Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 2

NYIMBO 132 Lomba Ndise Thupi Limodzi

Inu Amuna, Lemekezani Akazi Anu

Inu Amuna, Lemekezani Akazi Anu

“Inunso amuna, . . . muziwapatsa ulemu.”​—1 PET. 3:7.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene mwamuna angaonetsele kuti amalemekeza mkazi wake m’zokamba komanso zocita zake.

1. Kodi Yehova anapeleka mphatso ya ukwati pa colinga canji?

 YEHOVA ndi “Mulungu wacimwemwe,” ndipo amafuna kuti nafenso tikhale acimwemwe. (1 Tim. 1:11) Watipatsa mphatso zambili zotithandiza kusangalala ndi moyo. (Yak. 1:17) Imodzi mwa mphatso zimenezo ndi ukwati. Pamene mwamuna ndi mkazi akulowa m’banja, amalumbila kuti adzakondana, adzalemekezana, komanso kuti adzasamalilana. Mwamuna ndi mkazi akapitiliza kukondana, amakhala acimwemwe kwambili.​—Miy. 5:18.

2. N’ciyani cikucitikila mabanja ambili masiku ano?

2 N’zacisoni kuti okwatilana ambili masiku ano, sasunga malonjezo awo amene anapanga pa tsiku lawo la ukwati. Zotulukapo zake n’zakuti sakhala acimwemwe. Lipoti la posacedwa la Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linaonetsa kuti amuna ambili amawacita nkhanza akazi awo mwa kuwamenya, kuwakhadzulila mawu, komanso kuwacita nkhanza m’njila zina. Mwamuna amene amacita zimenezi, angamacite naye mwaulemu mkazi wake pamaso pa anthu, koma n’kumamucita nkhanza akakhala kunyumba. Amuna ambili okwatila amaonelela zamalisece, ndipo izi zimapangitsa akazi awo kumva kuti sakondedwa, ndipo sakhalanso acimwemwe.

3. N’ciyani cingapangitse mwamuna kumucita nkhanza mkazi wake?

3 N’ciyani cingapangitse mwamuna kumacita nkhanza kwa mkazi wake? N’kutheka kuti mwamunayo analeledwa ndi tate amene anali wankhanza. Conco angamaone kuti palibe colakwika kumamucita nkhanza mkazi wake. Ena angakhale kuti analeledwa m’cikhalidwe cimene cimalimbikitsa kaganizidwe kolakwika kakuti “mwamuna weniweni” ayenela kugwilitsa nchito mphamvu poonetsa mkazi wake kuti wamkulu ndani. Ndipo amuna ena sanaphunzitsidwe kuugwila mtima akakwiya. Amuna ena amaonelela kwambili zamalisece. Izi zimawapangitsa kuganiza kuti akazi ndi pongothetsela cilakolako ca kugonana basi. Kuwonjezela apo, akatswili apeza kuti mavuto ocita nkhanza kwa akazi anawonjezeka kwambili pa nthawi ya mlili wa COVID-19. Ngakhale n’telo, mwamuna sayenela kumucita nkhanza mkazi wake pa cifukwa ciliconse.

4. Kodi amuna acikhristu okwatila ayenela kusamala ndi ciyani? Ndipo n’cifukwa ciyani?

4 Amuna acikhristu okwatila, ayenela kupewa kutengela kaganizidwe kofala ka m’dzikoli ponena za akazi. a Cifukwa ciyani? Cifukwa cimodzi n’cakuti nthawi zambili zimene munthu amakonda kuganiza n’zimenenso amadzacita. Mtumwi Paulo anacenjeza Akhristu odzozedwa a ku Roma kuti ‘asamatengele nzelu za nthawi ino.’ (Aroma 12:​1, 2) Pomwe Paulo anawalembela kalata Akhristuwo, mpingowo unali utakhalapo kwa zaka ndithu. Komabe, mawu a Paulo aonetsa kuti kaganizidwe ka ena mu mpingomo, kanali kusonkhezeledwa ndi miyambo komanso kaganizidwe ka dziko. Ndiye cifukwa cake anawalimbikitsa kuti asinthe kaganizidwe kawo, komanso kacitidwe kawo ka zinthu. Malangizo amenewa agwilanso nchito kwa amuna acikhristu okwatila masiku ano. N’zacisoni kuti ena mwa amuna acikhristu asonkhezeledwa ndi kaganizidwe ka dzikoli, ndipo afika mpaka powacita nkhanza akazi awo. b Koma kodi Yehova amafuna kuti mwamuna azicita naye motani mkazi wake? Tipeza yankho pa lemba la mutu wa nkhani yathu.

5. Malinga ndi 1 Petulo 3:​7, kodi mwamuna ayenela kucita naye motani mkazi wake?

5 Welengani 1 Petulo 3:7. Yehova analamula amuna kuti azilemekeza akazi awo. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake, amacita naye mokoma mtima komanso mwacikondi. M’nkhani ino, tikambilana mmene mwamuna angaonetsele ulemu kwa mkazi wake. Koma coyamba tiyeni tikambilane makhalidwe amene amacotsela ulemu akazi.

PEWANI MAKHALIDWE OCOTSELA ULEMU MKAZI WANU

6. Kodi Yehova amamva bwanji ndi amuna amene amazunza akazi awo? (Akolose 3:19)

6 Mwamuna sayenela kumenya mkazi wake. Yehova amadana ndi munthu aliyense waciwawa. (Sal. 11:5) Iye amadana makamaka ndi amuna amene amazunza akazi awo. (Mal. 2:16; welengani Akolose 3:​19, komanso mawu a m’munsi.) Malinga ndi lemba la mutu wa nkhani ino, 1 Petulo 3:​7, ngati mwamuna sacita naye mwaulemu mkazi wake, ubale wake ndi Yehova umakhudzidwa. Yehova angafike ngakhale poleka kumva mapemphelo ake.

7. Malinga ndi Aefeso 4:​31, 32, ndi malankhulidwe otani amene amuna ayenela kupewa? (Onaninso “Kufotokozela Mawu Ena.”)

7 Mwamuna sayenela kulankhula mokhadzula kwa mkazi wake. Amuna ena amacita nkhanza kwa akazi awo mwa kuwalankhulila mawu aukali komanso opweteka. Koma Yehova amadana ndi “kupsa mtima, mkwiyo, kulalata, komanso mawu acipongwe.” c (Welengani Aefeso 4:​31, 32.) Iye amamva zonse. Conco mmene mwamuna amakambila kwa mkazi wake, ngakhale akakhala kunyumba kwaokha, zimam’khudza Yehova. Mwamuna amene amalankhula mokhadzula kwa mkazi wake, amasokoneza ukwati wake, komanso ubwenzi wake ndi Mulungu.​—Yak. 1:26.

8. Kodi Yehova amaziona motani zamalisece? Nanga n’cifukwa ciyani amaziona conco?

8 Mwamuna sayenela kupenyelela zamalisece. Kodi Yehova amaziona motani zamalisece? Amanyansidwa nazo. Conco mwamuna amene amayang’ana zamalisece, amawononga ubale wake ndi Yehova ndipo amacotsela ulemu mkazi wake. d Yehova amafuna kuti mwamuna akhale wokhulupilika kwa mkazi wake, osati cabe m’zocita zake, koma ngakhalenso m’maganizo ake. Yesu anakamba kuti, mwamuna amene amayang’ana mkazi wina momukhumbila, amakhala kuti wacita naye kale cigololo “mumtima mwake.” e​—Mat. 5:​28, 29.

9. N’cifukwa ciyani Yehova amanyansidwa ngati mwamuna akakamiza mkazi wake kucita zinthu zimene iye safuna pa nkhani yakucipinda?

9 Pa nkhani yakucipinda, mwamuna sayenela kukakamiza mkazi wake kucita zimene mkaziyo sakufuna kapena zimene zingavutitse cikumbumtima cake. Pa nkhani yopatsana mangawa amuukwati, amuna ena amaumiliza akazi awo macitidwe acilendo opepula wamkazi, moti mkazi amadzimva wodetsedwa kapena wosakondedwa. Yehova amanyansidwa nalo khalidwe lopanda cikondi losaganizila mnzako lotelo. Iye amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake, kucita naye mokoma mtima, komanso kulemekeza cikumbumtima cake. (Aef. 5:​28, 29) Conco, bwanji ngati zimenezi n’zimene mwamuna wa Cikhristu amacita, zokakamiza mkazi wake, kumucita nkhanza, kapena kupenyelela zamalisece? Kodi angacite ciyani kuti asinthe kaganizidwe kake ndi khalidwe lake?

ZIMENE MWAMUNA ANGACITE KUTI ALEKE ZINTHU ZOCOTSELA ULEMU MKAZI WAKE

10. Kodi citsanzo ca Yesu cingawathandize bwanji amuna okwatila?

10 Kodi mwamuna angacite ciyani kuti aleke kucita nkhanza kwa mkazi wake komanso kumucotsela ulemu? Angatelo mwa kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu. Ngakhale kuti Yesu sanakwatilepo, mmene iye anali kucitila kwa ophunzila ake, anapeleka citsanzo ca mmene mwamuna ayenela kucitila ndi mkazi wake. (Aef. 5:25) Mwacitsanzo, onani zimene amuna angaphunzileko kwa Yesu poona mmene iye anali kucitila ndi atumwi ake, komanso mmene anali kulankhulila nawo.

11. Kodi Yesu anali kucita nawo motani atumwi ake?

11 Yesu anali kucita nawo mokoma mtima komanso mwaulemu atumwi ake. Iye sanali kucita nawo mwankhanza kapena mowapepula. Ngakhale kuti anali Mbuye wawo komanso anali wamphamvu kuposa iwo, iye sanacite nawo m’njila yowacititsa kuti azimuopa kapena kuwaonetsa kuti ndi ofookelapo. M’malomwake, anali kuwatumikila modzicepetsa. (Yoh. 13:​12-17) Anauza ophunzila ake kuti: “Phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:​28-30) Onani kuti Yesu anali wofatsa. Munthu wofatsa si wofooka. M’malomwake, iye ali ndi mphamvu zokwanitsa kudziletsa. Akaputidwa, iye amakhalabe wodekha, ndipo amaika mtima wake m’malo.

12. Kodi Yesu anali kukamba nawo motani anthu ena?

12 Yesu anali kulankhula motonthoza komanso motsitsimula. Sanali kukamba nawo mwaukali otsatila ake. (Luka 8:​47, 48) Ngakhale pamene omutsutsa anali kumunyoza, “sanabwezele zacipongwe.” (1 Pet. 2:​21-23) Nthawi zina, Yesu anali kungokhala cete m’malo moyankha mwaukali. (Mat. 27:​12-14) Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwambili kwa amuna acikhristu okwatila!

13. Malinga ndi Mateyo 19:​4-6, kodi mwamuna angadziphatike bwanji kwa mkazi wake? (Onaninso cithunzi.)

13 Yesu analangiza amuna kuti ayenela kukhala okhulupilika kwa akazi awo. Anatelo mwa kugwila mawu a Atate wake pomwe anakamba kuti mwamuna ayenela ‘kudziphatika kwa mkazi wake.’ (Welengani Mateyo 19:​4-6.) Mawu a Cigiriki amene anagwilitsidwa nchito pa lembali akuti “kudziphatika,” tanthauzo lake lenileni n’lakuti “kumata ndi guluu.” Conco mgwilizano wa pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, uyenela kukhala wolimba kwambili monga kuti awiliwo anamatikidwa ndi guluu. Mgwilizano wawo ukatha, onse awili amavutika. Mwamuna yemwe ali ndi ubale wotele ndi mkazi wake, amapewa kuonelela zamalisece za mtundu uliwonse. Iye mwamsanga ‘amapewa kuyang’ana zinthu zopanda pake.’ (Sal. 119:37) Ndipo monga mmene Yobu anacitila, nayenso mwamunayo amacita pangano ndi maso ake kuti apewe kuyang’ana mkazi aliyense momukhumbila kupatulapo mkazi wake.​—Yobu 31:1.

Mwamuna wokhulupilika amapewa kuonelela zamalisece (Onani ndime 13) g


14. Ndi masitepe ati amene mwamuna amene amacita nkhanza kwa mkazi wake ayenela kutsatila kuti akonze ubale wake ndi Yehova komanso ubale wake ndi mkazi wake?

14 Mwamuna wokwatila amene amamucita nkhanza mkazi wake kapena kumukhadzulila mawu, ayenela kucita zinthu zina kuti akonze ubale wake ndi Yehova, komanso ubale wake ndi mkazi wake. Kodi ayenela kutsatila masitepe ati kuti acite zimenezi? Coyamba, iye ayenela kuvomeleza kuti ali ndi vuto lalikulu. Palibe cobisika m’maso mwa Yehova. (Sal. 44:21; Mlal. 12:14; Aheb. 4:13) Caciwili, ayenela kuleka kucita nkhanza kwa mkazi wake, ndipo ayenelanso kusintha khalidwe lake. (Miy. 28:13) Cacitatu, ayenela kupepesa kwa mkazi wake komanso kwa Yehova, komanso kuwapempha kuti amukhululukile. (Mac. 3:19) Ayenelanso kucondelela Yehova kuti amupatse cikhumbo cofuna kusintha khalidwe lake. Kuwonjezela apo, ayenela kumupempha kuti amuthandize kuwongolela kaganizidwe kake, kakambidwe kake, komanso zocita zake. (Sal. 51:​10-12; 2 Akor. 10:5; Afil. 2:13) Cacinayi, ayenela kucitapo kanthu pa zimene amapempha mwa kudana ndi zaciwawa za mtundu uliwonse, komanso mawu alionse acipongwe. (Sal. 97:10) Cacisanu, ayenela kupempha thandizo mwamsanga kwa abusa acikondi mu mpingo. (Yak. 5:​14-16) Cothela, ayenela kukhala ndi pulani imene idzamuthandiza kupewa makhalidwe otelewa m’tsogolo. Mwamuna wokwatila amene amapenyelela zamalisece, nayenso ayenela kutsatila masitepe 6 amene tachula pamwambapa. Yehova adzathandiza mwamunayo kusintha khalidwe lake. (Sal. 37:5) Koma kungoleka khalidwe lopepula mkazi wake sikokwanila. Ayenelanso kulemekeza mkazi wake. Koma kodi angacite bwanji zimenezi?

MMENE MUNGAONETSELE ULEMU KWA MKAZI WANU

15. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amamukonda mkazi wake?

15 Onetsani kuti mumamukonda. Amuna ena amene ali mu ukwati wacimwemwe, ali ndi cizolowezi cocitako cinacake tsiku lililonse coonetsa kukula kwa cikondi cimene ali naco pa akazi awo. (1 Yoh. 3:18) Mwamuna angaonetse kuti amamukonda mkazi wake mwa kumucitila zinthu zing’onozing’ono, monga kumugwila dzanja, kapena kumukumbatila mwacikondi. Mwamunayo angamulembele uthenga wapafoni mkazi wake wakuti “Ndakusowa” kapena kumufunsa kuti “Kodi tsiku la lelo likuyenda bwanji?” Mwa apa ndi apo, angamuonetse cikondi cake mwa kumulembela kakhadi kokhala ndi mawu osankhidwa bwino acikondi kapena kumugulila kamphatso. Mwamuna akamacitila mkazi wake zinthu ngati zimenezi, amaonetsa kuti amamulemekeza mkaziyo ndipo amalimbitsa ukwati wawo.

16. N’cifukwa ciyani mwamuna ayenela kutamanda mkazi wake?

16 Onetsani kuti mumamuyamikila. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake, amamuona kukhala wamtengo wapatali ndipo amamulimbikitsa. Njila imodzi angacitile zimenezi ndi kumuonetsa kuti amamuyamikila pa zonse zimene mkaziyo amacita kuti amuthandize. (Akol. 3:15) Mwamuna yemwe amayamikila mkazi wake mocokela pansi pa mtima, amamucititsa kumva bwino mumtima mwake. Mkaziyo amamva kuti ndi wotetezeka, wokondeka, komanso wolemekezeka.​—Miy. 31:28.

17. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?

17 Citani naye mokoma mtima komanso mwaulemu. Mwamuna yemwe amakonda mkazi wake, amamuona kukhala wamtengo wapatali ndipo amamucengeta. Amamuona ngati mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Yehova. (Miy. 18:22; 31:10) Mwa kutelo, iye amacita naye mokoma mtima, komanso mwaulemu ngakhale pa nkhani yakucipinda. Conco, mwamunayo sangakakamize mkazi wake kucita naye zinthu zimene zingapangitse mkaziyo kukhala wosamasuka, kumva kuti akucitidwa nkhanza, komanso kuvutitsa cikumbumtima cake. f Mwamuna nayenso adzapewa kucita ciliconse cimene cingavutitse cikumbumtima cake pa nkhani imeneyi.​—Mac. 24:16.

18. Kodi amuna ayenela kutsimikiza mtima kucita ciyani? (Onaninso danga lakuti “ Njila Zinayi Zimene Mwamuna Angaonetsele Ulemu kwa Mkazi Wake.”)

18 Inu amuna okwatila, dziwani kuti Yehova amaona ndi kuyamikila kuyesetsa kwanu poonetsa kuti mumalemekeza mkazi wanu m’mbali zonse za umoyo wanu. Khalani otsimikiza mtima kuonetsa kuti mumamulemekeza mkazi wanu mwa kupewa khalidwe lililonse limene lingamucotsele ulemu. M’malomwake, citani naye mokoma mtima, mwaulemu, komanso mwacikondi. Mwa kucita zimenezo, mudzamuonetsa kuti mumamukonda komanso kuti mumamuona kuti ndi wamtengo wapatali. Mukamalemekeza mkazi wanu, mudzateteza cinthu camtengo wapatali kwambili kwa inu, comwe ndi ubwenzi wanu ndi Yehova.​—Sal. 25:14.

NYIMBO 131 “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”

a Amuna okwatila angapindule kwambili mwa kuwelenga nkhani yakuti “Kodi Mumacita Zinthu na Akazi Mmene Yehova Amacitila Nawo?” mu Nsanja ya Mlonda ya January 2024.

b Ngati munacitidwapo nkhanza, mungapindule mwa kuwelenga nkhani ku Chichewa yakuti “Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana.” Nkhaniyi ipezeka pa mpambo wa nkhani wakuti “Nkhani Zina” pa jw.org komanso mu JW Library®.

c KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Mawu acipongwe” amaphatikizapo kukamba mawu onyoza kapena kudzudzula munthu mobwelezabweleza. Conco mawu alionse amene mwamuna angakambe omwe angacititse mkazi kuwawidwa mtima kapena kumva kuti akutukwanidwa, ndi acipongwe.

d Onani nkhani ku Chichewa pa jw.org komanso mu JW Library yakuti “Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu.”

e Mkazi yemwe mwamuna wake amaonelela zamalisece, angapindule ndi nkhani yakuti “Ngati Mnzanu wa mu Ukwati Amaonelela Zamalisece,” mu Nsanja ya Mlonda ya August 2023.

f Baibulo silikamba mwachuchuchu zoyenela kapena zosayenela kucita pa nkhani yakucipinda pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Mwamuna aliyense wokwatila wacikhristu pamodzi ndi mkazi wake, ayenela kupanga zisankho pa nkhani imeneyi zoonetsa kuti amalemekeza Yehova, amafuna kusangalatsana bwino, komanso zimene zidzawasiya ndi cikumbumtima coyela. Koma iwo sayenela kukambilana cisawawa ndi anthu ena mmene amaonetselana cikondi mu ukwati wawo.

g MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Anchito anzake a m’bale omwe si Mboni akuyesa kumunyengelela kuti aoneko magazini yawo ya zolaula.