Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 4

NYIMBO 18 Tikuyamikilani Cifukwa ca Dipo

Kodi Dipo Limatiphunzitsa Ciyani?

Kodi Dipo Limatiphunzitsa Ciyani?

“Zimene anacita potisonyeza cikondi cake ndi izi.”​—1 YOH. 4:9.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene dipo limatiphunzitsa ponena za makhalidwe abwino a Yehova Mulungu ndi a Yesu Khristu.

1. N’cifukwa ciyani tiyenela kupezeka pa mwambo wokumbukila imfa ya Yesu caka ciliconse?

 N’ZOSACITA kufunsa kuti inunso mumaona kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali. (2 Akor. 9:15) Imfa ya Yesu inatheketsa kuti inu mukhale paubwenzi wathithithi ndi Yehova Mulungu. Mulinso ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Tili ndi zifukwa zambili zomuyamikilila Yehova amene anatipatsa dipo cifukwa cakuti amatikonda kwambili. (Aroma 5:8) Pofuna kutithandiza kukhalabe oyamikila, komanso kuti tisaiwale zimene Yehova ndi Yesu anaticitila, Yesu anatilamula kuti tizikumbukila imfa yake caka ciliconse.​—Luka 22:​19, 20.

2. Tikambilana ciyani m’nkhani ino?

2 Caka cino, Cikumbutso cidzakhalako pa Ciwelu, April 12, 2025. N’zosakaikitsa kuti tonse tikukonzekela kukapezekapo. Tidzapindula kwambili ngati pa nyengo ya Cikumbutso tasinkhasinkha a zimene Yehova ndi Mwana wake aticitila. M’nkhani ino, tikambilane zimene dipo limatiphunzitsa ponena za Yehova ndi Mwana wake. M’nkhani yotsatila tidzakambilana mmene timapindulila ndi dipo limeneli, komanso mmene tingaonetsele kuyamikila.

ZIMENE DIPO LIMATIPHUNZITSA PONENA ZA YEHOVA

3. Kodi zingatheke bwanji imfa ya munthu mmodzi kumasula anthu mamiliyoni? (Onaninso cithunzi.)

3 Dipo limatiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu wacilungamo. (Deut. 32:4) Motani? Ganizilani izi: Kusamvela kwa Adamu kunapangitsa kuti titengele ucimo umene umabweletsa imfa. (Aroma 5:12) Kuti atimasule ku ucimo ndi imfa, Yehova anatuma Yesu kuti adzapeleke dipo. Koma kodi zingatheke bwanji kuti nsembe ya munthu mmodzi wangwilo imasule anthu mamiliyoni? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Popeza kusamvela kwa munthu mmodziyo [Adamu] kunacititsa kuti ambili akhale ocimwa, kumvela kwa munthu mmodziyu [Yesu] kudzacititsanso kuti ambili akhale olungama.” (Aroma 5:19; 1 Tim. 2:6) M’mawu ena, kusamvela kwa munthu mmodzi wangwilo, kunapangitsa kuti tikhale akapolo a ucimo ndi imfa. Mofananamo, kumvela kwa munthu mmodzi wangwilo kunatimasula.

Mwamuna mmodzi, Adamu, anapangitsa kuti tikhale akapolo a ucimo ndi imfa. Mofananamo, mwamuna mmodzi anatimasula (Onani ndime 3)


4. N’cifukwa ciyani Yehova sanangolola mbadwa za Adamu za mtima wabwino kukhala ndi moyo kwamuyaya?

4 Kodi Yesu anafunikiladi kufa kuti atipulumutse? N’cifukwa ciyani Yehova sanangolola mbadwa za Adamu za mtima wabwino kukhala ndi moyo kwamuyaya? Kwa anthu opanda ungwilo, kumeneku kungaoneke ngati kukoma mtima komanso cinthu canzelu kucita. Koma kwa Yehova, kucita izi sikungakhale cilungamo. Popeza Yehova ndi wolungama, kucita izi kukanakhala ngati kuti Yehova akupeputsa colakwa cacikulu cimene Adamu anacita.

5. N’ciyani cimatitsimikizila kuti Yehova adzacita zinthu mwacilungamo nthawi zonse?

5 Koma bwanji ngati Yehova sanapeleke dipo, ndipo anasankha kunyalanyaza cilungamo mwa kulola ana a Adamu opanda ungwilo kukhala ndi moyo kwamuyaya? Akanacita izi, anthu akanaganiza kuti Mulungu angadzanyalanyazenso cilungamo cake pa zocitika zina. Mwacitsanzo, angamaganizenso kuti Yehova sadzasunga malonjezo ake onse. Koma sitiyenela kuda nkhawa kuti zimenezi zingacitike. N’cifukwa ciyani? Cifukwa n’cakuti Yehova anacita kupelekelapo Mwana wake nsembe pofuna kuonetsetsa kuti cilungamo cacitika. Izi zimatitsimikizila kuti nthawi zonse, iye adzacita zinthu mwacilungamo.

6. Kodi dipo limaonetsa motani kuti Yehova amatikonda? (1 Yohane 4:​9, 10)

6 Dipo limatithandiza kuona kuti Yehova ndi wacilungamo. Koma koposa pamenepo, limatithandizanso kumvetsa kuzama kwa cikondi cake pa ife. (Yoh. 3:16; welengani 1 Yohane 4:​9, 10.) Nkhani ya dipo imatiphunzitsa kuti Yehova amafuna kuti tikakhale ndi moyo kwamuyaya. Kuwonjezela apo, imatiphunzitsanso kuti amafuna tikhale m’banja mwake. Ganizilani izi: Adamu atacimwa, Yehova anamuthamangitsa m’banja la alambili ake. Pa cifukwa cimeneci, tonse tinabadwila kunja kwa banja la Mulungu. Pa maziko a dipo, Yehova amatikhululukila macimo athu, ndipo m’tsogolo anthu onse omvela komanso acikhulupililo, adzawalowetsa m’banja mwake. Komabe ngakhale palipano, tingakhale paubale wolimba ndi Yehova komanso ndi alambili anzathu. Kunena zoona, Yehova amatikonda kwambili!​—Aroma 5:​10, 11.

7. Kodi mmene Yesu anavutikila zimaonetsa bwanji kuzama kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa ife?

7 Kuti timvetse mmene Yehova amatikondela, tiyenela kuganizila mmene zinamupwetekela kuona Mwana wake akuvutika. Satana amakamba kuti palibe angakhalebe wokhulupilika kwa Mulungu panthawi zovuta. Pofuna kuonetsa kuti zimenezo n’zabodza, Yehova analola Yesu kuvutika asanamwalile. (Yobu 2:​1-5; 1 Pet. 2:21) Yehova anali kuona pamene anthu anali kunyoza Yesu, pamene asilikali anali kumumenya, komanso pamene anali kumukhomelela pamtengo. Kenako Yehova anaona pamene Mwana wake wokondeka anali kufa imfa yowawa. (Mat. 27:​28-31, 39) Yehova anali nazo mphamvu zothetsa kuvutika kwa Mwana wake. Mwacitsanzo, pamene anthu anali kukamba kuti: ‘Mulungu amupulumutse ngati akumufunadi,’ Yehova akanam’pulutsadi. (Mat. 27:​42, 43) Komabe, Mulungu akanacita zimenezo, dipo silikanapelekedwa, ndipo anthufe tikanakhala opanda ciyembekezo. Conco, Yehova analola Mwana wake kuvutika mpaka pamene anatsilizika.

8. Kodi Yehova anapwetekedwa mtima poona Mwana wake akuvutika? Fotokozani. (Onaninso cithunzi.)

8 Koma tisaganize kuti popeza Mulungu ndi wamphamvuzonse ndiye kuti sangakhudzike mtima. Popeza tinalengedwa m’cifanizilo cake, ndipo tinapangidwa m’njila yakuti tizikhudzika mtima, m’pomveka kuti Yehova nayenso amakhudzika mtima. Baibulo limaonetsa kuti Mulungu amakhumudwa komanso amamva cisoni. (Sal. 78:​40, 41) Ganizilani nkhani ya Abulahamu ndi Isaki. Mungakumbukile kuti Abulahamu analamulidwa kupeleka mwana wake nsembe. (Gen. 22:​9-12; Aheb. 11:​17-19) Ganizilani cisoni cimene anali naco pamene anali kukonzekela kupha Isaki mwana wake. Ngati munthu angakhale ndi cisoni cacikulu conci, ndiye kuti Yehova anali ndi cisoni cacikulu kwambili kuposa pamenepo, pomwe anali kuona Mwana wake akuzunzidwa mpaka kufa.​—Onani vidiyo yakuti Tsanzilani Cikhulupililo Cawo​—Abulahamu, Gawo Laciwili pa jw.org.

Yehova anapwetekedwa mtima kuona Mwana wake akuvutika (Onani ndime 8)


9. Kodi Aroma 8:​32, 38, 39, limakuphunzitsani ciyani ponena za cikondi ca Yehova?

9 Dipo limatiphunzitsa kuti palibe angatikonde mmene Yehova amatikondela, ngakhale wacibale wathu wokondeka, kapena bwenzi lathu lapamtima. (Welengani Aroma 8:​32, 38, 39.) N’zosakaikitsa kuti Yehova amatikonda kwambili kuposa mmene timadzikondela ife eni. Kodi mumafuna kukhala ndi moyo kwamuyaya? Dziwani kuti Yehova amafuna kuti mukakhale kwamuyaya kuposa mmene inu mumafunila. Kodi mumafuna kuti macimo anu akhululukidwe? Dziwani kuti Yehova amafuna kukukhululukilani kuposa mmene inuyo mukufunila. Cimene amangofuna n’cakuti tilandile mphatso yamtengo wapatali imeneyi mwa kukhala ndi cikhulupililo komanso kukhala omvela. Kunena zoona, dipo ndilo njila yaikulu imene Mulungu anaonetsela cikondi cake. M’dziko latsopano, tidzaphunzila njila zinanso zimene Yehova wationetsela cikondi cake.​—Mla. 3:11.

ZIMENE DIPO LIMATIPHUNZITSA PONENA ZA YESU

10. (a) N’cifukwa ciyani Yesu anali ndi cisoni cacikulu poganizila imfa yake? (b) Kodi Yesu anayeletsa dzina la Yehova m’njila ziti? (Onaninso danga lakuti “ Kukhulupilika kwa Yesu Kunayeletsa Dzina la Yehova.”)

10 Yesu amakhudzika kwambili ndi mmene anthu amaonela Atate wake. (Yoh. 14:31) Yesu anali ndi cisoni cacikulu poganizila kuti mbili ya Atate wake idzaipitsidwa cifukwa cakuti iye anali kudzapatsidwa mlandu wakuti ndi wonyoza Mulungu komanso kuti ndi cigawenga. N’cifukwa cake anapemphela kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka lolani kuti kapu iyi indipitilile.” (Mat. 26:39) Koma pamene iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mpaka imfa, anayeletsa dzina la Atate wake.

11. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti amawakonda kwambili anthu? (Yohane 13:1)

11 Dipo limatiphunzitsa kuti Yesu amasamala kwambili za anthu, makamaka za ophunzila ake. (Miy. 8:31; welengani Yohane 13:1.) Mwacitsanzo, Yesu anadziwa kuti mbali zina za utumiki wake zidzakhala zovuta kwambili, makamaka imfa yake yowawa. Ngakhale n’telo, pocita utumiki wake, iye sanacite zinthu mwamwambo cabe. M’malomwake, Yesu anali kulalikila, kuphunzitsa, ndi kutumikila ena ndi mtima wake wonse. Ngakhale pa tsiku limene anafa, iye anawasambitsa mapazi atumwi ake, anawaphunzitsa, komanso anawalimbikitsa. (Yoh. 13:​12-15) Kenako ali pamtengo wozunzikilapo, Yesu anapeleka ciyembekezo kwa cigawenga, komanso anapanga makonzedwe akuti amayi ake atsale osamalidwa bwino. (Luka 23:​42, 43; Yoh. 19:​26, 27) Conco, Yesu anaonetsa kuti amawakonda anthu osati cabe powafela, koma anaonetsanso zimenezi mwa kucita nawo mwacikondi komanso mokoma mtima.

12. Kodi Yesu akuticitila ciyani palipano?

12 Ngakhale kuti Khristu anatifela “kamodzi kokha basi,” akali kucitabe zinthu zotithandiza. (Aroma 6:10) Motani? Akali kupitiliza kutithandiza kupindula ndi dipo. Ganizilani zimene akucita palipano. Akutumikila monga Mfumu, Mkulu wa Ansembe, komanso mutu wa mpingo. (1 Akor. 15:25; Aef. 5:23; Aheb. 2:17) Cina, ndi amenenso akuyang’anila nchito yosonkhanitsa odzozedwa ndi a khamu lalikulu. Nchito imeneyi idzatha cisautso b cacikulu cisanathe. (Mat. 25:32; Maliko 13:27) Kuwonjezela apo, kudzela mwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yesu amapatsa cakudya cauzimu atumiki ake okhulupilika m’masiku ano otsiliza. (Mat. 24:45) Ndipo mu ulamulilo wake wa zaka 1,000, adzapitiliza kuticitila zinthu zabwino. Pamene Yehova anapeleka Mwana wake, sanangomupeleka kuti atifele ayi, koma kuti aticitilenso zinthu zina zambili zabwino!

MUSALEKE KUPHUNZILA

13. Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kupitiliza kuphunzila za cikondi cimene Mulungu ndi Khristu ali naco pa ife?

13 Mukapitiliza kusinkhasinkha zimene Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu akucitilani, mudzaphunzila zinthu zatsopano zokhudza cikondi cawo. Pa nyengo ya Cikumbutso ca caka cino, mungawelenge mwacifatse buku limodzi kapena kuposelapo la Uthenga Wabwino. Musamawelenge macaputala ambilimbili pa nthawi imodzi. M’malomwake, muziwelenga modekha ndi kuyesetsa kupeza zifukwa zowonjezela zokondela Yehova ndi Yesu. Ndipo musalephele kuuzako ena zimene mwaphunzila.

14. Kodi kufufuza kungatithandize motani kupitiliza kuphunzila zinthu zatsopano pa nkhani ya dipo komanso ziphunzitso zina? (Salimo 119:97 komanso mawu a m’munsi) (Onaninso cithunzi.)

14 Ngati mwakhala m’coonadi kwa zaka zambili, mungaganize kuti n’zosatheka kuphunzila mfundo zatsopano pankhani zodziwika bwino monga cilungamo ca Mulungu, cikondi cake, komanso dipo. Koma zoona zake n’zakuti, tidzapitilizabe kuphunzila zinthu zatsopano zokhudza nkhani zimenezi komanso zina. Ndiye kodi mungatani? Muziwelenga zofalitsa zathu zozikika m’Baibulo. Mukapeza mfundo ina imene simunamvetse, muzifufuza. Ndipo kwa tsiku lonse, sinkhasinkhani mfundo zimene mwapeza ndi kuona zimene muphunzilapo ponena za Yehova, Mwana wake, ndi cikondi cawo pa inu.​—Welengani Salimo 119:97 komanso mawu a m’munsi.

Ngakhale takhala m’coonadi kwa zaka zambili, n’zotheka kuphunzila zinthu zatsopano zokhudza dipo zimene zingakulitse ciyamikilo cathu (Onani ndime 14)


15. N’cifukwa ciyani tiyenela kupitiliza kufunafuna mfundo zatsopano tikamawelenga Baibulo?

15 Musalefuke ngati simunapeze mfundo yatsopano kapena yocititsa cidwi powelenga kapena pofufuza. Ganizilani za munthu amene amafunafuna golide. Moleza mtima, munthuyo amathela maola ambili ngakhalenso masiku kuti apeze ngakhale kacidutswa kakang’ono kwambili ka golide. Ngakhale n’telo, amalimbikila cifukwa kacidutswa kalikonse ka golide n’kamtengo wapatali kwa iye. Ndiye kuli bwanji kupeza mfundo zatsopano za coonadi! (Sal. 119:127; Miy. 8:10) Conco khalani oleza mtima, ndipo pitilizani kutsatila ndandanda yanu ya kuwelenga Baibulo.​—Sal. 1:2.

16. Kodi tingatengele bwanji Yehova ndi Yesu?

16 Mukamawelenga, ganizilani mmene mungagwilitsile nchito zimene mukuwelengazo. Mwacitsanzo, tengelani cilungamo ca Yehova mwa kucita zinthu mopanda tsankho ndi ena. Tengelani cikondi cimene Yesu ali naco pa Yehova komanso pa anthu mwa kukhala okonzeka kuvutika kaamba ka dzina lake, komanso kudzipeleka pothandiza Akhristu anzanu. Cina, tengelani citsanzo ca Yesu mwa kupitiliza kulalikila ena, kuti nawonso akhale ndi mwayi woonetsa cikhulupililo mu nsembe yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa.

17. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

17 Tikapitiliza kuphunzila za dipo, tidzawonjezela cikondi cathu pa Yehova ndi Mwana wake. Zotulukapo zake n’zakuti iwonso adzatikonda mowilikiza. (Yoh. 14:21; Yak. 4:8) Conco, tiyeni tigwilitse nchito zinthu zimene Yehova watipatsa kuti tiphunzile za dipo. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene timapindulila ndi dipo, komanso mmene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova.

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Kusinkhasinkha” kutanthauza kuganizila kwambili za nkhani inayake ndi kuona mfundo zowonjezela kuti mumvetsetse nkhaniyo.

b Kusonkhanitsa “zinthu zakumwamba” kumene Paulo anachula pa Aefeso 1:​10, n’kosiyana ndi kusonkhanitsa “osankhidwa” kumene Yesu anachula pa Mateyo 24:31 ndi pa Maliko 13:27. Paulo anali kukamba za nthawi pamene Yehova amasankha amene adzalamulila ndi Yesu mwa kuwadzoza ndi mzimu woyela. Koma Yesu anali kukamba za nthawi pamene otsalila odzozedwa adzatengedwele kumwamba cisautso cacikulu cili mkati.