Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Yesu anakhala liti Mkulu wa Ansembe? Nanga kodi pali kusiyana pakati pa nthawi imene pangano latsopano linayenelezedwa mwalamulo komanso pamene linayamba kugwila nchito?

Pali umboni woonetsa kuti Yesu anakhala Mkulu wa Ansembe pamene anabatizika mu 29 C.E. Kodi umboniwo ni wotani? Pa ubatizo wake, Yesu anadzipeleka pa guwa lansembe lophiphilitsila, limene ni “cifunilo” ca Mulungu. (Agal. 1:4; Aheb. 10:5-10) Guwa lansembe lophiphilitsila limenelo lakhalapo kungocokela pamene Yesu anabatizidwa. Zioneka kuti kacisi wamkulu wauzimu nayenso anakhazikitsidwa pa nthawi ya ubatizo wa Yesu. Kacisi wauzimu ameneyu aimila makonzedwe a kulambila koyela kwa Yehova kozikidwa pa nsembe ya dipo. Guwa lansembe limeneli ni mbali yofunika ya kacisi.—Mat. 3:16, 17; Aheb. 5:4-6.

Kacisi wamkulu wauzimu atakhazikitsidwa, panafunikanso mkulu wa ansembe wotumikila mmenemo. Conco, Yehova anadzoza Yesu na “mzimu woyela ndi mphamvu” kuti akhale mkulu wa ansembe. (Mac. 10:37, 38; Maliko 1:9-11) Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Yesu anaikidwa kukhala Mkulu wa Ansembe asanaphedwe na kuukitsidwa? Citsanzo ca Aroni komanso akulu ansembe ena amene anamuloŵa m’malo, cingatithandize kupeza yankho pa funso limeneli.

Mogwilizana na Cilamulo ca Mose, mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa a cihema. Ndipo kacisi atamangidwa, mkulu wa ansembe yekha ndiyenso anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa a kacisi. Pakati pa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa, panali kukhala nsalu yochinga. Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo cabe, m’pamene mkulu wa ansembe anali kudutsa nsalu yochingayo kuloŵa m’Malo Oyela Koposa. (Aheb. 9:1-3, 6, 7) Aroni na ena omuloŵa m’malo anadzozedwa monga akulu ansembe asanadutse “nsalu [yeni-yeni] yochinga” ya cihema kuloŵa m’Malo Oyela Koposa. Nayenso Yesu ayenela kuti anaikidwa kukhala Mkulu wa Ansembe wa kacisi wamkulu wauzimu asanaphedwe. Ndipo pambuyo pophedwa anadutsa “nsalu yochinga, imene ndi thupi lake,” n’kuukitsidwila kumoyo wakumwamba. (Aheb. 10:20) Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anakamba kuti Yesu anabwela monga “mkulu wa ansembe,” ndipo pambuyo pake anadutsa “m’cihema cacikulu ndi cangwilo kwambili cimene sicinapangidwe ndi manja a anthu,” n’kuloŵa “kumwamba kwenikweniko.”—Aheb. 9:11, 24.

Palibe kusiyana pakati pa nthawi imene pangano latsopano linayenelezedwa mwalamulo komanso pamene linayamba kugwila nchito. N’cifukwa ciani takamba conco? Pamene Yesu anapita kumwamba kukapeleka mtengo wa moyo wake wangwilo monga dipo lotiwombola, anacita zinthu ziŵili pa zinthu zitatu zofunikila poyeneleza mwalamulo pangano latsopano. Zimene anacitazo zinapangitsanso kuti pangano latsopano liyambe kugwila nchito. Kodi zinthu zimenezo n’ziti?

Coyamba, Yesu anaonekela pamaso pa Yehova. Caciŵili, anapeleka mtengo wa nsembe yake kwa Yehova. Ndipo pamapeto pake, Yehova analandila mtengo wa magazi a Yesu, amene anakhetsedwa monga nsembe. Zinthu zimenezi zitacitika, m’pamene pangano latsopano linayamba kugwila nchito.

Baibo sikamba nthawi yeni-yeni pamene Yehova analandila mtengo wa nsembe ya Yesu. Conco sitingachule nthawi yeni-yeni pamene pangano latsopano linayenelezedwa mwalamulo komanso pamene linayamba kugwila nchito. Komabe, tidziŵa kuti Yesu anapita kumwamba kutatsala masiku 10 kuti Pentekosite acitike. (Mac. 1:3) Pa nthawi ina mkati mwa masiku 10 amenewo, Yesu anapeleka mtengo wa nsembe yake kwa Yehova, ndipo Yehova analandila. (Aheb. 9:12) Umboni wa zimenezi unaonekela bwino pa Pentekosite. (Mac. 2:1-4, 32, 33) Pa nthawi imeneyo, zinaonekelatu kuti pangano latsopano linali litayenelezedwa mwalamulo ndiponso linali litayamba kugwila nchito.

Mwacidule, pangano latsopano linayenelezedwa mwalamulo komanso linayamba kugwila nchito pamene Yehova analandila mtengo wa magazi a Yesu, amene anakhetsedwa monga nsembe. Ndipo Mkulu wa Ansembe Yesu ndiye anali Mkhalapakati wa panganolo.—Aheb. 7:25; 8:1-3, 6; 9:13-15.