Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 29

“Pamene Ndili Wofooka, M’pamene Ndimakhala Wamphamvu”

“Pamene Ndili Wofooka, M’pamene Ndimakhala Wamphamvu”

“Ndimasangalala ndi kufooka, zitonzo, zosowa zanga, mazunzo ndi zovuta zina, cifukwa ca Khristu.”—2 AKOR. 12:10.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi mtumwi Paulo anavomeleza za ciani?

MTUMWI Paulo anavomeleza kuti nthawi zina anali kufooka. Iye anakamba kuti munthu wake wakunja anali ‘kutha.’ Anakambanso kuti anali kuvutika kucita cabwino, komanso kuti nthawi zina Yehova sanali kuyankha mapemphelo ake m’njila imene iye anali kuyembekezela. (2 Akor. 4:16; 12:7-9; Aroma 7:21-23) Cinanso, Paulo anali kudziŵa kuti anthu otsutsa anali kumuona monga wofooka. * Koma iye sanalole zinthu zoipa zimene anthu ena anali kumukambila, kapena zofooka zake kumupangitsa kudziona ngati munthu wosafunika.—2 Akor. 10:10-12, 17, 18.

2. Mogwilizana na 2 Akorinto 12:9, 10, kodi Paulo anaphunzila mfundo yofunika kwambili iti?

2 Paulo anaphunzila mfundo yofunika kwambili yakuti munthu angakhale wolimba olo kuti amadziona ngati wofooka. (Ŵelengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Palembali, Yehova anauza Paulo kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.” Apa Yehova anali kutsimikizila Paulo kuti adzamupatsa mphamvu zimene anali kufunikila. Tsopano, tiyeni tione cifukwa cake sitiyenela kukhumudwa pamene anthu otsutsa akutinyoza.

“NDIMASANGALALA NDI . . . ZITONZO”

3. N’cifukwa ciani n’zotheka kukhalabe osangalala tikamanyozedwa?

3 Palibe amene amakondwela akamanyozedwa. Komabe, ngati tikhumudwa kwambili adani athu akamatinyoza, tikhoza kufooka. (Miy. 24:10) Ndiye kodi tiyenela kumvela bwanji otsutsa akamatinyoza? Monga Paulo, n’zotheka ‘kusangalala ndi . . . zitonzo.’ (2 Akor. 12:10) Cifukwa ciani? Cifukwa kunyozedwa na kutsutsidwa kumaonetsa kuti ndifedi ophunzila a Yesu. (1 Pet. 4:14) Yesu anakamba kuti otsatila ake adzazunzidwa. (Yoh. 15:18-20) Izi n’zimene zinacitikila Akhristu oyambilila. Panthawiyo, anthu otengela cikhalidwe ca Agiriki anali kuona Akhristu ngati anthu osaphunzila komanso otsika. Nawonso Ayuda anali kuona Akhristu ngati “osaphunzila ndiponso anthu wamba,” monga mmene anali kuonela mtumwi Petulo na mtumwi Yohane. (Mac. 4:13) Akhristu anali kuonedwa ngati anthu ofooka cifukwa sanali kutengako mbali m’zandale kapena kuloŵa usilikali, ndipo anthu anali kuwasala.

4. Kodi Akhristu oyambilila anacita ciani pamene anthu anali kuwanenela zoipa?

4 Kodi Akhristu oyambililawo analola kuti zoipa zimene otsutsa anali kuwanenela ziwafooketse? Iyai. Mwacitsanzo, mtumwi Petulo na mtumwi Yohane anaona kuti unali mwayi kuzunzidwa cifukwa cotsatila Yesu, komanso cifukwa couzako ena ziphunzitso zake. (Mac. 4:18-21; 5:27-29, 40-42) Ophunzilawo analibe cifukwa cocitila manyazi. Ngakhale kuti anthu sanali kuwalemekeza Akhristu oyambilila, iwo anacita zambili pothandiza ena kuposa anthu otsutsawo. Mwacitsanzo, mabuku ouzilidwa amene Akhristuwo analemba apitiliza kuthandiza anthu mamiliyoni ambili na kuwapatsa ciyembekezo. Ufumu umene anali kulalikila ukulamulila kumwamba tsopano, moti posacedwa udzalamulila mtundu wonse wa anthu. (Mat. 24:14) Koma ufumu wamphamvu wa Roma, umene unali kuzunza Akhristu panthawiyo unatha, ndipo tsopano ni mbili cabe ya makedzana, pamene ophunzila okhulupilikawo, pano tikamba ni mafumu kumwamba. Cinanso, otsutsawo anafa. Ndipo ngati angadzaukitsidwe, adzakhala nzika za Ufumu wa Mulungu, umene unali kulalikidwa na Akhristu amene iwo anali kuwazonda.—Chiv. 5:10.

5. Malinga na Yohane 15:19 n’cifukwa ciani anthu m’dzikoli salemekeza atumiki a Yehova?

5 Masiku ano, nthawi zina anthu satilemekeza ife Mboni za Yehova, ndipo amatiseka na kutiona monga anthu osaphunzila komanso ofooka. Cifukwa ciani? Cifukwa khalidwe lathu n’losiyana ndi la anthu a m’dzikoli. Ife timayesetsa kukhala odzicepetsa, ofatsa, komanso omvela. Koma anthu masiku ano amakonda kutamanda anthu onyada, odzikuza, komanso opanduka. Cina, popeza kuti sititengako mbali m’zandale ndipo sitiloŵa usilikali, ndife osiyana ndi anthu a m’dzikoli moti amationa ngati otsika.—Ŵelengani Yohane 15:19; Aroma 12:2.

6. Ni nchito yaikulu iti imene Yehova akuthandiza anthu ake kugwila?

6 Ngakhale kuti anthu m’dzikoli amationa monga ofooka, Yehova akutigwilitsila nchito kucita zinthu zazikulu. Iye akutithandiza kugwila nchito yaikulu yolalikila imene sinacitikepo m’mbili yonse ya anthu. Masiku ano, ife atumiki ake timamasulila na kufalitsa magazini m’vitundu vambili padziko lapansi. Komanso timaseŵenzetsa Baibo pothandiza anthu mamiliyoni ambili kukhala na umoyo wabwino. Pa zonsezi, Yehova ndiye ayenela kutamandidwa. Iye akucita zinthu zazikulu poseŵenzetsa ife anthu amene dzikoli limationa ngati ofooka. Koma bwanji za aliyense wa ife payekha? Kodi Yehova angatithandize kukhala amphamvu? Ngati n’conco, n’ciani cimene tingacite kuti atithandize? Tsopano, tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene tingaphunzile pa citsanzo ca mtumwi Paulo.

MUSADALILE MPHAMVU ZANU

7. Fotokozani phunzilo limene titengapo pa citsanzo ca Paulo.

7 Phunzilo limodzi limene titengapo pa citsanzo ca Paulo n’lakuti, sitiyenela kudalila mphamvu kapena maluso athu potumikila Yehova. Mkaonedwe ka umunthu, Paulo anali na zifukwa zokhalila wonyada komanso wodzidalila. Iye anakulila ku Tariso, mzinda waukulu m’cigawo ca Roma ca Kilikiya. Mzinda umenewo unali wolemela komanso wochuka, ndipo kunali kucimake kwa maphunzilo. Paulo anali wophunzila kwambili. Iye anaphunzitsidwa na Gamaliyeli amene anali mmodzi wa atsogoleli aciyuda a m’nthawi yake. (Mac. 5:34; 22:3) Cinanso, panthawi ina Paulo anali munthu wolemekezeka kwambili pakati pa Ayuda anzake. Iye anati: “Ndinali kupita patsogolo kwambili m’Ciyuda kuposa anzanga ambili a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.” (Agal. 1:13, 14; Mac. 26:4) Koma Paulo sanali kudzidalila.

Zinthu zimene anthu a m’dzikoli amaziona kuti n’zofunika kwambili, Paulo anaziona kukhala “mulu wa zinyalala” poziyelekezela na mwayi umene anapeza wokhala wotsatila wa Khristu (Onani ndime 8) *

8. Mogwilizana na Afilipi 3:8, kodi Paulo anali kuziona bwanji zinthu zimene anasiya? Nanga n’cifukwa ciani anali ‘kusangalala ndi kufooka’ kwake?

8 Paulo sanadandaule kusiya zinthu zimene poyamba zinali kum’pangitsa kuoneka ngati wofunika kwambili kwa anthu ena. Ndipo anafika poona zinthu zimenezo ngati “mulu wa zinyalala.” (Ŵelengani Afilipi 3:8.) Paulo anakumana na zovuta zambili cifukwa cokhala wotsatila wa Khristu. Anazondewa ndi anthu a mtundu wake. (Mac. 23:12-14) Ndiponso anamenyedwa na kuikidwa m’ndende na Aroma anzake. (Mac. 16:19-24, 37) Kuwonjezela apo, Paulo anaona kuti cifukwa ca kupanda ungwilo, cinali covuta kwa iye kucita zoyenela, ndipo izi zinali kumuŵaŵa mumtima. (Aroma 7:21-25) Ngakhale n’conco, iye sanalole anthu otsutsa kapena kupanda ungwilo kwake kumufooketsa potsatila Khristu. M’malomwake, anali ‘kusangalala ndi kufooka’ kwake. Cifukwa ciani? Cifukwa pamene anali wofooka, m’pamene anali kuona mphamvu za Yehova zikugwila nchito pa iye.—2 Akor. 4:7; 12:10.

9. Kodi zovuta zimene zimatipangitsa kudziona ngati ofooka tiyenela kuziona bwanji?

9 Kuti Yehova atipatse mphamvu, sitiyenela kukhala na maganizo akuti mphamvu zakuthupi, maphunzilo, kumene tinakulila, kapena cuma, n’zimene zimatipangitsa kukhala anthu ofunika kwa Yehova. Ndipo pakati pa anthu a Mulungu “si ambili amene anthu amawaona kuti ndi anzelu, . . . si ambili amphamvu . . . si ambili a m’mabanja acifumu.” Yehova wasankha kuseŵenzetsa “zinthu zofooka za dziko.” (1 Akor. 1:26, 27) Conco, ngati pali zovuta zina zimene zimakupangitsani kudziona ngati ofooka, musalole kuti zikulefuleni potumikila Yehova. M’malomwake, muziona kuti zinthu zimenezo zimakupatsani mwayi woona mphamvu za Yehova zikugwila nchito pa inu. Mwacitsanzo, ngati mumaopa anthu amene amatsutsa zimene mumakhulupilila, pemphelani kwa Yehova kuti akulimbitseni mtima kuti mukwanitse kufotokoza zimene mumakhulupilila. (Aef. 6:19, 20) Ngati mukuvutika na matenda aakulu, pemphani Yehova kuti akupatseni mphamvu zofunikila kuti mupitilize kucita zilizonse zimene mungathe pom’tumikila. Mukamaona kuti Yehova akukuthandizani, cikhulupililo canu cimapitilizabe kukula ndipo mumakhala wolimba mwauzimu.

TENGELANI CITSANZO CA ANTHU OCHULIDWA M’BAIBO

10. N’cifukwa ciani tiyenela kuphunzila za atumiki okhulupilika akale monga ochulidwa pa Aheberi 11:32-34?

10 Paulo anali kuŵelenga Malemba mwakhama, ndipo anaphunzila zinthu zambili. Iye anaphunzilanso zambili pa zitsanzo za atumiki akale okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Mawu a Mulungu. Polembela Akhristu aciheberi, Paulo anawalimbikitsa kuti aziganizila zitsanzo zabwino za atumiki ambili akale okhulupilika a Yehova. (Ŵelengani Aheberi 11:32-34.) Mwacitsanzo, ganizilani za Mfumu Davide amene ni mmodzi wa atumiki akale amenewo. Iye anapilila citsutso cocokela kwa adani ake komanso kwa anthu amene panthawi ina anali mabwenzi ake. Kuganizila citsanzo ca Davide kuyenela kuti kunam’limbikitsa Paulo. Pamene tikambilana za Davide, tiona mmene Paulo analimbikitsidwila na citsanzo cake. Tionanso zimene tingacite potengela citsanzo ca Paulo.

Davide anali kuoneka monga wopanda mphamvu ndiponso anali wacicepele, koma sanaope kumenyana na Goliyati. Iye anadalila Yehova cifukwa anali kudziŵa kuti adzamupatsa mphamvu zomuthandiza kugonjetsa Goliyati, ndipo anamuthandizadi (Onani Ndime 11)

11. N’cifukwa ciani Davide anali kuoneka ngati wofooka? (Onani cithunzi pacikuto.)

11 Goliyati, amene anali msilikali wamphamvu, anali kuona kuti Davide ni wofooka. Iye ataona Davide, “anayamba kumudelela.” Goliyati anali cimunthu cacikulu, ndipo ananyamula zida zankhondo zoopsa, komanso anali wophunzitsidwa bwino kumenya nkhondo. Mosiyana na Goliyati, Davide anali kuoneka monga wopanda mphamvu cifukwa anali wacicepele, ndipo anali asanaphunzile kumenya nkhondo. Koma m’ceni-ceni, iye anali wolimba. Anadalila mphamvu za Yehova, moti anakwanitsa kugonjetsa mdani wake, Goliyati.—1 Sam. 17:41-45, 50.

12. Ni vuto lina liti limene Davide analimbana nalo?

12 Davide analimbananso na vuto lina limene likanamupangitsa kudziona ngati wofooka komanso wopanda mphamvu. Iye anali kutumikila mokhulupilika mfumu ya Isiraeli imene Yehova anasankha, dzina lake Sauli. Poyamba, Mfumu Sauli anali kumulemekeza Davide. Koma m’kupita kwa nthawi, kunyada kunapangitsa Sauli kuyamba kucitila nsanje Davide. Iye anayamba kucitila Davide zinthu zoipa, cakuti anafika mpaka pofuna kumupha.—1 Sam. 18:6-9, 29; 19:9-11.

13. Kodi Davide anacita ciani pamene Mfumu Sauli anali kumucitila zinthu zopanda cilungamo?

13 Davide anapitiliza kulemekeza Sauli monga mfumu yosankhidwa na Yehova, olo kuti Sauliyo anali kumucitila zinthu zopanda cilungamo. (1 Sam. 24:6) Sanaimbe mlandu Yehova cifukwa ca zoipa zimene Sauli anali kumucitila. M’malomwake, anadalila Yehova kuti amupatse mphamvu zomuthandiza kupilila mavuto amene anali kukumana nawo.—Sal. 18:1, tumawu twa pamwamba.

14. Ni mavuto otani amene Paulo anakumana nawo ofanana na a Davide?

14 Mtumwi Paulo anakumana na mavuto ofanana ndi a Davide. Adani a Paulo anali amphamvu kwambili kuposa iye. Atsogoleli ambili a m’nthawi yake anali kumuzonda. Kaŵili-kaŵili iwo anali kusonkhezela anthu kuti amumenye na kumuponya m’ndende. Mofanana na Davide, Paulo anali kucitilidwa zinthu zoipa ndi anthu amene anafunika kukhala mabwenzi ake. Ena mumpingo anali kumutsutsa. (2 Akor. 12:11; Afil. 3:18) Paulo anagonjetsa onse amene anali kumutsutsa. Motani? Anapitiliza kulalikila ngakhale kuti anthu anali kumutsutsa. Anakhalabe wokhulupilika kwa abale na alongo ake ngakhale pamene anacita zinthu zomukhumudwitsa. Koposa zonse, anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu mu umoyo wake wonse. (2 Tim. 4:8) Paulo anakwanitsa kupilila mavuto onsewa osati mwa mphamvu zake ayi, koma cifukwa codalila Yehova.

Muzikamba mwaulemu komanso mokoma mtima pofotokoza zimene mumakhulupilila kwa anthu otsutsa (Onani ndime 15) *

15. Kodi colinga cathu n’ciani? Nanga tingacikwanilitse bwanji?

15 Kodi mumanyozedwa kapena kuzunzidwa na anzanu a m’kilasi, anzanu a kunchito, kapena abululu anu amene si Mboni? Kodi wina mu mpingo anakucitilamponi zinthu mopanda cilungamo? Ngati n’conco, kumbukilani citsanzo ca Davide na Paulo. Pitilizani “kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.” (Aroma 12:21) Anthu akamatitsutsa, sitimenyana nawo mmene Davide anacitila na Goliyati. M’malomwake, colinga cathu ni kugonjetsa coipa mwa kuthandiza anthu kuphunzila za Yehova na Mawu ake. Timathandiza anthu kuphunzila za Yehova mwa kuseŵenzetsa Baibo poyankha mafunso awo, kucita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima ndi anthu amene amaticitila zoipa, ndiponso mwa kucitila onse zabwino, ngakhale adani athu.—Mat. 5:44; 1 Pet. 3:15-17.

LANDILANI THANDIZO KWA ENA

16-17. Kodi Paulo sanaiŵale ciani?

16 Mtumwi Paulo asanakhale wophunzila wa Khristu, anali mnyamata wacipongwe wozunza otsatila a Yesu. (Mac. 7:58; 1 Tim. 1:13) Yesu iyemwini analamula Paulo, amene anali kudziŵikanso kuti Saulo, kuti aleke kuzunza mpingo wacikhristu. Yesu anakamba na Paulo kucokela kumwamba, ndipo anamucititsa khungu. Kuti ayambenso kuona, iye anacita kupempha thandizo kwa anthu amene anali kuwazunzawo. Modzicepetsa, Paulo analandila thandizo kucokela kwa wophunzila wina wa Yesu dzina lake Hananiya, moti anayambanso kuona.—Mac. 9:3-9, 17, 18.

17 Pambuyo pake, Paulo anakhala m’bale wodziŵika kwambili mumpingo wacikhristu. Koma sanaiŵale zimene Yesu anamuphunzitsa pa njila yopita ku Damasiko. Paulo anakhalabe wodzicepetsa, ndipo anali kulandila thandizo kwa abale na alongo ake. Iye anakamba kuti Akhristu anzake ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’—Akol. 4:10, 11.

18. N’cifukwa ciani nthawi zina cingakhale covuta kulandila thandizo kwa ena?

18 Kodi tingaphunzile ciani kwa Paulo? Pamene tinayamba kugwilizana ndi anthu a Yehova, mwina tinali ofunitsitsa kulandila thandizo kucokela kwa ena, pozindikila kuti mwauzimu, tinali ngati tuŵana tosadziŵa zambili. (1 Akor. 3:1, 2) Koma bwanji panopa? Ngati takhala tikutumikila Yehova kwa zaka zoculuka ndipo tsopano timadziŵa zambili, mwina cingakhale covuta kulandila thandizo kwa Akhristu amene akhala zaka zocepa m’coonadi. Komabe, kumbukilani kuti nthawi zambili, Yehova amaseŵenzetsa abale na alongo potilimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Conco ngati tifuna kuti Yehova atipatse mphamvu, tifunika kukhala okonzeka kulandila thandizo kwa abale na alongo athu.

19. N’ciani cinathandiza Paulo kukhala na umoyo wopambana?

19 Atakhala Mkhristu, Paulo anacita zinthu zambili zotamandika. Cifukwa ciani? Cifukwa anaphunzila kuti ngati munthu afuna kukhala wopambana, sizidalila mphamvu zake, maphunzilo, cuma, kapena kumene amakhala. Cofunika ni kudzicepetsa na kudalila Yehova. Tiyeni tonse titsatile citsanzo ca Paulo mwa (1) kudalila Yehova, (2) kuphunzila pa zitsanzo za atumiki a Mulungu ochulidwa m’Baibo, ndi (3) kuvomela thandizo la Akhristu anzathu. Tikatelo, ndiye kuti olo timadziona ngati ofooka kwambili, Yehova adzatithandiza kukhala amphamvu.

NYIMBO 71 Ndife Asilikali a Yehova!

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilana citsanzo ca mtumwi Paulo. Pokambilana zimenezi, tiona kuti ngati ndife odzicepetsa, Yehova amatipatsa mphamvu zotithandiza kupilila pamene tikunyozedwa. Komanso amatipatsa mphamvu pamene tafooka.

^ ndime 1 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Anthufe tingadzione ngati ofooka pa zifukwa zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, tingadzione ngati ofooka cifukwa ca kupanda ungwilo, kusauka, kudwala, kapena cifukwa cakuti sindife ophunzila kweni-kweni. Kuwonjezela apo, adani athu amafuna kutipangitsa kudziona ngati anthu osafunika mwa kutinyoza kapena kutiukila.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene Paulo anayamba kulalikila za Khristu, anasiya zinthu zimene anali nazo pamene anali Mfarisi. Mwina zinthu zimenezi zinaphatikizapo mipukutu ya maphunzilo ake akudziko, komanso kaphukusi kokhala na malemba.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Anzake a m’bale ku nchito akum’kakamiza kuti acite nawo phwando lokondwelela tsiku la kubadwa la mnzawo wa ku nchito.