Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Nangocita Zimene N’nayenela Kucita

Nangocita Zimene N’nayenela Kucita

KWA zaka zoposa 30, Donald Ridley anali loya woimila Mboni za Yehova pa milandu ku makhoti. Iye anacita zambili poteteza ufulu umene odwala ali nawo wokana kuikidwa magazi. M’bale Donald Ridley anathandiza Mboni za Yehova kupambana milandu yambili ku makhoti akulu-akulu ku America. Iye anali wakhama pa nchito, wodzicepetsa, ndiponso wodzipeleka. Anzake anali kungomuchula kuti Don.

Mu 2019, Don anapezeka na matenda enaake osacilitsika amene si ofala. Matendawo anakula mwamsanga, ndipo iye anamwalila pa August 16, 2019. Nayi mbili yake.

N’nabadwa mu 1954 mu mzinda wa St. Paul, m’cigawo ca Minnesota, ku America. Banja lathu linali la Cikatolika, komanso losalemela kweni-kweni. Ndine waciŵili pa ana 5. Pamene n’nali mwana, n’nali kuphunzila pa sukulu ya Akatolika, ndipo ku chechi n’nali kamnyamata kotumikila wansembe. Olo n’telo, sin’nali kudziŵa zambili za Baibo. N’nali kukhulupilila kuti kuli Mulungu amene analenga zinthu zonse, koma n’naona kuti chechi ya Katolika sikananithandiza kumulambila moyenelela.

KUPHUNZILA COONADI

Nili m’caka coyamba pa koleji ya za malamulo ya William Mitchell, banja lina la Mboni za Yehova linafika panyumba panga. Pa tsikulo n’natangwanika na kucapa zovala. Ndipo mokoma mtima iwo anavomela kuti akabwelenso nthawi ina. Atabwela, n’nawafunsa mafunso aŵili akuti: “N’cifukwa ciani anthu abwino zinthu siziwayendela bwino m’dzikoli?” komanso lakuti “N’ciani cingathandize munthu kukhala wacimwemwe?” Ananipatsa buku lakuti, Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, na Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lacikuto ca gilini. Komanso, n’navomela kuyamba kuphunzila Baibo. Zimenezi zinanitsegula maso. N’nakondwela kwambili kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ni boma limene lidzalamulila dziko lonse. N’nali kuona kuti maboma a anthu alephelelatu kulamulila bwino cifukwa zoŵaŵa, kuvutika, kupanda cilungamo, na masoka zinali ponse-ponse.

N’nadzipatulila kwa Yehova kuciyambi kwa caka ca 1982, ndipo pambuyo pake n’nabatizika m’caka comweco pa Msonkhano Wacigawo wakuti “Coonadi ca Ufumu,” umene unacitikila ku St. Paul Civic Center. Pambuyo pa wiki imodzi, n’nabwelelanso kumeneko kukalemba mayeso a za uloya. Kuciyambi kwa mwezi wa October, n’namvela kuti naphasa mayesowo, ndipo nikanatha kugwila nchito ya uloya.

Pa msonkhano wacigawo umenewo, wakuti “Coonadi ca Ufumu,” n’nakumana na m’bale Mike Richardson, amene anali kutumikila pa Beteli ya ku Brooklyn. Iye ananiuza kuti ku likulu kunakhazikitsidwa Ofesi ya za Malamulo. N’nakumbukila mawu a nduna ya ku Itiyopiya opezeka pa Machitidwe 8:36. Ndipo mumtima n’nati, ‘N’ciani cikuniletsa kufunsila kukatumikila ku Ofesi ya Zamalamulo?’ Conco, n’nafunsila utumiki wa pa Beteli.

Makolo anga sanakondwele kuti n’nakhala Mboni ya Yehova. Atate ananifunsa kuti, ‘Udzapindula ciani na maphunzilo ako a uloya ukayamba kuseŵenza ku Watchtower?’ N’nawauza kuti nizikaseŵenza monga wanchito wongodzipeleka. N’nawauzanso kuti nizikalandila cabe alawansi yocepa pa mwezi mofanana na atumiki ena a pa Beteli.

Mu 1984, pambuyo potsiliza nchito imene n’nali kugwila pa khoti inayake, n’napita kukayamba utumiki wanga pa Beteli ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. N’nauzidwa kuti nizitumikila ku Ofesi ya Zamalamulo. Nchito imene n’nali kugwila ku khoti inanithandiza kukonzekela zobwela m’tsogolo.

KUKONZANSO CINYUMBA CA ZAMASEŴELA COCHEDWA STANLEY THEATER

Mmene cinyumba ca Stanley Theater cinali kuonekela citangogulidwa

Mu November 1983, gulu lathu linagula cinyumba ca zamaseŵela cochedwa Stanley Theater mumzinda wa Jersey, m’cigawo ca New Jersey. Abale anapita kuti akapemphe cilolezo cakuti akonzenso nthambo za magetsi komanso mapaipi a madzi m’cinyumbaco. Abale atakumana na akulu-akulu a boma a mumzindawo, anafotokoza kuti afuna kuti cinyumbaco azicitilamo misonkhano ikulu-ikulu ya Mboni za Yehova. Koma panali vuto linalake. Malamulo a mzinda wa Jersey okamba za moseŵenzetsela nyumba, anali akuti nyumba zolambililamo ziyenela kupezeka cabe m’malo okhala anthu osati m’malo amalonda. Cinyumba ca Stanley Theater cinali ku malo amalonda. Conco, akulu-akulu a boma anakana kutipatsa cilolezo. Abale anapitanso kukapempha cilolezo, koma anawakanila.

Mu wiki yanga yoyamba ya utumiki wa pa Beteli, gulu lathu linapeleka nkhaniyo ku khoti. Nkhani zotele n’nali kuzidziŵa bwino, cifukwa pa nthawiyo n’nali n’tangotsiliza kumene nchito ya uloya ya zaka ziŵili, imene n’nali kuseŵenzela pa khoti inayake mumzinda wa St. Paul, ku Minnesota. Mmodzi wa maloya athu anakamba kuti Cinyumba ca Stanley Theater cinali kugwilitsidwa nchito pa zocitika zosiyana-siyana, monga kutambitsilamo mafilimu, kuimbilamo nyimbo, na zina zotelo. Ndiye funso linali lakuti, n’cifukwa ciani akulu-akulu a mzindawo anali kukamba kuti kupemphelelamo n’kuphwanya malamulo? Khotiyo inapenda nkhaniyo, ndipo inagamula kuti akulu-akulu a boma a mumzinda wa Jersey anatiphwanyila ufulu wa kulambila, moti inawalamula kuti atipatse cilolezo kuti tiziseŵenzetsa cinyumbaco. Apa n’nayamba kuona mmene Yehova anali kudalitsila gulu lake kupitila mu ofesi ya zamalamulo popititsa patsogolo nchito yake. N’nakondwela kwambili kuti n’nathandizilako pa nkhaniyi.

Abale anaiyamba nchito yaikulu yokonzanso cinyumbaco. Caka cisanathe, nchitoyo inatha, ndipo pa September 8, 1985, mwambo wotsiliza maphunzilo a giliyadi a kilasi namba 79 unacitikila m’cinyumbaco, comwe cinakhala Bwalo la Misonkhano mu mzinda wa Jersey. Monga mmodzi wa oimilako gulu la Yehova pa milandu, n’naona kuti unali mwayi waukulu kuthandiza kupititsa patsogolo nchito ya Ufumu. Izi zinanipatsa cimwemwe kwambili kuposa nchito iliyonse imene n’nacitapo monga loya nikalibe kubwela ku Beteli. Sin’nali kudziŵa kuti m’tsogolo Yehova adzaniseŵenzetsanso pa milandu ina yambili.

KUTETEZA UFULU WA WODWALA WOLANDILA CITHANDIZO POPANDA KUSEŴENZETSA MAGAZI

M’zaka za m’ma 1980, nthawi zambili madokotala komanso akulu-akulu a zipatala sanali kulemekeza cosankha ca Mboni cakuti athandizidwe popanda kuseŵenzetsa magazi. Zinali kukhala zovuta kwambili kwa azimayi apakati, cifukwa nthawi zambili oweluza m’makhoti anali kuona kuti azimayi otelo analibe ufulu wokana kuikidwa magazi. Oweluzawo anali kukamba kuti ngati mayi wapakati sanaikidwe magazi, zingapangitse kuti amwalile n’kusiya mwanayo ali wamasiye.

Pa December 29, 1988, Mlongo Denise Nicoleau anataya magazi kwambili pambuyo pobeleka mwana wake wamwamuna. Magazi ake anacepa kwambili, ndipo a dokotala anamuuza kuti afunika kuikidwa magazi. Koma Mlongo Nicoleau anakana. M’maŵa tsiku lotsatila, akulu-akulu a cipatalaco anapita ku khoti kukapempha cilolezo cakuti amuike magazi mlongoyo, cifukwa anali kuona kuti kucita zimenezi kunali kofunika kwambili. Woweluza wa khotiyo anapeleka cilolezo kwa madokotala cakuti amuike magazi mlongo Nicoleau, popanda kumudziŵitsa kapena kumvelako maganizo ake kapenanso a mwamuna wake.

Pa Cisanu, pa December 30, madokotala a pacipatalaco anamuika magazi Mlongo Nicoleau, olo kuti mwamuna wake na acibululu ake amene anali kum’samalila anakana. Madzulo a tsikulo, acibululu angapo a mlongoyo komanso akulu ena a mumpingo anamangidwa, pa mlandu wakuti anali kutsekeleza madokotala kuti asamuike magazi mlongoyo. Ndipo tsiku lotsatila, nkhani imeneyi inafalitsidwa m’manyuzipepala, pa ma TV, komanso pa mawailesi mumzinda wa New York.

Nili na M’bale Philip Brumley tili acinyamata

Pa Mande m’maŵa, n’nakambilana na Milton Mollen, amene anali woweluza wa khoti yaikulu. N’namufotokozela zoona zake za nkhaniyo, na kumuuza momveka bwino kuti woweluza winayo anapeleka cilolezo kwa madokotala coika magazi Mlongo Nicoleau popanda kukambilana naye. Mollen, woweluza wa khoti yaikuluyo ananiuza kuti madzulo a tsikulo, nipite ku ofesi yake kuti tikakambilane zambili za nkhani imeneyo, kuphatikizapo malamulo okhudza nkhaniyo. Pokaonana na woweluzayo, n’napita na M’bale Philip Brumley. Woweluzayo anaitananso loya wa cipatalaco. Nkhani inakula, moti pa nthawi ina mkati mwa zokambilanazo, M’bale Brumley anacita kulemba tumawu pa kapepala twakuti, “ugwileni mtima m’bale wanga.” Niona kuti malangizo amenewa anali othandiza cifukwa n’nali n’tayamba kukamba mwaukali potsutsa zimene loyayo anali kufotokoza.

Kucokela kumanzele kupita kulamanja: Richard Moake, Gregory Olds, Paul Polidoro, Philip Brumley, ine, komanso Mario Moreno—maloya athu pa tsiku lokamba mlandu wa pakati pa Watchtower na Village of Strattonour m’khoti yaikulu kwambili ku America.—Onani Galamukani! ya January 8, 2003

Pambuyo pokambilana kwa ola limodzi, woweluzayo anakamba kuti nkhaniyo idzakhala yoyamba kukambidwa m’khoti tsiku lotsatila. Pamene tinali kucoka mu ofesi yake, Mollen anakamba kuti loya wa cipatalaco “adzakhala na nchito yaikulu maŵa.” Izi zinatanthauza kuti loyayo adzafunika kulimba kuti ateteze akulu-akulu a cipatala pa mlandu umene anacita. N’naona kuti Yehova anali kunitsimikizila kuti tidzapambana mlanduwo. N’nacita cidwi kuona kuti iye akutiseŵenzetsa pokwanilitsa cifunilo cake.

Tinaseŵenza mpaka usiku kukonzekela zimene tikakambe tsiku lotsatila. Popeza kuti khoti ili pafupi kwambili na ofesi ya nthambi ya ku Brooklyn, ambili a ife amene tinali kutumikila mu Ofesi ya Zamalamulo, tinangoyenda wapansi kupita kumeneko. Oweluza anayi a khotiyo atamvetsela nkhaniyo, anakamba kuti a cipatala sanafunike kupatsidwa cilolezo cakuti aike magazi mlongo Nicoleau. Khoti yaikuluyo inapeleka cigamulo mokomela Mlongo wathu. Inakambanso kuti cizoloŵezi cotenga cilolezo kukhoti cakuti munthu aikidwe magazi, kapena kupeleka cilolezo cotelo popanda kumvelako maganizo a wodwala, n’kumuphwanyila ufulu munthuyo.

Pambuyo pake, nayonso khoti yaikulu kwambili ku New York inagamula kuti Mlongo Nicoleau ali na ufulu wolandila cithandizo popanda kuikidwa magazi. Mlandu umenewu unali woyamba pa milandu inayi yokhudza kuikidwa magazi imene makhoti akulu-akulu anaweluza. Ndipo ine n’nali na mwayi wothandizilako pokamba milandu imeneyi. (Onani bokosi yakuti “ Milandu Imene Tinapambana ku Makhoti Akulu-Akulu.”) N’nalinso na mwayi woseŵenzela pamodzi na maloya ena a pa Beteli pa milandu yokhudza kusunga ana, kusudzulana, komanso ya malamulo okhudza kuseŵenzetsa malo na nyumba.

CIKWATI KOMANSO UMOYO WA BANJA

Nili na mkazi wanga, Dawn

Pamene n’napezana na mkazi wanga, Dawn, anali atasudzulana na mwamuna wake, ndipo anali kulela ana ake atatu. Iye anali kuyesetsa kupeza zosoŵa za banja lake, kwinaku akucita upainiya. Dawn anakumana na mavuto ambili mu umoyo wake, koma anali na khama potumikila Yehova, moti ine n’nakopeka naye. Mu 1992, tinapezeka pamsonkhano wacigawo wakuti “Onyamula Kuunika,” umene unacitikila mumzinda wa New York. Kumeneko, n’namufunsila kuti tikhale pa cibwenzi. Ndipo caka cotsatila, tinakwatilana. Nimaona kuti kukhala na mkazi wauzimu, wansangala, komanso wacikondi ngati ameneyu ni dalitso locokela kwa Yehova. Mkazi wanga wanipatsa zabwino masiku onse amene takhala limodzi monga banja.—Miy. 31:12.

Pamene tinakwatilana, mwana wamkulu anali na zaka 16, wina 13, ndipo wamng’ono anali na zaka 11. N’nali kufuna kukhala tate wabwino. Conco n’nali kuŵelenga mosamala malangizo alionse amene n’napeza m’zofalitsa zathu othandiza kwa makolo opeza. Ndipo n’nayesetsa kuwagwilitsila nchito. N’zoona kuti tinakumana na mavuto m’kupita kwa zaka. Koma nimakondwela kuti m’kupita kwa nthawi, anawo anayamba kuniona kuti ndine bwenzi lawo lodalilika komanso tate wawo. Mabwenzi a ana athu anali kukhala omasuka kubwela kunyumba kwathu, ndipo tinali kukondwela kukhala limodzi na acinyamata amenewo.

Mu 2013, ine na mkazi wanga tinakukila ku Wisconsin kuti tikasamalile makolo athu okalamba. N’nasangalala kuona kuti olo n’nakuka, utumiki wanga wa pa Beteli sunathe. N’napatsidwa mwayi wopitiliza kuthandiza gulu lathu pa nkhani za malamulo monga mtumiki wodzipeleka kwa kanthawi.

KUSINTHA KWADZIDZIDZI

Mu September 2018, n’naona kuti nikafuna kukamba, n’nali kukonza pammelo kaŵili-kaŵili. A dokotala athu atanipima sanapeze vuto lililonse. Patapita nthawi, a dokotala ena ananiuza kuti nikaonane na katswili wa matenda aubongo. Mu January 2019, dokotala ameneyo ananiuza kuti cioneka kuti nili na matenda enaake amene si ofala, amene m’kupita kwa nthawi adzafooketsa thupi langa lonse.

Patapita masiku atatu, nili mkati mocita maseŵela enaake amene nimakonda kwambili, n’nagwa na kuthyoka dzanja. Nakhala nikucita maseŵela amenewa kuyambila nili mwana, ndipo n’nali na luso kwambili pa maseŵelawa. Conco, pamene n’nagwa, n’nazindikila kuti thupi langa layamba kufooka. N’nadabwa kuona mmene matendawo anakulila. Posapita nthawi, n’nayamba kuvutika kulankhula, kuyenda, na kumeza zinthu.

Nimaona kuti unali mwayi waukulu kuseŵenzetsa luso langa la uloya pothandiza kupititsa patsogolo nchito za Ufumu. Komanso nakhala na mwayi wolemba nkhani zambili m’magazini olembedwela madokotala, maloya, ndiponso oweluza. N’nalinso na mwayi wopita ku maiko osiyana-siyana kukakambilana na maloya komanso madokotala, poteteza ufulu wa anthu a Yehova wosankha kucitidwa opaleshoni kapena kupatsidwa cithandizo ca mankhwala popanda kuikidwa magazi. Ngakhale n’conco, mogwilizana na Luka 17:10, nimaona kuti ‘ndine kapolo wopanda pake. Nangocita zimene n’nayenela kucita.’