Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

Patsani Yehova Ulemelelo

Patsani Yehova Ulemelelo

LEMBA LA CAKA CA 2025: “M’patseni Yehova ulemelelo woyenela dzina lake.”​—SAL. 96:8.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kudziwa mmene tingapatsile Yehova ulemelelo womuyenelela.

1. Kodi anthu ambili masiku ano amaika kwambili maganizo awo pa ciyani?

 KODI mumaona kuti anthu masiku ano amaika kwambili maganizo awo pa iwo eni kuposa pa ena? Mwacitsanzo, ena amatayila nthawi yawo yoculuka pa soshomidiya pofuna kukopela cidwi ca ena kwa iwo eni, komanso pa zimene akwanitsa kucita. Koma ndi anthu ocepa cabe masiku ano amene amapeleka ulemelelo kwa Yehova Mulungu. M’nkhani ino, tikambilane zimene kupatsa Yehova ulemelelo kumatanthauza, komanso zifukwa zimene tiyenela kutelo. Tikambilanenso mmene tingapatsile Mulungu ulemelelo womuyenelela, komanso mmene iyemwini adzalemekezela dzina lake posacedwa.

KODI KUPATSA YEHOVA ULEMELELO KUMATANTHAUZA CIYANI?

2. Kodi Yehova anaonetsa bwanji ulemelelo wake pa Phili la Sinai? (Onaninso cithunzi

2 Kodi ulemelelo n’ciyani? M’Baibulo, mawu akuti “ulemelelo” angatanthauze ciliconse cimene cingapangitse munthu kuoneka wapamwamba, wocititsa cidwi, kapena wolemekezeka. Yehova anaonetsa ulemelelo wake m’njila yapadela kwambili mtundu wa Aisiraeli utangomasulidwa kumene mu ukapolo ku Iguputo. Onani cocitika ici m’maganizo mwanu: Aisiraeli ofika m’mamiliyoni asonkhana m’tsinde mwa Phili la Sinai kuti akumane ndi Mulungu wawo. Mtambo wakuda bii ukuphimba phili lonselo. Mwadzidzidzi, kukucitika civomezi camphamvu cimene cikugwedeza nthaka imene aimililapo, ndipo n’kuthekanso kuti phililo likuphulika. Pamene izi zikucitika, pakuonekanso kung’anima kwa mphezi, kugunda kwa mabingu, ndipo kukumveka kulila kwa lipenga kogonthetsa m’khutu. (Eks. 19:​16-18; 24:17; Sal. 68:8) N’zosacita kufunsa kuti Aisiraeli anacita cidwi kwambili kuona ulemelelo wa Yehova m’njila yapadela imeneyi!

Yehova anaonetsa ulemelelo wake m’njila yapadela pa Phili la Sinai (Onani ndime 2)


3. Kodi kupatsa Yehova ulemelelo kutanthauza ciyani?

3 Koma kodi n’zothekanso kwa ife anthu kumupatsa ulemelelo Yehova? Inde n’zotheka. Njila imodzi imene timapatsila Yehova ulemelelo ndi kuuzako ena za mphamvu zake zodabwitsa, komanso makhalidwe ake ocititsa cidwi. Njila ina imene timapatsila Mulungu ulemelelo ndi kuonetsa kuti iye ndi amene amatithandiza kucita zimene timatha kucita. (Yes. 26:12) Mfumu Davide ndi citsanzo cabwino kwambili ca munthu amene anapatsa Yehova ulemelelo. M’pemphelo limene Davide anapeleka pamaso pa mpingo wonse wa Aisiraeli, anauza Mulungu kuti: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemelelo ndi ulemu ndi zanu, cifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu.” Davide atamaliza pemphelo lake, “anthu onsewo anayamba kutamanda Yehova.”​—1 Mbiri 29:​11, 20.

4. Ndi motani mmene Yesu anapatsila Yehova ulemelelo?

4 Yesu ali padziko lapansi, anapatsa Atate wake ulemelelo mwa kunena kuti iwo ndi amene anamupatsa mphamvu yocitila zozizwitsa. (Maliko 5:​18-20) Njila ina imene Yesu anali kupatsila Yehova ulemelelo ndi zimene anali kukamba ponena za Atate wake, komanso mmene anali kucitila ndi ena. Mwacitsanzo, panthawi ina Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge. Pakati pa anthu omwe anali kumumvetsela, panali mayi wina amene anali wogwidwa ndi ciwanda kwa zaka 18. Ciwandaco cinamupangitsa kukhala wopindika msana moti sanali kutha kuwelamuka. Zinali zosautsadi! Yesu atagwidwa ndi cifundo, anapita kwa mayiyo, ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” Kenako Yesu anaika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo mayiyo anawelamuka “n’kuyamba kutamanda Mulungu.” Mayiyo anayamika Yehova kwambili cifukwa thanzi lake linabwelela m’malo. (Luka 13:​10-13) Mayiyu anali ndi cifukwa cabwino copatsila Yehova ulemelelo. Ifenso tili ndi zifukwa zabwino zom’patsila ulemelelo.

N’CIYANI CIMATILIMBIKITSA KUPATSA YEHOVA ULEMELELO?

5. Kodi tili ndi zifukwa ziti zom’patsila ulemu Yehova?

5 Timamupatsa ulemelelo Yehova cifukwa timamulemekeza kwambili. Tili ndi zifukwa zambili zomulemekezela. Mwacitsanzo, Yehova ndi wamphamvuzonse, mphamvu zake zilibe malile. (Sal. 96:​4-7) Cina, ali ndi nzelu zakuya zimene zimaonekela bwino m’zinthu zimene anapanga. Kuwonjezela apo, iye ndiye kasupe wa moyo, ndipo watipatsa zonse zofunikila kuti tipitilize kukhala ndi moyo. (Chiv. 4:11) Cinanso n’cakuti ndi wokhulupilika. (Chiv. 15:4) Kuwonjezela pa izi, zonse zimene amacita zimayenda bwino, ndipo amasunga malonjezo ake nthawi zonse. (Yos. 23:14) Ndiye cifukwa cake ponena za Yehova, mneneli Yeremiya anati: “Pakati pa anzelu onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiletu aliyense wofanana ndi inu.” (Yer. 10:​6, 7) Kunena zoona, tili ndi zifukwa zabwino zolemekezela Atate wathu wakumwamba. Koma sikuti Yehova amangocita zinthu zimene zimapangitsa kuti tizimulemekeza. Iye alinso ndi makhalidwe abwino amene amatipangitsa kuti tizimukonda kwambili.

6. N’cifukwa ciyani timamukonda Yehova?

6 Timamupatsa ulemelelo Yehova cifukwa timamukonda mocokela pansi pa mtima. Onani makhalidwe angapo amene amatisonkhezela kuti timukonde. Iye ndi wacifundo. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Tikamavutika, iyenso zimam’khudza. (Zek. 2:8) Amacititsa kuti zikhale zosavuta kuti timufikile. (Sal. 25:14; Mac. 17:27) Kuwonjezela apo, Yehova ndi wodzicepetsa, moti “amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumucotsa m’fumbi.” (Sal. 113:​6, 7) Kunena zoona, kodi izi si zifukwa zamphamvu zotisonkhezela kum’patsa ulemelelo Mulungu wathu wamkulu?​—Sal. 86:12.

7. Kodi ndi mwayi wapadela uti umene tili nawo?

7 Timapatsa Yehova ulemelelo cifukwa timafuna kuti ena amudziwe. Ambili sadziwa zoona zake zokhudza Yehova. N’cifukwa ciyani? Cifukwa n’cakuti Satana waaphimba maganizo pofalitsa mabodza amkunkhuniza onena za iye. (2 Akor. 4:4) Satana wapangitsa anthu kukhulupilila kuti Yehova ndi wamkali, sasamala za anthu, komanso kuti ndiye wacititsa ambili mwa mavuto amene timakumana nawo m’dzikoli. Koma ife timadziwa zenizeni ponena za Mulungu wathu. Ndipo tili ndi mwayi wouza anthu coonadi ponena za Mulungu wathu, ndi kuwathandiza kuti nawonso ayambe kumupatsa ulemelelo. (Yes. 43:10) Nkhani yaikulu mu Salimo 96 ndi kupatsa Yehova ulemelelo. Pamene tikukambilana mawu ouzilidwa a mu Salimoli, ganizilani njila zimene mungapatsile Yehova ulemelelo womuyenelela.

KODI TINGAM’PATSE MOTANI YEHOVA ULEMELELO WOMUYENELELA?

8. Ndi motani mmene tingamupatsile ulemelelo Yehova? (Salimo 96:​1-3)

8 Welengani Salimo 96:​1-3. Tingapatse Yehova ulemelelo mwa zimene timakamba ponena za iye. Mavesiwa akutiuza kuti tiyenela ‘kuimbila Yehova,’ ‘kutamanda dzina lake,’ ‘kulengeza uthenga wabwino wa cipulumutso cake,’ komanso ‘kulengeza ulemelelo wake pakati pa anthu a mitundu ina.’ Zonsezi ndi njila zimene tingapatsile ulemelelo Atate wathu wakumwamba. Atumiki a Yehova akale anali ofunitsitsa kuuzako ena zinthu zabwino zimene Yehova anawacitila, komanso anali kumukhalila kumbuyo. (Dan. 3:​16-18; Mac. 4:29) Kodi tingatengele bwanji citsanzo cawo?

9-10. Kodi zimene zinacitikila Angelena zakuphunzitsani ciyani? (Onaninso cithunzi.)

9 Ganizilani citsanzo ici ca mlongo wina wa ku America dzina lake Angelena. a Iye anaonetsa kulimba mtima pokamba za Yehova ku nchito kwake. Pakampani pawo, anchito amapemphedwa kufotokoza za umoyo wawo kwa anchito anzawo. Pokhala watsopano, Angelena anapemphedwa kupezekapo pa miting’i imeneyi. Iye anakonza zakuti akaonetse zithunzi zosonyeza umoyo umene ali nawo monga wa Mboni za Yehova. Nthawi yakuti Angelena alankhulepo itatsala pang’ono kukwana, wanchito mnzake anayamba kufotokoza kuti iyeyo analeledwa monga wa Mboni za Yehova. Wanchito mnzakeyo anayamba kunena zoipa ponena za Mboni za Yehova, komanso zimene amakhulupilila. Angelena anati: “Mtima wanga unali kugunda ndi mantha. Koma mumtima n’nadzifunsa kuti: ‘Kodi n’dzalola munthu uyu kukamba mabodza ponena za Yehova? Kapena n’dzamukhalila kumbuyo Mulungu wanga?’”

10 Wanchito mnzakeyo atangotsiliza, Angelena anapeleka pemphelo lacidule camumtima. Mokoma mtima, Angelena anauza mwamunayo kuti: “Umoyo wanga ndi wofananako ndi umoyo wanu. Inenso n’naleledwa monga Mboni ya Yehova, ndipo mpaka pano ndikali Mboni.” Ngakhale kuti zinali zopanikiza kwambili, Angelena anaikabe mtima wake m’malo pamene anali kuwaonetsa zithunzi zosonyeza iye ndi anzake akusangalala potumikila Yehova, ndipo anaikila kumbuyo cikhulupililo cake mosamala. (1 Pet. 3:15) Kodi panakhala zotulukapo zotani? Pamene Angelena anali kumaliza kufotokoza, wanchito mnzake uja anali ataika mtima m’malo. Iye anafika ngakhale pochula zinthu zabwino zimene zinamucitikila pamene anali kukula monga wa Mboni za Yehova. Angelena anakamba kuti: “Yehova ndi woyenela kumukhalila kumbuyo. Ndi mwayi wapadela kukamba zoona ponena za iye.” Ifenso tili ndi mwayi wapadela wotamanda Yehova ndi kumupatsa ulemelelo ngakhale pamene ena akumunyoza.

Tingapatse Yehova ulemelelo kudzela m’zokamba zathu (Onani ndime 9-10) b


11. Kuyambila kale, kodi olambila oona akhala akugwilitsa nchito motani mfundo ya pa Salimo 96:8?

11 Welengani Salimo 96:8. Tingamupatse ulemelelo Yehova mwa kum’patsa zinthu zathu za mtengo wapatali. Olambila oona akhala akulemekeza Yehova mwa njila imeneyi. (Miy. 3:9) Mwacitsanzo, Aisiraeli anapeleka ndalama, komanso zinthu zawo za mtengo wapatali pothandizila nchito yomanga kacisi komanso kuisamalila. (2 Maf. 12:​4, 5; 1 Mbiri 29:​3-9) Ena mwa ophunzila a Khristu anali kutumikila Yesu ndi atumwi ake “pogwilitsa nchito cuma cawo.” (Luka 8:​1-3) Nawonso Akhristu a m’nthawi ya atumwi anatumiza ndalama kwa abale ndi alongo awo akuuzimu a kudela kumene kunagwa njala. (Mac. 11:​27-29) Masiku ano, ifenso tingapatse ulemelelo Yehova mwa kucita zopeleka zaufulu.

12. Kodi tingam’patse bwanji Yehova ulemelelo mwa zopeleka zathu? (Onaninso cithunzi.)

12 Onankoni citsanzo cimodzi cabe coonetsa mmene tingam’patsile ulemelelo Yehova mwa zopeleka zathu. Lipoti lina la mu 2020 linati ku Zimbabwe kunali cilala cimene cinatenga nthawi yaitali. Miyoyo ya anthu mamiliyoni inali pa ciopsezo cifukwa ca njala yadzaoneni. Mmodzi wa okhudzidwawo anali mlongo, dzina lake Prisca. Ngakhale kuti kunali njala, mlongoyu anapitiliza kulalikila pa Citatu komanso pa Cinayi paliponse, ngakhale pa nyengo yolima. Anthu a kudela kwawo anali kumunyoza cifukwa coti anali kupita muutumiki m’malo mokagwila nchito kumunda. Anali kumuuza kuti, “Udzafa ndi njala iwe.” Mwacidalilo, iye anali kuwauza kuti, “Yehova sanayambe wafulatilapo atumiki ake.” Pasanapite nthawi, mlongoyu analandila thandizo locokela ku gulu lathu. Prisca analandila cakudya komanso zinthu zina zimene anali kufunikila kaamba ka copeleka cimene timacita. Anthu a kudela kwawo anakhudzika mtima ndipo anamuuza kuti, “Mulungu sanakufulatile ngakhale pang’ono, conco tikufuna kuphunzila zambili zokhudza iye.” Anthu 7 mwa anthu akudela lake, anayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo.

Tingapatse Yehova ulemelelo pogwilitsa nchito zinthu zathu zamtengo wapatali (Onani ndime 12) c


13. Kodi makhalidwe athu angam’patse bwanji ulemelelo Yehova? (Salimo 96:9)

13 Welengani Salimo 96:9. Tingam’patse ulemelelo Yehova mwa makhalidwe athu. M’nthawi zakale, ansembe amene anali kutumikila pa kacisi wa Yehova anayenela kukhala oyela kuthupi. (Eks. 40:​30-32) Koma cofunika kwambili kuposa kukhala oyela kuthupi, ndi kukhala oyela m’makhalidwe athu. (Sal. 24:​3, 4; 1 Pet. 1:​15, 16) Tiyenela kucita khama kuvula “umunthu wakale,” womwe ndi kaganizidwe komanso makhalidwe odetsedwa. Koma tiyenela kuvala “umunthu watsopano,” womwe ndi kaganizidwe komanso kacitidwe ka zinthu komwe kamaonetsa makhalidwe a Yehova aulemelelo. (Akol. 3:​9, 10) Ndi thandizo la Yehova, ngakhale anthu a makhalidwe oipitsitsa angathe kusintha ndi kuvala umunthu watsopano.

14. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Jack? (Onaninso cithunzi.)

14 Ganizilani zimene zinacitikila mwamuna wina waciwawa komanso woopsa kwambili dzina lake Jack, amene anthu anamupatsa dzina lakuti Ciwanda. Cifukwa ca milandu yake, Jack anagamulidwa kuti akanyongedwe. Pamene Jack anali kuyembekezela kunyongedwa, m’bale wina amene anali kuyendela kundendeko, anamupempha kuti aziphunzila naye Baibulo ndipo Jack anavomela. Ngakhale kuti Jack anacita zinthu zambili zoipa, iye anasintha ndipo m’kupita kwa nthawi anabatizika n’kukhala wa Mboni za Yehova. Jack anali atasintha kwambili moti pa tsiku limene anali kukanyongedwa, ena mwa alonda a ndende anagwetsa misozi pomwe anali kulailana naye. Mkulu wa asilikali amene anali kugwila nchito pa ndendeyo anati, “Panthawi ina, Jack ndiye anali mkaidi woopsa kwambili kundende kuno, koma tsopano ndi mmodzi wa akaidi a makhalidwe abwino koposa.” Patapita mlungu umodzi Jack atanyongedwa, abale amene anali kupita kukacititsa misonkhano ku ndendeko, anakumana ndi mkaidi wina amene anapezeka pa msonkhanowo kwa nthawi yoyamba. N’ciyani cinam’sonkhezela kupezekapo? Anakhudzika mtima kwambili ndi mmene Jack anasinthila khalidwe lake, ndipo anafuna kudziwa zimene angacite kuti azilambila Yehova. Cocitikaci cionetsa bwino lomwe kuti Atate wathu wakumwamba tingam’patse ulemelelo mwa khalidwe lathu!​—1 Pet. 2:12.

Tingapatse Yehova ulemelelo mwa makhalidwe athu (Onani ndime 14) d


KODI YEHOVA ADZALILEMEKEZA MOTANI DZINA LAKE POSACEDWA?

15. Kodi posacedwa Yehova adzalilemekeza bwanji dzina lake kothelatu? (Salimo 96:​10-13)

15 Welengani Salimo 96:​10-13. Mavesi othela amenewa a Salimo 96, amafotokoza Yehova monga Woweluza komanso Mfumu yacilungamo. Kodi Yehova adzalilemekeza motani dzina lake posacedwa? Adzatelo mwa ziweluzo zake. Posacedwa, adzawononga Babulo Wamkulu cifukwa wabweletsa citonzo pa dzina lake loyela. (Chiv. 17:​5, 16; 19:​1, 2) Ena amene adzaone kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, angadzasankhe kugwilizana nafe pa kulambila koona. Pamapeto pake, Yehova adzawononga dongosolo lonse la Satanali pa Aramagedo, ndi kucotsa onse amene amamutsutsa ndi kunyoza dzina lake. Koma adzapulumutsa onse amene amamukonda ndi kumumvela, amenenso amanyadila kumupatsa ulemelelo. (Maliko 8:38; 2 Ates. 1:​6-10) Pambuyo pa ciyeso comaliza cimene cidzabwela pambuyo pa zaka 1,000 za ulamulilo wa Khristu, Yehova adzakhala atayeletsa dzina lake kothelatu. (Chiv. 20:​7-10) Panthawi imeneyo, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemelelo wa Yehova, ngati mmene madzi amadzazila nyanja.”​—Hab. 2:14.

16. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciyani? (Onaninso cithunzi.)

16 Zidzakhala zokondweletsa zedi pa nthawiyo pamene munthu aliyense adzapatse Yehova ulemelelo woyenelela dzina lake! Koma pamene tikuyembezela nthawi imeneyo, tingacite mbali yathu mwa kum’patsa ulemelelo Mulungu pa mpata uliwonse umene wapezeka. Pofuna kuonetsa kukula kwa nkhani imeneyi, Bungwe Lolamulila lasankha Salimo 96:8 kukhala lemba lathu la caka ca 2025: “Mʼpatseni Yehova ulemelelo woyenela dzina lake.”

Pa nthawi ina, aliyense adzapatsa Yehova ulemelelo woyenelela dzina lake! (Onani ndime 16)

NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova

a Maina ena asinthidwa.

b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Cithunzi coyelekezela zimene zinacitikila Angelena.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Cithunzi coyelekezela zimene zinacitikila Prisca.

d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Cithunzi coyelekezela zimene zinacitikila Jack.