathu?
5 Afilipi 4:7 imakambanso kuti mtendele wa Mulungu “udzateteza,” kapena kuti kucinjiliza “mitima yanu ndi maganizo anu.” Liwu limene linamasulidwa kuti “udzateteza” limapeleka lingalilo la asilikali amene anali kuteteza mzinda kuti usaukilidwe na adani. Anthu a mu mzindawo anali kugona mwamtendele podziŵa kuti asilikali akuuteteza mzindawo. Mofananamo, ngati mtendele wa Mulungu ukuteteza mitima na maganizo athu, timakhala odekha podziŵa kuti ndife otetezeka. (Sal. 4:8) Monga zinalili kwa Hana, ngakhale kuti zinthu sizingakhale bwino nthawi yomweyo, timapezabe mtendele. (1 Sam. 1:16-18) Ndipo tikakhala odekha, cimakhala copepuka kukhala woganiza bwino na kupanga zisankho zanzelu.
6. Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na mtendele wa Mulungu? (Onaninso cithunzi.)
6 Zimene tiyenela kucita. Tikavutika maganinzo, tizipempha Mulungu kuti atithandize, mwa kupemphela kwa iye mpaka titamva mtendele wake. (Luka 11:9; 1 Ates. 5:17) M’bale Luis amene tamuchula kuciyambi, anafotokoza cimene cinam’thandiza na mkazi wake kupilila pamene anadziŵa kuti watsala na miyezi yocepa cabe yokhala na moyo. Iye anati: “Pa zocitika ngati izi, cimakhala covuta kwambili kupanga zisankho zokhudza thanzi, komanso pa nkhani zina. Koma tinakwanitsa kupeza mtendele pa nthawi yovuta kwambili imeneyi cifukwa tinali kupemphela.” M’bale Luis na mkazi wake anakamba kuti, anali kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima, komanso mobweleza-bweleza kumupempha kuti awapatse mtendele wa mu mtima, mtima wodekha, komanso nzelu kuti apange zisankho zabwino. Ndipo iwo anaonadi thandizo lake. Ngati mukukumana na vuto lalikulu, limbikilani kupemphela, ndipo mudzaona mtendele wa Yehova ukuteteza mtima wanu na maganizo anu.—Aroma 12:12.
YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI KUKHAZIKITSA MAGANIZO ANU
7. Tingamve motani tikakumana na vuto lalikulu?
7 Vuto. Tikakumana na vuto lalikulu, cimakhala covuta kukhala woganiza bwino, komanso kucita zinthu moyenela. Tingadzimve monga ngalawa imene ikukankhidwila uku na uku cifukwa ca mafunde a pa nyanja. Mlongo Ana amene tamuchula uja, ananena kuti Luis atamwalila anayang’anizana na mikhalidwe yosiyanasiyana. Iye anati: “Nthawi zina n’nali kupsinjika maganizo, ndipo zikatelo, n’nali kudzimvela cisoni. N’nalinso kukhumudwa kuti anamwalila.” Kuwonjezela apo, Ana anali kudzimva kukhala yekha-yekha, komanso kupanikizika maganizo akamapanga zisankho pa nkhani zimene Luis anali kuzisamalila bwino. Nthawi zina, anali kudzimva ngati ngalawa imene ili pa nyanja ya mafunde. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikayamba kumila m’mikhalidwe yotele?
8. Malinga na Yesaya 33:6, kodi Yehova amatitsimikizila ciyani?
8 Zimene Yehova amacitapo. Anatilonjeza kuti adzatithandiza kukhala wokhazikika. (Ŵelengani Yesaya 33:6.) Ngalawa ikakumana na namondwe pa nyanja, imayamba kukankhidwila uku ni uku moopsa. Ngalawa zambili zimakhala na zipangizo zina m’mbali mwake zimene zimaponyedwa pansi pa madzi. Zipangizo zimenezi zimathandiza kuti ngalawa isamakankhidwe kwambili na mafunde, ndipo zimathandizanso anthu a m’ngalawayo kukhala otetezeka. Komabe, zambili mwa zipangizo zimenezi zimaseŵenza bwino kwambili ngati ngalawa ikupitabe patsogolo. Mofananamo, Yehova adzatithandiza kukhala okhazikika ngati tipitabe patsogolo pa nthawi ya mavuto.
9. Kodi zida zathu zofufuzila zingatithandize motani kukhalabe okhazikika maganizo? (Onaninso cithunzi.)
9 Zimene tiyenela kucita. Mukazingidwa na mavuto, citani zonse zotheka kuti mupitilize na pulogalamu yanu yauzimu. N’zoona kuti simungakwanitse kucita zinthu ngati mmene munali kucitila kale, koma kumbukilani kuti Yehova satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. (Yelekezelani na Luka 21:1-4.) Pa pulogalamu yanu yauzimu, mudzipatula nthawi yocita phunzilo la inu mwini, komanso yosinkha-sinkha. Cifukwa ciyani? Kupitila m’gulu lake, Yehova watipatsa mfundo zabwino ngako za m’Malemba zimene zingatithandize kukhala okhazikika pa nthawi ya mavuto. Kuti mupeze zimene mufuna, mungaseŵenzetse zida zofufuzila monga JW Library®, Watch Tower Publications Index, komanso Buku Lofufuzila la Mboni za Yehova, ngati zilimo m’cinenelo canu. Mlongo Monika, amene tam’chula kuciyambi, ananena kuti anaseŵenzetsa zida zofufuzila zimenezi pamene anaona kuti wayamba kuŵaŵidwa mtima kwambili. Mwacitsanzo, anafufuza liwu lakuti “mkwiyo.” Nthawi zina anali kufufuza mawu akuti “cinyengo” komanso “kukhulupilika.” Ndiyeno anali kuŵelenga mpaka atamvako bwino. Iye anati: “Pamene n’nayamba kufufuza n’nali na nkhawa kwambili, koma n’napitiliza kuŵelenga, ndipo n’namva monga Yehova wanikumbatila mwacikondi. Pamene n’nali kuŵelenga, n’nazindikila kuti Yehova anali kumvetsa mikhalidwe yosiyanasiyana imene n’nali kupitamo, ndipo anali kunithandiza.” Thandizo lotelo locokela kwa Yehova lingakuthandizeni kukhalabe woganiza bwino mpaka pamene mutafika kumene kuli madzi a bata.—Sal. 119:143, 144.
YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI
10. Kodi tingamve bwanji pambuyo pokumana na vuto lalikulu?
10 Vuto. Pambuyo pokumana na tsoka lalikulu, tingadzimve wofooka masiku ena. Tingadzimve monga wothamanga pa mpikisano yemwe anali kuthamanga kwambili, koma akuyenda motsimphina cifukwa anadzipweteka. Tingayambe kuvutika kucita zinthu zomwe kalelo tinali kuzicita mosavuta, kapena tingakhale tilibe cifuno cocitanso zinthu zomwe tinali kukonda kucita kalelo. Mofanana na Eliya, sitingafune kuuka kapena kucita ciliconse. Koma tingafune kugona cabe. (1 Maf. 19:5-7) Kodi Yehova analonjeza kuti adzacita ciyani tikafooka?
11. Ni njila inanso iti imene Yehova amatithandizila? (Salimo 94:18)
11 Zimene Yehova amacitapo. Iye analonjeza kutithandiza. (Ŵelengani Salimo 94:18.) Monga mmene wothamanga yemwe wadzipweteka amafunikila thandizo kuti acite zina zake, nafenso tifunikila thandizo kuti tipitilizebe kutumikila Yehova. Panthawi zovuta zimenezo, Yehova analonjeza kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yes. 41:13) Mfumu Davide analandilapo thandizo limeneli. Atakumana na mavuto komanso adani, iye anauza Yehova kuti: “Dzanja lanu lamanja lidzandicilikiza.” (Sal. 18:35) Koma kodi Yehova amapeleka bwanji thandizo lake?
12. Kodi Yehova angaseŵenzetse ndani kuti atithandize tikafooka?
12 Yehova angasonkhezele anthu ena kuti atithandize. Mwacitsanzo, panthawi ina Davide atafooka, mnzake Yonatani anamuyendela na kumulimbikitsa. (1 Sam. 23:16, 17) Mofananamo, Yehova anasankha Elisa kuti azithandiza Eliya. (1 Maf. 19:16, 21; 2 Maf. 2:2) Masiku ano, Yehova angaseŵenzetse a m’banja lathu, anzathu, kapena akulu kuti atithandize. Komabe, ngati mavutowo atilefula kwambili, tingakane thandizo lawo, ndipo tingadzipatule na kukhala kwa tokha. Ndipo n’zomveka kumva conco. Ndiye, kodi tingatani kuti tilandile thandizo la Yehova?
13. Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na thandizo la Yehova? (Onaninso cithunzi.)
13 Zimene tiyenela kucita. Pewani kudzipatula. Tikadzipatula timaona zinthu m’njila yosiyana, ndipo timayamba kuganizila za ife tokha na mavuto amene tikukumana nawo. Kaganizidwe ka conco kangakhudzenso zisankho zimene tingapange. (Miy. 18:1) Komabe, nthawi zina timafuna kukhala kwa tokha, maka-maka ngati tikukumana na vuto lalikulu. Koma ngati takhala kwa tokha kwa nthawi yaitali, zikhoza kukhala ngati tikukana njila imene Yehova akufuna kutithandizila. Conco, ngakhale kuti sicingakhale copepuka, yesetsani kulandila thandizo la a m’banja lanu, mabwenzi, komanso akulu. Muziona thandizo lawo monga njila imene Yehova akugwilitsa nchito kuti akuthandizeni.—Miy. 17:17; Yes. 32:1, 2.
YEHOVA ADZAKUTONTHOZANI
14. Ni zocititsa mantha ziti zimene zingaticitikile?
14 Vuto. Tingakumane na mavuto amene angaticititse mantha kwambili. M’Baibo, atumiki okhulupilika a Mulungu, anafotokozapo za nthawi imene anali m’mavuto, komanso pamene anacita mantha cifukwa ca adani awo kapena zovuta zina. (Sal. 18:4; 55:1, 5) Mofananamo, tingakumane na citsutso ku sukulu, ku nchito, m’banja lathu, kapena kucokela ku boma. Tingakhalenso na mantha akuti tidzamwalila cifukwa ca matenda ena ake. Panthawi ngati zimenezo, tingadzimve wopanda thandizo monga kamwana kakang’ono. Kodi Yehova amatithandiza motani panthawi ngati zimenezi?
15. Kodi Salimo 94:19 limapeleka citsimikizo cotani?
15 Zimene Yehova amacitapo. Iye amatitonthoza. (Ŵelengani Salimo 94:19.) Salimoli liticititsa kuganizila za mwana wamng’ono yemwe ali na mantha, ndipo akulephela kugona cifukwa ca mvula ya mabingu. Koma atate ake akupita ku cipinda cake, kumunyamula, kumukumbatila, mpaka mwanayo atagona bwino-bwino. Ngakhale kuti mvulayo siinathe, kumukumbatila kumene atate ake acita kukucititsa mwanayo kumva kuti ni wotetezeka. Nafenso tikakumana na mavuto, tingafunikile Atate wathu wa kumwamba kutikumbatila mophiphilitsa mpaka mtima utakhala m’malo. Kodi tingacilandile motani citonthozo cimeneco kucokela kwa Yehova?
16. Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na citonthozo ca Yehova? (Onaninso cithunzi.)
16 Zimene tiyenela kucita. Muzikamba na Yehova nthawi na nthawi, mwa kupemphela, komanso kuŵelenga Mawu ake. (Sal. 77:1, 12-14) Mukamatelo, cinthu coyamba cimene mudzayamba kucita mukakumana na vuto, ni kupita kwa Atate wanu wa kumwamba. Uzani Yehova nkhawa zanu komanso mmene mukumvela, ndipo muloleni kuti akambe nanu, komanso kukutonthozani kupitila m’Malemba. (Sal. 119:28) Kuŵelenga mabuku ena a m’Baibo pa nthawi ngati zimenezi kungakutonthozeni. Mwacitsanzo, mungapeze mawu olimbikitsa m’mabuku monga Yobu, Masalimo, komanso Miyambo, kuphatikizapo mawu a Yesu opezeka mu Mateyu caputala 6. Mudzalandila citonthozo ca Yehova mwa kupemphela na kuŵelenga Mawu ake.
17. Kodi tingakhale na cidalilo cotani?
17 Ndife otsimikiza kuti Yehova adzakhala nafe m’nthawi zovuta pa umoyo wathu. Ndipo sangatisiye tokha. (Sal. 23:4; 94:14) Yehova analonjeza kutiteteza, kutithandiza kukhala okhazikika, kupeleka thandizo lofunikila, komanso kutitonthoza. Ponena za Yehova, Yesaya 26:3 imati: “Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendele wosatha, cifukwa amadalila inu.” Conco, m’dalileni Yehova, na kulandila njila imene akuseŵenzetsa pokuthandizani. Mukatelo, mudzakhalanso amphamvu ngakhale pa nthawi zovuta.
MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Ni pa nthawi iti maka-maka pamene timafunikila thandizo la Yehova?
-
Ni m’njila zinayi ziti zimene Yehova amatithandizila tikakumana na mavuto?
-
Tiyenela kucita ciyani kuti tipindule na thandizo la Yehova?
NYIMBO 12 Mulungu Wamkhulu, Yehova
a Maina ena asinthidwa.