Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu

Mmene Timapindulila ndi Cikondi ca Yehova

Mmene Timapindulila ndi Cikondi ca Yehova

“Khristu Yesu anabwela mʼdziko kudzapulumutsa ocimwa.” ​—1 TIM. 1:15.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mapindu amene timapeza cifukwa ca dipo, komanso mmene tingaonetsele Yehova kuti timaiyamikila mphatso imeneyi.

1. Kodi tingacite ciyani kuti timukondweletse Yehova?

 YELEKEZANI kuti mwapatsa munthu amene mumakonda mphatso yokongola komanso yothandiza kwambili. N’zosacita kufunsa kuti mungakhumudwe kwambili ngati munthuyo angaike mphatsoyo m’bokosi lake losungilamo zinthu popanda kuiganizilapo! Kumbali ina, mungamve bwino ngati munthuyo akuigwilitsa nchito mphatsoyo ndipo amaiyamikila. Mfundo yake ndi yotani pamenepa? Nayenso Yehova anatipatsa Mwana wake monga mphatso. Mosakaikila, amasangalala kwambili tikamaonetsa kuti timaiyamikila mphatso imeneyi komanso cikondi cake, cimene cinamusonkhezela kupeleka dipo!​—Yoh. 3:16; Aroma 5:​7, 8.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 Komabe, nthawi ikamapita tingaleke kuona dipo monga mphatso yamtengo wapatali. Kucita zimenezi kungakhale ngati kuika mphatso ya Mulungu m’bokosi losungilamo zinthu, popanda kuionanso kapena kuiganizila. Kuti izi zisacitike, nthawi zambili tiyenela kumaganizila zimene Mulungu ndi Khristu aticitila. Nkhani ino itithandiza kucita zimenezi. Tikambilane mapindu amene timapeza kaamba ka dipo palipano, komanso amene tidzapeza m’tsogolo. Tikambilanenso mmene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova, makamaka m’nyengo ino ya Cikumbutso.

MAPINDU AMENE TIMAPEZA PALIPANO

3. Chulani phindu limodzi limene timapeza palipano cifukwa ca dipo.

3 Ngakhale palipano, timapeza mapindu kaamba ka nsembe ya dipo limene Khristu anapeleka. Mwacitsanzo, pa maziko a dipo, Yehova amakhululuka macimo athu. Koma sakakamizika kutelo. Amatikhululukila mwakufuna kwake. Moyamikila, wamasalimo analemba kuti: “Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”​—Sal. 86:5; 103:​3, 10-13.

4. Kodi Yehova anapeleka dipo kaamba ka ndani? (Luka 5:32; 1 Timoteyo 1:15)

4 Ena amaona kuti si oyenela kukhululukidwa ndi Yehova. Koma kunena zoona, palibe woyenelela. Mtumwi Paulo anazindikila kuti sanali “woyenela kuchedwa mtumwi.” Koma ngakhale n’telo, anakamba kuti: “Cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili mmene ndililimu.” (1 Akor. 15:​9, 10) Tikalapa macimo athu, Yehova amatikhululukila. N’cifukwa ciyani? Si cifukwa cakuti ndife oyenelela, koma n’cifukwa cakuti amatikonda. Ngati mumadziona wosanunkha kanthu, kumbukilani kuti Yehova sanapeleke dipo kaamba ka anthu angwilo, koma analipeleka kaamba ka ocimwa amene alapa.​—Welengani Luka 5:32; 1 Timoteyo 1:15.

5. Fotokozani cifukwa cake n’kulakwa kuganiza kuti ndife oyenelela kukhululukidwa ndi Yehova cifukwa ca zimene tacita pomutumikila.

5 Palibe aliyense wa ife ayenela kumva kuti ndi woyenelela cifundo ca Yehova ngakhale kuti watumikila Yehova kwa zaka zambili. Koma izi sizitanthauza kuti Yehova sayamikila kukhulupilika kumene takhala tikuonetsa. (Aheb. 6:10) Komabe mfundo ndi yakuti, Yehova anapeleka Mwana wake monga mphatso yaulele osati monga malipilo a utumiki umene tacita. Conco, n’kulakwa kuganiza kuti ndife oyenelela cifundo ca Yehova cifukwa ca utumiki wathu. Kuganiza motelo kungakhale ngati kunena kuti Khristu anafa pacabe.​—Yelekezelani ndi Agalatiya 2:21.

6. N’cifukwa ciyani Paulo anali kucita khama potumikila Yehova?

6 Paulo anali kudziwa kuti sangagule cifundo ca Mulungu. Ndiye n’cifukwa ciyani anali kugwila nchito molimbika potumikila Yehova? Anali kucita izi poonetsa kuyamikila cisomo ca Yehova osati pofuna kuonetsa kuti ndi woyenelela cifundo cake. (Aef. 3:7) Potengela citsanzo ca Paulo, ifenso timamutumikila mokangalika, osati kuti tigule cifundo cake, koma kuti tionetse kuti timaciyamikila.

7. Kodi dipo limatheketsanso ciyani palipano? (Aroma 5:1; Yakobo 2:23)

7 Dipo limatheketsanso kuti tikhale paubale wolimba ndi Yehova. a Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, palibe aliyense wa ife amene anabadwa ali kale paubale ndi Yehova. Koma cifukwa ca dipo, “tingathe kukhala pa mtendele ndi Mulungu” ndipo tingamuyandikile.​—Welengani Aroma 5:1; Yakobo 2:23.

8. N’cifukwa ciyani tiyenela kumuyamikila Yehova cifukwa ca mwayi wokamba naye m’pemphelo?

8 Cimodzi mwa zinthu zimene zimatheka cifukwa cokhala paubale ndi Yehova, ndi mwayi wapadela wokamba naye m’pemphelo. Yehova amamvetsela mapemphelo a atumiki ake akasonkhana pamodzi monga gulu. Kuwonjezela apo, amamvetsela mapemphelo a mtumiki wake aliyense payekhapayekha. Pemphelo limatithandiza kuika mtima m’malo ndipo limatithandiza kukhala ndi mtendele wamumtima. Koma limacita zambili kuposa pa kutithandiza kumvako bwino. Lingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. (Sal. 65:2; Yak. 4:8; 1 Yoh. 5:14) Yesu ali padziko lapansi, anali kupemphela kawilikawili cifukwa anali kudziwa kuti Atate wake adzamumvetsela, komanso kuti pemphelo lidzamuthandiza kulimbitsa ubale wake ndi Atate wake. (Luka 5:16) Ndife oyamikila kuti pa maziko a nsembe ya Yesu, n’zotheka kukhala mabwenzi a Yehova, ngakhale kukamba naye m’pemphelo!

MAPINDU AM’TSOGOLO

9. Kodi alambili okhulupilika adzapeza mapindu otani m’tsogolo kaamba ka dipo?

9 Ndi mapindu otani amene alambili okhulupilika a Yehova adzapeza m’tsogolo kaamba ka dipo? Adzalandila moyo wosatha. Anthu ambili amaganiza kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo wosatha cifukwa anthu akhala akumwalila kwa zaka masauzande. Koma colinga ca Yehova coyambilila cinali cakuti anthu akhale ndi moyo kosatha. Adamu akanapanda kucimwa, kukhala ndi moyo kosatha sikukanaoneka ngati cinthu cosatheka. Ngakhale kuti palipano kungakhale kovuta kuganizila mmene kukhala ndi moyo wosatha kudzakhalile, timakhulupilila ndi mtima wonse kuti n’zotheka ndithu kukhala ndi moyo wosatha. Timatelo cifukwa Yehova anapeleka mtengo wokwela kwambili kuti zimenezi zitheke. Mtengo umenewo ndi mphatso ya Mwana wake wokondeka.​—Aroma 8:32.

10. Kodi odzozedwa ndi a nkhosa zina, akuyembekezela madalitso otani?

10 Ngakhale kuti dalitso la kukhala ndi moyo wosatha lili m’tsogolo, Yehova amafuna kuti tiziliyembekezela mwacidwi. Odzozedwa akuyembekezela kukakhala ndi moyo wosangalatsa kumwamba pomwe azikalamulila dziko lapansi pamodzi ndi Khristu. (Chiv. 20:6) Nawonso a nkhosa zina amayembekezela mwacidwi kudzakhala m’Paradaiso padziko lapansi momwe simudzakhala zopweteka komanso cisoni. (Chiv. 21:​3, 4) Kodi ndinu wa nkhosa zina ndipo mukuyembekezela kukakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? Ngati n’telo, dziwani kuti mphoto imeneyi si cipukuta misozi copatsidwa kwa munthu amene walephela kupita kumwamba. Kumbukilani kuti Yehova analenga anthu kuti azikhala padziko lapansi. Conco, moyo wosatha pano padziko lapansi udzakhala wosangalatsa kopambana.

11-12. Ndi madalitso ena ati amene tikuyembekezela m’Paradaiso? (Onaninso zithunzi.)

11 Ganizilani mmene umoyo udzakhalile kwa inu m’Paradaiso padziko lapansi. Simudzakhala ndi nkhawa poopa kuti mudzadwala kapena kumwalila. (Yes. 25:8; 33:24) Yehova adzakwanilitsa cokhumba cabwino ciliconse cimene muli naco. Kodi mumalakalaka kumvetsa mmene cilengedwe cimagwilila nchito? Kapena mumafuna kuphunzila mozamilapo zokhudza makemiko? Kodi mumalakalaka kuphunzila zowonjezela ponena za nyama? Kapena mumafuna kuphunzila kuliza cipangizo cinacake coimbila, kapena kujambula? Mosakaikila, m’Paradaiso tidzafunikila alimi, anthu amene adzakwanitsa kulemba mapulani a nyumba ndi kuwamanga. Tidzafunikilanso anthu amene azidzakonza ndi kusamalila zinthu, kuphika cakudya, kukonza zida zogwilitsa nchito, komanso kuthandiza kusunga malo kuti akhalebe okongola. (Yes. 35:1; 65:21) Popeza tidzakhala kwamuyaya, zidzakhala zotheka kuphunzila luso lililonse limene mungaliganizile.

12 Zidzakhala zosangalatsa zedi kulandila anthu amene adzaukitsidwa. (Mac. 24:15) Ganizilaninso cimwemwe cimene mudzakhala naco pophunzila za Yehova mwa kusanthula cilengedwe cake cocititsa cidwi. (Sal. 104:24; Yes. 11:9) Koma koposa pamenepo, zidzakhala zokondweletsa kwambili kutumikila Yehova popanda kucimwa. Kodi zoona mungalole kusinthanitsa madalitso amenewa ndi umoyo wocita “macimo n’kusangalala kwa nthawi yocepa”? (Aheb. 11:25) Kutalitali! M’poyenela kutayilapo ciliconse kuti tikalandile madalitso amenewa. Kumbukilani kuti nthawi idzafika pomwe sitidzayembekezelanso Paradaiso. Paradaiso ameneyu adzakhala atafika. Zimenezi sizikanatheka Yehova akanapanda kutikonda kwambili conci mpaka kupeleka Mwana wake monga mphatso.

Ndi madalitso ati amene mukuyembekezela mwacidwi m’Paradaiso? (Onani ndime 11-12)


ONETSANI KUTI MUMAYAMIKILA CIKONDI CA YEHOVA

13. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila cikondi ca Yehova? (2 Akorinto 6:1)

13 Tingaonetse bwanji kuti timamuyamikila Yehova kaamba kotipatsa dipo? Mwa kutsogoza nchito yake mu umoyo wathu. (Mat. 6:33) Ndi iko komwe, Yesu anafa “kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafela nʼkuukitsidwa.” (2 Akor. 5:15) Conde tisaphonye colinga ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.​—Welengani 2 Akorinto 6:1.

14. Tingaonetse bwanji kuti timakhulupilila citsogozo ca Yehova?

14 Njila ina imene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova, ndi kukhulupilila Yehova ndi kutsatila citsogozo cake. Koma kodi tingaonetse bwanji kuti timam’khulupilila? Tikafuna kupanga cisankho pankhani monga zokhudza maphunzilo kapena nchito, tiyenela kuganizila zimene Yehova afuna kuti ticite. (1 Akor. 10:31; 2 Akor. 5:7) Cikhulupililo cathu cikamaonekela m’zocita zathu, cikhulupililoco cimalimba. Nawonso ubwenzi wathu ndi Yehova umalimbilako, ndipo zimenezi zimacititsanso kuti ciyembekezo cathu cikhale cotsimikizika.​—Aroma 5:​3-5; Yak. 2:​21, 22.

15. Tingaonetse bwanji ciyamikilo cathu pa nyengo ya Cikumbutso?

15 Palinso njila ina imene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova. Njilayo ndi kuyesetsa kucita zonse zimene tingathe pa nyengo ino ya Cikumbutso poonetsa Yehova kuti timayamikila dipo. Kuwonjezela pa kukhala ndi colinga cokapezekapo pa Cikumbutso ca caka cino, tingaitanilekonso ena kuti akapezekepo. (1 Tim. 2:4) Afotokozeleni mmene Cikumbutso cimacitikila. N’cifukwa Ciani Yesu Anafa? komanso yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu. Akulu afunika kucita khama kuitanila ozilala kuti akapezekeko. Ganizilani cimwemwe cosaneneka cimene cimakhalako kumwamba komanso padziko lapansi, ngati zina mwa nkhosa zosocela za Yehova zathandizidwa kubwelela kwa iye! (Luka 15:​4-7) Pa Cikumbutso, sitiyenela kungopatsa moni abale ndi alongo amene tikuwadziwa kale ayi. Koma tiyenelanso kupatsa moni acatsopano, komanso amene akhala sakupezeka pa misonkhano kwa nthawi yaitali. Tiyenela kuwapangitsa kumva kuti ndi olandilidwa!​—Aroma 12:13.

16. N’cifukwa ciyani tiyenela kuganizila zowonjezela zimene timacita muulaliki pa nyengo ya Cikumbutso?

16 Kodi mungawonjezeleko nthawi imene mumathela muulaliki pa nyengo ino ya Cikumbutso? Kucita izi ndi njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timayamikila zonse zimene Mulungu ndi Khristu aticitila. Tikamathela nthawi yaitali muulaliki, timakhalanso ndi mipata yoona mmene iye akutithandizila. Zimenezi zimalimbitsa cidalilo cathu mwa iye. (1 Akor. 3:9) Cinanso, muzitsatila ndandanda ya kuwelenga Baibulo pa nyengo ya Cikumbutso yopezeka m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku kapena mu chati yopezeka m’kabuku ka msonkhano. Ngati mungakonde, mungagwilitse nchito Malembawo monga maziko a zimene mufuna kumvetsa mozamilapo.

17. Kodi n’ciyani cimamusangalatsa Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “ Njila Zoonetsela Kuti Timayamikila Cikondi ca Yehova.”)

17 Ngati mikhalidwe yanu singakuloleni kucita zonse zimene tafotokoza m’nkhani ino, muzikumbukila kuti Yehova sayelekezela kuculuka kwa zimene tacita ndi zimene wina wacita ayi. M’malomwake, iye amaona mumtima. Amasangalala akaona kuti mumayamikila mocokela pansi pamtima mphatso yamtengo wapatali ya dipo.​—1 Sam. 16:7; Maliko 12:​41-44.

18. N’cifukwa ciyani timamuyamikila Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu?

18 Popanda dipo, sizikanatheka kukhululukidwa macimo, kukhala paubwenzi ndi Yehova, komanso kukhala ndi ciyembekezo ca moyo wosatha. Tisaleke kuyamikila cikondi ca Yehova cimene cinatheketsa kuti tikhale ndi madalitso amenewa. (1 Yoh. 4:19) Tiyeninso tionetse ciyamikilo cathu kwa Yesu amene anatikonda kwambili conci mpaka kupeleka moyo wake kaamba ka ife!​—Yoh. 15:13.

NYIMBO 154 Cikondi Sicitha

a Yehova anali kukhululukila macimo a anthu amene analiko ngakhale Khristu asanapeleke dipo. Yehova anali kucita zimenezi cifukwa anali kumudalila Mwana wake kuti adzakhalabe wokhulupilika mpaka imfa. Telo kwa Yehova zinali ngati dipo linali litalipilidwa kale.​—Aroma 3:25.