NKHANI YOPHUNZILA 4
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
Yehova Amakukonda Kwambili
“Yehova ndi wacikondi cacikulu.”—YAK. 5:11.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene mkhalidwe wacikondi wa Yehova umatithandizila kumuyandikila, kudzimva kukhala wotetezeka, wosamalidwa bwino, komanso wotsitsimulidwa.
1. Kodi mumaganiza ciyani mukamva za Yehova?
KODI munayamba mwaganizilapo mmene Yehova amaonekela? N’ciyani cimabwela m’maganizo mwanu mukamapemphela kwa iye? Ngakhale kuti Yehova saoneka, Baibo imamufotokoza m’njila zosiyana-siyana. Amachedwa “dzuŵa, ndiponso cishango” komanso “moto wowononga.” (Sal. 84:11; Aheb. 12:29) Baibo imayelekezela maonekedwe ake na mwala wa safilo, citsulo cowala, komanso utawaleza wowala. (Ezek. 1:26-28) Ena mwa mafotokozedwe amenewa angaticititse cidwi kwambili, kapena angaticititse mantha.
2. N’ciyani cingalepheletse munthu kuyandikila Yehova?
2 Popeza sitimatha kuona Yehova, cingakhale covuta kwa ife kukhulupilila kuti iye amatikonda. Ena amaganiza kuti Yehova sangawakonde cifukwa ca zimene anapitamo pa umoyo wawo. Mwina sanakhalepo na tate wowakonda. Yehova amamvetsa zimenezi, komanso mmene zimatikhudzila. Pofuna kutithandiza kuona kuti amatikonda, amavumbula makhalidwe ake abwino kupitila m’Mawu ake.
3. N’cifukwa ciyani tiyenela kukambitsilana cikondi ca Yehova mozama?
3 Liwu limodzi limene limam’fotokoza bwino kwambili Yehova ni cikondi. (1 Yoh. 4:8) Mulungu ndiye cikondi. Zocita zake zonse zimasonkhezeledwa na cikondi. Cikondi cake n’copanda tsankho, komanso n’camphamvu moti amacionetsa ngakhale kwa aja amene samukonda. (Mat. 5:44, 45) M’nkhani ino, tikambilane mozama za Yehova, komanso za cikondi cake. Kuphunzila zambili za Mulungu wathu kudzatithandiza kum’konda kwambili.
YEHOVA AMATIKONDA KWAMBILI
4. Kodi cikondi cacikulu ca Yehova cimakupangitsani kumva bwanji? (Onaninso cithunzi)
4 “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.” (Yak. 5:11) M’Baibo iye amadziyelekezela na mayi wacikondi. (Yes. 66:) Ganizilani cabe mmene mayi wacikondi amasamalila mwana wake wa mng’ono. Amaika mwanayo pa mendo, na kukamba naye mwacikondi komanso mwansangala. Mwanayo akamva kupweteka kapena akayamba kulila, nakubala amaonetsetsa kuti wamupatsa zonse zimene akufuna. Tikavutika na cinacake, timadalila cikondi ca Yehova. Wamasalimo analemba kuti: “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”— 12, 13Sal. 94:19.
5. Kodi cikondi cosasintha ca Yehova cimatanthauzanji kwa inu?
5 Yehova ni wokoma mtima. (Sal. 103:8) Iye saleka kutikonda tikalakwitsa zinazake. Mtundu wa Isiraeli unali kulakwila Yehova mobweleza-bweleza. Ngakhale n’telo, iye mokoma mtima anauza anthu olapa kuti: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4, 5) Cikondi ca Mulungu sicinasinthe. Tingapitilizebe kucidalila. Yehova satisiya ngakhale pamene talakwitsa zinthu zazikulu. Tikalapa na kubwelela kwa Yehova, timapeza kuti cikondi cake pa ife cikali cimodzi-modzi. Iye analonjeza kuti “amakhululuka ndi mtima wonse.” (Yes. 55:7) Baibo imafotokoza kuti kukhululuka kotelo, kumabweletsa “nyengo zotsitsimula” zocokela kwa Yehova.”—Mac. 3:19.
6. Kodi Zekariya 2:8 imatiphunzitsanji za Yehova?
6 Ŵelengani Zekariya 2:8. Cifukwa cakuti Yehova amatikonda, iye amakhudzika na mmene timamvela ndipo ni wofunitsitsa kutiteteza. Zimamupweteka ngati tikumana na mavuto. Ndiye cifukwa cake m’poyenela kupemphela kuti: “Ndisungeni monga mwana wa diso.” (Sal. 17:8) Diso ni mbali ya mtengo wapatali ya thupi lathu. Conco, pomwe Yehova akutiyelekezela na mwana wa m’diso lake, zili monga akutiuza kuti, ‘aliyense amene wakuvulazani anthu anga, akuvulaza cinthu ca mtengo wapatali kwa ine.’
7. N’cifukwa ciyani tiyenela kulimbitsa cidalilo cakuti Yehova amatikonda?
7 Yehova afuna kuti tikhale otsimikiza kuti amatikonda aliyense payekha-payekha. Komabe, iye amadziŵa kuti cifukwa ca zimene zinaticitikila kumbuyo, tingakaikile ngati angatikonde. Kapena tingakhale kuti tikukumana na zinthu zina zake pali pano, zomwe zingatipangitse kukaikila ngati Yehova amatikonda. N’ciyani cingalimbikitse cidalilo cathu mwa iye? Ni kuphunzila mmene Yehova amaonetsela cikondi cake pa Yesu, odzozedwa, komanso ife tonse.
MMENE YEHOVA AMAONETSELA CIKONDI CAKE
8. N’ciyani cinatsimikizila Yesu kuti Atate ake amamukonda?
8 Kwa zaka zosaŵelengeka, Yehova na Mwana wake wokondeka anasangalala na ubwenzi wathithithi wa cikondi. Ubale wawo ndiwo wakhalitsa kwambili m’cilengedwe conse. Pa Mateyu 17:5, Yehova anaonetsa bwino mmene amam’kondela Yesu. Akanafuna Yehova akanangonena kuti, ‘Uyu ndiye amene ndikukondwela naye.’ Komabe iye anafuna kuti tidziŵe mmene amakondela Yesu. Conco iye anamucha “Mwana wanga wokondedwa.” Yehova anam’nyandila Yesu maka-maka cifukwa cakuti anali kudzapeleka moyo wake. (Aef. 1:7) Ndipo Yesu anali kudziŵa mmene Atate wake anali kumvela pa iye. Cikondi ca Yehova pa Yesu cinali ceni-ceni, ndipo Yesu anali kudziŵa kuti Atate ake amamukonda. Mobweleza-bweleza Yesu ananena motsimikiza kuti Atate wake amamukonda—Yoh. 3:35; 10:17; 17:24.
9. Ni mawu ati amene amafotokoza cikondi ca Yehova kwa odzozedwa? Fotokozani. (Aroma 5:5)
9 Yehova waonetsanso cikondi cake kwa odzozedwa. Onani mawu amene aseŵenzetsedwa pa Aroma 5:5 (Ŵelengani.) poonetsa mmene Yehova amawakondela. Pamati ‘Mulungu wadzaza mitima yawo na cikondi cake.’ Buku lina lofotokozela Baibo linanena kuti cikondi ca Mulungu “cili monga mtsinje wa madzi.” Mawu amenewa aonetsa kuculuka kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa odzozedwa! Ndipo odzozedwa amadziŵa kuti ni “okondedwa ndi Mulungu.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvela pomwe analemba kuti: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza. Watichula kuti ndife ana a Mulungu!” (1 Yoh. 3:1) Kodi ni Akhristu odzozedwa okha amene amakondedwa na Yehova? Ayi, Yehova waonetsa cikondi cake kwa tonsefe.
10. N’cinthu cacikulu citi cimene Yehova anacita cimene cimakutsimikizilani kuti akukondani?
10 Kodi n’ciyani cinatsimikizila kuti Yehova amatikondadi? Ni dipo. Ndiwo mcitidwe woonetsa cikondi copambana m’cilengedwe conse! (Yoh. 3:16; Aroma 5:8) Yehova anapeleka Mwana wake wokondedwa, kumulola kuti afele mtundu wonse wa anthu kuti macimo athu akhululukidwe, komanso kuti tikhale mabwenzi Ake. (1 Yoh. 4:10) Kusinkhasinkha za zinthu zimene Yehova na Yesu anatailapo kuti apeleke dipo, kumatithandiza kumvetsa kukula kwa cikondi cawo pa wina aliyense wa ife. (Agal. 2:20) Dipo silinapelekedwe kuti likwanilitse cilungamo ca Yehova cabe, ayi. Koma ni mphatso ya cikondi. Yehova anatsimikizila cikondi cake pa ife mwa kupeleka nsembe Yesu—munthu wofunika kwambili kwa iye. Yehova analola Mwana wake kuvutika na kufa m’malo mwathu.
11. Tiphunzilapo ciyani pa Yeremiya 31:3?
11 Monga taonela, sikuti Yehova amangomva cabe mu mtima mwake kuti amatikonda, koma amatiuza ndithu kuti amatikonda. (Ŵelengani Yeremiya 31:3.) Yehova watikokela kwa iye cifukwa cotikonda. (Yelekezelani na Deuteronomo 7:7, 8.) Kulibe ciliconse kapena munthu aliyense amene angatilekanitse na cikondi cimeneco. (Aroma 8:38, 39) Kodi cikondi cimeneci cikupangitsani kumva bwanji? Ŵelengani Salimo 23, kuti muone mmene cikondi ca Yehova komanso cisamalilo cake cinakhudzila Davide komanso mmene cingatikhudzile tonsefe.
KODI CIKONDI CA YEHOVA CIMATIPANGITSA KUMVA BWANJI?
12. Kodi mwacidule mungalifotokoze motani Salimo 23?
12 Ŵelengani Salimo 23:1-6. Salimo 23 ni nyimbo imene imafotokoza cidalilo cimene tili naco pa cikondi ca Yehova komanso mmene amatisamalila. Davide, amene analemba salimoli, anafotokoza ubwenzi wolimba umene unalipo pakati pa iye na M’busa wake, Yehova. Davide anadzimva kukhala wotetezeka polola Yehova kuti am’tsogolele, ndipo anali kumudalila na mtima wonse. Davide anali kudziŵa kuti Yehova adzamuonetsa cikondi masiku onse a moyo wake. N’cifukwa ciyani anali na cidalilo cacikulu conci?
13. N’ciyani cinacititsa Davide kukhala wotsimikiza kuti Yehova anali kumusamalila?
13 “Sindidzasowa kanthu.” Davide anadzimva kuti ni wosamalidwa bwino cifukwa nthawi zonse Yehova anali kumupatsa zofunikila. Davide anasangalalanso na ubwenzi komanso ciyanjo ca Yehova. Ndiye cifukwa cake anali wotsimikiza kuti mulimonse mmene zinthu zidzakhalile m’tsogolo, Yehova adzapitilizabe kumusamalila pa zosoŵa zake. Cifukwa cakuti Davide anali kudziŵa kuti Yehova amamukonda komanso kuti adzamusamalila, zinamuthandiza kuti asakhale na nkhawa iliyonse pa mavuto ake. M’malo mwake anali wokhutila komanso wosangalala.—Sal. 16:11.
14. Kodi Yehova angaonetse motani kuti amatikonda?
14 Yehova amatisamalila mwacikondi, maka-maka ngati zinthu zoipa zaticitikila mu umoyo wathu. Claire, a amene watumikila pa Beteli kwa zaka zoposa 20, anasoŵa cocita pomwe banja lawo linakumana na mavuto motsatizana. Atate ake anadwala sitiloko yotsiliza mphamvu m’thupi, mng’ono wake anacotsedwa mu mpingo, bizinesi yaing’ono ya banja lawo inagwa, ndipo anasoŵa pokhala. Kodi Yehova anawaonetsa bwanji cikondi? Claire anati: “Yehova anaonetsetsa kuti akupeleka zonse zofunikila ku banja langa tsiku lililonse. Mobweleza-bweleza Yehova anali kutipatsa kuposa pa zimene n’nali kuyembekezela! Nthawi zambili nimakumbukila nthawi pamene Yehova anatisamalila mwacikondi, ndipo sinidzaiŵala cikondi cimeneco. Kukumbukila zimenezo kwanithandiza kuti nipitilizebe kutumikila Yehova mwacimwemwe mosasamala kanthu za mavuto amene nimakumana nawo.”
15. N’ciyani cinacititsa Davide kumva kutsitsimulidwa? (Onaninso cithunzi)
15 “Amatsitsimula moyo wanga.” Nthawi zina, Davide anali kukhala wopanikizika maganizo cifukwa ca mavuto amene anali kukumana nawo. (Sal. 18:4-6) Ngakhale n’telo, cikondi ca Yehova na cisamalilo cake, zinali kumutsitsimula. Yehova anali kutsogolela mnzake wopanikizika maganizoyo “m’mabusa a msipu wambili” komanso “m’malo opumila a madzi ambili.” Zotsatila zake n’zakuti, Davide anakwanitsa kupezanso mphamvu ndipo anapitilizabe kumutumikila Yehova mwacimwemwe.—Sal. 18:28-32.
16. Kodi cikondi ca Yehova cakutsitsimulani motani?
16 Mofananamo, masiku ano “cifukwa ca kukoma mtima kosatha kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe” pomwe takumana na mavuto. (Maliro 3:22; Akol. 1:11) Ganizilani citsanzo ca Rachel. Iye anakhwethemuka maganizo pomwe mwamuna wake anasankha kumusiya komanso kusiya Yehova pa nthawi ya mlili wa COVID-19. Kodi Yehova anamusamalila motani? Iye anati: “Yehova anaonetsetsa kuti nikuonetsedwa cikondi. Ananipatsa mabwenzi amene anali kuceza nane, kunibweletsela cakudya, kunilembela mauthenga olimbikitsa komanso Malemba, ndiponso kuseka nane. Iwo anapitiliza kunikumbutsa kuti Yehova anali kunisamalila. Nthawi zonse nimayamikila Yehova ponipatsa banja la cikondi limeneli.”
17. N’ciyani cinacititsa Davide ‘kusaopa kanthu’?
17 “Sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine.” Nthawi zambili moyo wa Davide unali paciswe, ndipo anali na adani amphamvu. Komabe, cikondi ca Yehova cinamupangitsa kumva kuti ni wotetezeka. Davide anali wotsimikiza mtima kuti Yehova anali naye pa zonse zimene anali kukumana nazo. Ndiye cifukwa cake iye anaimba kuti: “Pakuthawathawa kwanga konse iye [Yehova] anandilanditsa.” (Sal. 34:4) Mantha a Davide anali enieni, koma cikondi ca Yehova cinali colimba kuposa mantha amenewo.
18. Kodi kudziŵa kuti Yehova amakukondani kungakulimbikitseni motani mukacita mantha?
18 Kodi kudziŵa kuti Yehova amatikonda kumatithandiza bwanji kupilila pomwe tikukumana na mavuto? Mpainiya wina dzina lake Susi anafotokoza mmene iye na mwamuna wake anamvela pomwe mwana wawo anadzipha. Iye anati: “Cinthu coipa cikakucitikila mwadzidzidzi cimakusoŵetsa mtengo wogwila. Koma cikondi ca Yehova catipangitsa kumva kuti ndife otetezeka.” Rachel, amene tamuchula kale, anati: “Usiku wina pamene mtima wanga unali kupweteka zedi komanso pomwe n’nali na nkhawa na mantha, ninafuulila Yehova m’pemphelo. Nthawi yomweyo, Yehova ananitonthoza na kunikhazika mtima pansi, monga mmene mayi amacitila kwa mwana wake. Kenako n’nagona. Sinidzaiŵala nthawi imeneyo.” Mkulu wina dzina lake Tasos anakhala m’ndende zaka 4 cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Kodi Yehova anamuonetsa bwanji cikondi na cisamalilo? Iye anati: “Yehova anacita zambili kuposa pa kusamalila zosoŵa zanga zonse. Izi zinalimbikitsa cikhulupililo canga mwa iye cakuti nikhoza kumudalila na mtima wonse. Komanso, Yehova ananipatsa cimwemwe kupitila mwa mzimu wake woyela, mosasamala kanthu za malo amene ninaliko. Izi zinanitsimikizila kuti pamene nikhala pafupi naye m’pamenenso nidzaona ubwino wake. Conco n’nayamba kumutumikila monga mpainiya wa nthawi zonse pamene n’nali m’ndende.”
MUYANDIKILENI MULUNGU WANU WACIKONDI
19. (a) Kodi kudziŵa kuti Yehova amatikonda kungakhudze motani zimene tingakambe m’mapemphelo athu? (b) Ni kafotokozedwe kati ka cikondi ca Yehova kamene kamakukhudzani kwambili inuyo panokha? (Onani danga lakuti “ Mawu Omwe Amatithandiza Kuona Cikondi ca Yehova.”)
19 Zocitika zimene takambilana m’nkhani ino, zionetsa kuti Yehova, “Mulungu wacikondi,” ali nafe! (2 Akor. 13:11) Iye amationetsa cidwi aliyense payekha-payekha. Ndife otsimikiza kuti ndife ‘wozungulilidwa ndi kukoma mtima kosatha.’ (Sal. 32:10) Tikapitiliza kusinkhasinkha za mmene iye waonetsela cikondi cake pa ife, m’pamene iyenso amakhala weniweni kwa ife. Ndipo timamva kuti tikuyandikana naye. Tingamufikile momasuka na kumuuza kufunika kwa cikondi cake kwa ife. Tingamufotokozele nkhawa zathu zonse tili na cidalilo kuti amatimvetsa, komanso kuti ni wofunitsitsa kutithandiza.—Sal. 145:18, 19.
20. Kodi cikondi ca Yehova cimatithandiza bwanji kuti timuyandikile?
20 Monga mmene timafunila moto kukazizila, tifunikilanso cikondi ca Yehova. Ngakhale kuti cikondi ca Yehova n’camphamvu, cimapelekedwa mokoma mtima. Conco mudzikhala wosangalala podziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili. Ndipo tonsefe tiyeni tinene mofuula za cikondi cake kuti: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi cikondi”!—Sal. 116:1.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Mungacifotokoze motani cikondi ca Yehova?
-
N’ciyani cimakutsimikizilani kuti Yehova amakukondani ngako?
-
Kodi cikondi ca Yehova cimakupangitsani kumva bwanji?
NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu
a Maina ena asinthidwa.